Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 83 - Al-Mutaffifin
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Mutaffifin 83:1
“Kuonongeka koopsa kukawapeza opunguza miyeso ya malonda
Verse 2 — Surah Al-Mutaffifin 83:2
“Amene amati akamadziyezera zinthu kwa anthu amafuna kulandira miyeso yodzadza
Verse 3 — Surah Al-Mutaffifin 83:3
“Koma pamene iwo akamawayesera pa muyeso wa mbale kapena wa sikelo amapungula (choyenera kulandira ogulawo)
Verse 4 — Surah Al-Mutaffifin 83:4
“Kodi amenewa (akupungula miyeso pamalondawo) sakuganiza kuti adzaukitsidwa
Verse 5 — Surah Al-Mutaffifin 83:5
“Pa tsiku lalikulu (ndiponso loopsa)
Verse 6 — Surah Al-Mutaffifin 83:6
“Tsiku limene adzaimilira anthu pamaso pa Mbuye wa zolengedwa
Verse 7 — Surah Al-Mutaffifin 83:7
“Ayi! Ndithu (siyani chinyengo pamalonda ndi kusalabadira kuuka mmanda); zolembedwa za ntchito ya oipa zili mu Sijjin
Verse 8 — Surah Al-Mutaffifin 83:8
“Nanga nchiyani chitakudziwitse za Sijjin
Verse 9 — Surah Al-Mutaffifin 83:9
“Ameneyu ndi kaundula wamkulu yemwe walembedwa (mkati mwake ntchito za anthu oipa)
Verse 10 — Surah Al-Mutaffifin 83:10
“Chilango chaukali tsiku limenelo chili pa otsutsa
Verse 11 — Surah Al-Mutaffifin 83:11
“Amene akutsutsa za tsiku la malipiro
Verse 12 — Surah Al-Mutaffifin 83:12
“Ndipo palibe angalitsutse koma yekhayo wopyola malire (pochita zoipa), wa machimo ambiri
Verse 13 — Surah Al-Mutaffifin 83:13
“Pamene ma Ayah Athu akuwerengedwa kwa iye (onena za tsiku la malipiro ndikuuka mmanda) amanena kuti: “Izi ndi nthano za anthu akale.”
Verse 14 — Surah Al-Mutaffifin 83:14
“Iyayi, sichoncho! Koma yaphimbidwa mitima yawo ndi dzimbiri (la machimo) omwe akhala akukolola
Verse 15 — Surah Al-Mutaffifin 83:15
“Ayi ndithu iwo (okanira) tsiku limenelo) adzatchingidwa kwa Mbuye wawo; (sadzamuona)
Verse 16 — Surah Al-Mutaffifin 83:16
“Pambuyo pake adzalowa ku Moto; (oyaka)
Verse 17 — Surah Al-Mutaffifin 83:17
“Kenaka adzauzidwa (powaliritsa) “Ichi nchilango chomwe mudali kuchitsutsa (pa dziko lapansi).”
Verse 18 — Surah Al-Mutaffifin 83:18
“Zoona, ndithu kaundula wa anthu abwino (ochita ntchito zabwino) ali mu Illiyyun
Verse 19 — Surah Al-Mutaffifin 83:19
“Nanga nchiyani chitakudziwitse za Illiyyun
Verse 20 — Surah Al-Mutaffifin 83:20
“Ameneyu ndi kaundula (wamkulu) yemwe walembedwa (mkati mwake ntchito za anthu abwino)
Verse 21 — Surah Al-Mutaffifin 83:21
“Amamuyikira umboni (angelo) amene ayandikitsidwa (kwa Allah)
Verse 22 — Surah Al-Mutaffifin 83:22
“Ndithu ochita zabwino adzakhala mu mtendere
Verse 23 — Surah Al-Mutaffifin 83:23
“Atakhala pa mipando ya ulemu uku akuyang’ana (zimene Allah wawapatsa monga mtendere ndi ulemelero)
Verse 24 — Surah Al-Mutaffifin 83:24
“Udzaona kuwala kwa mtendere pa nkhope zawo
Verse 25 — Surah Al-Mutaffifin 83:25
“Adzamwetsedwa vinyo (woyeretsedwa) wotsekeredwa ndi zitsekerero zolimba
Verse 26 — Surah Al-Mutaffifin 83:26
“Komalizira kwake (kwa vinyoyo) kuzikatuluka fungo la misk; kuti akapeze zimenezi, apikisane opikisana
Verse 27 — Surah Al-Mutaffifin 83:27
“Ndipo chosakanizira cha vinyoyo ndi madzi a Tasnim
Verse 28 — Surah Al-Mutaffifin 83:28
“(Tasnim ameneyo) ndi kasupe amene azikamwa amene ayandikitsidwa (kwa Allah)
Verse 29 — Surah Al-Mutaffifin 83:29
“Ndithu amene adachita machimo adali kuwaseka (mwachipongwe) okhulupirira (pa dziko lapansi)
Verse 30 — Surah Al-Mutaffifin 83:30
“(Okhulupirira) akadutsa pafupi ndi iwo ankakodolerana maso (mwachipongwe)
Verse 31 — Surah Al-Mutaffifin 83:31
“Ndipo akabwerera kwa anzawo amabwerera akusangalala (ndi kunyozedwa kwa okhulupirira)
Verse 32 — Surah Al-Mutaffifin 83:32
“Ndipo (nthawi zonse) akawaona Asilamu amanena: “Ndithu awa ndi osokera (chifukwa chomkhulupirira Mtumiki).” (s.a.w)
Verse 33 — Surah Al-Mutaffifin 83:33
“Sanatumizidwe (Akafiri) kukhala ayang’aniri kwa okhulupirira (ndikuwaweruza zakulungama ndi kusokera)
Verse 34 — Surah Al-Mutaffifin 83:34
“Basi lero okhulupirira awaseka osakhulupirira (powabwezera chipongwe chawo chimene ankachita pa dziko lapansi)
Verse 35 — Surah Al-Mutaffifin 83:35
“Atakhala pa mipando ya ulemu uku akuyang’ana (mtendere umene Allah wawapatsa)
Verse 36 — Surah Al-Mutaffifin 83:36
“Kodi alipidwa osakhulupirira pa zomwe ankachita zija (pa dziko lapansi)