Back to Languages
Chichewa - Chapter 26
Translation by Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula
Verse 1
Ta Sin Mim
Verse 2
Awa ndi mawu omveka a Buku la Korani
Verse 3
Iwe mwina ukhoza kudziononga ndi madandaulo chifukwa cha kusakhulupirira kwawo
Verse 4
Ngati Ife tifuna, tikhoza kuwavumbulutsira chizindikiro chochokera kumwamba chimene makosi awo adzakhota modzichepetsa
Verse 5
Palibe chenjezo latsopano limene limadza kuchokera kwa Mwini chisoni chosatha koma iwo amalikana
Verse 6
Ndithudi iwo amakana mawu a Mulungu koma nkhani zidzadza kwa iwo zokhudza zinthu zimene iwo amazichita chipongwe
Verse 7
Kodi iwo saona nthaka, mmene ife tameretsamo mbewu zabwino zosiyanasiyana
Verse 8
Ndithudi m’menemu muli chizindikiro komabe ambiri a iwo sakhulupirira ayi
Verse 9
Ndithudi Ambuye wako ndiye Mwini mphamvu zonse ndiponso Mwini chisoni chosatha
Verse 10
Ndipo pamene Ambuye wako adamuitana Mose adanena kuti, “Pita kwa anthu opanda chilungamo.”
Verse 11
Kodi anthu a Farawo sangaope
Verse 12
Iye adati, “Ambuye wanga! Ndithudi ine ndili kuopa kuti adzandikana.”
Verse 13
“Ndipondikhozakupsamtimandikulepherakuyankhula. Tumizani Aroni.”
Verse 14
“Ndipo iwo ali ndi mangawa ndi ine ndipo ndichita mantha kuti akhoza kukandipha.”
Verse 15
Mulungu adati, “Nkosatheka kutero! Kotero pitani nonse awiri ndi zizindikiro zathu. Ife tidzakhala ndi inu ndipo tidzamva.”
Verse 16
Ndipo mukakafika kwa Farawo mukamuuze kuti, “Ife ndife Atumwi ochokera kwa Ambuye wa zolengedwa zonse.”
Verse 17
“Motero alekeni ana a Israyeli kuti apite ndi ife.”
Verse 18
(Farawo) adati, “Kodi ife sitidakurere iwe pamene udali wamng’ono? Ndipo iwe unakhala pakati pathu zaka zambiri.”
Verse 19
“Ndipo iwe udachita chimene udachita. Ndithudi iwe ndiwe mmodzi wa anthu osathokoza.”
Verse 20
(Mose) adati, “Ine ndidachita chimenecho popeza nthawi imeneyo ndidali wosadziwa china chilichonse.”
Verse 21
“Motero ine ndidathawa inu nonse pa nthawi imene ndidakuopani koma tsopano Ambuye wanga wandipatsa luntha ndiponso wandipanga ine kukhala mmodzi mwa Atumwi ake.”
Verse 22
“Ndipo uwu ndi mwayi umene ubwino wake iwe uli kundinyogodola. Iwe wasandutsa ana a Israyeli kukhala akapolo ako.”
Verse 23
Farawo adati, “Kodi Ambuye wa zolengedwa zonse ndani?”
Verse 24
(Mose) adati, “Ambuye wa kumwamba ndi dziko lapansi ndi zonse zimene zili pakati pawo ngati inu mufuna kukhulupirira.”
Verse 25
(Farawo) adawafunsa anthu amene adamuzungulira! “Kodi muli kumva zimene ali kunenazi.”
Verse 26
(Mose) adapitiriza kuti, “Ambuye wanu ndiponso Ambuye wa makolo anu akale.”
Verse 27
(Farawo) adati, “Ndithudi Mtumwi amene watumizidwa kwa inu ndi wopenga.”
Verse 28
(Mose) adati, “Iye ndi Ambuye wa kum’mawa ndi kumadzulo ndi zonse zimene zikhala kumeneko ngati muli ozindikira.”
Verse 29
(Farawo) adayankha kuti, “Ngati iwe utumikira mulungu wina kupatula ine, ndithudi ndikupanga kukhala mmodzi wa anthu okhala ku ndende.”
