Back to Languages

    Chichewa - Chapter 11

    Translation by Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

    Verse 1

    Alif Lam Ra. Ndi Buku limene mavesi ake akonzedwa bwino. Ndipo adafotokozedwa mwatsatane tsatane kuchokera kwa Mwini nzeru ndi wodziwa

    Verse 2

    Kuti musapembedze wina aliyense koma Mulungu. Ndithudi ine ndine wochokera kwa Iye wochenjeza ndi wobweretsa nkhani zabwino

    Verse 3

    Ndikuti mupemphe chikhululukiro kwa Ambuye wanu ndipo lapani kwa Iye yekha kuti Iye akupatseni zinthu zabwino mpaka pa nthawi yoikidwa. Ndi kupereka kwa aliyense wochita zabwino chisomo chake chomuyenera. Ndipo ngati inu mukana, ine ndichita mantha ndi chilango chimene chingadze pa inu patsiku lalikulu

    Verse 4

    Ndi kwa Mulungu kumene nonse mudzabwerera ndipo Iye ali ndi mphamvu pa zinthu zonse

    Verse 5

    Zoonadi! Iwo amakuta mitima yawo kuti akhoza kubisala kwa Iye. Ndithudi ngakhale pamene iwo avala zovala zawo, Iye amadziwa zonse zimene akubisa ndi zimene akuulula. Iye amadziwa zonse zimene zili m’mitima mwawo

    Verse 6

    Ndipo palibe cholengedwa padziko lapansi chimene chakudya chake sichichokera kwa Mulungu. Ndipo Iye amadziwa malo ake okhala ndi malo ake a mpumulo. Zonse zili m’Buku lofotokozera bwino zinthu

    Verse 7

    Iye ndi amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi m’masiku asanu ndi limodzi ndipo Mpando wake udali pamwamba pa madzi kuti akuyeseni kuti ndani wa inu amene ali ndi ntchito zabwino. Ndipo iwe ukadanena kuti: “Inu ndithudi mudzaukitsidwa pambuyo pa kufa,” anthu osakhulupirira akadanena kuti: “Ichi si china chilichonse koma matsenga enieni.”

    Verse 8

    Ndipo ngati Ife titachedwetsa chilango chawo mpaka pa tsiku lokhazikitsidwa, iwo adzafunsa kuti: “Nanga ndi chifukwa chiyani tsikulo lili kuchedwa?” Ndithudi pa tsiku limene izi zidzachitika, palibe chilichonse chimene chingadzapirikitse chilangocho ndipo zoopsa zimene iwo ali kuseka zidzawazungulira iwo onse

    Verse 9

    Ndipo ngati Ife timulawitsa munthu chifundo chathu kenaka ndi kumulanda, ndithudi, iye amadandaula ndiponso amakhala osuliza

    Verse 10

    Koma ngati Ife titamuonetsa munthu chisoni chathu, pambuyo pa mavuto amene adapeza, iye adzati: “Mavuto atha kwa ine” Ndithudi iye amakhala mosalabadira ndiponso modzikweza kwambiri

    Verse 11

    Kupatula iwo amene amapirira ndi kuchita ntchito zabwino. Iwo adzakhala ndi chikhululukiro ndi malipiro akulu

    Verse 12

    Mwina iwe ukhoza kusiya kunena zina za zimene zavumbulutsidwa kwa iwe ndi kukhala ovutika mu mtima chifukwa chakuti iwo amanena kuti, “Bwanji chuma sichidatumizidwe kwa iye kapena bwanji Mngelo sadadze pamodzi ndi iye?” Komatu iwe ndiwe wochenjeza. Ndipo Mulungu ndiye Msungi wa zinthu zonse

    Verse 13

    Kapena iwo akunena kuti: “Iye wapeka yekha!” Nena, “Nanunso bweretsani mitu khumi yofanana ndi yopekedwayi. Ndipo itananiwinaamenemungathekumuitanakupatulaMulungu ngati muli kunena zoona.”

