Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 70 - Al-Maarij
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Maarij 70:1
“Wopempha adapempha kuti chiwadzere msanga chilango chopezekacho, (m’kupempha kwa chipongwe ndi kotsutsa)
Verse 2 — Surah Al-Maarij 70:2
“Kwa okanira palibe angachitsekereze
Verse 3 — Surah Al-Maarij 70:3
“Chochokera kwa Allah Mwini makwelero
Verse 4 — Surah Al-Maarij 70:4
“Angelo ndi Jiburil amakwera kwa Iye (Allah) m’tsiku lomwe kutalika kwake kuli ngati zaka zikwi makumi asanu
Verse 5 — Surah Al-Maarij 70:5
“Choncho, pirira (iwe Mtumiki (s.a.w) kupirira kwabwino
Verse 6 — Surah Al-Maarij 70:6
“Ndithu iwo akuliona (tsiku la Qiyâma) kuti lili kutali (silingachitike)
Verse 7 — Surah Al-Maarij 70:7
“Koma Ife tikuliona kuti lilipafupi (ndilochitika)
Verse 8 — Surah Al-Maarij 70:8
“Tsiku limene thambo lidzakhala ngati mtovu wosungunuka
Verse 9 — Surah Al-Maarij 70:9
“Ndipo mapiri adzakhala ngati ubweya (wongouluka wokha)
Verse 10 — Surah Al-Maarij 70:10
“Ndipo m’bale sadzafunsa za m’bale wake
Verse 11 — Surah Al-Maarij 70:11
“Ngakhale adzawalole kuti aonane ndi kudziwana pakati pawo (sadzafunsana). Wochimwa adzalakalaka kuti akadaziwombola ku chilango cha tsiku limenelo ndi ana ake
Verse 12 — Surah Al-Maarij 70:12
“Ndi mkazi wake, ndi m’bale wake
Verse 13 — Surah Al-Maarij 70:13
“Ndi akumtundu wake amene amamsunga
Verse 14 — Surah Al-Maarij 70:14
“Ndi (kulipira) zonse za m’dziko, kuti zimpulumutse
Verse 15 — Surah Al-Maarij 70:15
“Iyayi, (siya iwe wamachimo zimene ukulakalakazo)! Ndithu umenewu ndi Moto wa malawi
Verse 16 — Surah Al-Maarij 70:16
“Wosupula mwamphamvu khungu
Verse 17 — Surah Al-Maarij 70:17
“Udzaitana (potchula dzina la aliyense) amene adachitembenuzira msana choona ndi kunyoza
Verse 18 — Surah Al-Maarij 70:18
“Adasonkhanitsa (chuma) ndi kusunga (m’nkhokwe zake popanda kuperekera chopereka cha Allah)
Verse 19 — Surah Al-Maarij 70:19
“Ndithu munthu walengedwa kukhala wosapirira
Verse 20 — Surah Al-Maarij 70:20
“Mavuto akamkhudza amada nkhawa
Verse 21 — Surah Al-Maarij 70:21
“Koma zabwino zikamkhudza amamana (ena ndi kuiwala mavuto amene adali nawo)
Verse 22 — Surah Al-Maarij 70:22
“Kupatula opemphera Swala, (iwo alibe mbiri zoipazi)
Verse 23 — Surah Al-Maarij 70:23
“Iwo amene sadukiza mapemphero awo a swala; (sakuwaleka ngakhale zivute chotani)
Verse 24 — Surah Al-Maarij 70:24
“Ndi amene mchuma chawo muli gawo lodziwika (Zakaat)
Verse 25 — Surah Al-Maarij 70:25
“La wopempha ndi wosapempha
Verse 26 — Surah Al-Maarij 70:26
“Ndi amene akuvomereza za tsiku la malipiro (ndi kumalikonzekera)
Verse 27 — Surah Al-Maarij 70:27
“Ndi iwo amene akuopa chilango chochokera kwa Mbuye wawo
Verse 28 — Surah Al-Maarij 70:28
“Ndithu chilango cha Mbuye wawo nchosapulumuka nacho (munthu woipa)
Verse 29 — Surah Al-Maarij 70:29
“Ndiponso iwo amene akusunga umaliseche wawo (posachita chiwerewere)
Verse 30 — Surah Al-Maarij 70:30
“Kupatula kwa akazi awo ndi amene manja awo akumanja apeza; ndithu pazimenezo iwo sangadzudzulidwe
Verse 31 — Surah Al-Maarij 70:31
“Koma amene angafune (zina) kusiya zimenezi iwowo ndiwo olumpha malire
Verse 32 — Surah Al-Maarij 70:32
“Ndi iwo amene amasunga mwaubwino zimene amasungitsidwa ndi zimene alonjeza
Verse 33 — Surah Al-Maarij 70:33
“Ndi iwo amene amaima molungama popereka umboni wawo
Verse 34 — Surah Al-Maarij 70:34
“Ndiponso iwo amene amasunga (mwaubwino) mapemphero awo a swala
Verse 35 — Surah Al-Maarij 70:35
“Amene ali ndi mbiri zimenezi adzakhala m’Minda (yamtendere) ali olemekezedwa
Verse 36 — Surah Al-Maarij 70:36
“Kodi kuli chiyani kwa amene akana (chikhulupiliro) akuthamangira kwa iwe (maso ali pamtunda)
Verse 37 — Surah Al-Maarij 70:37
“Atakuzungulira ena chakumanja ena chakumanzere
Verse 38 — Surah Al-Maarij 70:38
“Kodi akulakalaka aliyense mwa iwo kuti akalowetsedwe ku Munda wamtendere
Verse 39 — Surah Al-Maarij 70:39
“Asiye (kukhumba kwawo kokalowa ku Munda wamtendere)! Ndithu Ife tidawalenga kuchokera m’zimene akudziwa (madzi opanda pake)
Verse 40 — Surah Al-Maarij 70:40
“Ndikulumbilira Mbuye wa kuvuma ndi kuzambwe konse ndithu Ndife Wokhoza
Verse 41 — Surah Al-Maarij 70:41
“Kuwasintha ndi kudzetsa abwino kuposa iwo; Ife palibe (chilichonse) chotipambana
Verse 42 — Surah Al-Maarij 70:42
“Asiye azingolankhula zopanda pake ndi kumangosewera mpaka adzakumane ndi tsiku lawo limene akulonjezedwa
Verse 43 — Surah Al-Maarij 70:43
“Tsiku limene adzatuluke m’manda uku akuthamanga (kudza kwa woitana) ngati kuti akuthamangira kumafano awo (amene adali kuwapembedza)
Verse 44 — Surah Al-Maarij 70:44
“Maso awo ali zyoli, (osatha kuwakweza); kuyaluka kutawaphimba! Limenelo ndilo tsiku lomwe adali kulonjezedwa (pomwe adali padziko lapansi)