Back to Languages

Chichewa - Chapter 76 - Al-Insan

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Insan 76:1

“Ndithu munthu idampita nthawi yaitali kwambiri (asanauziridwe mzimu) pomwe sadali chinthu chotchulidwa

Verse 2 — Surah Al-Insan 76:2

“Ndithu Ife tamlenga munthu kuchokera ku mbewu ya munthu yosakanikirana (ya mkazi ndi ya mwamuna) kuti timuyese mayeso (ndi malamulo Athu); choncho tidampanga kukhala wakumva ndi wopenya; (amve mawu a Allah ndi kuti aone zisonyezo Zake)

Verse 3 — Surah Al-Insan 76:3

“Ndithu Ife tidamlongosolera njira yoongoka: kukhala wokhulupirira kapena wotsutsa (Zonse zili kwa iye)

Verse 4 — Surah Al-Insan 76:4

“Ndithu Ife okana tawakonzera unyolo (wam’miyendo yawo) ndi magoli (am’manja ndi m’makosi awo) ndi Moto waukali woyaka

Verse 5 — Surah Al-Insan 76:5

“Ndithu ochita zabwino adzamwa vinyo, chosakanizira chake chidzakhala (madzi a) kaafura

Verse 6 — Surah Al-Insan 76:6

“(Kaafura ameneyo) ndikasupe amene adzikamwapo akapolo a Allah ndi kumtulutsa (paliponse pamene afuna) kumtulutsa mofewa

Verse 7 — Surah Al-Insan 76:7

“(Amene) akukwaniritsa zimene adalonjeza (okha kwa Allah), ndiponso akuopa tsiku (lalikulu) limene zoipa zake zidzakhala zofalikira ponseponse

Verse 8 — Surah Al-Insan 76:8

“Ndipo amadyetsa chakudya masikini, amasiye ndi ogwidwa pa nkhondo, pomwe iwo akuchifunanso

Verse 9 — Surah Al-Insan 76:9

“Amanena (chamumtima akamapereka chakudyacho): “Tikukudyetsani chifukwa chofuna chikondi cha Allah basi; sitikufuna kwa inu malipiro kapena kuthokoza

Verse 10 — Surah Al-Insan 76:10

“Ndithu ife tikuopa kwa Mbuye wathu tsiku lokhwinyata nkhope ndi mavuto akulu.”

Verse 11 — Surah Al-Insan 76:11

“Ndipo Allah adzawateteza mu mavuto a tsiku limenelo ndiponso adzawapatsa mtendere ndi chisangalalo

Verse 12 — Surah Al-Insan 76:12

“Ndipo adzawalipira chifukwa cha kupirira kwawo Munda wamtendere ndi nsalu zaveleveti

Verse 13 — Surah Al-Insan 76:13

“Atatsamira m’menemo pa makama (amtengo wapatali); sadzamva m’menemo kutentha kwa dzuwa kapena kuzizira

Verse 14 — Surah Al-Insan 76:14

“Mithunzi yake ikawayandikira iwo ndipo mikoko yazipatso idzatewa pafupi (moti munthu atha kuthyola ali chigonere)

Verse 15 — Surah Al-Insan 76:15

“Ndipo adzakhala akuzunguliridwa (ndi otumikira) uku atatenga zomwera za siliva ndi matambula onyezimira ndiponso olangala

Verse 16 — Surah Al-Insan 76:16

“Zolangala zopangidwa ku siliva, atalinga bwino zakumwazo (malinga ndi kufuna kwawo)

Verse 17 — Surah Al-Insan 76:17

“Ndipo (anthu abwino) akamwetsedwa kumeneko vinyo, chosakanizira chake chikafanana ndi Zanjabila (chikasu)

Verse 18 — Surah Al-Insan 76:18

“M’menemo muli kasupe wotchedwa Salisabila

Verse 19 — Surah Al-Insan 76:19

“Ndipo azikawazungulira anyamata osasinthika (chilengedwe chawo,) utawaona (chifukwa cha kukongola kwawo ndi kuwala kwa nkhope zawo) ungawaganizire kuti ndi ngale zomwazidwa

Verse 20 — Surah Al-Insan 76:20

“Ndipo ukadzaona kumeneko (ku Jannah) ukaona mtendere ndi ufumu waukulu

Verse 21 — Surah Al-Insan 76:21

“Pamwamba pawo padzakhala nsalu zaveleveti zopyapyala, zobiriwira ndi nsalu zaveleveti zochindikala, akavekedwa m’manja mwawo zibangiri zasiliva; Mbuye wawo akawamwetsa chakumwa china choyera kwambiri

Verse 22 — Surah Al-Insan 76:22

“(Akawauza kuti:) “Ndithu iyi ndi mphoto yanu ndipo ntchito zanu ndi zolandiridwa.”

Verse 23 — Surah Al-Insan 76:23

“Ndithu Ife taivumbulutsa kwa iwe Qur’an mwapang’onopang’ono (kuti uisunge bwino, usaiwale)

Verse 24 — Surah Al-Insan 76:24

“Choncho, pirira ndi lamulo la Mbuye wako ndipo usamvere wamachimo kapena wokanira aliyense mwa iwo

Verse 25 — Surah Al-Insan 76:25

“Ndipo kumbukira dzina la Mbuye wako; mmawa, ndi madzulo (Swala za Subuhi, Dhuhr ndi Asri)

Verse 26 — Surah Al-Insan 76:26

“Ndipo usiku mlambire Iye, (Swala ya Maghrib ndi Isha); ndiponso umulemekeze usiku nthawi yaitali (popemphera sunna za tahajjudi)

Verse 27 — Surah Al-Insan 76:27

“Ndithu awa akukonda moyo wa dziko lapansi, ndipo akulisiya kumbuyo kwao tsiku lovuta

Verse 28 — Surah Al-Insan 76:28

“Ife ndi amene tidawalenga ndipo tidalimbika kalengedwe kawo; ndipo titafuna tingabweretse ena onga iwo (omvera Allah) kulowa m’malo mwawo

Verse 29 — Surah Al-Insan 76:29

“Ndithu ichi ndichikumbutso choncho amene afuna atsata njira yopitira kwa Mbuye wake (pomukhulupirira ndi kumumvera)

Verse 30 — Surah Al-Insan 76:30

“Koma simungafune nokha chilichonse pokhapokha atafuna Allah, ndithu Allah ndi Wodziwa zedi, Wanzeru zakuya

Verse 31 — Surah Al-Insan 76:31

“Akumlowetsa amene wamfuna ku chifundo Chake; koma oyipa wawalinganizira chilango chowawa kwambiri