    Verse 14

    Akapanda kukuyankha, dziwa kuti chivumbulutso chatumizidwa ndi nzeru ya Mulungu. Ndipo kuti kulibe wina woti apembedzedwe kupatula Iye yekha. Kodi tsopano mudzakhala ogonjera

    Verse 15

    Aliyense amene afuna moyo wa m’dziko lino pamodzi ndi zokondweretsa zake, Ife tidzawalipira molingana ndi ntchito zawo , mopanda kuchotsera chilichonse

    Verse 16

    Awa ndiwo anthu amene sadzapeza chilichonse m’moyo umene uli nkudza kupatula moto ndipo zonse zimene amachita pa dziko lapansi zidzaonongeka ndiponso ntchito zawo zimene ankachita zidzakhala zopanda pake

    Verse 17

    Kodi iwo amene amadalira umboni wooneka wochokera kwa Ambuye wawo, umene mboni yochokera kwa Iye amautsatira, ndipo iwo usanadze, linadza Buku la Mose, ulangizi ndi chisomo, iwo amakhulupirira koma a mpatuko amene amalikana, kumoto ndiko kudzakhala malo awo okumana. Motero iwe usakaike za ilo. Ndithudi ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wako koma anthu ambiri sakhulupirira

    Verse 18

    Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu? Anthu otero adzaonetsedwa pamaso pa Ambuye wawo ndipo mboni zidzati: “Awa ndiwo amene anali kunamizira Ambuye wawo.” Mosakaika! Matemberero a Mulungu ali pa anthu ochita zoipa

    Verse 19

    Iwo amene amaletsa anzawo kuti asatsatire njira ya Mulungu ndipo amafuna kuti njira ya Mulungu ikhale yopindika ndiponso amakana kuti kuli moyo wina umene uli nkudza

    Verse 20

    Wotere sadzathawa padziko lapansi ndiponso alibe owateteza kupatula Mulungu! Chilango chawo chidzaonjezeredwa chifukwa chakuti iwo samafuna kumva ndiponso samaona

    Verse 21

    Awa ndiwo amene ataya mizimu yawo ndipo zinthu zawo zonse zabodza zidzawathawira

    Verse 22

    Ndithudi iwo ndiwo amene sadzapindula zambiri mmoyo umene uli nkudza

    Verse 23

    Ndithudi iwo amene akhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, ndipo amadzichepetsa kwambiri pamaso pa Ambuye wawo, iwo adzakhala eni ake a Paradiso ndipo kumeneko adzakhalako mpaka kalekale

    Verse 24

    Fanizo la magulu awiri a anthu lili ngati munthu wakhungu ndi wosamva, wopenya ndi wakumva. Kodi magulu awiriwa ndi ofanana? Kodi simungaganize pamenepa

    Verse 25

    Zoonadi tidamutumiza Nowa kwa anthu ake nati: “Ndithudi ine ndine mchenjezi wanu weniweni

    Verse 26

    Kuti musapembedze wina aliyense koma Mulungu, ndithudi, ine ndili kukuderani nkhawa pa chilango cha tsiku lowawa.”

    Verse 27

    Akuluakulu osakhulupirira amene adali pakati pa anthu ake adati: “Ife tili kukuona iwe ngati munthu onga ife tomwe ndiponso tili kuona kuti onse amene ali kukutsatira kuti ndi anthu apansi kwambiri pakati pathu ndiponso iwo akutsatira iwe osaganiza. Ndipo ife sitili kuona china chilichonse mwa iwe chopambana ife ndipo, kunena moona, tikuganiza kuti inu ndinu abodza.”

    Verse 28

    Iye adati: “Oh inu anthu anga! Mukuona bwanji? Ngati ine ndili ndi umboni wochokera kwa Ambuye wanga ndiponso wandipatsa chifundo kuchokera kwa Iye, ndipo umboniwo wabisika kwa inu. Kodi ife tingakuumirizeni kuti mumvomere pamene mukunyansidwa nawo?”

    Verse 29

    “oh inu anthu anga! Ine sindikukupemphani chuma chifukwa cha ichi, malipiro anga sali kwa wina koma Mulungu yekha. Ndipo ine sindiwathamangitsa amene akhulupirira. Ndithudi, iwo adzakumana ndi Ambuye wawo. Koma ine ndikukuonani kuti ndinu anthu osadziwa.”

    Verse 30

    “oh inu anthu anga! Ndani anganditeteze ine kwa Mulungu ngati nditawapitikitsa iwo? Kodi inu simungaganizire pamenepa?”

