Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 79 - An-Naziat
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah An-Naziat 79:1
“Ndikulumbilira (angelo) amene amazula mwamphamvu (mizimu ya osakhulupirira)
Verse 2 — Surah An-Naziat 79:2
“Ndikulumbiliranso (angelo) amene amachotsa moleza (mizimu ya okhulupirira)
Verse 3 — Surah An-Naziat 79:3
“Ndi omwe amasambira (nayo mizimuyo) mu mlengalenga (ponka nayo ku malo ake oyembekezera)
Verse 4 — Surah An-Naziat 79:4
“Ndi iwo amene akupikisana pokwaniritsa malamulo a Allah
Verse 5 — Surah An-Naziat 79:5
“Ndi iwo (angelo) amene akulongosola malamulo (Ake). (Ndithudi inu anthu mudzauka kwa akufa)
Verse 6 — Surah An-Naziat 79:6
“Patsiku lomwe (lipenga loyamba lidzaimbidwa), dziko lapansi ndi mapiri ake zidzagwedezeka (ndipo aliyense adzafa)
Verse 7 — Surah An-Naziat 79:7
“Ndipo kudzatsatira kuyimba kwa lipenga lachiwiri (kumene kudzaukitsa akufa onse)
Verse 8 — Surah An-Naziat 79:8
“Tsiku limenelo mitima idzanjenjemera ndi kuopa
Verse 9 — Surah An-Naziat 79:9
“Maso a eni mitimayo adzakhala ozyolika (chifukwa chamadandaulo)
Verse 10 — Surah An-Naziat 79:10
“(Osakhulupirira) akunena: “Kodi nzoona tidzabwezedwa pambuyo pa imfa monga tidalili kale?”
Verse 11 — Surah An-Naziat 79:11
““Pomwe ife titakhala mafupa ofumbwa (tingabwezedwe ndi kuukitsidwa mwa tsopano)?”
Verse 12 — Surah An-Naziat 79:12
“Adanena (mokanira ndi mwachipongwe): “Choncho kubwerera kumeneko ngati kudzakhalepodi kudzakhala kotaika (ndi kopanda phindu kwa ife. Pomwe ife sindife oyenera kutaika).”
Verse 13 — Surah An-Naziat 79:13
“(Musaganize kubwererako nchinthu chovuta). Ndithundithu Kiyamayo ndi nkuwo umodzi
Verse 14 — Surah An-Naziat 79:14
“Mwadzidzidzi (zolengedwa zonse) zidzangoona zili pa dziko latsopano (zili zamoyo)
Verse 15 — Surah An-Naziat 79:15
“Kodi yakufika (iwe Mtumiki) (s.a.w) nkhani ya Mûsa
Verse 16 — Surah An-Naziat 79:16
“Pamene Mbuye wake adamuitana pa chigwa choyera (chotchedwa) Tuwaa
Verse 17 — Surah An-Naziat 79:17
“(Adamuuza kuti) pita kwa Farawo ndithu iye wapyola malire, (mkudzitukumula kwake ndikupondereza anthu)
Verse 18 — Surah An-Naziat 79:18
“Choncho ukamuuze kuti: “Kodi ukufuna kudziyeretsa?”
Verse 19 — Surah An-Naziat 79:19
““Ndikuti ndikuongolere kwa Mbuye wako kuti uzimuopa?”
Verse 20 — Surah An-Naziat 79:20
“(Basi Mûsa) adamuonetsa (Farawo) chozizwitsa chachikulu
Verse 21 — Surah An-Naziat 79:21
“Koma (Farawo) adatsutsa (Mûsa pazimene adadza nazo zija) ndi kunyoza
Verse 22 — Surah An-Naziat 79:22
“Kenaka adabwerera uku akulimbika kutsutsana naye (Allah)
Verse 23 — Surah An-Naziat 79:23
“Adawasonkhanitsa (afiti) uku akuitana anthu
Verse 24 — Surah An-Naziat 79:24
“Nanena: “Ine ndine mbuye wanu wapamwambamwamba!”
Verse 25 — Surah An-Naziat 79:25
“Pamenepo Allah adamulanga chifukwa cha mawu ake omaliza ndi oyamba
Verse 26 — Surah An-Naziat 79:26
“Ndithu pa zimenezi pali phunziro (lalikulu) kwa yemwe akuopa Allah
Verse 27 — Surah An-Naziat 79:27
“Kodi kulengedwa kwanu, (inu osakhulupirira kuti muuke) nkovuta kapena thambo limene adalimanga (posonkhanitsa mbali zake zosiyanasiyana ndikukhala chinthu chimodzi)
Verse 28 — Surah An-Naziat 79:28
“Adatukula nsinkhu wake ndikulikonza bwino (popanda pena pong’ambika kapena posiyana ndi pena)
Verse 29 — Surah An-Naziat 79:29
“Ndipo amauvindikira usiku wake ndi mdima ndipo amatulutsa kuwala wake
Verse 30 — Surah An-Naziat 79:30
“Ndipo pambuyo pazimenezo, nthaka adaiyala (kuti ikhale yoyenera kuikhala)
Verse 31 — Surah An-Naziat 79:31
“Adatulutsa m’menemo madzi ake (potulutsa akasupe) ndikumeretsa msipu wake
Verse 32 — Surah An-Naziat 79:32
“Ndipo mapiri adawakhazikitsa (ndikuwalimbika)
Verse 33 — Surah An-Naziat 79:33
“(Adachita zonsezi) chifukwa chokusangalatsani inu ndi ziweto zanu
Verse 34 — Surah An-Naziat 79:34
“Choncho likadzafika tsoka lalikulu (tsiku la Qiyâma)
Verse 35 — Surah An-Naziat 79:35
“Tsiku limenelo munthu adzakumbukira zimene adachita, (zabwino ndi zoipa)
Verse 36 — Surah An-Naziat 79:36
“Ndipo Moto waukali udzawonetsedwa kwa yense openya
Verse 37 — Surah An-Naziat 79:37
“Tsono amene adapyola malire (pochita machimo)
Verse 38 — Surah An-Naziat 79:38
“Ndikudzisankhira (yekha) moyo wa pa dziko lapansi
Verse 39 — Surah An-Naziat 79:39
“Ndithu Jahannam ndiwo malo ake
Verse 40 — Surah An-Naziat 79:40
“Tsono amene akuopa kuti adzaimilira pamaso pa Mbuye wake, nauletsa mtima wake ku zilakolako zoipa
Verse 41 — Surah An-Naziat 79:41
“Ndithu Munda wamtendere ndiwo adzakhale malo ake
Verse 42 — Surah An-Naziat 79:42
“Akukufunsa (iwe Mtumiki) (s.a.w) za nthawi (ya tsiku lachimaliziro kuti): “Idzakhala liti?”
Verse 43 — Surah An-Naziat 79:43
“Uli ndi mphamvu yanji iwe yofotokozera za tsikulo? (Iwe ulibe kuzindikira za nthawiyo kotero kuti ungaitchule kwa iwo)
Verse 44 — Surah An-Naziat 79:44
“Kwa Mbuye wako ndiko kuli mathero ake
Verse 45 — Surah An-Naziat 79:45
“Iwe (ntchito yako) ndikuwachenjeza amene akuiopa; (osati kulengeza zanthawi yake)
Verse 46 — Surah An-Naziat 79:46
“Tsiku limene adzaiona adzakhala ngati sadakhale (pa dziko nthawi yayitali), koma ngati madzulo amodzi kapena masana ake (nthawi ya m’mawa)