Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 86 - At-Tariq
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah At-Tariq 86:1
“Ndikulumbilira ku mwamba ndi Nyenyezi imene imadza usiku
Verse 2 — Surah At-Tariq 86:2
“Chitakudziwitse nchiyani za Nyenyezi yodza usikuyo
Verse 3 — Surah At-Tariq 86:3
“Imeneyo ndi nyenyezi yowala kwambiri (mu mdima)
Verse 4 — Surah At-Tariq 86:4
“Ndithudi palibe mzimu uliwonse koma uli ndi msungi wake (amene akuuyang’anira ndikulemba zonse zochita zake)
Verse 5 — Surah At-Tariq 86:5
“Aganizire munthu, kodi adalengedwa kuchokera kuchiyani
Verse 6 — Surah At-Tariq 86:6
“Adalengedwa kuchokera ku madzi ofwamphuka
Verse 7 — Surah At-Tariq 86:7
“Amatuluka kuchokera pakati pa mafupa a msana (wa mwamuna) ndi chifuwa (cha mkazi)
Verse 8 — Surah At-Tariq 86:8
“Ndithu Iye ndiwakutha, kumbwezeranso (ku moyo pa mbuyo pa imfa)
Verse 9 — Surah At-Tariq 86:9
“Tsiku limene zobisika zonse zidzaonekera poyera
Verse 10 — Surah At-Tariq 86:10
“Munthu sadzakhala ndi mphamvu (tsiku limenelo zodzitetezera iye mwini) ndiponso sadzakhala ndi mtetezi
Verse 11 — Surah At-Tariq 86:11
“Ndikulumbiliranso mitambo yobweretsabweretsa mvula
Verse 12 — Surah At-Tariq 86:12
“Ndi nthaka imene imang’ambika (potulutsa m’mera)
Verse 13 — Surah At-Tariq 86:13
“Ndithudi iyi (Qur’an) ndi mawu olekanitsa (Haqq ndi Bâtwil - choona ndi chonama)
Verse 14 — Surah At-Tariq 86:14
“Imeneyi sinkhambakamwa
Verse 15 — Surah At-Tariq 86:15
“Ndithudi iwo akukonza chiwembu
Verse 16 — Surah At-Tariq 86:16
“Nanenso ndikuwakonzera chiwembu (champhamvu kwambiri chimene sangathe kuchipewa)
Verse 17 — Surah At-Tariq 86:17
“Basi, apatse nthawi osakhulupirira apatse nthawi pang’ono, (aona posachedwa)