Back to Languages
Chichewa - Chapter 23
Translation by Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula
Verse 1
Anthu okhulupirira ndiwo opambana
Verse 2
Iwo amene amadzichepetsa akamapemphera
Verse 3
Ndi iwo amene amalewa nkhani zabodza
Verse 4
Ndipo amapereka zaulere kwa anthu osauka
Verse 5
Ndi iwo amene amadziteteza ku chiwerewere
Verse 6
Kupatula kwa akazi awo kapena akapolo awo akazi, chifukwa iwo sangadzudzulidwe
Verse 7
Koma amene angafune zina pamwamba pa zimene tawaloleza anthu otere ndi ochimwa
Verse 8
Amene amakwaniritsa malonjezo ndi mapangano awo
Verse 9
Ndi iwo amene amasunga mapemphero awo
Verse 10
Amenewa ndithudi ndiwo amene adzalowa
Verse 11
Iwo adzalowa ku Paradiso ya pamwamba ndipo adzakhalamo mpaka kalekale
Verse 12
Ndithudi Ife tidapanga munthu kuchokera ku dothi labwino
Verse 13
Titatero tidamukonza iye kukhala dontho la umuna m’malo otetezedwa mu msana
Verse 14
dontho la umunali tidalipanga kukhala dontho la magazi ndipo dontho lamagazili tidalipanga kukhala m’bulu wa mnofu. Ndipo mnofu umenewu tidaukonza kukhala mafupa ndipo tidakuta mafupa ndi mnofu. Kotero tidamupanga iye kukhala chilengedwe china. odalitsa akhale Mulungu, Namalenga wabwino kwambiri mwa onse
Verse 15
Ndipo pambuyo pake inu nonse mudzafa
Verse 16
Ndipo mudzapatsidwanso moyo patsiku la kuuka kwa akufa
Verse 17
Ife tidalenga miyamba isanu ndi iwiri pamwamba panu ndipo kwa zolengedwa zathu. Ndipo Ife sitikhala osalabadira ayi
Verse 18
Ife timatumiza madzi kuchokera kumwamba m’muyeso wokwana ndipo timawalowetsa pansi pa nthaka. Ndipo Ife tili ndi mphamvu yowachotsa madziwo
Verse 19
Ndipo Ife timakutulutsirani mmenemo minda ya tende ndi mphesa, m’mene muli zipatso zanu zambiri zimene zina mwa izo mumadya
Verse 20
Mtengo umene umamera pa phiri la Sinai, umapereka mafuta ndiponso ndiwo kwa anthu
Verse 21
M’nyama namonso muli chizindikiro choonetsa mphamvu zathu. Inu timakumwetsani zimene zili m’mimba mwake ndipo mumadya nyama yake ndiponso mumapeza phindu lambiri
Verse 22
Ndipo pa izo ndi m’zombo zimene zimayenda pa nyanja, inu mumanyamulidwa
Verse 23
Tidamutumiza Nowa kwa anthu ake ndipo iye adati, “Tumikirani Mulungu anthu anga chifukwa mulibe mulungu wina koma Iye yekha. Kodi simungamuope Iye?”
Verse 24
Akuluakulu osakhulupirira a anthu ake adati, “Munthu uyu ndi wolingana ndi inu, iye ali kungodziyenereza kuti ndi wopambana pakati panu.” Mulungu akadafuna, akadatumiza angelo. Ndiponso zinthu za mtundu uwu sitidamvepo kuchokera kwa makolo athu akalekale
Verse 25
Ndithudi ameneyu ndi wopenga, ndipo mumuyang’anire pa kanthawi.”
Verse 26
Iye adati, “Ambuye! Ndithandizeni ine chifukwa iwo ali kundikana.”
Verse 27
Ife tidavumbulutsa chifuniro chathu kwa iye ponena kuti, “Khoma chombo chimene Ife tidzayang’anira molingana ndi chilangizo chathu. Pamene chiweruzo chathu chidza ndipo madzi asefukira kuchokera ku ng’anjo, utenge zolengedwa ziwiriziwiri, zazimuna ndi zazikazi ndiponso kuchokera kwa iwo a m’nyumba mwako kupatula okhawo amene adanenedwa kuti adzaonongeka. Usandipemphe kuti ndipulumutse iwo amene adachita zoipa chifukwa iwo adzamizidwa.”
Verse 28
Ndipo pamene iwe ndi iwo amene akutsata iwe mulowa m’chombo, nena, “Kuyamikidwa kukhale kwa Mulungu amene watipulumutsa ife kuchoka ku mtundu wa anthu oipa.”
Verse 29
Ndipo nena: “Ambuye wanga! Ndithandizeni kuti ndikafike pamalo podalitsika chifukwa Inu ndinu wabwino wa onse amene amafikitsa pamalo okocheza.”
