Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 74 - Al-Muddaththir
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Muddaththir 74:1
“E iwe wadziphimba (nsalu)
Verse 2 — Surah Al-Muddaththir 74:2
“Imilira ndipo uwachenjeze (anthu za chilango cha Allah)
Verse 3 — Surah Al-Muddaththir 74:3
“Ndipo Mbuye wako (Yekha) umkulitse (pomulemekeza)
Verse 4 — Surah Al-Muddaththir 74:4
“Ndipo nsalu zako uziyeretse (ndi madzi ku uve)
Verse 5 — Surah Al-Muddaththir 74:5
“Ndiponso zoipa (monga mafano ndi zina zonse ) zipewe
Verse 6 — Surah Al-Muddaththir 74:6
“Usapatse (anthu) ncholinga choti ulandire zambiri
Verse 7 — Surah Al-Muddaththir 74:7
“Chifukwa cha Mbuye wako, pirira (ku malamulo Ake poleka zomwe waletsa ndi kuchita zimene walamula)
Verse 8 — Surah Al-Muddaththir 74:8
“Ndipo likadzaimbidwa lipenga
Verse 9 — Surah Al-Muddaththir 74:9
“Tsiku limenelo lidzakhala tsiku lovuta
Verse 10 — Surah Al-Muddaththir 74:10
“Kwa osakhulupirira, silidzakhala lofewa
Verse 11 — Surah Al-Muddaththir 74:11
“Ndisiye ndiamene ndidamlenga Ndekha
Verse 12 — Surah Al-Muddaththir 74:12
“Ndipo ndampatsa chuma chambiri
Verse 13 — Surah Al-Muddaththir 74:13
“Ndi ana okhala nawo (paliponse)
Verse 14 — Surah Al-Muddaththir 74:14
“Ndipo ndamkonzera (ulemelero), kumkonzera (kwabwino)
Verse 15 — Surah Al-Muddaththir 74:15
“Kenako ali ndi dyera kuti ndimuonjezere (zina popanda kuthokoza)
Verse 16 — Surah Al-Muddaththir 74:16
“Koma sichoncho! Ndithu iye adali kutsutsa zizindikiro Zathu
Verse 17 — Surah Al-Muddaththir 74:17
“Ndidzamkakamiza kuchilango chovuta; (kukwera phiri la ku Moto limene sakatha kulikwera)
Verse 18 — Surah Al-Muddaththir 74:18
“Iye adalingalira (mu mtima mwake) ndi kukonza bwino (chonena chonyoza Qur’an)
Verse 19 — Surah Al-Muddaththir 74:19
“Choncho waonongeka! Adakonza bwanji (poinyoza Qur’an)
Verse 20 — Surah Al-Muddaththir 74:20
“Ndiponso waonongeka! Adakonza bwanji (poinyoza Qur’an)
Verse 21 — Surah Al-Muddaththir 74:21
“Kenako adayang’anayang’ana (nkhope za anthu)
Verse 22 — Surah Al-Muddaththir 74:22
“Kenakonso adachita tsinya ndikukwinya nkhope (kwambiri ndi mkwiyo)
Verse 23 — Surah Al-Muddaththir 74:23
“Kenakonso adanyoza choonadi ndi kudzikweza (posachivomereza)
Verse 24 — Surah Al-Muddaththir 74:24
“Adati: “Sichina ichi (Qur’an) koma ndi matsenga amene adalandiridwa (kuchokera kwa amatsenga akale)
Verse 25 — Surah Al-Muddaththir 74:25
“Sichina ichi koma ndi mawu a anthu!”
Verse 26 — Surah Al-Muddaththir 74:26
“Posachedwa ndimlowetsa ku ‘Saqara.’
Verse 27 — Surah Al-Muddaththir 74:27
“Nanga ndi chiyani chingakudziwitse za ‘Saqara?’