Verse 30
(Mose) adafunsa kuti, “Kodi zingakhale choncho ngakhale nditakulangiza chizindikiro choonekeratu? “
Verse 31
(Farawo) adati, “Tilangize chizindikiro chako ngati zonse zimene unena ndi zoona.”
Verse 32
Motero Mose adaponya ndodo yake pansi ndipo nthawi yomweyo idasanduka njoka yeniyeni
Verse 33
Ndipo Iye adatulutsa dzanja lake ndipo nthawi yomweyo lidasanduka loyera kwa iwo amene adaliona
Verse 34
Farawo adauza nduna zake kuti, “Ndithudi munthu uyu ndi wodziwa matsenga.”
Verse 35
“Iyeyu afuna kukuchotsani m’dziko lanu ndi matsenga ake. Kodi ulangizi wanu ndi wotani ndipo ukupereka langizo lanji?”
Verse 36
Iwo adati, “Muyambe mwawasunga iye pamodzi ndi m’bale wake kwa kanthawi kochepa. Tumizani mithenga ku mizinda yanu
Verse 37
Abweretse kwa inu munthu aliyense yemwe ndi wodziwa matsenga kwambiri.”
Verse 38
Motero anthu amatsengawa adasonkhanitsidwa patsiku lodziwika lomwe adagwirizana
Verse 39
Ndipo anthu adafunsidwa kuti, “Kodi nonse mudzasonkhana?”
Verse 40
“Kuti mwina ife tikhoza kudzatsatira a matsenga ngati iwo atapambana.”
Verse 41
Ndipo pamene anthu onse amatsenga adadza kwa Farawo, iwo adati kwa Farawo, “Kodi mudzatilipira ngati titapambana?”
Verse 42
Iye adati, “Inde. Ndipo ndithudi inu mudzakhala kufupi ndi Ine.”
Verse 43
Mose adawauza kuti, “Ponyani pansi chilichonse chimene mufuna kuponya.”
Verse 44
Ndipo iwo adaponya zingwe ndi ndodo zawo ndipo adati: “Mwa mphamvu ya Farawo, ndithudi, ife tipambana.”
Verse 45
Ndipo Mose adaponya ndodo yake ndipo nthawi yomweyo idameza zonse zabodza zimene iwo adapanga
Verse 46
Ndipo anthu amatsenga onse aja adagwa pansi mogwada
Verse 47
Iwo adati, “Ife takhulupirira mwa Ambuye wa zolengedwa zonse.”
Verse 48
“Ambuye wa Mose ndi Aroni”
Verse 49
Farawo adati, “Kodi inu mwakhulupirira mwa iye pamene ine sindinakupatseni chilolezo? Ndithudi iye ndi mtsogoleri wanu amene adakuphunzitsani matsenga. Ndithudi posachedwapa mudzazindikira. Ndithudi ine ndidzadula manja anu ndi miyendo yanu moisiyanitsa. Ndidzakudulani dzanja lamanja ndi mwendo wamanzere ndiponso ndidzakupachikani pa mtanda.”
Verse 50
Iwo adati, “Zilibe kanthu chifukwa ndithudi ife tidzabwerera kwa Ambuye wathu.”
Verse 51
“Ndithudi Ife tili ndi chiyembekezo kuti Ambuye wathu adzatikhululukira machimo athu popeza ndife oyamba kukhulupirira.”
Verse 52
Ndipo tidamulamula Mose kuti, “Nyamuka nthawi ya usiku ndi akapolo anga chifukwa, ndithudi, inu mulondoledwa ndi gulu la adani anu.”
Verse 53
Ndipo Farawo adatumiza mithenga ku mizinda yonse
Verse 54
“Ndithudi anthu amenewa ndi kagulu ka anthu ochepa.”
Verse 55
“Ndithudi anthu amenewa atipsetsa mtima.”
Verse 56
“Ife tonse tili tcheru.”