Verse 30
Ndithudi mu zimenezi muli zizindikiro zooneka. Ndithudi Ife timawaika anthu m’mayesero
Verse 31
Potero Ife tidapanga mtundu wa anthu a tsopano pambuyo pawo
Verse 32
Ndipo tidatumiza kwa iwo Mtumwi wa mtundu wawo amene adati, “Tumikirani Mulungu chifukwa inu mulibe mulungu wina koma Iye yekha. Kodi simungamuope Mulungu?”
Verse 33
Koma akuluakulu a anthu osakhulupirira a anthu ake, amene adakana za moyo umene uli nkudza ndi amene tidawapatsa zinthu zabwino za m’moyo uno adati, “Munthu uyu ndi munthu monga inu nomwe amene akudya zimene mumadya inu ndi kumwa zimene inu mumamwa.”
Verse 34
“Ngati inu mumvera munthu wonga inu nomwe, ndithudi, inu mudzatayika.”
Verse 35
“Kodi iye ali kukuopsezani kuti pamene inu mutafa ndi kusanduka dothi ndi mafupa mudzadzuka ndi kukhalanso ndi moyo?”
Verse 36
“Zimene inu muli kuopsezedwa nazo zili kutali.”
Verse 37
“Kulibenso moyo wina koma moyo wathu wapadziko lapansi basi. Ife timafa ndi kukhala ndi moyo ndipo ife sitidzadzukanso ayi.”
Verse 38
“Munthu uyu ndi odziyenereza amene ali kunena za Mulungu zimene sizili zoona ayi. Ife sitidzamukhulupirira.”
Verse 39
Iye adati, “Ambuye! Ndithandizeni ine chifukwa iwo ali kunditsutsa.”
Verse 40
Iye adati, “Posachedwapa iwo adzanong’oneza bombono.”
Verse 41
Chilango chathu chidawapeza mwachilungamo ndipo tidawafafaniza monga zinyalala. Chionongeko kwa anthu onse ochimwa
Verse 42
Atapita awa tidalenganso mitundu ina ya anthu
Verse 43
Palibeanthuameneangafulumizitsekapenakuchedwetsa chionongeko chawo
Verse 44
Ndipo Ife tidatumiza Atumwi ena motsagana ndipo nthawi iliyonse Mtumwi amadza kwa iwo ndipo amamukana nati ndi wabodza. Ndipo Ife tidawaononga ena pambuyo pawo ndipo tidawapanga iwo kukhala chitsanzo cha mbiri ya anthu olakwa. Ichi chidali chionongeko cha anthu osakhulupirira
Verse 45
Ndipo Ife tidamutumiza Mose pamodzi ndi m’bale wake Aroni ndi zizindikiro ndiponso ulamuliro wathu
Verse 46
Kwa Farawo ndi nduna zake ndipo iwo adawalandira mwamwano chifukwa iwo adali anthu a chipongwe
Verse 47
Ndipo iwo adati, “Kodi ife tikhulupirire anthu awiri olingana ndi ife amene anthu awo ndi akapolo athu?”
Verse 48
Iwo adawakana iwo kotero iwo adalandira chionongeko
Verse 49
Ndipo Ife tidamupatsa Mose Buku la Chipangano Chakale kuti anthu ake akhoza kutsogozedwa bwino
Verse 50
Ife tidamupanga mwana wamwamuna wa Maria pamodzi ndi amayi ake kukhala chizindikiro kwa anthu onse ndipo tidawapatsa mnthunzi pa malo okwera ndi malo a mtendere amene anali kuthiriridwa ndi madzi a pa kasupe
Verse 51
Oh Atumwi! Idyani zinthu zabwino ndipo muzichita ntchito zabwino. Ndithudi Ine ndimadziwa zonse zimene mumachita
Verse 52
Ndithudi chipembedzo chanu ndi chimodzi ndipo Ine ndine Ambuye wanu. Kotero ndiopeni Ine
Verse 53
Koma anthu adagawanika m’magulu osiyanasiyana, gulu lililonse limasangalala ndi ziphunzitso zawo
Verse 54
Alekeni ayambe achimwa mpaka pamene imfa iwapeza
Verse 55
Kodi iwo amaganiza kuti popeza tawapatsa chuma ndi ana
Verse 56
Ndiye kuti Ife tili kuwafunira zabwino? Iyayi. Iwo sadziwa kanthu ayi
Verse 57
Ndithudi iwo ndi anthu amene amaopa Ambuye wawo
Verse 58
Amene amakhulupirira zizindikiro za Ambuye wawo
Verse 59
Amene sapembedza wina aliyense poonjezera pa Ambuye wawo
Verse 60
Amene amapereka chaulere mitima ili yoopa Ambuye wawo chifukwa chakuti adzabwerera kwa Iye
