Back to Languages

Chichewa - Chapter 75 - Al-Qiyamah

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Qiyamah 75:1

“Ndikulumbilira tsiku lachimaliziro

Verse 2 — Surah Al-Qiyamah 75:2

“Ndikulumbiliranso mzimu wodzidzudzula (pa cholakwa chimene wachita. Ndithu mudzaukitsidwa; mafupa anu omwazikana atasonkhanitsidwa)

Verse 3 — Surah Al-Qiyamah 75:3

“Kodi munthu akuganiza kuti Ife (Amene tidamlenga kuchokera popanda chilichonse) sitidzatha kusonkhanitsa mafupa ake (ofumbwa)

Verse 4 — Surah Al-Qiyamah 75:4

“Iyayi, Ife tikhoza (kutisonkhanitsa) ndi kutilongosola bwino timizere takunsonga kwa zala zake. (Mafupa ake ndiye osanena)

Verse 5 — Surah Al-Qiyamah 75:5

“Koma munthu akufuna kuti apitirize kuchimwa (mmasiku akudza) mtsogolo mwake

Verse 6 — Surah Al-Qiyamah 75:6

“Akufunsa (mwa chipongwe): “Kodi lidzakhala liti tsiku la chimaliziro?”

Verse 7 — Surah Al-Qiyamah 75:7

“Pamene maso adzangoti tong’oo (ndi mantha)

Verse 8 — Surah Al-Qiyamah 75:8

“Ndi kuchoka kuwala kwa mwezi

Verse 9 — Surah Al-Qiyamah 75:9

“Ndipo dzuwa ndi mwezi ndikusonkhanitsidwa

Verse 10 — Surah Al-Qiyamah 75:10

“Munthu adzanena tsiku limenelo: “Nkuti kothawira (chilangochi?)”

Verse 11 — Surah Al-Qiyamah 75:11

“(Adzauzidwa): “Iyayi, (iwe munthu) palibe pothawira (pako)!”

Verse 12 — Surah Al-Qiyamah 75:12

“Tsiku limenelo kobwerera (anthu) ndi kwa Mbuye wako basi

Verse 13 — Surah Al-Qiyamah 75:13

“Tsiku limenelo munthu adzauzidwa zochita zake zimene adazitsogoza ndi zimene adazichedwetsa

Verse 14 — Surah Al-Qiyamah 75:14

“Koma munthu adzadzichitira umboni yekha pa mzimu wake

Verse 15 — Surah Al-Qiyamah 75:15

“Ngakhale atapereka madandaulo ake (otani kuti apulumuke nawo sadzapulumuka)

Verse 16 — Surah Al-Qiyamah 75:16

“Usaigwedezere (Qur’an) lirime lako (pamene ikuvumbulutsidwa) kuti uifulumilire (kuiwerenga ndi kuisunga mu mtima)

Verse 17 — Surah Al-Qiyamah 75:17

“Ndithu ndiudindo wathu kuisonkhanitsa (mu mtima mwako) ndi kukhazikitsa kawerengedwe kake (palirime lako)

Verse 18 — Surah Al-Qiyamah 75:18

“Choncho pamene tikukuwerengera iwe tsatira kuwerenga kwakeko (uku uli chete)

Verse 19 — Surah Al-Qiyamah 75:19

“Kenako, ndithu ndiudindo Wathu kulongosola (zimene siukumvetsa)

Verse 20 — Surah Al-Qiyamah 75:20

“Iyayi koma mukukonda moyo wa pa dziko

Verse 21 — Surah Al-Qiyamah 75:21

“Ndipo mukusiya moyo wa tsiku lachimaliziro

Verse 22 — Surah Al-Qiyamah 75:22

“Nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zowala

Verse 23 — Surah Al-Qiyamah 75:23

“Zili kumuyang’ana Mbuye wawo

Verse 24 — Surah Al-Qiyamah 75:24

“Ndipo nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zoziya (zokhwinyata)

Verse 25 — Surah Al-Qiyamah 75:25

“Zikuyembekezeka kuti zilandira tsoka lodula msana

Verse 26 — Surah Al-Qiyamah 75:26

“Sichoncho! Pamene mzimu udzafika pa nthitimtima, (pomwe pakumana mafupa am’mapewa)

Verse 27 — Surah Al-Qiyamah 75:27

“Ndipo ndikunenedwa ndani angamchiritse

Verse 28 — Surah Al-Qiyamah 75:28

“Ndipo (iye mwini wake), nkutsimikiza kuti ndithu uku ndikusiyana (ndi dziko lapansi)

Verse 29 — Surah Al-Qiyamah 75:29

“Ndipo miyendo idzasanjikizana; (iyi ndi nthawi yochoka mzimu)

Verse 30 — Surah Al-Qiyamah 75:30

“Tsiku limenelo koperekedwa (anthu onse) nkwa Mbuye wako

Verse 31 — Surah Al-Qiyamah 75:31

“Ndipo sadakhulupirire komanso sadapemphere Swala (zisanu)

Verse 32 — Surah Al-Qiyamah 75:32

“Koma (m’malo mwake) adatsutsa ndi kunyoza

Verse 33 — Surah Al-Qiyamah 75:33

“Kenaka adapita kubanja lake (uku akuyenda) monyada

Verse 34 — Surah Al-Qiyamah 75:34

“Kuonongeka nkwako (iwe wotsutsa)! Kuonongeka zedi

Verse 35 — Surah Al-Qiyamah 75:35

“Ndiponso kuonongeka nkwako! kuonongeka zedi

Verse 36 — Surah Al-Qiyamah 75:36

“Kodi munthu akuganiza kuti angosiidwa chabe? (Sadzaweruzidwa)

Verse 37 — Surah Al-Qiyamah 75:37

“Kodi sadali dontho la umuna umene udafwamphukira (m’chiberekero)

Verse 38 — Surah Al-Qiyamah 75:38

“Kenako adakhala nthinthi (ntchintchi) ya magazi, ndipo adamlenga ndi kumlinganiza (monga munthu)

Verse 39 — Surah Al-Qiyamah 75:39

“Ndipo adalenga kuchokera mmenemo mitundu iwiri: mwamuna ndi mkazi

Verse 40 — Surah Al-Qiyamah 75:40

“Kodi (Iye amene adayambitsa chilengedwe choyambachi) sangathe kuwapatsa moyo akufa