Back to Languages

Chichewa - Chapter 85 - Al-Buruj

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Buruj 85:1

“Ndikulumbilira thambo lomwe liri ndi Buruj (Nyenyezi zikuluzikulu)

Verse 2 — Surah Al-Buruj 85:2

“Ndi tsiku lolonjezedwa (kuwerengedwa ndi kulipidwa)

Verse 3 — Surah Al-Buruj 85:3

“Ndi woikira umboni, ndi woikiridwa umboni

Verse 4 — Surah Al-Buruj 85:4

“Atembeleredwa eni ngalande zamoto (zomwe adali kuwazunzira okhulupirira Allah, achimuna ndi achikazi)

Verse 5 — Surah Al-Buruj 85:5

“(Ngalande) za moto wankhuni (zambiri zomwe adali kuzikoleza ndikuotchera okhulupirira)

Verse 6 — Surah Al-Buruj 85:6

“Pamene iwo adali chikhalire m’mphepete mwa ngalandezo

Verse 7 — Surah Al-Buruj 85:7

“Uku iwo akuyang’ana zomwe amawachitira okhulupirira, (pootchedwa ndi moto)

Verse 8 — Surah Al-Buruj 85:8

“Sadaone choipa chilichonse mwa iwo koma chifukwa choti adakhulupirira Allah mwini mphamvu zonse ndiponso mwini kuyamikidwa

Verse 9 — Surah Al-Buruj 85:9

“Yemwe ufumu wakumwamba ndi pansi ndiWake; ndipo Allah ndi mboni pachilichonse

Verse 10 — Surah Al-Buruj 85:10

“Ndithu amene ayesa mayeso okhulupirira achimuna ndi achikazi (pa chipembedzo chawo ndi mazunzo ndi chilango cha moto), pambuyo pake osalapa (pa zimenezi), adzalandira chilango cha Jahena ndiponso chilango cha moto wopsereza

Verse 11 — Surah Al-Buruj 85:11

“Ndithudi amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, adzakhala ndi Minda yamtendere (momwe) mitsinje ikuyenda pansi pake; kumeneko ndiko kupambana kwakukulu

Verse 12 — Surah Al-Buruj 85:12

“Ndithu kulanga kwa Mbuye wako (kwa anthu achinyengo), ndi kwaukali kwambiri

Verse 13 — Surah Al-Buruj 85:13

“Iye, (Mmodzi yekha) ndi amene adayambitsa zolengedwa ndiponso ndi Yemwe adzazibweze (pambuyo poonongeka)

Verse 14 — Surah Al-Buruj 85:14

“Iye, ndi Wokhululuka (kwa amene walapa kwa Iye), ndiponso Wokonda kwambiri (amene akumkonda ndi kumumvera)

Verse 15 — Surah Al-Buruj 85:15

“Mwini Arsh (Mpando wachifumu), (ndiponso) Wolemekezeka (mmene alili ndi mbiri Zake)

Verse 16 — Surah Al-Buruj 85:16

“Wochita zimene wafuna, (ndipo chimene wafuna sichikanika)

Verse 17 — Surah Al-Buruj 85:17

“Kodi yakufika nkhani ya magulu a nkhondo

Verse 18 — Surah Al-Buruj 85:18

“Firiaun (Farawo) ndi Samudu, (ndi chilango chimene chidawapeza chifukwa chakulimbikira kwawo pa zinthu zopanda pake)

Verse 19 — Surah Al-Buruj 85:19

“Koma amene sadakhulupirire ali mkati motsutsa basi

Verse 20 — Surah Al-Buruj 85:20

“Koma Allah awazinga mbali zonse

Verse 21 — Surah Al-Buruj 85:21

“Koma iyi ndi Qur’an yolemekezeka

Verse 22 — Surah Al-Buruj 85:22

“Yomwe idachokera mu ubawo (chisileti chachikulu) wotetezedwa (ndi manja alionse, osintha kanthu kapena kuonjezerapo)