Verse 61
Awa ndiwo amene amapikisana wina ndi mnzake pochita zabwino ndipo amakhala oyamba pozindikira
Verse 62
Ife sitinyamulitsa mzimu wina uliwonse katundu amene iwo sangathe kunyamula. M’buku lathu mudalembedwa zoona zokhazokha. Ndipo palibe munthu amene adzaponderezedwa
Verse 63
Koma mitima ya anthu osakhulupirira siyizidziwa zimenezi ayi. Iwo ali ndi ntchito zina zoipa kupatula zimene iwo amachita
Verse 64
Koma pamene chilango chathu chidza pa iwo amene amakhala mu mtendere, iwo adzafuula kufuna chithandizo
Verse 65
Musalire tsiku la lero chifukwa inu simudzalandira chithandizo china chilichonse kuchokera kwa Ife
Verse 66
Chivumbulutso changa chinali kulakatulidwa kwa inu nthawi zambiri koma inu munali kuthawa ndi kuchikana mwamwano
Verse 67
Inu mumachinyoza usana ndi usiku uliwonse
Verse 68
Kodi iwo sangathe kulingalira mozama pa mawu a Mulungu kapena pali china chake chimene chidavumbulutsidwa kwa iwo chimene sichidavumbulutsidwe kwa makolo awo
Verse 69
Kapena iwo sadziwa kuti akukana Mtumwi wawo
Verse 70
Kapena iwo akuti Iye ndi wopenga? Koma iye wawabweretsera iwo onse zoonadi. Koma ambiri amakana choonadi
Verse 71
Kukadakhala kuti choonadi chimatsatira zofuna zawo, ndithudi, kumwamba, dziko lapansi ndi onse okhala m’menemo akadaonongeka. Ife tawapatsa chikumbutso komabe iwo safuna kumvera chikumbutsocho
Verse 72
Kapena iwe uli kuwapemphera mphotho? Chithandizo cha Ambuye wawo ndicho chabwino. Ndipo Iye ndiye wopereka moolowa manja kuposa onse amene amapereka
Verse 73
Ndithudi iwe uli kuwaitana kuti adze kunjira yoyenera
Verse 74
Ndithudi iwo amene amakana moyo umene uli nkudza adzakhala ali kusochera ku njira yoyenerayi
Verse 75
Ngati Ife tikadawalangiza chisoni chathu ndi kuwachotsera mavuto, iwo akadakhala ali kulakwabe m’njira zawo zoipa ndi kusokonezeka ndi zoipazo
Verse 76
Ndithudi tidawalanga kale koma iwo sadafunefune Ambuye wawo kapena kukhala odzichepetsa pamaso pake
Verse 77
Mpaka pamene tidzawatsekulira khomo la chilango chowawa, iwo adzakhala okhumudwa
Verse 78
Iye ndiye amene adakupatsani makutu, maso ndi mitima. Komabe inu simuthokoza mokwanira
Verse 79
Iye ndiye amene adakulengani ndi kukuchulukitsani padziko lapansi ndipo nonsenu mudzasonkhanitsidwa kudza pamaso pake
Verse 80
Iye ndiye amene amapereka moyo ndiponso imfa ndipo ndi Iyenso amene amasithanitsa usiku ndi usana. Kodi simungazindikire
Verse 81
Iwo amanena zimene anthu akale ankanena
Verse 82
Iwo amati, “Pamene ife tafa ndi kusanduka dothi ndi mafupa, kodi tidzadzukanso ndi kukhala ndi moyo?”
Verse 83
Ndithudi ife tidalonjedzedwa zimenezi kale pamodzi ndi makolo athu. Izi si zina ayi koma nkhani zabodza za anthu a makedzana
Verse 84
Nena, “Kodi Mwini wake wa dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo ndani? Ndiuzeni ngati mumudziwa.”
Verse 85
Iwo adzati, “Mwini wake ndi Mulungu.” Nena, “Kodi inu simungachenjezedwe?”
Verse 86
Nena, “Kodi Ambuye wa miyamba isanu ndi iwiri ndiponso Mwini Ufumu ndani?”
Verse 87
Iwo adzati, “Mwini wake ndi Mulungu.” Nena, “Nanga kodi simungasiye kuchita zoipa?”
Verse 88
Nena, “Kodi ulamuliro wa zinthu zonse zili m’manja mwa yani? Kodi ndani amene amaziteteza zonse pamene Iye safuna chitetezo cha wina aliyense ngati inu mukudziwa?”
Verse 89
Iwo adzati, “M’manja mwa Mulungu.” Nena, “Nanga ndi chifukwa chiyani inu mwanyengedwa?”
