Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 84 - Al-Inshiqaq
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Inshiqaq 84:1
Pamene thambo lidzang’ambike (kusonyeza mapeto ake)
Verse 2 — Surah Al-Inshiqaq 84:2
“Ndikudzamvera lamulo la Mbuye wake; ndipo lidzayenera kutero
Verse 3 — Surah Al-Inshiqaq 84:3
“Ndiponso pamene nthaka idzatambasulidwe (pogumuka mapiri ake ndikuchoka zitunda zake)
Verse 4 — Surah Al-Inshiqaq 84:4
“Ndi kutaya zomwe zidali mkati mwake ndi kukhala yopanda kanthu
Verse 5 — Surah Al-Inshiqaq 84:5
“Ndikudzamvera lamulo la Mbuye wake; ndipo lidzayenera kutero. (Choncho zikadzachitika zimenezi ndiye kuti munthu adzalandira mphoto ya zochita zake)
Verse 6 — Surah Al-Inshiqaq 84:6
“E iwe munthu! Ndithudi iwe ukubwerera kwa Mbuye wako (ndi zochita zako zabwino kapena zoipa), kubwerera kotsimikizika, ndipo iwe ukumana (ndi zotsatira za zochitachita zako)
Verse 7 — Surah Al-Inshiqaq 84:7
“Tsono amene adzapatsidwe kaundula wa zochita zake kudzanja la manja
Verse 8 — Surah Al-Inshiqaq 84:8
“Basi iye, adzawerengedwa, kuwerengedwa kopepuka
Verse 9 — Surah Al-Inshiqaq 84:9
“Ndipo adzabwerera kwa anthu ake (okhulupirira) ali wokondwa
Verse 10 — Surah Al-Inshiqaq 84:10
“Koma yemwe adzapatsidwe kaundula wa zochita zake chakumanzere kudzera kumbuyo kwa msana wake (chifukwa chomunyoza)
Verse 11 — Surah Al-Inshiqaq 84:11
“Basi, iye adzaitana imfa (kuti imufikire; kuti afe apumule, koma siidzamufikira)
Verse 12 — Surah Al-Inshiqaq 84:12
“Ndipo adzalowa ku Moto woyaka
Verse 13 — Surah Al-Inshiqaq 84:13
“Kamba kakuti iye adali wokondwa; (kukondwa kwa machimo) pamodzi ndi anthu ake (osaganizira za mathero ake)
Verse 14 — Surah Al-Inshiqaq 84:14
“Ndithudi, amaganiza kuti sadzabwerera (kwa Allah ndiponso sadzawerengedwa)
Verse 15 — Surah Al-Inshiqaq 84:15
“Chifukwa ninji (asabwelere)? Ndithu Mbuye wake adali kumuona. (Choncho alipidwa zimene adachita)
Verse 16 — Surah Al-Inshiqaq 84:16
“Choncho ndikulumbilira kufiira kwa dzuwa (pamene likulowa)
Verse 17 — Surah Al-Inshiqaq 84:17
“Ndi usiku ndi zimene wasonkhanitsa
Verse 18 — Surah Al-Inshiqaq 84:18
“Ndi mwezi ukakwanira dangalira (lake)
Verse 19 — Surah Al-Inshiqaq 84:19
“Ndithudi mudzachoka apa kunka apa (pa moyo uno mpakana umene uli nkudza)
Verse 20 — Surah Al-Inshiqaq 84:20
“Kodi nchiyani chikuwaletsa iwo (okanira) kukhulupirira (Allah ndi kuuka kumanda, zisonyezo zake zitaonekera poyera)
Verse 21 — Surah Al-Inshiqaq 84:21
“Ndipo ikawerengedwa kwa iwo Qur’an, sagwetsa pansi nkhope zawo (modzichepetsa)
Verse 22 — Surah Al-Inshiqaq 84:22
“Koma amene sadakhulupirire akutsutsa basi (chifukwa cha makani ndi kudzikweza)
Verse 23 — Surah Al-Inshiqaq 84:23
“Ndipo Allah akudziwa (bwinobwino) zimene akuzisonkhanitsa
Verse 24 — Surah Al-Inshiqaq 84:24
“Choncho, auze nkhani yachilango chopweteka
Verse 25 — Surah Al-Inshiqaq 84:25
“Kupatula awo amene akhulupirira ndikuchita ntchito zabwino, kwa iwo kuli malipiro osatha