Back to Languages

Chichewa - Chapter 90 - Al-Balad

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Balad 90:1

“Ndikulumbilira mzinda uwu (wa Makka)

Verse 2 — Surah Al-Balad 90:2

“Ndipo iwe udzatsikira mu mzindawu mwa ufulu (ndi kuuonjezera ulemelero)

Verse 3 — Surah Al-Balad 90:3

“Ndiponso ndikulumbilira chobereka ndi choberekedwa, (kudzera mwa iwo mtundu wa anthu udasungidwa)

Verse 4 — Surah Al-Balad 90:4

“Ndithudi tamulenga munthu mmavuto (kuyambira chiyambi chake mpaka malekezero a moyo wake)

Verse 5 — Surah Al-Balad 90:5

“Kodi (munthu wolengedwa ndi mavutoyu) akuganiza kuti palibe amene angamuthe

Verse 6 — Surah Al-Balad 90:6

“Akunena (monyadira kuti): “Ndaononga chuma chambiri (chifukwa choletsa Chisilamu kufala).”

Verse 7 — Surah Al-Balad 90:7

“Kodi akuganiza kuti palibe akumuona

Verse 8 — Surah Al-Balad 90:8

“Kodi sitidampangire maso awiri (amene akuyang’anira)

Verse 9 — Surah Al-Balad 90:9

“Ndilirime ndi milomo iwiri (zimene akulankhulira)

Verse 10 — Surah Al-Balad 90:10

“Ndipo tamlongosolera njira ziwiri: (yabwino ndi yoipa, ndipo tampatsa mphamvu yosankhira njira imene akufuna)

Verse 11 — Surah Al-Balad 90:11

“Kodi walikwera phiri lovutalo (lomwe lingakamfikitse ku Jannah)

Verse 12 — Surah Al-Balad 90:12

“Nanga nchiyani chakudziwitsa za kukwera phiri lovutalo

Verse 13 — Surah Al-Balad 90:13

“(Kutero ndiko) kupereka ufulu kwa kapolo

Verse 14 — Surah Al-Balad 90:14

“Kapena kuwadyetsa (osowa) pa tsiku la njala

Verse 15 — Surah Al-Balad 90:15

Verse 16 — Surah Al-Balad 90:16

“Kapena wosauka wa fumbi lokhalokha (chifukwa cha kuvutika kwambiri)

Verse 17 — Surah Al-Balad 90:17

“Komanso nakhala mmodzi mwa okhulupirira ndikumalangizana za kupirira, ndi kumalangizananso za chifundo

Verse 18 — Surah Al-Balad 90:18

“Otero ndiwo (anthu abwino) a ku dzanja lamanja

Verse 19 — Surah Al-Balad 90:19

“Koma amene sanakhulupirire Ayah Zathu, ndi anthu a kudzanja lamanzere (oipa)

Verse 20 — Surah Al-Balad 90:20

“Moto wozungulira mbali zonse udzakhala pa iwo (ndikuwatsekera makomo)