“(Allah) adati: “Nchiyani chakuletsa kumgwadira pamene ndakulamula?” (Satana) anati: “Ine ndine wabwino kuposa iye. Ine munandilenga ndi moto koma iye mudamulenga ndi dongo.”
“Iye (chifukwa cha njiru yake yoopsa pa Adam) adati: “Tsono chifukwa chakuti mwandichita ine kukhala wopotoka, ndidzawakhalira (akapolo Anu ndi kuwabisalira) pa njira Yanu yoongoka (ndi cholinga chowasokeretsa).”
“(Allah) adati: “Tuluka m’menemo, uli wonyozeka ndi wothamangitsidwa. Amene adzakutsata iwe mwa iwo, ndithudi, (ndikamponya ku Moto). Ndipo ndikaidzadzitsa Jahannam ndi inu nonse.”
“(Kenako Allah adanena kwa Adam) “E iwe Adam! Khala ndi mkazi wako m’Munda wamtendere (sangalalani ndi zomwe zili m’menemo), idyani paliponse pamene mwafuna. Koma mtego uwu musawuyandikire kuopera kuti mungakhale m’gulu la odzichitira okha zoipa.”
“E inu ana a Adam! Ndithu tatsitsa kwa inu chovala chobisa umaliseche wanu ndi chodzikongoletsera nacho. Koma chovala choopa nacho Allah (pakudziyeretsa ku zoletsedwa) chimenecho ndicho chabwino koposa. Zimenezo ndi zizindikiro za (chisomo cha) Allah kuti iwo akumbukire
“E inu ana a Adam! Satana asakusokonezeni monga momwe adawatulutsira makolo anu m’Munda wamtendere ndi kuwavula onse awiri chovala chawo kuti awasonyeze umaliseche wawo. Ndithu iye ndi mtundu wake akukuonani pomwe inu simukuwaona. Ndithu asatana tawachita kukhala abwenzi a osakhulupirira
“E inu ana a Adam! Tengani (valani) zovala zanu zabwino pamene mukukapemphera Swala iliyonse ndipo idyani ndi kumwa; koma musapyoze muyeso. Iye (Allah) sakonda opyoza muyeso (oononga)
“Nena: “Ndani waletsa zokongoletsa za Allah (zovala), zomwe Iye (Allah) adawatulutsira akapolo Ake ndi zakudya zabwino?” Nena: “Zinthu zimenezo nzololedwa kwa amene akhulupirira (Asilamu) pamoyo wa pa dziko lapansi. (Zidzakhala) zawozawo tsiku la chimaliziro. M’menemo ndi momwe tikulongosolera Ayah (Zathu) kwa anthu ozindikira.”
“Nena (kwa iwo): “Ndithu Mbuye wanga waletsa zinthu zauve zoonekera ndi zobisika, ndi machimo, ndi kuwukira (atsogoleri) popanda choonadi, ndi kumphatikiza Allah ndi chomwe sadachitsitsire umboni (wakuti chiphatikizidwe ndi Iye); ndiponso (waletsa) kumunenera Allah zimene simukuzidziwa.”
“E inu ana a Adam! Akakudzerani Atumiki ochokera mwa inu namakuuzani zivumbulutso Zanga, (avomereni), choncho omwe adzitchinjiriza ku zoletsedwa ndi kuchita zabwino, sipadzakhala mantha pa iwo ndiponso sadzadandaula
“(Allah) adzati (pa tsiku la chiweruziro): “Lowani ku Moto pamodzi ndi mibadwo imene idamuka kale (inu musanabwere) yochokera m’ziwanda ndi mu anthu. M’badwo uliwonse pamene uzikalowa, udzatembelera unzake, kufikira pamene onse adzasonkhana m’menemo. Adzanena apambuyo kwa oyambilira awo: “Mbuye wathu! Awa, adatisokeretsa. Apatseni chilango cha Moto chochuluka.” (Allah) adzanena: “Aliyense mwa inu akhala ndi chilango chochuluka; koma izi inu simukudziwa.”
““Omwe ankaletsa anthu kuyenda pa njira ya Allah nafuna kuikhotetsa njirayo (kuti ioneke yokhota pamaso pa anthu), omwenso sadakhulupirire za tsiku lachimaliziro.”
“Ndipo pakati pawo (pa anthu a ku Munda wamtendere ndi a ku Moto) padzakhala chotchinga. Ndipo pamwamba pachikweza padzakhala anthu ena (ofanana ntchito zawo zabwino ndi zoyipa) omwe akazindikira onse (a ku Jannah ndi ku Moto), ndi zizindikiro zawo. Ndipo akawaitana anthu a ku Jannah (kuti): “Salaamun Alayikum (mtendere ukhale pa inu).” Koma asanailowe uku ali ndi chikhulupiliro (kuti ailowa)
“Ndipo maso awo akakatembenuzidwa (kuyang’ana) ku mbali ya anthu a ku Moto, adzanena: “Mbuye wathu musatiike pamodzi ndi anthu ochita zoipa. (Tikhululukireni zolakwa zathu. Tilowetseni ku Jannah).”