Verse 57
Ndipo tidawachotsa m’minda ndi mu a kasupe
Verse 58
Ndiponso m’chuma ndi m’malo alionse olemekezeka
Verse 59
Kotero tidawapanga ana a Israyeli kukhala alowa m’malo a zinthu za anthu a Farawo
Verse 60
Pamene dzuwa linali kutuluka, iwo adalondoledwa ndi adani awo
Verse 61
Ndipo pamene magulu awiriwa adaonana wina ndi mnzake, anthu a Mose adati, “Ndithudi atipeza.”
Verse 62
Mose adati, “Iyayi. Ndithudi Ambuye wanga ali ndi ine ndipo adzanditsogolera.”
Verse 63
Ndipo tidalamulira Mose kuti, “Menya madzi a m’nyanja ndi ndodo yako.” Ndipo nyanja idagawanika pakati, mbali iliyonse idali ngati phiri lalikulu
Verse 64
Ndipo anthu a Farawo tidawayandikitsa ndi nyanja ija
Verse 65
Ndipo Ife tidapulumutsa Mose ndi onse amene adali ndi iye
Verse 66
Ndipo tidamiza ena
Verse 67
Ndithudi mu ichi muli phunziro komabe anthu ambiri sakhulupirira ayi
Verse 68
Ndithudi Ambuye wako! Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini chisoni chosatha
Verse 69
Ndipo afotokozere nkhani za Abrahamu
Verse 70
Pamenepo iye adanena kwa abambo ake ndiponso kwa anthu ake kuti, “Kodi ndi chiyani chimene inu muli kupembedza?”
Verse 71
Iwo adati, “Timatumikira mafano ndipo timapempha kwa iwo modzipereka kwambiri.”
Verse 72
Ndipo adati, “Kodi iwo amakumvani pamene mumawapempha?”
Verse 73
“Kodi amakuthandizani kapena kukuonongani?”
Verse 74
Iwo adati, “Iyayi. Koma ife tidawapeza makolo athu akupembedza mafano.”
Verse 75
Iye adati, “Kodi inu muli kuzidziwa zimene muli kuzipembedza?”
Verse 76
“Inu ndiponso makolo anu akale?”
Verse 77
“Ndithudi onse ndi adani anga kupatula Ambuye wachilengedwe.”
Verse 78
“Amene adandipanga ine ndipo ndiye amene amandipatsa chilangizo.”
Verse 79
“Ndipo ndiye amene amandipatsa chakudya ndi chakumwa.”
Verse 80
“Ndipo ndikadwala, ndi Iye amene amandichiza.”
Verse 81
“Ndipo ndiye amene adzandipangitsa kuti ndife ndi kudzandibwezeranso moyo.”
Verse 82
“Ndi amene ine ndimayembekezera kuti adzandikhululukira machimo anga pa tsiku lachiweruzo”
Verse 83
Ambuye ndipatseni luntha ndipo mundilole kuti ndikhale pakati pa anthu ochita zabwino
Verse 84
Ndipatseni ulemerero umene udzatchulidwe ndi mibadwo yomwe ikubwera mtsogolo
Verse 85
Ndipo ndiikeni m’gulu la anthu amene adzakhala kumalo a mtendere a ku Paradiso
Verse 86
Akhululukireni abambo anga ndithudi iwo ali mmodzi mwa anthu osochera
Verse 87
Musadzandichititse manyazi patsiku limene anthu adzaukitsidwa kwa akufa
Verse 88
Tsiku limene chuma ndi ana sizidzathandiza wina aliyense
Verse 89
Kupatula yekhayo amene adzadza kwa Mulungu ndi mtima woyera
Verse 90
Pamenepo Paradiso idzayandikiritsidwa kwa anthu angwiro
Verse 91
Ndipo Gahena idzaonetsedwa poyera kwa anthu ochimwa
Verse 92
Mawu adzanenedwa kwa iwo kuti, “Kodi mafano anu aja amene mumatumikira ali kuti?”
Verse 93
Kuwonjezera pa Mulungu weniweni? Kodi iwo akhoza kukuthandizani inu kapena kudzithandiza okha?”
Verse 94
Ndipo iwo ndi onse ochimwa adzaponyedwa ku Gahena
Verse 95
Ndiponso pamodzi ndi magulu onse a Satana
Verse 96
Iwo adzati pamene adzakhala ali kukangana kumeneko
Verse 97
“Pali Mulungu, ndithudi, ife tidali ochimwa moonekeratu.”
