Back to Languages

    Chichewa - Chapter 102

    Translation by Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

    Verse 1

    Mpikisano wosonkhanitsa chuma cha padziko wakutangwanikitsani inu

    Verse 2

    Mpaka pamene inu mulowa m’manda

    Verse 3

    Iyayi! Inu mudzadziwa

    Verse 4

    Kachiwiri, Iyayi! Inu mudzadziwa

    Verse 5

    Iyayi! Inu mukanadziwa kwenikweni

    Verse 6

    Ndithudi inu mudzaona moto woyaka

    Verse 7

    Kachiwiri inu mudzauona ndi maso anu

    Verse 8

    Ndipo patsiku limeneli inu mudzafunsidwa za chisangalalo chimene munali kuchita