Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 72 - Al-Jinn
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Jinn 72:1
“Nena (iwe Mtumiki (s.a.w), kwa anthu ako): “Kwavumbulutsidwa kwa ine kuti gulu la ziwanda lidamvetsera (kuwerenga kwanga kwa Qur’an) ndipo lidanena (kumtundu wawo): ndithu tamvetsera Qur’an yodabwitsa (ikuwerengedwa)
Verse 2 — Surah Al-Jinn 72:2
“Ikuitanira kuchilungamo, ndipo taikhulupirira. Ndipo sitimphatikiza aliyense ndi Mbuye wathu, (pa mapemphero)
Verse 3 — Surah Al-Jinn 72:3
“Ndipo ndithu ukulu ndi ulemelero wa Mbuye wathu watukuka; sadadzipangire mkazi kapena mwana
Verse 4 — Surah Al-Jinn 72:4
“Ndipo ndithu mbuli za mwa ife zakhala zikunenera Allah mawu abodza (okhala kutali ndi choonadi)
Verse 5 — Surah Al-Jinn 72:5
“Ndipo ndithu ife tinkaganiza kuti anthu ndi ziwanda sangamnenere Allah zabodza (zosayenera ulemelero Wake)
Verse 6 — Surah Al-Jinn 72:6
“Ndipo ndithu padali amuna a mu wanthu amapempha chitetezo kwa amuna amziwanda, ndipo adawaonjezera (amuna amziwanda) kupitiriza machimo (awo, kupulikira ndi kuchenjelera anthu)
Verse 7 — Surah Al-Jinn 72:7
“Ndipo ndithu iwo amaganiza monga momwe mumaganizira inu kuti Allah sadzaukitsa aliyense
Verse 8 — Surah Al-Jinn 72:8
“Ndithu ife tidafuna kukafika kumwamba; tidakupeza kutadzala alonda (angelo) amphamvu ndi zenje za moto
Verse 9 — Surah Al-Jinn 72:9
“Ndithu ife tidali kukhala m’menemo (kale) mokhala momvetsera; (mobera nkhani zakumwamba). Koma amene afune kumvetsera tsopano apeza chenje cha moto chikudikilira (kuti chimgwere iye ndi kumuononga)
Verse 10 — Surah Al-Jinn 72:10
“Ndithu ife sitikudziwa chilango chimene akuwafunira a m’dziko (polondera kumwamba, kuletsa kumvetsera nkhani zakumeneko); kapena Mbuye wawo akuwafunira zabwino ndi chilungamo (pa zimenezo)
Verse 11 — Surah Al-Jinn 72:11
“Ndithu ena mwa ife ndi abwino koma ena sali choncho. Tili njira zosiyanasiyana
Verse 12 — Surah Al-Jinn 72:12
“Ndithu ife tidadziwa kuti Allah sitingathe kumlepheretsa (lamulo Lake pa ife paliponse tingakhale) pa dziko lapansi, ndipo sitingamlepheretsenso pomzemba ndi kuthawira (kumwamba)
Verse 13 — Surah Al-Jinn 72:13
“Ndipo ife pamene tachimva chiongoko (Qur’an) tachikhulupirira ndipo amene ati akhulupirire mwa Mbuye wake saopa kumchepetsera (chabwino kapena kumuonjezera machimo ake)
Verse 14 — Surah Al-Jinn 72:14
“Ndithu mwa ife alipo Asilamu ndiponso mwa ife alipo opatuka (mu njira ya chilungamo); amene walowa m’Chisilamu, iwowo ndi amene alunjika njira ya choonadi
Verse 15 — Surah Al-Jinn 72:15
“Koma opatuka (kunjira ya chilungamo) adzakhala nkhuni za Jahannam.”
Verse 16 — Surah Al-Jinn 72:16
“Ndithu (anthu ndi ziwanda) akadalungama panjira ya chilungamo tikadawamwetsa madzi ambiri (okwanira nyengo zonse)
Verse 17 — Surah Al-Jinn 72:17
“Kuti tiwayese ndi zimenezo (mmene angamyamikire Allah pa mtendere Wake pa iwo). Koma amene anyozera kupembedza Mbuye wake, amlowetsa ku chilango chovuta (chimene sangathe kupirira nacho)
Verse 18 — Surah Al-Jinn 72:18
“Ndithu misikiti ndi ya Allah yekha! Choncho, musapembedze aliyense pamodzi ndi Allah
Verse 19 — Surah Al-Jinn 72:19
“Ndipo ndithu pamene adaima kapolo wa Allah (Muhammad{s.a.w}, pa Swala yake) uku akumpembedza (Allah), ziwanda zidatsala pang’ono kumgwera (chifukwa cha kuchuluka kwawo ndi kumzinga podabwa ndi zimene adaziona ndi kuzimva)
Verse 20 — Surah Al-Jinn 72:20
“Nena: “Ndikumpembedza Mbuye wanga M’modzi (Yekha) ndipo sindingamphatikize ndi aliyense (m’mapemphero Ake).”
Verse 21 — Surah Al-Jinn 72:21
“Nena: “Ine ndilibe udindo wokupatsani mavuto kapena chilungamo (ndi zabwino).”
Verse 22 — Surah Al-Jinn 72:22
“Nena: “Ine palibe anganditeteze ku chilango cha Allah (ngati nditamnyoza) sindingapeze malo (othawira kuchilango Chake) kupatula kwa Iye.”
Verse 23 — Surah Al-Jinn 72:23
““Koma (mphamvu imene ndili nayo) ndikufikitsa uthenga wa Allah umene adanditumizira; ndithu amene anyoza Allah ndi Mtumiki Wake (ndi kupatuka pa chipembedzo cha (Allah) ndithu moto wa Jahannam ndi wake, akakhala m’menemo muyaya.”
Verse 24 — Surah Al-Jinn 72:24
“Mpaka pomwe adzaziona zimene alonjezedwa ndipamene adzadziwa (kuti) kodi ndani mwini mthandizi wofooka ndiponso wochepekedwa mchiwerengero (cha omtsatira, iwo kapena Asilamu).”
Verse 25 — Surah Al-Jinn 72:25
“Nena (kuti): “Sindikudziwa ngati zomwe mukulonjezedwa (za chilango) zili pafupi, kapena Mbuye wanga azitalikitsa.”
Verse 26 — Surah Al-Jinn 72:26
““(Iye) ndi wodziwa zobisika; sazionetsa zobisika Zake kwa aliyense (mzolengedwa Zake),”
Verse 27 — Surah Al-Jinn 72:27
““Kupatula Mtumiki (Wake) amene wamuyanja; (iyeyo amamdziwitsa zobisikazo) ndipo ndithu amamuikira alonda kutsogolo kwake ndi kumbuyo kwake (omulonda).”
Verse 28 — Surah Al-Jinn 72:28
““Kuti adziwe ngati afikitsa uthenga wa Mbuye wawo, ndipo wawazungulira (podziwa zonse zili kwa iwo) ndipo wadziwa kuchuluka kwa zinthu zonse zimene zilipo; (palibe chobisika kwa Iye).”