Back to Languages

Chichewa - Chapter 93 - Ad-Duhaa

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Ad-Duhaa 93:1

“Ndikulumbilira mmawa dzuwa litakwera (imene ili nthawi yantchito)

Verse 2 — Surah Ad-Duhaa 93:2

“Ndi usiku pamene ukuvindikira

Verse 3 — Surah Ad-Duhaa 93:3

“Sadakusiye Mbuye wako (iwe Mneneri) (s.a.w) ndiponso sadakude

Verse 4 — Surah Ad-Duhaa 93:4

“Ndithu moyo watsiku lirimkudza ndi wabwino kwa iwe kuposa umoyo woyambawu

Verse 5 — Surah Ad-Duhaa 93:5

“Ndithu posachedwapa akupatsa Mbuye wako (zabwino zamdziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro) ndipo ukondwera

Verse 6 — Surah Ad-Duhaa 93:6

“Kodi sadakupeze uli wa masiye ndipo adakupatsa pokhala pabwino

Verse 7 — Surah Ad-Duhaa 93:7

“Ndipo adakupeza uli wosazindikira (Qur’an) nakuongola (pokuzindikiritsa Qur’aniyo ndi malamulo a chipembedzo)

Verse 8 — Surah Ad-Duhaa 93:8

“Ndiponso adakupeza uli wosauka nakulemeretsa

Verse 9 — Surah Ad-Duhaa 93:9

“Basi, wamasiye usamchitire nkhanza

Verse 10 — Surah Ad-Duhaa 93:10

“Ndiponso wopempha usamukalipire

Verse 11 — Surah Ad-Duhaa 93:11

“Tsono mtendere wa Mbuye wako uwutchule (pothokoza ndi kugwira ntchito zabwino)