Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 99 - Az-Zalzalah
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Az-Zalzalah 99:1
“Likadzagwedezedwa dziko lapansi kugwedezeka kwake kwamphamvu
Verse 2 — Surah Az-Zalzalah 99:2
“Ndipo nthaka idzatulutsa mitolo yake (zinthu zomwe zidali mkati mwake, monga akufa ndi miyala ya mtengo wapatali)
Verse 3 — Surah Az-Zalzalah 99:3
“Ndipo munthu adzanena (mwa mantha, ndikudabwa nthawi imeneyo). Ha! Yatani nthaka, (kodi Qiyâma yafika)
Verse 4 — Surah Az-Zalzalah 99:4
“Tsiku limenelo idzanena nkhani zake zonse, (zabwino kapena zoipa)
Verse 5 — Surah Az-Zalzalah 99:5
“Pakuti Mbuye wako adzailamula kutero (kuti igwedezeke ndikunena zimene zinkachitika pamwamba pake)
Verse 6 — Surah Az-Zalzalah 99:6
“Tsiku limenelo anthu adzachoka (m’manda) ali m’magulu obalalika kuti akasonyezedwe ntchito zawo (ndikudziwa chiwerengero chawo chimene chili kwa Allah)
Verse 7 — Surah Az-Zalzalah 99:7
“Choncho, amene angachite chabwino cholemera ngati kanjere kakang’ono, adzaona malipiro ake
Verse 8 — Surah Az-Zalzalah 99:8
“Ndipo amene angachite choipa cholemera ngati kanjere kakang’ono, adzaona malipiro ake. (Allah sachitira chinyengo aliyense)