Back to Languages

Chichewa - Chapter 81 - At-Takwir

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah At-Takwir 81:1

“Pamene dzuwa lidzakulungidwe (ndikuchotsedwa kuwala kwake)

Verse 2 — Surah At-Takwir 81:2

“Ndi pamene nyenyezi zidzathothoke (ndi kuchoka dangalira lake)

Verse 3 — Surah At-Takwir 81:3

“Ndi pamene mapiri adzayendetsedwe (kuchoka mmalo mwake)

Verse 4 — Surah At-Takwir 81:4

“Ndi pamene ngamira zabere lamiyezi khumi zidzasiidwe (zopanda oziyang’anira)

Verse 5 — Surah At-Takwir 81:5

“Ndi pamene nyama za mtchire zidzasonkhanitsidwe pamodzi (kuchokera mmalo osiyanasiyana chifukwa chakuopsa kwakukulu kwa tsikulo)

Verse 6 — Surah At-Takwir 81:6

“Ndi pamene nyanja zidzayatsidwe moto

Verse 7 — Surah At-Takwir 81:7

“Ndi pamene mizimu idzalumikizidwe (ndi matupi ake)

Verse 8 — Surah At-Takwir 81:8

“Ndi pamene mwana wamkazi yemwe adaikidwa m’manda wamoyo adzafunsidwe

Verse 9 — Surah At-Takwir 81:9

“Ndi tchimo lanji adaphedwera

Verse 10 — Surah At-Takwir 81:10

“Ndi pamene makalata (momwe mudalembedwa zochita za aliyense) adzatambasulidwe ndi kugawidwa (kuti awerengedwe)

Verse 11 — Surah At-Takwir 81:11

“Ndi pamene thambo lidzayalulidwe (kuchoka mmalo mwake)

Verse 12 — Surah At-Takwir 81:12

“Ndi pamene Jahena idzasonkhezeredwe mwamphamvu

Verse 13 — Surah At-Takwir 81:13

“Ndi pamene Jannah idzayandikitsidwe

Verse 14 — Surah At-Takwir 81:14

“(Zikadzachitika zimenezi) mzimu uliwonse udzadziwa zimene wabweretsa (zabwino ndi zoipa)

Verse 15 — Surah At-Takwir 81:15

“Ndikulumbilira nyenyezi zimene zimabwerera masana ndi kutulukanso usiku

Verse 16 — Surah At-Takwir 81:16

“Zomwe zimayenda kenako nkubisika

Verse 17 — Surah At-Takwir 81:17

“Ndi usiku pamene ukulowa

Verse 18 — Surah At-Takwir 81:18

“Ndi m’mawa kukamacha

Verse 19 — Surah At-Takwir 81:19

“Ndithu iyi (Qur’an) ndi liwu la mthenga wa Allah (Jibril) wolemekezeka

Verse 20 — Surah At-Takwir 81:20

“Mwini mphamvu ndi mwini ulemelero kwa Mwini Arsh (Mpando wa chifumu)

Verse 21 — Surah At-Takwir 81:21

“Womveredwa kumeneko ndiponso wokhulupirika (pachivumbulutso)

Verse 22 — Surah At-Takwir 81:22

“Ndipo m’bale wanuyu siwamisala ayi

Verse 23 — Surah At-Takwir 81:23

“Ndithu ndikulumbira kuti (iye Mtumiki) (s.a.w) adamuona (Jibril) mchizimezime (chakum’mawa) chooneka bwino

Verse 24 — Surah At-Takwir 81:24

“Ndipo sali iye (Mtumiki) waumbombo ndi chivumbulutso (koma amafikitsa zonse ndi kuziphunzitsa kwa anthu)

Verse 25 — Surah At-Takwir 81:25

“(Chivumbulutso chomwe chavumbulutsidwachi kwa iye) si mawu a satana wothamangitsidwa (mchifundo cha Allah)

Verse 26 — Surah At-Takwir 81:26

“Nanga mukupita kuti

Verse 27 — Surah At-Takwir 81:27

“(Qur’ani) iyi sichina koma ndi chikumbutso cha zolengedwa zonse

Verse 28 — Surah At-Takwir 81:28

“Kwa yemwe mwa inu akufuna kuyenda mu njira yoongoka

Verse 29 — Surah At-Takwir 81:29

“Ndipo simungafune chinthu mwa inu nokha pokhapokha atafuna Allah Mbuye wa zolengedwa zonse