“Naonso anthu a ku Moto adzaitana a ku Jannah (ndikuwauza kuti): “Tatipungulirani madzi kapena chinthu chimene Allah wakupatsani.” (Anthu a ku Jannah) adzanena kuti:“Ndithu Allah waletsa kupereka zonse ziwirizo kwa osakhulupirira.”
“Ndithudi, Mbuye wanu ndi Allah Yemwe adalenga thambo ndi nthaka m’masiku asanu ndi limodzi. Kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu). Amauchita usiku kuti uvindikire usana, zimatsatana mwamsangamsanga. Ndipo dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi nzofewetsedwa, (zikuyenda mogonjera) ndi Lamulo Lake. Dziwani kuti kulenga ndi kulamula Nkwake. Ndithudi, watukuka Allah Mbuye Wazolengedwa (zonse)
“Ndipo musaononge pa dziko pambuyo popakonza. Mpempheni (Allah) mwamantha ndi mwakhumbo. Ndithu chifundo cha Allah chili pafupi kwa (anthu Ake ) ochita zabwino
“Ndipo m’nthaka yabwino umatuluka mmera wake (mwachangu) mwachilolezo cha Mbuye wake. Ndipo nthaka yomwe ili yoipa siitulutsa (mmera wake) koma movutikira. M’menemo ndi momwe Tikuchifotokozera chivumbulutso momveka kwa anthu oyamika
““Kodi mukudabwa kukudzerani ulaliki wochokera kwa Mbuye wanu kudzera mwa munthu wa mwa inu, (yemwe wadza) kuti akuchenjezeni ndi kuti muope (Allah), ndikutinso muchitiridwe chifundo?”
“Akuluakulu a mwa anthu ake omwe sadakhulupirire adanena: “Ife tili kukuona kuti uli mu uchidzete, ndipo ife tikukuganizira kuti ndiwe m’modzi wa a bodza.”
““Kodi mukudabwa pokudzerani ulaliki kuchokera kwa Mbuye wanu kupyolera mwa munthu wochokera mwa inu kuti akuchenjezeni? Kumbukirani (mtendere wa Allah) pamene adakuikani kukhala amlowam’malo pambuyo pa anthu a Nuh, ndipo akuonjezerani m’kalengedwe kukhala a misinkhu itali-itali ndi amphamvu. Kumbukiraninso mtendere wa Allah (pothokoza) kuti mupambane.”
“(Iye) adati: “Palibe chikaiko, chilango ndi mkwiyo wochokera kwa Mbuye wanu zakugwerani. Kodi mukukangana nane pa za maina (a mafano) omwe mudawatcha inu ndi makolo anu, pomwe Allah sadatsitse umboni uliwonse pa milungu yanu yabodzayo? Choncho, dikirani. Inenso ndili pamodzi nanu mwa odikira.”
“Ndipo kwa Asamudu tidamtumiza m’bale wawo Swaleh. Adati: “E inu anthu anga! Gwadirani Allah; inu mulibe mulungu wina koma Iye basi. Chizindikiro chochokera kwa Mbuye wanu chadza kwa inu. Iyi ndi ngamira ya Allah monga chisonyezo chanu (chizizwa chanu), choncho, isiyeni izidya m’dziko la Allah, ndipo musaikhudze ndi choipa kuopera kuti chingakugwereni chilango chowawa kwambiri.”
““Ndipo kumbukirani pamene (Allah) adakupangani kukhala amlowammalo pambuyo pa mtundu wa Âdi. Ndipo adakukhazikani pa dziko (mwa ubwino). Mukudzimangira nyumba zikuluzikulu mchigwa, ndiponso kusema ndi kuboola mapiri kukhala nyumba. Choncho kumbukirani mtendere wa Allah, ndipo musaononge pa dziko pofalitsa chisokonezo.”
“Kuyankha kwa anthu ake sikudali kwa mtundu wina koma kuti: “Apirikitseni m’mudzi wanu. Ndithu iwowo ndi anthu odziyeretsa. (Choncho akhaliranji m’mudzi wa uve? Akakhale ndi anzawo ochita zaukhondo).”
““Ndipo musamawakhalire anthu pa njira iliyonse mowabisalira ndi kumawaopseza, ndi kuwatsekereza kuyenda pa njira ya Allah amene amkhulupirira Iye, ndi kufuna kuikhotetsa njirayo (kuti anthu asaitsate). Ndipo kumbukirani pamene mudali ochepa nakuchulukitsani. Ndipo onani momwe adalili mapeto a owononga.”
