Back to Languages

Chichewa - Chapter 73 - Al-Muzzammil

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Muzzammil 73:1

“E iwe wadzifunditsa (ndi nsalu)

Verse 2 — Surah Al-Muzzammil 73:2

“Imilira usiku (upemphere), kupatula nthawi yochepa

Verse 3 — Surah Al-Muzzammil 73:3

“Theka lake kapena chepetsa thekalo pang’ono (mpaka ufike chimodzi mwa zigawo zitatu za usiku)

Verse 4 — Surah Al-Muzzammil 73:4

“Kapena wonjezapo (mpaka ufike zigawo ziwiri mwa zigawo zitatu za usiku;) ndipo werenga Qur’an mofatsa (lemba ndi lemba)

Verse 5 — Surah Al-Muzzammil 73:5

“Ife tikuvumbulutsira iwe (Mneneri) mawu olemera (yomwe ndi Qur’an)

Verse 6 — Surah Al-Muzzammil 73:6

“Ndithu kudzuka usiku ndi kuchita mapemphero kumalowelera (mu mtima) kwambiri, ndipo zoyankhula zake zimakhala zoongoka ndi zolunjika bwino (kuposa mapemphero amasana)

Verse 7 — Surah Al-Muzzammil 73:7

“Ndithu masana uli ndi zochitachita zambiri; (umatanganidwa ndi ntchito yauthenga; dzipatse danga usiku polimbika kupemphera)

Verse 8 — Surah Al-Muzzammil 73:8

“Ndipo tchula dzina la Mbuye wako (Amene adalenga ndi kulera zinthu), ndipo udzipereke kwathunthu kwa Iye

Verse 9 — Surah Al-Muzzammil 73:9

“(Iye ndiye) Mbuye wa kuvuma ndi kuzambwe; palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Mchiteni kukhala Mtetezi (wanu pa zinthu zanu zonse)

Verse 10 — Surah Al-Muzzammil 73:10

“Ndipo pirira pa zimene akunena. Ndipo apewe (ndi mtima wako); kupewa kwabwino

Verse 11 — Surah Al-Muzzammil 73:11

“Ndisiye Ine ndi otsutsa eni kupeza bwino; ndipo alekelere kanthawi kochepa

Verse 12 — Surah Al-Muzzammil 73:12

“Ndithudi, tili ndi mitundumitundu ya unyolo ndi Moto woyaka

Verse 13 — Surah Al-Muzzammil 73:13

“Ndi chakudya chotsamwitsa ndi chilango chowawa

Verse 14 — Surah Al-Muzzammil 73:14

“Tsiku limene nthaka ndi mapiri zidzagwedezeka; (kugwedezeka kwa mphamvu kotero kuti) mapiri adzakhala ngati mulu wa mchenga woyoyoka

Verse 15 — Surah Al-Muzzammil 73:15

“Ndithu Ife takutumizirani Mthenga amene adzakhala mboni yanu (tsiku la chimaliziro; monga momwe tidamtumizira (Mûsa) kukhala Mtumiki kwa Firiauni

Verse 16 — Surah Al-Muzzammil 73:16

“Koma Firiauni adamnyoza Mtumikiyo; ndipo tidamulanga chilango chokhwima

Verse 17 — Surah Al-Muzzammil 73:17

“Kodi mungadzitchinjirize chotani ngati mukana (chilango cha) tsiku (lomwe) lidzachititsa ana kukhala ndi imvi

Verse 18 — Surah Al-Muzzammil 73:18

“Thambo (pamodzi ndi mphamvu zake ndi kukula kwake), lidzang’ambika (tsiku limenelo) chifukwa cha kuopsa kwa tsikulo, lonjezo la (Allah) lidzakwaniritsidwa (palibe wolipinga)

Verse 19 — Surah Al-Muzzammil 73:19

“Ndithudi, ma Ayah awa (amene akunena za kuwopsa kwa Qiyâma) ndichikumbutso. Choncho amene akufuna (kuthandizika nawo) ayende panjira ya Mbuye wake (pokwaniritsa malamulo Ake ndi kuleka zoipa)

Verse 20 — Surah Al-Muzzammil 73:20

“Ndithu Mbuye wako akudziwa kuti iwe ukuima (kupemphera) pafupifupi magawo awiri mwa magawo atatu a usiku kapena theka lake, kape’nanso gawo limodzi mwa magawo atatu a usiku, pamodzi ndi gulu la omwe uli nawo. Ndipo Allah ndi Amene amadziwa bwino muyeso wa (nthawi za) usiku ndi usana, wadziwa kuti simungathe kuwerengera zimenezo, choncho wakukhululukirani. Werengani ndime imene yapepuka yochokera m’Qur’an. Wadziwa kuti ena mwa inu adzakhala odwala; (kudzawavuta kuimilira ndi kuchezera usiku), ndipo ena adzakhala akuyendayenda pa dziko (ndi cholinga cha malonda ndi ntchito) kunka nafunafuna ubwino wa Allah. Ndipo ena adzakhala akumenya nkhondo pa njira ya Allah (ncholinga chotukula mawu Ake), werengani chimene chapepuka chochokera mmenemo (m’Qur’an). Ndipo pitirizani kupemphera Swala, perekani chopereka (chimene chakakamizidwa kwa inu). Ndipo mkongozeni Allah ngongole yabwino. Ndipo chilichonse chabwino chimene mwadzitsogozera mudzachipeza kwa Allah chili chabwino (kuposa zomwe mudazisiya m’mbuyo) ndi malipiro akulu zedi ndipo mpempheni Allah chikhululuko (pa uchimo wanu ndi chikhululuko pakunyozera kwanu kuchita zabwino). Ndithu Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha