Back to Languages
Chichewa - Chapter 104
Translation by Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula
Verse 1
Tsoka kwa aliyense amene amajeda ndi kuononga mbiri ya anzake
Verse 2
Amene amasonkhanitsa chuma chake ndi kumachiwerenga
Verse 3
Iye amaganiza kuti chuma chake chidzamuchititsa iye kukhala ndi moyo wamuyaya
Verse 4
Iyayi! Ndithudi iye adzaponyedwa ku moto woononga
Verse 5
Kodi chidzakuuza kuti moto woononga ndi chiyani
Verse 6
Ndi moto wa Mulungu umene Mwini wake anauyatsa
Verse 7
Umene umafuka m’mitima ya anthu
Verse 8
Ndithudi udzawatsekereza mbali iliyonse
Verse 9
M’sanamila zoima