““Ndipo ngati pali gulu la anthu mwa inu amene akhulupirira uthenga umene ndatumidwa nawo, ndi gulu la anthu limene silidakhulupirire, pirirani mpaka Allah aweruze pakati pathu. Iye Ngwabwino poweruza kuposa oweruza.”
“Ndipo palibe pamene tidamtuma mneneri aliyense m’mudzi uliwonse (nkumukana) koma tinkawalanga eni mudziwo ndi masautso ndi mavuto kuti afatse (ndi kulambira Allah; koma ayi adakanika)
“Iyo ndi midzi (ikuluikulu) yomwe tikukusimbira iwe zina mwa nkhani zake. Ndithudi, adawadzera atumiki awo ndi zizindikiro (zoonekera poyera zosonyeza kuti iwo ndi atumiki a Allah). Koma sadali oti nkukhulupirira pa zomwe adazitsutsapo kale. Umo ndi mmene Allah amadindira ndi kuitseka mitima ya osakhulupirira (kotero kuti sangathandizike ndi malangizo a mtundu uliwonse)
““Ndikofunika kwa ine kuti ndisamnenere Allah chilichonse koma choonadi basi. Ndithu ndakudzerani ndi chizindikiro choonekera kuchokera kwa Mbuye wanu. Choncho, aleke ndinke nawo ana a Israyeli.”
“Farawo adati: “Mwamkhulupirira chotani iye ndisanakupatseni chilolezo? Ndithu iyi ndi ndale yomwe mwaichita mu mzindamu (inu ndi Mûsa) kuti muwatulutsemo eni mzindawo. Koma posachedwa mudziwa (chimene ndikuchiteni).”
““Ndithudi, nditseteka manja anu ndi miyendo yanu mosinthanitsa; (kudula dzanja lakudzanjadzanja ndi mwendo wa kumanzere, kapena dzanja la kumanzere ndi mwendo wakudzanjadzanja). Kenako ndikupachikani nonsenu.”
“Ndipo nduna za mwa anthu a Farawo zidati (kwa Farawo): “Kodi umuleka Mûsa ndi anthu ake kuti abwere ndi chisokonezo m’dziko, ndi kuti akusiye iwe ndi milungu yako (yomwe adatilangiza makolo athu kuti tipembedze pamodzi ndi iwe)? (Farawo) Adati: “Tipha ana awo achimuna ndikuwasiya amoyo (ana awo) achikazi. Ndithudi ife pa iwo tili ndi mphamvu zowagonjetsera.”
“Mûsa adauza anthu ake: “Pemphani chithandizo kwa Allah, ndipo pirirani. Ndithu dzikoli ndi la Allah; amalipereka kwa amene wamfuna mwa akapolo Ake. Ndipo mapeto abwino nga anthu olungama.”
“Ndipo anthu omwe adali kuponderezedwa tidawachita kukhala amlowammalo a kuvuma kwa dziko ndi kuzambwe kwake, lomwe tidaikamo madalitso (ambiri). Ndipo mawu abwino a Mbuye wako adakwaniritsidwa kwa ana a Israyeli chifukwa cha kupirira kwawo (pa zomwe adakumana nazo). Ndipo tidazigumula ndi kuziononga zomwe Farawo ndi anthu ake ankapanga ndi zomwe ankamanga
“Ndipo kumbukirani pamene tidakupulumutsani (m’manja) mwa anthu a Farawo omwe adali kukuzunzani ndi chilango choyipa ndipo anali kupha ana anu aamuna ndi kusiya ana anu aakazi. Pa ichi padali mayeso aakulu ochokera kwa Mbuye wanu
“(Allah) adati: “E iwe Mûsa! Ndithu Ine ndakusankha iwe mwa anthu onse, (kukusankhira) uthenga Wanga ndi kuyankhulana Nane. Choncho landira chimene ndakupatsa, ndipo khala m’modzi wa anthu othokoza.”
“Ndithu omwe adapanga (fano la ) Thole uwafika mkwiyo wa Mbuye wawo ndi kunyozeka pa moyo wa dziko lapansi. M’menemo ndi momwe timawalipirira anthu opeka (zinthu za chipembedzo)
““Omwe akutsata Mtumiki, mneneri wosatha kuwerenga ndi kulemba (ngakhale ali choncho, akuphunzitsa zophunzitsa zodabwitsa); yemwe akumpeza atalembedwa kwa iwo m’buku la Taurat ndi Injili. Akuwalamula zabwino ndi kuwaletsa zoipa, ndi kuwaloleza zabwino ndi kuwaletsa zodetsedwa (zoipa); ndi kuwatula mitolo yawo ndi magoli omwe adali pa iwo (malamulo ovuta kuwatsata). Choncho, amene amkhulupirira (Muhammad {s.a.w}) ndi kumamlemekeza ndi kumuthangata, natsata kuunika (Quran) komwe kudavumbulutsidwa pamodzi ndi iye, iwo ndiwo opambana.”
