Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 80 - Abasa
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Abasa 80:1
“Adachita tsinya (Mneneri) ndi kuyang’ana kumbali
Verse 2 — Surah Abasa 80:2
“Chifukwa chakuti adamdzera wakhungu (kudzamfunsa zokhudzana ndi chipembedzo chake pamene iye adali kuyankhula ndi atsogoleri Achiquraishi)
Verse 3 — Surah Abasa 80:3
“Nanga chingakudziwitse nchiyani kuti mwina iye angadziyeretse (pomvera ulaliki wako watsopano)
Verse 4 — Surah Abasa 80:4
“Kapena akumbukira, ndipo kukumbukirako kumthandiza
Verse 5 — Surah Abasa 80:5
“Koma amene wadzikwaniritsa (ndi chuma chake ndi mphamvu zake)
Verse 6 — Surah Abasa 80:6
“Ameneyo ndi yemwe ukumchitira chidwi
Verse 7 — Surah Abasa 80:7
“Palibe chilichonse pa iwe ngati sadziyeretsa
Verse 8 — Surah Abasa 80:8
“Koma amene wakudzera uku akuthamanga (kufuna maphunziro ndi chiongoko)
Verse 9 — Surah Abasa 80:9
“Ndipo iye akuopa (Allah mu mtima mwake)
Verse 10 — Surah Abasa 80:10
“Za iye, iwe sukusamala, (ukuyikira chidwi kwa wina)
Verse 11 — Surah Abasa 80:11
“Sichoncho! Ndithudi iyi (Qur’an) ndi chikumbutso (chenjezo)
Verse 12 — Surah Abasa 80:12
“Basi, amene wafuna alangizika (ndi Qur’an, ndipo amene sakufuna msiye)
Verse 13 — Surah Abasa 80:13
“(Malangizowa akuchokera) mmakalata olemekezeka (kwa Allah)
Verse 14 — Surah Abasa 80:14
“Apamwamba ndiponso oyeretsedwa (kumbiri iliyonse yopunguka)
Verse 15 — Surah Abasa 80:15
“Omwe ali m’manja mwa Alembi (Angelo)
Verse 16 — Surah Abasa 80:16
“Olemekezeka, omvera
Verse 17 — Surah Abasa 80:17
“Waonongeka (watembeleredwa) munthu. Nkotani kusayamika kwake kotereku
Verse 18 — Surah Abasa 80:18
“Kuchokera mchinthu chanji chimene iye adamulenga
Verse 19 — Surah Abasa 80:19
“Kuchokera ku dontho lamadzi (onyozeka) adamulenga, namkonzeratu mkalengedwe kosiyanasiyana
Verse 20 — Surah Abasa 80:20
“Kenako adamfewetsera njira (yotulukira m’mimba mwa mai ake)
Verse 21 — Surah Abasa 80:21
“Ndipo amamchititsa kuti amwalire namukumbula m’manda
Verse 22 — Surah Abasa 80:22
“Kenako akadzafuna adzamuukitsa (pambuyo pa imfa)
Verse 23 — Surah Abasa 80:23
“Ayi ndithu (munthu) sanakwaniritsebe zimene adamulamula Mbuye wake (Allah chingakhale wakhala nthawi yaitali pa dziko lapansi)
Verse 24 — Surah Abasa 80:24
“Alingalire munthu (mmene chilili) chakudya chake
Verse 25 — Surah Abasa 80:25
“Ndithu Ife timagwetsa mvula yambiri (kuchokera ku mitambo)
Verse 26 — Surah Abasa 80:26
“Kenako timaing’amba nthaka kuti mmera utuluke
Verse 27 — Surah Abasa 80:27
“Ndipo timameretsa m’menemo njere (ya chakudya cha anthu ndi zina zimene amasunga mnkhokwe)
Verse 28 — Surah Abasa 80:28
“Ndi mphesa ndi msipu
Verse 29 — Surah Abasa 80:29
“Ndi mzitona (wabwino) ndi (zipatso za) kanjedza
Verse 30 — Surah Abasa 80:30
“Ndi minda yothothana nthambi za mitengo
Verse 31 — Surah Abasa 80:31
“Ndi zipatso (zodyedwa ndi anthu) ndi msipu (wodyedwa ndi nyama)
Verse 32 — Surah Abasa 80:32
“(Tazimeretsa zimenezo kuti) zikondweretse inu ndi ziweto zanu
Verse 33 — Surah Abasa 80:33
“Choncho likadzafika lipenga logonthetsa mkhutu (ndi kuumitsa makosi)
Verse 34 — Surah Abasa 80:34
“Patsikuli munthu adzathawa m’bale wake
Verse 35 — Surah Abasa 80:35
“Mayi wake ndi bambo wake
Verse 36 — Surah Abasa 80:36
“Mkazi wake ndi ana ake
Verse 37 — Surah Abasa 80:37
“Munthu aliyense mwa iwo, tsiku limenelo adzakhala ndi zakezake zotangwanika nazo. (Sadzalabadira za anzake)
Verse 38 — Surah Abasa 80:38
“Tsiku limenelo nkhope zina zidzakhala zowala
Verse 39 — Surah Abasa 80:39
“Zosekelera ndi zachimwemwe (chifukwa cha nkhani yabwino ya ku Munda wamtendere)
Verse 40 — Surah Abasa 80:40
“Ndipo nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zokutidwa ndi fumbi
Verse 41 — Surah Abasa 80:41
“Mdima udzazikuta
Verse 42 — Surah Abasa 80:42
“Iwo ndi anthu osakhulupirira oipa (olakwira Allah)