Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 68 - Al-Qalam
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Qalam 68:1
“Nûn. Ndikulumbilira cholembera (chimene akulembera angelo), ndi zimene amalemba
Verse 2 — Surah Al-Qalam 68:2
“Pa chisomo cha Mbuye wako iwe sindiwe wamisala (pokupatsa uneneri)
Verse 3 — Surah Al-Qalam 68:3
“Ndipo ndithu udzakhala ndi malipiro akulu osaduka, (onkerankera mtsogolo chifukwa cha mavuto amene ukukumana nawo pofikitsa uthenga)
Verse 4 — Surah Al-Qalam 68:4
“Ndipo ndithu uli nawo makhalidwe abwino kwambiri (omwe Allah adakulenga nawo)
Verse 5 — Surah Al-Qalam 68:5
“Basi, posachedwapa uona, iwonso aona
Verse 6 — Surah Al-Qalam 68:6
“Kuti ndani mwa inu wamisala (iwe kapena iwo)
Verse 7 — Surah Al-Qalam 68:7
“Ndithu Mbuye wako akum’dziwa bwino amene wasokera panjira yake. Ndiponso akuwadziwa bwino amene ali oongoka
Verse 8 — Surah Al-Qalam 68:8
“Choncho, usawamvere otsutsa; (usasiye zimene uli nazo ngakhale sakugwirizana nazo)
Verse 9 — Surah Al-Qalam 68:9
“Akufuna kuti ukadakhala wofewa kwa iwo (pa zinthu zina) nawo akadakhala ofewa (kwa iwe)
Verse 10 — Surah Al-Qalam 68:10
“Ndipo usamumvere aliyense wochulukitsa kulumbira, woyaluka
Verse 11 — Surah Al-Qalam 68:11
“Wojeda, woyenda ndi ukazitape (ndi cholinga choononga umodzi wawo)
Verse 12 — Surah Al-Qalam 68:12
“Wotsekereza zabwino, wamtopola, wamachimo ambiri
Verse 13 — Surah Al-Qalam 68:13
“Wouma mtima; pamwamba pa izi ndi wodzipachika mu mtundu wa ena (pomwe iye sali m’menemo)
Verse 14 — Surah Al-Qalam 68:14
“Chifukwa choti iye ndi mwini chuma ndi ana (ndi zimene ali kunyadira)
Verse 15 — Surah Al-Qalam 68:15
“Zikawerengedwa kwa iye Ayah Zathu amanena: “Izi ndi nthano za akale (ndi zabodza zawo, zopeka).”
Verse 16 — Surah Al-Qalam 68:16
“Timuika pamphuno pake chizindikiro (chosasiyana nacho kuti ayaluke nacho pamaso pa anthu)
Verse 17 — Surah Al-Qalam 68:17
“Ndithu ife tidawayesa (eni mzinda wa Makka ndi mtendere omwe udali pa iwo, koma adakana monga) momwe tidawayesera eni munda, pamene adalumbira kuti akathyola (zipatso za m’munda wawozo) mbandakucha (kuti osauka asawaone angawapemphe)
Verse 18 — Surah Al-Qalam 68:18
“Ndipo sadapatule (ngakhale wosauka ndi m’modzi yemwe ponena kuti uje timpatse, uje tisampatse, kapena sadanene kuti: “Ngati Allah afuna).”
Verse 19 — Surah Al-Qalam 68:19
“Mliri woopsa wochokera kwa Mbuye wako udauzinga (mundawo nthawi yausiku) iwo ali mtulo
Verse 20 — Surah Al-Qalam 68:20
“Choncho udakhala ngati wokololedwa (chifukwa cha mliri uja)
Verse 21 — Surah Al-Qalam 68:21
“Tero adaitanizana nthawi ya mbandakucha
Verse 22 — Surah Al-Qalam 68:22
““Lawilirani kumunda wanu kuja ngati mukufuna kukolola (kuopera kuti angakuoneni osauka).”
Verse 23 — Surah Al-Qalam 68:23
“Adanyamuka uku akunong’ onezana
Verse 24 — Surah Al-Qalam 68:24
“(Akunena kuti): “Asakulowelereni wosauka lero mmenemo.”
Verse 25 — Surah Al-Qalam 68:25
“Ndipo adalawilira ali ndi chitsimikizo choti atha kuwamana (osauka)
Verse 26 — Surah Al-Qalam 68:26
“Choncho pamene adauona, adanena (uku akunjenjemera): “Ndithu ife tasokera (sikuno ayi, munda wathu uja siuno).”
Verse 27 — Surah Al-Qalam 68:27
““Iyayi, ndiwomwewu; koma tamanidwa zinthu zake.”
Verse 28 — Surah Al-Qalam 68:28
“Wolungama mwa iwo adanena: “Kodi sindinakuuzeni (pamene mudali kulangizana zomana osowa) kuti bwanji osamkumbukira Allah (ndi kusintha cholinga chanu)?”
Verse 29 — Surah Al-Qalam 68:29
“(Iwo) adanena: “Alemekezeke Mbuye wathu ndithu ife tidali achinyengo (chifukwa cha kuipa kwa cholinga chathu).”
