Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 77 - Al-Mursalat
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Mursalat 77:1
“Ndikulumbilira mphepo yomwe ikuomba motsatizana
Verse 2 — Surah Al-Mursalat 77:2
“Ndi mphepo yamkuntho ikamakuntha
Verse 3 — Surah Al-Mursalat 77:3
“Ndi mphepo yobalalitsa mitambo ndi mvula
Verse 4 — Surah Al-Mursalat 77:4
“Ndi ma Ayah osiyanitsa pakati pachoona ndi chonama
Verse 5 — Surah Al-Mursalat 77:5
“Ndi angelo opereka chivumbulutso kwa aneneri
Verse 6 — Surah Al-Mursalat 77:6
“Kuti chichotse madandaulo kapena chikhale chenjezo
Verse 7 — Surah Al-Mursalat 77:7
“Ndithu zimene mukulonjezedwa (kuti chimaliziro chidzakhalapo) zidzachitikadi (popanda chipeneko)
Verse 8 — Surah Al-Mursalat 77:8
“Pamene nyenyezi zidzafafanizidwa (kuwala kwake ndi kuchotsedwa m’malo mwake)
Verse 9 — Surah Al-Mursalat 77:9
“Ndiponso pamene thambo lidzang‘ambidwa
Verse 10 — Surah Al-Mursalat 77:10
“Ndi pamenenso mapiri adzachotsedwa m’malo mwake ndi kuperedwa (kukhala fumbi)
Verse 11 — Surah Al-Mursalat 77:11
“Ndi pamene atumiki adzasonkhanitsidwa pa nthawi yake, (kuti apereke umboni ku mibadwo yawo)
Verse 12 — Surah Al-Mursalat 77:12
“Kodi nditsiku lanji azichedwetsera (zinthu zikuluzikulu kuti zidzachitike)
Verse 13 — Surah Al-Mursalat 77:13
“Nditsiku loweruza (pakati pa zolengedwa)
Verse 14 — Surah Al-Mursalat 77:14
“Nchiyani chingakudziwitse za tsiku la chiweruzirolo
Verse 15 — Surah Al-Mursalat 77:15
“Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa)
Verse 16 — Surah Al-Mursalat 77:16
“Kodi sitidawaononge (anthu) akale (chifukwa cha machimo awo, monga anthu a Nuh, Âdi ndi Samudu)
Verse 17 — Surah Al-Mursalat 77:17
“Kenako titsatiza ena (okana Allah m’kuonongekako monga tidawachitira oyamba)
Verse 18 — Surah Al-Mursalat 77:18
“Chomwecho tiwachitiranso ochimwa
Verse 19 — Surah Al-Mursalat 77:19
“Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa)
Verse 20 — Surah Al-Mursalat 77:20
“Kodi sitidakulengeni kuchokera ku madzi onyozeka, (madzi ambewu ya munthu)
Verse 21 — Surah Al-Mursalat 77:21
“Kenako tidawaika pamalo okhazikika (kuti chilengedwe chake chikwanire pamenepo)
Verse 22 — Surah Al-Mursalat 77:22
“Mpaka nyengo yodziwika (imene tidaipima kuti mwana abadwe)
Verse 23 — Surah Al-Mursalat 77:23
“Tidaipima nyengoyo; taonani kupima bwino Ife opima
Verse 24 — Surah Al-Mursalat 77:24
“Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa)
Verse 25 — Surah Al-Mursalat 77:25
“Kodi sitidaichite nthaka kukhala yofungatira
Verse 26 — Surah Al-Mursalat 77:26
“Amoyo ndi akufa
Verse 27 — Surah Al-Mursalat 77:27
“Ndipo tidaika m’menemo mapiri ataliatali (olimbitsa nthaka), ndipo takumwetsani madzi okoma
Verse 28 — Surah Al-Mursalat 77:28
“Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa)
Verse 29 — Surah Al-Mursalat 77:29
“(Kudzanenedwa kwa okana tsiku la chimaliziro:) Pitani kuzimene mudali kuzitsutsa zija
Verse 30 — Surah Al-Mursalat 77:30
“Pitani kumthunzi (wautsi wa ku Moto) wa nthambi zitatu
Verse 31 — Surah Al-Mursalat 77:31
“Simthunzi (wamtendere) ndiponso siwotchinjiriza ku malawi a Moto.”
Verse 32 — Surah Al-Mursalat 77:32
“Ndithu motowo umaponya mphalikira (mbaliwali) zazikulu ngati nyumba
Verse 33 — Surah Al-Mursalat 77:33
“Zonga ngati ngamira zachikasu
Verse 34 — Surah Al-Mursalat 77:34
“Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (zimenezi)
Verse 35 — Surah Al-Mursalat 77:35
“Ili ndi tsiku lomwe sadzayankhula
Verse 36 — Surah Al-Mursalat 77:36
“Ndipo sadzapatsidwa chilolezo (choyankhulira) kuti apereke madandaulo awo
Verse 37 — Surah Al-Mursalat 77:37
“Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (za tsiku limenelo)
Verse 38 — Surah Al-Mursalat 77:38
“(Adzauzidwa kuti): Ili ndi tsiku loweruza (pakati pa abwino ndi oipa takusonkhanitsani inu (otsutsa Muhammad {s.a.w}), ndi akale (otsutsa aneneri akale)
Verse 39 — Surah Al-Mursalat 77:39
“Ngati muli ndi ndale (yodzipulumutsira ku chilango Changa) ndichiteni ndaleyo
Verse 40 — Surah Al-Mursalat 77:40
“Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo la Allah)
Verse 41 — Surah Al-Mursalat 77:41
“Ndithu oopa (Allah tsiku limenelo) adzakhala mu mthunzi ndi mitsinje
Verse 42 — Surah Al-Mursalat 77:42
“Ndipo adzakhala ndi zipatso zomwe azidzazifuna
Verse 43 — Surah Al-Mursalat 77:43
“(Kudzanenedwa kwa iwo): “Idyani, imwani mokondwa chifukwa cha zabwino zomwe mudali kuchita (mu moyo wa dziko lapansi)
Verse 44 — Surah Al-Mursalat 77:44
“Ndithu umo ndi mmene Ife timawalipirira ochita zabwino
Verse 45 — Surah Al-Mursalat 77:45
“Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (mtendere wa Allah)
Verse 46 — Surah Al-Mursalat 77:46
“Idyani, sangalalani pang’ono m’kanthawi kochepa; ndithu inu ndinu ochimwa (chifukwa chakumphatikiza Allah ndi zolengedwa)
Verse 47 — Surah Al-Mursalat 77:47
“Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (mtendere wa Allah)
Verse 48 — Surah Al-Mursalat 77:48
“Ndipo kukanenedwa kwa iwo: “Weramani, (pembedzani Allah).” sawerengera
Verse 49 — Surah Al-Mursalat 77:49
“Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (malamulo a Allah)
Verse 50 — Surah Al-Mursalat 77:50
“Kodi ndi nkhani iti imene adzaikhulupirira pambuyo pa Iyi (Qur’an)