Verse 90
Iyayi, Ife tawavumbulutsira choonadi. Koma onsewa ndi anthu abodza
Verse 91
Palibe nthawi imene Mulungu adabala mwana ndipo kulibe Mulungu wina woonjezera pa Iye. Ngati izi zikadakhala choncho, bwezi Mulungu aliyense akumatenga zolengedwa zake zokha ndi kumaziika pamwamba pa zolengedwa za Mulungu wina. Ulemerero ukhale kwa Mulungu woposa zina zilizonse
Verse 92
Iye amadziwa zonse zooneka ndiponso zobisika. Mulungu akhale wopambana milungu ina imene iwo amaitumikira
Verse 93
Nena, “Ambuye wanga! Ngati Inu mukadandionetsa chilango chimene muli kuwopseza
Verse 94
Ambuye wanga! Pulumutsani ndipo musandisiye ine pakati pa mtundu wa anthu oipawu.”
Verse 95
Ndithudi, Ife tili ndi mphamvu zoti ukhoza kuona chilango chimene tawaopseza
Verse 96
Dzitetezeni ndi chabwino pothamangitsa choipa. Ife tili kudziwa zonse zimene ali kukunamizirani
Verse 97
Ndipo iwe unene kuti, “Ambuye wanga, Ine ndili kufuna chitetezo chanu pothawa zoipa za Satana.”
Verse 98
“Ambuye! Ine ndili kupempha chitetezo chanu kuti asabwere kumene ndili ine.”
Verse 99
Mpaka pamene imfa idza kwa munthu wolakwa iye adzati, “Ambuye wanga! Bwezeni.”
Verse 100
“Kuti ndikachite ntchitozabwinozimenendidalepherakuchita.” Kosatheka! Amenewa ndiwo mawu chabe amene akungolankhula. Kumbuyo kwawo kudzakhala chipupa mpaka pa tsiku la kuuka kwa akufa
Verse 101
Ndipo pamene lipenga lidzaombedwa, pa tsiku limeneli, ubale wawo wonse udzathera pomwepo ndiponso sadzafunsana chithandizo chochokera kwa wina ndi mnzake
Verse 102
Aliyense amene muyeso wake udzakhala wolemera, adzapambana
Verse 103
Koma aliyense amene muyeso wake udzakhala wopepuka adzataya moyo wake ndipo adzakhala ku Gahena nthawi zonse
Verse 104
Moto udzatentha nkhope zawo ndipo izo zidzakwinyikakwinyika chifukwa chaululu
Verse 105
“Kodi chivumbulutso chathu sichidalakatulidwe kwa inu? Kodi simudachikane?”
Verse 106
Iwo adzati, “Ambuye wathu! Zilakolako zathu zidatigonjetsa ife ndipo tidali anthu osochera.”
Verse 107
“Ambuye wathu! tipulumutseni ife ku ichi. Ngati ife tidzabwereranso ku zoipa, ndithudi, ife tidzakhala anthu oipa kwambiri.”
Verse 108
Iye adzati, “Khalani mu icho mwamanyazi ndipo musandiyankhulitse Ine ayi.”
Verse 109
Ndithudi padali gulu la Atumiki anga amene adati, “Ambuye wathu! Ife timakhulupirira mwa inu. Tikhululukireni ndipo mutichitire chisoni. Inu ndinu wabwino pochita chisoni kuposa a chisoni onse.”
Verse 110
Koma inu munali kuwanyogodola mpaka pamene inu mudandiiwala Ine ndipo inu munali kuwaseka iwo
Verse 111
Ndithudi lero Ine ndawalipira chifukwa cha kupirira kwawo ndipo iwo ndi amene apambana
Verse 112
Ndipo Iye adzafunsa kuti, “Kodi inu munakhala padziko lapansi zaka zingati?”
Verse 113
Iwo adzayankha kuti, “Takhala tsiku limodzi kapena mphindi zochepa zokha. Afunseni iwo amene amasunga chiwerengero.”
Verse 114
Iye adzawayankha kuti, “Inu mukadadziwa ndi nthawi yochepa kwambiri imene inu munakhala.”
Verse 115
“Kodi inu mumaganiza kuti tidangokulengani inu opanda cholinga ndipo kuti simudzabwerera kwa Ife?”
Verse 116
Motero alemekezeke Mulungu, Mfumu ya chilungamo. Palibe Mulungu wina koma Iye yekha, Ambuye wa Mpando wolemekezeka ndi Wachifumu
Verse 117
Aliyense amene apembedza mulungu wina woonjezera pa Mulungu, pamene Iye alibe umboni wa chimenecho, Ambuye wake adzamufunsa. Ndithudi anthu osakhulupirira sadzapambana ayi
Verse 118
Nena, “Ambuye wanga! Ndikhululukireni machimo anga ndipo mundichitire chisoni chifukwa Inu ndinu wachisoni choposa a chisoni onse.”