    Verse 31

    “Ine sindili kunena kwa inu kuti ndili ndi Nkhokwe za chuma cha Mulungu kapena kuti ndimadziwa zinthu zobisika. Ine sindili kunena kuti ndine Mngelo ayi ndiponso ine sindinena za iwo amene maso anu akuwanyoza kuti Mulungu sadzawapatsa zokoma zake. Mulungu amadziwa bwinobwino zonse zimene zili m’mitima mwawo, chifukwa nditatero, ndithudi, ine ndidzakhala m’modzi wa anthu olakwa.”

    Verse 32

    Iwo anati, “Iwe Nowa! Iwe watsutsana nafe kwambiri. Tsopano bweretsa msangamsanga chilango chimene uli nkutiopsyeza nacho ngati uli mmodzi wa anthu onena zoona!”

    Verse 33

    Iye adati, “Mulungu yekha adzakubweretserani chilango chake pamene Iye afuna. Ndipo inu simudzathawa ai.”

    Verse 34

    “Ndiponso ulangizi wanga siudzakuthandizani ngakhale nditafuna kukulangizani ngati chifuniro cha Mulungu ndi kukusocheretsani. Iye ndi Ambuye wanu ndipo ndi kwa Iye mudzabwerera.”

    Verse 35

    Kapena iwo akunena kuti, “Iye wapeka.” Nena, “Ngati ine ndapeka, tchimo ndi langa koma ine ndili nazo kutali zoipa zimene mukuchita.”

    Verse 36

    Ndipo Mau a Mulungu adavumbulutsidwa kwa Nowa ponena kuti: “Palibe mmodzi mwa anthu ako amene adzakhulupirira kupatula okhawo amene akhulupirira kale. Motero usamve chisoni chifukwa cha zimene anali kuchita.”

    Verse 37

    “Ndipo panga chombo pamaso pathu ndi chilamulo chathu ndipo usalankhule mmalo mwa anthu ochimwa. Ndithudi onse adzamizidwa m’madzi.”

    Verse 38

    Pamene iye adayamba kupanga chombo, ndipo nthawi zonse pamene akuluakulu a anthu ake anali kudutsa pafupi ndi iye, iwo amamuchita chipongwe. Iye adati: “Ngati mukutichita chipongwe, nafenso tidzakubwezerani chipongwe monga mmene mukutichitira ife.”

    Verse 39

    “Ndipo inu mudzadziwa posachedwa yemwe chilango chochititsa manyazi chidzamfikira, ndiponso iwo amene adzalandira chilango chosatha.”

    Verse 40

    Kufikira pamene chilamulo chathu chidadza, ndipo nthaka idayamba kutulutsa madzi. Ife tinati: “Lowetsa m’chombo zinthu ziwiriziwiri, (chachimuna ndi chachikazi), anthu a banja lako kupatula iye amene chiweruzo chaperekedwa kale ndi iwo amene akhulupilira. Koma si ambiri amene adali okhulupirira ndi iye kupatula ochepa okha

    Verse 41

    Iye adati, “Kwerani m’menemo, M’dzina la Mulungu chidzayenda mnjira yake ndipo chidzaima pamalo pofunikira. Ndithudi Ambuye wanga ndi wokhululukira ndipo ndi wachisoni chosatha.”

    Verse 42

    Motere icho chinayenda pa mafunde okhala ngati mapiri, ndipo Nowa adamuitana mwana wake amene adaima pambali. “oh mwana wanga! Kwerachombopamodzindiifendipousakhalepamodzindi anthu osakhulupirira.”

    Verse 43

    Iye adati: “Ine ndidzathawira ku phiri limene lidzanditeteza ku chigumula cha madzi.” Nowa adati, “Lero palibe woteteza wina ku lamulo la Mulungu kupatula yekhayo amene Mulungu adzamuonetsera chisomo chake.” Ndipo funde lidatchinga pakati pawo ndipo mwana wa Nowa anali mmodzi wa omizidwa

    Verse 44

    Ndipo kudanenedwa: “Nthaka meza madzi ako! Ndi kumwamba siya kugwetsa mvula.” Chigumula chinasiya ndipo chifuniro cha Mulungu chinakwaniritsidwa. Ndipo chombo chinadzaima pa phiri la Al Judi ndipo panamveka mawu onena kuti: “Chionongeko chili kwa anthu ochita zoipa.”

