Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 71 - Nuh
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Nuh 71:1
“Ndithu Ife tidamtuma Nuh kwa anthu ake, (ndikumuuza kuti): “Chenjeza anthu ako chisadawafike chilango chowawa.”
Verse 2 — Surah Nuh 71:2
“Adanena (Nuh): “E inu anthu anga! Ndithu ine ndimchenjezi kwa inu woonekera poyera (wolongosola za uthenga wa Mbuye wanu m’chiyankhulo chimene mukuchidziwa).”
Verse 3 — Surah Nuh 71:3
““Mpembedzeni Allah ndipo rnuopeni ndikutinso mundimvere (pazimene ndikukulangizani).”
Verse 4 — Surah Nuh 71:4
““(Ngati mutero) adzakukhululukirani machimo anu ndi kukutalikitsirani moyo wanu kufikira m’nthawi imene yaikidwa (kuti ndiwo malire a kutalika kwa moyo). Ndithu nthawi ya Allah ikabwera siyichedwetsedwa (ngakhale pang’ono) mukadakhala mukudziwa.”
Verse 5 — Surah Nuh 71:5
“Adanena (Nuh): “E Mbuye wanga! Ndithu ine ndaitanira anthu anga (ku chikhulupiliro) usiku ndi usana (popanda kufooka).”
Verse 6 — Surah Nuh 71:6
““Kuitana kwanga sikudaonjezere (chilichonse) koma kuthawa basi (kuchikhulupiliro Chanu).”
Verse 7 — Surah Nuh 71:7
“Ndipo ine nthawi iliyonse ndikawaitanira (ku chikhulupiliro Chanu) kuti mwakhululukire, akuika zala zawo m’makutu mwawo (kuti asamve uthenga Wanu), ndipo akudziphimba ndi nsalu zawo (kuti asaone nkhope yanga), ndipo akupitiriza kukana kwawo ndi kudzikweza kwakukulu
Verse 8 — Surah Nuh 71:8
“Kenaka ine ndawaitanira (kwa Inu) ndi mawu ofuula
Verse 9 — Surah Nuh 71:9
“Kenakanso (ine ndawaitanira) molengeza poyera ndiponso mwachinsinsi mobisa
Verse 10 — Surah Nuh 71:10
“Choncho ndidati (kwa anthu anga): Pemphani kwa Mbuye wanu chikhululuko (pa kukana kwanu ndi kutonza kwanu), ndithu Iye ali Wokhululuka kwambiri
Verse 11 — Surah Nuh 71:11
“Akutumizirani mvula yotsika mochuluka
Verse 12 — Surah Nuh 71:12
“Ndikukupatsani chuma ndi ana, (zomwe ndi zokongoletsa za dziko lapansi), ndi kukupangirani minda (yokongola) ndi kukupangirani mitsinje (yothilira mbewu zanu ndi kumwetsa ziweto zanu)
Verse 13 — Surah Nuh 71:13
“Kodi chifukwa ninji simupereka ulemu kwa Allah (woyenera Umulungu Wake kuti akakuchitireni chifundo ndi kukupulumutsani ku chilango)
Verse 14 — Surah Nuh 71:14
“Pomwe Iye adakulengani mnjira zosiyanasiyana; (madzi a umunthu, kenako magazi, kenako magazi ochindikala, kenako mafupa ndipo kenako mnofu)
Verse 15 — Surah Nuh 71:15
“Kodi simudaone momwe Allah adalengera thambo zisanu ndi ziwiri mosanjikizana
Verse 16 — Surah Nuh 71:16
“Ndi kuyika mwezi mthambomo kukhala kuunika, ndiponso kuyika dzuwa kukhala nyali
Verse 17 — Surah Nuh 71:17
“Ndipo Allah adakulengani kuchokera m’nthaka monga mmera
Verse 18 — Surah Nuh 71:18
“Kenako adzakubwezerani momwemo ndikudzakutulutsaninso (popanda cholepheretsa)
Verse 19 — Surah Nuh 71:19
“Ndipo Allah wakupangirani nthaka kukhala ngati choyala
Verse 20 — Surah Nuh 71:20
“Kuti muziyendayenda m’menemo m’njira zazikulu.”
Verse 21 — Surah Nuh 71:21
“Adanena Nuh: “Mbuye wanga! Ndithu anthu anga andinyoza (pa zimene ndawalamula kuti akhulupirire Inu ndi kupempha chikhululuko chanu), ndipo (ofooka mwa iwo) amtsatira yemwe chuma chake ndi ana ake sizidzamuonjezera (chilichonse chabwino) koma kutaika (ndi kuonongeka pa tsiku lachimaliziro)
Verse 22 — Surah Nuh 71:22
“Ndipo (eni chuma ndi ana) awatchera (otsatira awo) ndale zazikulu (ndi zopyola muyeso kuti asakhulupirire).”
Verse 23 — Surah Nuh 71:23
“Ndipo adanena (kwa owatsatira awo): “Musasiye kupembedza milungu yanu; musamusiye Wadda, Suwaa’, Yaghutha, Ya’uqa ndi Nasra” (maina a mafano awo)
Verse 24 — Surah Nuh 71:24
“Ndipo ndithu iwo asokeretsa (anthu) ambiri; ndipo musawaonjezere ochita zoipa (china chake) koma kusokera basi.”
Verse 25 — Surah Nuh 71:25
“Chifukwa cha zochimwa zawo adamizidwa ndi kulowetsedwa ku Moto (waukulu woyaka); sadapeze owapulumutsa ndi kuwateteza m’malo mwa Allah
Verse 26 — Surah Nuh 71:26
“Ndipo adanena Nuh (atataya mtima za anthu ake): “Mbuye wanga! Musasiye aliyense mwa osakhulupirira kukhala pa dziko.”
Verse 27 — Surah Nuh 71:27
““Ndithu Inu Mbuye wanga ngati muwasiya (popanda kuwaononga ndi kuwathetsa) asokeretsa akapolo anu (kunjira yolungama). Ndipo sangabereke (ana abwino) koma oipa; osakhulupirira (okhala kutali ndi choonadi, ndiponso onyoza Inu).”
Verse 28 — Surah Nuh 71:28
““Mbuye wanga! Ndikhululukireni ndi makolo anga, ndi aliyense walowa m’nyumba yanga ali okhulupirira ndi okhulupirira amuna ndi okhulupirira akazi. Ndipo musawaonjezere anthu achinyengo chinachake koma kuwaononga basi.”