Back to Languages

Chichewa - Chapter 95 - At-Tin

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah At-Tin 95:1

“Ndikulumbilira mitengo ya Mkuyu ndi Zitona (pansi pa mitengo imeneyi Ibrahim ndi Nuh (Nowa) adapeza uneneri

Verse 2 — Surah At-Tin 95:2

“Ndi phiri la Sinai (pamene Allah adamulankhulira Mûsa)

Verse 3 — Surah At-Tin 95:3

“Ndiponso mzinda uwu (wolemekezeka) wamtendere; (Makka, womwe adapatsiridwa uneneri Muhammad) (s.a.w)

Verse 4 — Surah At-Tin 95:4

“Palibe chikaiko, tamulenga munthu mkalengedwe kabwino, kolingana (ndipo ali ndi mbiri zabwino)

Verse 5 — Surah At-Tin 95:5

“Pambuyo pake tamubwezera pansi kumposa wa pansi

Verse 6 — Surah At-Tin 95:6

“Kupatula amene akhulupirira ndikumachita zabwino, adzakhala nawo iwo malipiro osatha

Verse 7 — Surah At-Tin 95:7

“Tsono nchiyani chakuchititsa kuti ukanire kuuka ndi malipiro pambuyo (poona mphamvu zathu pa chilichonse)

Verse 8 — Surah At-Tin 95:8

“Kodi Allah si Muweruzi wa nzeru kuposa aweruzi onse