    Verse 45

    Ndipo Nowa adaitana kwa Ambuye wake nati: “Ambuye! Ndithudi mwana wanga ndi mmodzi wa anthu a banja langa. Lonjezo lanu, ndithudi, ndi loona. Inu ndinu oweruza bwino kuposa oweruza onse.”

    Verse 46

    Mulungu adati: “Iwe Nowa! Ndithudi iye si wabanja lako ayi. Ndithudi ntchito zake si zabwino motero usandifunse zinthu zimene iwe siudziwa. Ndili kukuchenjeza kuti usakhale mugulu la mbuli ayi.”

    Verse 47

    Nowa adati: “Ine ndipempha chitetezo chanu, Ambuye, chifukwa chokupemphani zinthu zimene ine sindili kuzidziwa. Ndipo Inu ngati simundikhululukira ndi kundimvera ine chisoni, ndithudi, ine ndidzakhala mmodzi wa anthu olephera.”

    Verse 48

    Kudanenedwa: “Iwe Nowa! Tsika pa mtunda ndi mtendere wochokera kwa Ife ndi madalitso akhale kwa iwe ndi kugulu la anthu amene ali nawe, koma anthu onse tidzawasangalatsa pa kanthawi ndipo pambuyo pake chidzawapezanso chilango chowawa chochokera kwa Ife.”

    Verse 49

    Zimenezi ndi nkhani zobisika zimene tikuvumbulutsa kwa iwe, zimene iwe kapena anthu ako samazidziwa chisanabwere chivumbulutso ichi. Motero pirira. Ndithudi mapeto abwino ndi a iwo amene amuopa Mulungu

    Verse 50

    Ndipo kwa mtundu wa Aad, tidatumiza m’bale wawo Hud. Iye adati: “Oh anthu anga! Pembedzani Mulungu. Inu mulibe mulungu wina kupatula Iye yekha. Ndithudi inu simuchita china chili chonse koma kupeka bodza basi.”

    Verse 51

    “oh anthu anga! Ine sindikukupemphani malipiro pazimenezi. Malipiro anga sali ndi wina koma ali ndi Iye amene adandilenga. Kodi simutha kumva zimenezi?”

    Verse 52

    “oh Anthu anga! Mpempheni Ambuye wanu chikhululukiro ndipo lapani kwa Iye chifukwa Iye adzakutumizirani mvula yambiri ndipo adzakuonjezerani mphamvu pamwamba pa mphamvu zanu. Kotero musatembenuke kukhala anthu oipa.”

    Verse 53

    Iwo adati, “oh iwe Hud! Iwe siunatibweretsere umboni wokwana. Ndipo ife sitidzasiya kupembedza milungu yathu chifukwa cha mawu ako! Ndipo ife sitikukhulupirira iwe ayi.”

    Verse 54

    “Zimene tilikunena ndizakuti ina ya milungu yathu yakupatsa iwe tsoka.” Iye adati: “Ndithudi Mulungu ndiye mboni yanga ndipo nanunso chitirani umboni kuti ine ndatalikirana nazo zimene mukamapembedza mulikuonjezera.”

    Verse 55

    “Motero nonsenu konzani chiwembu chanu pa ine ndipo musandichedwetse.”

    Verse 56

    “Ine ndaika chikhulupiliro changa mwa Mulungu, Ambuye wanga ndiponso Ambuye wanu. Palibe chinthu cha moyo pa dziko lapansi chimene tsogolo lake sililamulidwa ndi Iye. Ndithudi Ambuye wanga ndi amene ali pa njira yoyenera.”

    Verse 57

    “Ndipo ngati mutembenuka, ine ndakuuzani Uthenga umene ndatumizidwa kwa inu. Ambuye wanga adzaika, m’malo mwanu, anthu ena ndipo inu simungamuchite chinthu choipa chilichonse. Ndithudi Ambuye wanga ndi Msungi wa zinthu zonse.”

