Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 78 - An-Naba
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah An-Naba 78:1
“۞ Kodi akufunsana zachiyani
Verse 2 — Surah An-Naba 78:2
“Za nkhani yayikulu ija
Verse 3 — Surah An-Naba 78:3
“Imene iwo akusiyana (maganizo)
Verse 4 — Surah An-Naba 78:4
“Aleke (zimenezo) adzadziwa posachedwapa
Verse 5 — Surah An-Naba 78:5
“Ayi, ndithu aleke (zimenezo); posachedwapa adzadziwa zoona zake (pamene chilango chidzawatsikira)
Verse 6 — Surah An-Naba 78:6
“Kodi sitidachite nthaka kukhala ngati choyala
Verse 7 — Surah An-Naba 78:7
“Ndi mapiri ngati zichiri (zolimbitsa nthaka)
Verse 8 — Surah An-Naba 78:8
“Ndipo takulengani mitundu iwiri (amuna ndi akazi)
Verse 9 — Surah An-Naba 78:9
“Ndipo tidachita tulo tanu kukhala mpumulo (ku mavuto a ntchito)
Verse 10 — Surah An-Naba 78:10
“Ndipo taupanga usiku kukhala ngati chovala (pokuvindikirani ndi mdima wake)
Verse 11 — Surah An-Naba 78:11
“Ndipo tapanga masana kukhala nthawi yopezera zofunika pa moyo
Verse 12 — Surah An-Naba 78:12
“Ndipo tamanga pamwamba panu thambo zisanu ndi ziwiri zolimba
Verse 13 — Surah An-Naba 78:13
“Ndipo tidapanga nyali yowala ndi yotentha kwambiri (dzuwa)
Verse 14 — Surah An-Naba 78:14
“Ndipo tawatsitsa madzi otsika mwamphamvu kuchokera ku mitambo, ya mvula
Verse 15 — Surah An-Naba 78:15
“Kuti titulutse ndi madziwo mbewu ndi m’mera, (chomwe ndi chakudya cha anthu ndi nyama)
Verse 16 — Surah An-Naba 78:16
“Ndi minda yothothana nthambi za mitengo
Verse 17 — Surah An-Naba 78:17
“Ndithu tsiku la chiweruziro ndinthawi imene idakhazikitsidwa kale
Verse 18 — Surah An-Naba 78:18
“Tsiku limene lipenga (lakuuka) lidzaimbidwa ndipo inu mudzabwera (kubwalo losonkhanirana) muli magulumagulu
Verse 19 — Surah An-Naba 78:19
“Ndipo thambo lidzatsegulidwa (mbali zonse): choncho lidzakhala makomomakomo
Verse 20 — Surah An-Naba 78:20
“Ndipo mapiri adzachotsedwa m’malo mwake, adzakhala ngati zideruderu
Verse 21 — Surah An-Naba 78:21
“Ndithu moto wa Jahannam ukuwadikilira (oipa)
Verse 22 — Surah An-Naba 78:22
“Mbuto ya opyola malire
Verse 23 — Surah An-Naba 78:23
“Adzakhala m’menemo muyaya
Verse 24 — Surah An-Naba 78:24
“Sadzalawa m’menemo kuzizira (kowachotsera kutentha), kapena chakumwa (chowachotsera ludzu lawo)
Verse 25 — Surah An-Naba 78:25
“Kupatula madzi otentha kwambiri ndi mafinya (otuluka mmatupi a anthu a ku Moto)
Verse 26 — Surah An-Naba 78:26
“Kukhala malipiro olingana ndi ntchito zawo
Verse 27 — Surah An-Naba 78:27
“Ndithu iwo sadali kuyembekezera chiwerengero (cha Allah)
Verse 28 — Surah An-Naba 78:28
“Adatsutsa zizindikiro Zathu (zosonyeza kuuka kwa akufa) ndi mtsutso waukulu
Verse 29 — Surah An-Naba 78:29
“Ndipo chinthu chilichonse tachisunga mochilemba
Verse 30 — Surah An-Naba 78:30
“Basi, lawani (lero chilango Changa); sitikuonjezerani chinthu china koma chilango pamwamba pa chilango
Verse 31 — Surah An-Naba 78:31
“Ndithu anthu oopa Allah adzakhala ndi malo wopambana
Verse 32 — Surah An-Naba 78:32
“Minda ndi zipatso za mphesa
Verse 33 — Surah An-Naba 78:33
“Ndi mabuthu (anamwali) ofanana misinkhu
Verse 34 — Surah An-Naba 78:34
“Ndi zipanda zodzaza ndi zakumwa
Verse 35 — Surah An-Naba 78:35
“Sakamva m’menemo mawu opanda pake kapena bodza
Verse 36 — Surah An-Naba 78:36
“Amenewa ndi malipiro ochokera kwa Mbuye wako zopereka zokwanira
Verse 37 — Surah An-Naba 78:37
“Mbuye wa kumwamba ndi pansi ndi zimene zili pakati pake; Wachifundo chambiri. Palibe amene adzakhala ndi mphamvu yolankhulana naye (pa tsiku limenero)
Verse 38 — Surah An-Naba 78:38
“Tsiku limene adzaima Jibril ndi angelo pa mzere (ali odzichepetsa); sadzayankhula aliyense mwa iwo kupatula yekhayo amene adzaloledwa ndi (Allah) Wachifundo chambiri (kuyankhula) ndipo adzanena zolondola
Verse 39 — Surah An-Naba 78:39
“Limenelo ndi tsiku loona, (lopanda chikaiko); choncho amene akufuna adzipezere malo (njira yonkera) kwa Mbuye wake. (Pomugonjera Iye pa moyo uno wadziko lapansi)
Verse 40 — Surah An-Naba 78:40
“Ndithu tikukuchenjezani zachilango chomwe chili pafupi kudza; tsiku limene munthu adzayang’ana zimene adatsogoza manja ake, ndipo wosakhulupirira adzanena: Kalanga ine! Ndikadakhala dothi, (kuti ndisalangidwe chilango chikundiyembekezachi)