Verse 28 — Surah Al-Muddaththir 74:28
“(Ndi moto umene) siusiya (mnofu) ndiponso siusiya (fupa)
Verse 29 — Surah Al-Muddaththir 74:29
“Wopsereza ndi kudetsa khungu
Verse 30 — Surah Al-Muddaththir 74:30
“Kumeneko kuli khumi ndi asanu ndi anayi (alonda oyang’anira Motowo)
Verse 31 — Surah Al-Muddaththir 74:31
“Ndipo sitidaike oyang’anira ku Moto (kukhala anthu) koma angelo; ndipo sitidaike chiwerengero chawo koma ndimayesero kwa amene sadakhulupirire, kuti atsimikize amene adapatsidwa mabuku (zimene Qur’an ikunena za chiwerengero cha angelo a ku Moto) ndiponso kuti chionjezeke chikhulupiliro kwa amene akhulupirira, ndikuti asapeneke amene adapatsidwa mabuku pamodzi ndi okhulupirira. Ndiponso kuti amene m’mitima mwawo muli matenda (matenda achinyengo) komanso osakhulupirira anene: “Kodi Allah akulinganji pa fanizo limeneli?” Momwemo Allah akumulekelera kusokera amene wamfuna, ndipo akumuongola amene wamfuna ndipo palibe amene angadziwe magulu a nkhondo a Mbuye wako kupatula Iye mwini. (Kutchula moto ndi zam’kati mwake) sichina koma ndichenjezo kwa anthu
Verse 32 — Surah Al-Muddaththir 74:32
“Sichoncho; ndikulumbilira mwezi
Verse 33 — Surah Al-Muddaththir 74:33
“Ndi usiku pamene ukuchoka
Verse 34 — Surah Al-Muddaththir 74:34
“Ndi m’bandakucha pamene kukuyera
Verse 35 — Surah Al-Muddaththir 74:35
“Ndithu uwo, (moto wa Jahannam) ndi chimodzi mwa malodza akulu
Verse 36 — Surah Al-Muddaththir 74:36
“Ndi chenjezo kwa anthu
Verse 37 — Surah Al-Muddaththir 74:37
“Kwa yemwe wafuna mwa inu kutsogola (pochita zabwino zokamthandiza tsiku louka kwa akufa) kapena kutsalira (ndi za m’dziko)
Verse 38 — Surah Al-Muddaththir 74:38
“Mzimu uliwonse ukakhala chikole ndi zimene udachita
Verse 39 — Surah Al-Muddaththir 74:39
“Kupatula akudzanja lamanja (Asilamu amene adadzimasula okha potembenukira kwa Allah)
Verse 40 — Surah Al-Muddaththir 74:40
“(Iwo) adzakhala m’minda (yosasimbika kukongola kwake) akufunsana wina ndi mnzake
Verse 41 — Surah Al-Muddaththir 74:41
“Za anthu oipa
Verse 42 — Surah Al-Muddaththir 74:42
“(Kuti): “Nchiyani chakulowetsani ku Moto?”
Verse 43 — Surah Al-Muddaththir 74:43
“Adzanena: “Sitidali m’gulu la omwe adali kupemphera (Swala)
Verse 44 — Surah Al-Muddaththir 74:44
“Ndiponso sitidali kuwadyetsa masikini
Verse 45 — Surah Al-Muddaththir 74:45
“Koma tinkangomira (m’zachabe ndi zabodza) pamodzi ndi omira (m’menemo)
Verse 46 — Surah Al-Muddaththir 74:46
“Ndiponso tidali kutsutsa za tsiku la malipiro
Verse 47 — Surah Al-Muddaththir 74:47
“Mpaka imfa idatifika.”
Verse 48 — Surah Al-Muddaththir 74:48
“Choncho siwudzawathandiza uwomboli wa awomboli
Verse 49 — Surah Al-Muddaththir 74:49
“Kodi ali ndi chiyani iwo pakuti azinyozera chenjezoli (limene lili Qur’an)
Verse 50 — Surah Al-Muddaththir 74:50
“(Akuyenda mothamanga kuti asamve chenjezoli) ngati kuti iwo ndi mbidzi zothawa
Verse 51 — Surah Al-Muddaththir 74:51
“(Zimene) zikuthawa mkango
Verse 52 — Surah Al-Muddaththir 74:52
“Ati akufuna aliyense mwa iwo apatsidwe kalata zotambasulidwa (zimene zitsimikize uthenga wa Mneneri Muhammad{s.a.w)
Verse 53 — Surah Al-Muddaththir 74:53
“Sichoncho! Koma kuti iwo sakuopa tsiku lachimaliziro
Verse 54 — Surah Al-Muddaththir 74:54
“Sichoncho! Ndithu ichi (Qur’an) ndichikumbutso (chokwanira)
Verse 55 — Surah Al-Muddaththir 74:55
“Choncho amene wafuna achikumbukire (amene sakufuna ndizake)
Verse 56 — Surah Al-Muddaththir 74:56
“Ndipo sangakumbukire pokhapokha Allah atafuna. Iye ndiye Amene ali woyenera kumuopa, ndiponso ndiye Mwini kukhululukira (amene akumuopa)