    Verse 58

    Ndipo pamene chiweruzo chathu chidadza, Ife tidamupulumutsa Hud, kudzera mu Chisomo chathu, pamodzi ndi amene adakhulupirira ndi iye. Ife tidawapulumutsa ku chilango chokhwima

    Verse 59

    Amenewa anali anthu a Aad. Iwo adakana Mawu a Ambuye wawo, ndipo adanyoza Atumwi ake ndipo anatsata malamulo a atsogoleri awo a nkhanza ndi okana chilungamo

    Verse 60

    Ndipo iwo adatsatiridwa ndi temberero m’dziko lino ndipo adzakhala otembereredwa pa tsiku la chiweruzo. Mosakaika, ndithudi, anthu a Ad adamukana Ambuye wawo. Motero tinathana nawo Ad, anthu a Hud

    Verse 61

    Ndipo kwa Thamoud, tidatumiza m’bale wawo Saleh. Iye adati: “Oh anthu anga! Mpembedzeni Mulungu, chifukwa inu mulibe mulungu wina kupatula Iye yekha. Iye ndiye amene adakulengani inu kuchokera ku nthaka, ndipo adakupatsani inu malo okhala pa nthakayo. Motero funani chikhululukiro kwa Iye ndipo idzani kwa Iye ndi kulapa. Ndithudi Ambuye wanga ali pafupi nanu ndipo Iye adzamva mapemphero anu.”

    Verse 62

    Iwo adati: “Iwe Saleh! Ndithudi iwe wakhala pakati pathu ndipo udali chiyembekezo chathu. Kodi iwe utiletsa kupembedza zimene amapembedza makolo athu? Ndithudi ife tili ndi chikaiko chambiri ndi chipembedzo chimene uli kutiitanira.”

    Verse 63

    Iye adati: “Oh anthu anga! Ndiuzeni ngati ine ndili ndi umboni wokwanira wochokera kwa Ambuye wanga ndipo Iye wandipatsa chisomo kuchokera kwa Iye, ndani angandipulumutse ine kuchokera ku chilango cha Mulungu ngati nditamunyoza? Inu simungaonjezere china chilichonse kwa ine koma kutayika.”

    Verse 64

    “Oh Anthu anga! Iyi ndi Ngamira yaikazi, mwini wake ndi Mulungu, ndipo ndi chizindikiro chooneka kwa inu. Isiyeni kuti izidya mwachifuniro cha Mulungu m’dziko lake ndipo musaizunze chifukwa chilango chingadze pa inu mwamsanga.”

    Verse 65

    Koma iwo adaipha ngamirayo ndipo iye adati: “Inu basangalalani m’nyumba zanu masiku atatu. Chimenecho ndi chipangano chimene sichili chabodza.”

    Verse 66

    Ndipo pamene chiweruzo chathu chimadza, Ife tinamupulumutsa Saleh pamodzi ndi amene adakhulupirira ndi iye kudzera m’Chisomo chathu, kuchokera m’masautso a tsiku limeneli. Ndithudi Ambuye wako ndi wanyonga, ndi wopambana

    Verse 67

    Ndipo mkuwo wowopsa udawaononga anthu ochita zoipa ndipo anthu onse adali lambilambi m’nyumba zawo atafa

    Verse 68

    Kukhala ngati sadakhalepo pa malo amenewo. Mosakaika, ndithudi, a Thamoud sadakhulupirire mwa Ambuye wawo. Motero anatha anthu a Thamoud

    Verse 69

    Ndithudi Atumwi athu adadza kwa Abrahamu ndi nkhani yabwino. Iwo adati: “Mtendere!” Iye anayankha: “Mtendere” ndipo posakhalitsa iye adabweretsa nyama ya ng’ombe yowotcha

    Verse 70

    Ndipo pamene iye adaona kuti manja awo sakukhudza nyamayo adawadabwa, nachita mantha. Iwo adati: “Usaope. Ife tatumidwa kwa anthu a Loti.”

    Verse 71

    Ndipo mkazi wake adali chiimire pompo, naseka. Ife tidamuuza kuti adzabereka Isake ndipo kuti Isake adzabala Yakobo

    Verse 72

    Iye adati: “Kalanga ine! Kodi ine ndingabereke pamene ndine wokalamba ndipo mwamuna wanga ndi wokalambanso? Ndithudi ichi ndi chinthu chododometsa.”