Verse 30 — Surah Al-Qalam 68:30
“Ndipo adatembenukirana ndikuyamba kudzudzulana
Verse 31 — Surah Al-Qalam 68:31
“Adati: “E chionongeko chathu! Ndithu Ife tidapyola malire (m’chinyengo chathu).”
Verse 32 — Surah Al-Qalam 68:32
““Mwina Mbuye wathu angatipatse zabwino m’malo mwa munda wathuwu. Ndithu ife tikufunitsitsa kwa Mbuye wathu (chikhululuko Chake).”
Verse 33 — Surah Al-Qalam 68:33
“Umo ndi mmene chimakhalira chilango (Changa chomwe ndimachitsitsa pa dziko lapansi kwa amene chamuyenera); koma chilango cha tsiku lachimaliziro nchachikulu zedi, akadakhala akudziwa
Verse 34 — Surah Al-Qalam 68:34
“Ndithu oopa Allah adzakhala ndi Minda ya mtendere kwa Mbuye wawo
Verse 35 — Surah Al-Qalam 68:35
“Kodi tiwachite Asilamu monga ochimwa
Verse 36 — Surah Al-Qalam 68:36
“Kodi nchiyani chakupezani! Nanga mukuweruza bwanji (maweruzo opanda chilungamo)
Verse 37 — Surah Al-Qalam 68:37
“Kapena muli ndi buku limene mukuwerenga
Verse 38 — Surah Al-Qalam 68:38
“Kuti ndithu mulinazo mmenemo zomwe mukudzisankhira
Verse 39 — Surah Al-Qalam 68:39
“Kapena muli nawo mapangano ndi Ife okafika mpaka tsiku lachimaliziro akuti inu mudzapeza zimene mukudziweruzira
Verse 40 — Surah Al-Qalam 68:40
“Afunse (iwe Mtumiki) ndani mwa iwo amene ali mtsogoleri (pa malamulo amenewa)
Verse 41 — Surah Al-Qalam 68:41
“Kapena iwo ali nawo othandidzana nawo (pa mau awa)? Chomwecho atabweretsa othandizana nawo ngati akunena zowona
Verse 42 — Surah Al-Qalam 68:42
“(Akumbukire) tsiku la mavuto okhwima, ndipo adzaitanidwa (akafiri) kuti achite sijida (polambira Allah) koma sadzatha
Verse 43 — Surah Al-Qalam 68:43
“Maso awo adzangoti pansi zyoli, manyazi ndi kunyozeka kudzawaphimba; chikhalirecho adali kuitanidwa (pa dziko lapansi) kuti agwetse nkhope pansi pomwe iwo adali ndi moyo wa ngwiro (koma ankakana)
Verse 44 — Surah Al-Qalam 68:44
“Choncho ndisiye, (iwe Mtumiki), ndi amene akukanira nkhani iyi tiwakokera kuchilango pang’onopang’ono pamene iwo sakudziwa (mmene chiti chiwadzere chilangochi)
Verse 45 — Surah Al-Qalam 68:45
“Ndipo ndikuwalekelera (pochedwetsa chilango); ndithudi makonzedwe Anga ngokhwima, (palibe angapulumuke mmenemo)
Verse 46 — Surah Al-Qalam 68:46
“Kapena ukuwapempha malipiro (pofikitsa uthenga) kotero kuti iwo akulemedwa ndi kulipira
Verse 47 — Surah Al-Qalam 68:47
“Kapena ali nazo (nzeru) zobisika kotero kuti iwo akulemba (zimene akuweruzazo)
Verse 48 — Surah Al-Qalam 68:48
“Choncho pirira ndi lamulo la Mbuye wako (chifukwa chowalekelera ndi kuchedwetsa chipulumutso chako); ndipo usakhale ngati mwini nsomba (Yunusu pa changu ndi mkwiyo kwa anthu ake) pamene adaitana (Mbuye wake) uku ali wodzazidwa ndi mkwiyo (kupempha kuti chidze mwachangu chilango kwa anthu ake)
Verse 49 — Surah Al-Qalam 68:49
“Chikadapanda kumfikira chisomo chochokera kwa Mbuye wake (ndi kuvomera kulapa kwake), akadaponyedwa (kuchokera m’mimba mwa chinsomba chija) pagombe (popanda kanthu) ali wodzudzulidwa
Verse 50 — Surah Al-Qalam 68:50
“Koma adamsankha Mbuye wake (povomera kulapa kwake) ndipo adamchita kukhala mmodzi wa anthu abwino
Verse 51 — Surah Al-Qalam 68:51
“Ndithudi anthu amene sadakhulupirire adayandikira kukuteleretsa ndi kunyogodola kwa maso awo (chifukwa chachidani ndi mkwiyo) pamene adamva chikumbutso (Qur’an), ndipo akunena kuti iyeyo ngwamisala
Verse 52 — Surah Al-Qalam 68:52
“Ndipo ichi sichina, koma (ndi phunziro, ndi nzeru) ndi chikumbutso kwa zolengedwa zonse