Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 92 - Al-Layl
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Layl 92:1
“Ndikulumbilira usiku pamene ukuphimba (chilichonse)
Verse 2 — Surah Al-Layl 92:2
“Ndi usana pamene kukuyera
Verse 3 — Surah Al-Layl 92:3
“Ndiponso Yemwe adalenga chachimuna ndi chachikazi
Verse 4 — Surah Al-Layl 92:4
“Ndithu zochita zanu nzosiyanasiyana
Verse 5 — Surah Al-Layl 92:5
“Tsono yemwe akupereka (pa njira ya Allah) ndikumamuopa (Mbuye wake ndikupewa zoletsedwa)
Verse 6 — Surah Al-Layl 92:6
“Ndikumavomereza zinthu zabwino; (komwe kuli kukhulupirira Allah mwanzeru)
Verse 7 — Surah Al-Layl 92:7
“Choncho timufewetsera njira yompititsa ku zabwino
Verse 8 — Surah Al-Layl 92:8
“Koma uyo achite umbombo ndikuganiza za kuti iye payekha ngokwana
Verse 9 — Surah Al-Layl 92:9
“Ndi kumatsutsa zinthu zabwino
Verse 10 — Surah Al-Layl 92:10
“Choncho timufewetsera njira yompititsa ku mavuto (a muyaya)
Verse 11 — Surah Al-Layl 92:11
“Ndipo chuma chake sichidzamthandiza (chilichonse) akadzagwera ku Moto
Verse 12 — Surah Al-Layl 92:12
“Ndithu Ife ndi amene timawalongosolera anthu njira yabwino ndi njira yoipa
Verse 13 — Surah Al-Layl 92:13
“Ndipo ndithu moyo womaliza ndi moyo woyamba uli m’manja mwathu
Verse 14 — Surah Al-Layl 92:14
“Basi, ndikukuchenjezani za Moto woyaka mwa mphamvu
Verse 15 — Surah Al-Layl 92:15
“Sakaulowa koma (kafiri) woipitsitsa kwambiri
Verse 16 — Surah Al-Layl 92:16
“Yemwe amatsutsa (choona) ndi kunyoza (zisonyezo za Allah)
Verse 17 — Surah Al-Layl 92:17
“Koma yemwe akuopa Allah kwambiri akatalikitsidwa ndi Moto
Verse 18 — Surah Al-Layl 92:18
“Amene akupereka chuma chake ndi cholinga chodziyeretsa
Verse 19 — Surah Al-Layl 92:19
“Ndipo palibe aliyense kwa iye, amene adamchitira za chifundo zomwe zikulipidwa
Verse 20 — Surah Al-Layl 92:20
“Koma (akuchita zimenezi) kufuna chikondi cha Mbuye wake Wapamwambamwamba
Verse 21 — Surah Al-Layl 92:21
“Ndipo posachedwa adzasangalala