    Verse 73

    Iwo adati: “Kodi iwe uli kuwadabwa malamulo a Mulungu? Madalitso ndi chisomo cha Mulungu chikhale pa inu a m’banja la Abrahamu. Ndithudi Iye ndi wotamandidwa ndiponso wolemekezeka.”

    Verse 74

    Ndipo pamene Abrahamu adamuchoka mantha ndi kumfikirankhaniyabwino, iyeadatifunsa Ifezaanthua Loti

    Verse 75

    Ndithudi Abrahamu anali woleza mtima, wodzichepetsa ndiponso munthu wodzipereka kwa Mulungu

    Verse 76

    Angelo adati: “Iwe Abrahamu! Siya zimenezo. Ndithudi lamulo la Ambuye wako ladza. Ndithudi kudzadza chilango kwa iwo chimene sichingaletsedwe.”

    Verse 77

    Ndipo pamene Atumwi athu adadza kwa Loti, iye adali wodandaula kwambiri ndi kubanika mumtima chifukwa cha iwo. Ndipo adati: “Ndithudi ili ndi tsiku loopsa.”

    Verse 78

    Anthu ake adadza kwa iye akuthamanga ndipo pambuyo adali kuchita zinthu zoipa. Iye adati: “Oh! Anthu anga, awa ndi ana anga akazi, amene ali oyera kwa inu. Opani Mulungu ndipo musandiyalutse kwa alendo anga. Kodi palibe pakati panu munthu mmodzi wangwiro?”

    Verse 79

    Iwo adati: “Iwe ukudziwa kuti tilibe khumbo mu ana ako akazi ayi. Ndiponso iwe ukudziwa zimene tikufuna.”

    Verse 80

    Iye adati: “Ine ndikadakhala ndi mphamvu zoti ndikugonjetseni kapena ndikanapeza munthu wina wamphamvu zambiri ndikadamenyana nanu.”

    Verse 81

    Iwo adati: “Iwe Loti! Ndithudi ife ndife Atumwi Ambuye wako, iwo sakukhudza, choka pamodzi ndi anthu ako pakati pa usiku. Ndipo usalole wina wa inu kuti ayang’ane m’mbuyo kupatula mkazi wako, ndithudi, adzaona zonse zimene ena adzaone. Ndithudi lonjezo lawo ndi m’mamawa. Kodi m’mawa si pafupi?”

    Verse 82

    Ndipo pamene chilamulo chathu chidadza, Ife tidatembenuza pamwamba pa Mzinda kukhala pansi ndipo tidagwetsa pa iwo miyala youmbidwa ndi nthaka ya makande younjikika

    Verse 83

    Yokhala ndi zizindikiro, yochokera kwa Ambuye wako ndipo iyo siili kutali ndi anthu wosalungama

    Verse 84

    Ndipo kwa anthu a ku Midiyani tidawatumizira m’bale wawo Shoaib. Iye adati: “oh Anthu anga! Pembedzani Mulungu, chifukwa inu mulibe mulungu wina koma Mulungu mmodzi yekha ndipo musapungule miyeso ya zinthu. Ine ndikuona kuti inu ndinu anthu a chuma. Ine, ndithudi, ndili kuchita mantha ndi chilango cha tsiku limene lidzakuzungulirani inu.”

    Verse 85

    “Anthu anga! Kwaniritsani muyeso wa zinthu ndipo yesani mwachilungamo ndipo musawapungulire anthu katundu wawo ndipo musachite zoipa padziko ndikuyambitsa chisokonezo.”

    Verse 86

    “Zimene Mulungu wakusiyirani inu ndi zimene zili zabwino kwa inu ngati muli okhulupirira. Ndipo ine sindine wokuyang’anirani ayi.”

    Verse 87

    Iwo adati: “Iwe Shoaib! Kodi mapemphero ako akulamulira kuti ife tiyenera kuleka kupembedza milungu ya makolo athu kapena kuti sitiyenera kuchita zimene tifuna ndi chuma chathu? Ndithudi iwe ndiwe wopirira ndiponso wa nzeru zokhazikika.”

    Verse 88

    Iye adati: “Ndiuzeni! Ngati ine ndili ndi umboni woonekera wochokera kwa Ambuye wanga ndipo Iye wandipatsa gawo labwino. Ine sindifuna kusemphana nanu pochita chinthu chimene ndili kukuletsani. Palibe chilichonse chimene ndifuna koma kukonza mmene ndingathere. Ndipo ulangizi wanga siubwera kuchokera kwa wina aliyense kupatula Mulungu. Mwa Iye ndaika chikhulupiriro changa ndipo kwa Iye ndiko ndimalapa.”