“Nena: “E inu anthu! Ndithu ine ndine Mtumiki wa Allah kwa inu nonse. (Allah) Yemwe ali nawo ufumu wa kumwamba ndi pansi. Palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye. Amapatsa moyo ndi imfa. Choncho, khulupirirani mwa Allah ndi Mtumiki Wake yemwe ndi Mneneri wosadziwa kulemba ndi kuwerenga, yemwe akukhulupirira Allah ndi mawu Ake. Ndipo mtsatireni kuti muongoke.”
“Ndipo tidawalekanitsa pakati pawo (Ayuda), ndi kuwabalalitsa pa dziko lonse kukhala mafuko osiyanasiyana. Ena mwa iwo abwino (olungama) ndipo ena sali choncho (oipa). Tinawayesa mayeso a zabwino ndi zoipa kuti abwelere (koma ayi, sanabwelere)
“Choncho, anawatsatira pambuyo (anthu abwinowo), otsatira atsopano omwe analandira buku (la Allah nalowa mmalo mwa iwo koma popanda kulitsata ndi kulilingalira). Ankatenga zinthu zoletsedwa za pa dziko lapansi uku akunena: “Tidzakhululukidwa, (Allah adzatikhululukira).” Ngati zina zonga izo zitawapeza, amazitenganso. Kodi silidatengedwe pangano kwa iwo la m’buku kuti sadzamunenera Allah bodza koma zoona zokhazokha? (Nanga akuneneranji kuti Allah adzawakhululukira pomwe akupitiriza machimo)? Pomwe iwo aphunzira zomwe zili mmenemo. Komatu nyumba ya chimaliziro idzawakhalira bwino amene akuopa (Allah). Nanga bwanji simukuzindikira
“Ndipo amene akugwirisitsa buku (la Allah potsata zophunzitsa zake) ndi kumapemphera Swala, (tidzawalipira zabwino). Ndithu Ife sitipititsa pachabe malipiro a ochita zabwino
“Ndithudi, ziwanda zambiri ndi anthu tidawalengera kukalowa ku (Moto wa) Jahannam. Mitima ali nayo koma sazindikira nayo kanthu; ndipo maso ali nawo koma sapenyera nawo (zodabwitsa za Allah); ndipo makutu ali nawo koma samvera nawo (zowapindulitsa). Iwo ali ngati ziweto, kapena iwo ndi osokera zedi kuposa Ziweto. Iwo ndi osalabadira
“Kodi saona ufumu wa kumwamba ndi pansi, ndi zinthu zomwe Allah adalenga? Mwina mwake nthawi yawo yofera yayandikira. (Nanga adzalingalira liti zolengedwa za Allah)? Kodi ndi nkhani iti pambuyo pa iyi (Qur’an) imene adzaikhulupirira
“Akukufunsa za nthawi (ya Qiyâma) kuti idzakhalako liti? Nena: “Kudziwika kwa nthawi yake kuli kwa Mbuye wanga. palibe amene angaionetse poyera nthawi yake koma Iye. Nkovuta kwambiri kumwamba ndi pansi (kuizindikira nthawi yake). Siidzakudzerani koma mwadzidzidzi.” Akukufunsa ngati kuti iwe ukudziwa bwino za nthawiyo. Nena: “Kudziwika kwa nthawi yake kuli kwa Allah. Koma anthu ambiri sadziwa.”
“Choncho, pamene adawapatsa mwana wabwino (yemwe adapempha) adamchitira Allah anzake (mafano) pa chimene adawapatsacho. Koma Allah watukuka kuzimene akumphatikiza nazozo
“Ngati siudawabweretsere chozizwitsa, akunena: “Bwanji wosachibweretsa pa iwe wekha? Nena: “Ndithudi ndikutsatira zimene zikuvumbulitsidwa kwa ine kuchokera kwa Mbuye wanga. (Sindichita chinthu mwa ine ndekha). Iyi (Qur’an) ndi umboni (waukulu pa zoyankhula zanga) kuchokera kwa Mbuye wanu. (Izo) ndi chiongoko ndi chifundo kwa anthu okhulupirira.”
“Ndipo mtchule Mbuye wako mu mtima mwako modzichepetsa, mwa mantha ndi mosakweza mawu m’mawa ndi madzulo; ndipo usakhale mwa osalabadila (malamulo a Allah)