    Verse 89

    “Oh anthu anga! Musalole kuti kusagwirizana kwanu ndi ine kuti kubweretse pa inu mavuto amene adadza pa anthu a Nowa, kapena pa anthu a Hud ndi Saleh ndiponso sikale pamene anthu a Loti adaonongeka.”

    Verse 90

    “Ndipo funani chikhululukiro cha Ambuye wanu, ndiponso lapani kwa Iye. Ndithudi Ambuye wanga ndi wa Chisoni ndiponso wa Chikondi chosatha.”

    Verse 91

    Iwo adati: “Oh Shoaib! Zambiri zimene unena ife sitili kuzizindikira ndipo ife tili kuona kuti ulibe mphamvu pakati pathu. Pakadapanda mtundu wako, ndithudi, ife tikadakuponya miyala ndiponso iwe ulibe mphamvu zoposa zathu.”

    Verse 92

    Iye adati: “oh anthu anga! Kodi mtundu wanga ndi olemekezeka kwambiri kuposa Mulungu? Ndipo inu mwamuponya Iye kumbuyo kwanu? Ndithudi Ambuye wanga ndi wodziwa zonse zimene muchita.”

    Verse 93

    “oh anthu anga! Chitani chimene mufuna kuti muchite, nanenso ndidzachita zanga. Inu mudzadziwa kuti ndani adzalangidwa ndi chilango chochititsa manyazi ndiponso kuti kodi ndani amene ali kunama! Ndithudi dikirani nanenso ndili kudikira pamodzi ndi inu.”

    Verse 94

    Ndipo pamene lamulo lathu lidadza tidamupulumutsa Shoaib, pamodzi ndi anzake onse amene anali wokhulupirira mwa chisomo chathu. Ndipo mkuwo waukulu udawaononga anthu onse ochita zoipa ndipo onse adali lambilambi m’nyumba zawo

    Verse 95

    Kukhala ngati iwo sadakhalemo m’menemo! Motero adaonongeka anthu a ku Midiyani monga momwe adaonongekera anthu a ku Thamoud

    Verse 96

    Zoonadi tidamutumiza Mose ndi zizindikiro zathu ndiponso umboni wooneka

    Verse 97

    Kwa Farao ndi nduna zake, iwo anatsatira malamulo a Farao ndipo malamulo a Farao sanali olungama

    Verse 98

    Iye adzawatsogolera anthu ake pa tsiku la chiweruzo ndipo adzawalowetsa ku moto. Aipirenji malo omwe adatengedwerako

    Verse 99

    Ndipo anatsatiridwa ndi matemberero m’moyo wa m’dziko lino ndi patsiku la chiweruzo. Iyipirenji mphotho yomwe adzapatsidwe

    Verse 100

    Iyi ndi nkhani, ya m’mizinda imene tinaononga ndipo tili kukufotokozera iwe, ndipo ina mwa Mizindayo ilipo pamene ina idaonongeka

    Verse 101

    Ife sitinawapondereze ayi koma adadzipondereza okha. Motero milungu yawo imene analikuipembedzakuonjezerapa Mulungusiidawathandize chilichonse pamene chiweruzo cha Ambuye wako chidadza ndiponso milungu yawo sidawaonjezere kalikonse koma chionongeko

    Verse 102

    Chimenecho ndicho chilango cha Ambuye wako akafuna kulanga mzinda wa anthu ochita zoipa. Ndithudi chilango chake ndi chokhwima ndi chowawa kwambiri

    Verse 103

    Ndithudi mu izo muli chizindikiro kwa iye amene aopa chilango cha moyo umene uli nkudza. Ndi tsiku limene anthu onse adzasonkhanitsidwa pamodzi ndiponso ili ndi tsiku lomwe chilichonse chidzakhalapo

    Verse 104

    Ife tili kulichedwetsa mpaka pa nthawi yokhazikitsidwa

    Verse 105

    Ndipo pamene tsikuli lidza, palibe munthu amene adzalankhula opanda chilolezo cha Mulungu. Ena a iwo adzakhala a tsoka pamene ena adzakhala amwayi

    Verse 106

    Akhala iwo amene adzakhala a tsoka, iwo akakhala m’moto ali kubuula mokweza ndiponso motsitsa

    Verse 107

    Iwo adzakhala komweko mpaka pamene kumwamba ndi dziko lapansi zidzakhale zilipobe kupatula ngati Ambuye wako afuna kusintha. Ndithudi Ambuye wako amachita zimene afuna

    Verse 108

    Akakhala anthu odala, iwo adzakhala ku Paradiso mpaka pamene kumwamba ndi dziko lapansi zidzakhale zilipobe kupatula ngati Ambuye wako afuna kusintha, mphatso yosatha mpaka kalekale

    Verse 109

    Motero usakaike pa zimene anthu awa apembedza. Iwo sali kupembedza koma kungotsatira mmene makolo awo amapembedzera kale. Ndipo ndithudi Ife tidzawalipira malipiro awo mopanda kuchepetsa

    Verse 110

    Ndithudi Ife tidamupatsa Mose Buku koma mikangano inabuka pakati pawo ndipo kukadapanda kuti liwu lochokera kwa Ambuye wako lidatsogola kale, lamulo likadadza pa iwo. Ndithudi iwo ndi okaika kwambiri za ili

    Verse 111

    Ndithudi Ambuye wako adzalipira anthu molingana ndi ntchito zawo. Ndithudi Iye amadziwa zonse zimene akuchita

    Verse 112

    Motero pitiriza kukhala m’njira yoyenera monga momwe walamulidwira pamodzi ndi onse amene alapa pamodzi ndi iwe ndipo usapyole malire. Ndithudi Iye amaona zonse zimene mumachita

    Verse 113

    Ndipo usatsatire anthu ochita zoipa chifukwa moto ungakupezeni ndiponso palibe wina wokuthandizani kupatula Mulungu ndiponso palibe wokuthandizani

    Verse 114

    Ndipo chita mapemphero ako nthawi ziwiri za masana ndi m’maola oyambirira a usiku. Ndithudi ntchito zabwino zimafafaniza machimo. Chimenechi ndi chikumbutso kwa anthu okumbukira

    Verse 115

    Kotero pirira. Ndithudi Mulungu sasokoneza mphotho ya ochita zabwino

    Verse 116

    Kukadakhala kuti pakati pa mibadwo imene inalipo kale, panali anthu a nzeru oletsa anthu kuchita zoipa padziko lapansi kupatula owerengeka amene Ife tidawapulumutsa pakati pawo. Iwo amene amachita zoipa anali kutsatira zokoma za m’moyo uno ndipo adali kupitiliza kuchita zoipa

    Verse 117

    Ndipo sizinali koyenera kuti Ambuye wako aononge mizinda mwankhanza pamene anthu ake anali kuchita zabwino

    Verse 118

    Ndipo Ambuye wako akadafuna, ndithudi, akadawapanga anthu onse kukhala a chipembedzo chimodzi koma akadapitiriza kukhala osiyana

    Verse 119

    Kupatula yekhayo amene Ambuye wako wamuonetsera chisomo chake ndipo ndicho chifukwa chake chimene Mulungu adawalengera. Mawu a Ambuye wako adzakwaniritsidwa “Ndithudi Ine ndidzadzadza Gahena ndi Majini ndi anthu onse pamodzi.”

    Verse 120

    Ndipo zonse zimene tili kukuuza iwe za nkhani za Atumwi ndi kulimbikitsa mtima wako. Kudzera mu izi choonadi ndi ulangizi wadza kwa iwe ndiponso uthenga wa chikumbutso kwa anthu okhulupirira

    Verse 121

    Auze anthu osakhulupirira kuti: “Chitani mmene mungathere, nafenso tidzachita chimodzimodzi.”

    Verse 122

    dikirani! Ndithudi nafenso tili kudikira

    Verse 123

    Zobisika zonse zimene zili kumwamba ndi pa dziko lapansi ndi za Mulungu ndipo zonse zimabwerera kwa Iye. Motero mpembedzeni Iye ndipo ika chikhulupiriro chako mwa Iye. Ambuye wako saiwala zimene mukuchita