Verse 98
Pamene tidakusandutsani inu kukhala ofanana ndi Ambuye wa zolengedwa zonse
Verse 99
Palibe ena koma anthu ochita zoipa amene adatisocheretsa ife
Verse 100
Palibe wina woti angatipepesere ife
Verse 101
Ndiponso palibe bwenzi lenileni
Verse 102
Koma tikadakhalanso ndi moyo, tikadakhala anthu okhulupirira
Verse 103
Ndithudi mu zimenezi muli chizindikiro koma anthu ambiri sakhulupirira ayi
Verse 104
Ndithudi Ambuye wanu! Ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini chisoni chosatha
Verse 105
Anthu a m’badwo wa Nowa adakana Atumwi awo
Verse 106
Pamene Nowa adati, “Kodi inu simungaope Mulungu ndi kumumvera Iye?”
Verse 107
“Ndithudi ine ndine Mtumwi wanu wokhulupirika.”
Verse 108
“Motero opani Mulungu ndipo mundimvere ine.”
Verse 109
“Ine sindikupemphani malipiro ena alionse chifukwa palibe wina aliyense amene angandilipire ine kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.”
Verse 110
“Kotero opani Mulungu ndipo mundimvere ine.”
Verse 111
Iwo adati, “Kodi ife tikukhulupirire iwe pamene anthu onyozeka ndiwo amene amakutsatira iwe?”
Verse 112
Nowa adati, “Kodi ine ndikudziwa chiyani za chimene iwo amachita?”
Verse 113
“Ambuye wanga ndiye amene akhoza kuweruza ngati mumazindikira.”
Verse 114
“Ndipo ine sindidzathamangitsa anthu okhulupirira moona.”
Verse 115
“Ine ndine wopereka chenjezo poyera.”
Verse 116
Iwo adati, “Iwe Nowa; ngati siusiya zimene uchita udzaponyedwa miyala.”
Verse 117
Iye adati, “Ambuye wanga! Ndithudi anthu anga akundikana.”
Verse 118
Motero weruzani mwachilungamo pakati pa ine ndi iwo. Ndipulumutseni ine pamodzi ndi anthu okhulupirira amene ali ndi ine
Verse 119
Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi iwo amene adali naye m’chombo
Verse 120
Ndipo pambuyo pake tidamiza ena onse ndi chigumula
Verse 121
Ndithudi mu chimenechi muli phunziro komabe ambiri sakhulupirira
Verse 122
Ndithudi Ambuye wako ndi Mwini mphamvu ndi Mwini chisoni chosatha
Verse 123
Anthu a ku Aad sanakhulupirire Atumwi awo
Verse 124
Pamene m’bale wawo Houd adati, “Kodi inu simungakhale ndi mantha ndi Mulungu?”
Verse 125
“Ndithudi ine ndine Mtumwi wanu wokhulupirika.”
Verse 126
“opani Mulungu ndipo munditsate ine.”
Verse 127
“Pa ntchito iyi, ine sindipempha malipiro kuchokera kwa inu chifukwa palibe wina amene angandilipire kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.”
Verse 128
“Kodi inu mukumamanga nyumba pamalo paliponse pokwera mofuna kudzisangalatsa?”
Verse 129
“Kodi muli kumanga nyumba zokongola ndi zolimba ngati kuti mudzakhalamo mpaka kalekale?”
Verse 130
“Ndipo pamene mumenya anthu mumamenya ngati anthu ankhanza.”
Verse 131
“Motero opani Mulungu, ndipo mundimvere ine.”
Verse 132
“Ndipo muopeni Iye amene wakupatsani inu zinthu zonse zimene mumazidziwa.”
Verse 133
“Iye wakupatsani nyama ndi ana,”
Verse 134
“Ndiponso minda ndi a kasupe;”
Verse 135
“Ndithudi ine ndili kuchita mantha ndi chilango chimene chidzadza pa inu pa tsiku loopsa.”
Verse 136
Iwo adati, “Ndi chimodzimodzi kwa ife kaya utilalikira kapena ayi.”
Verse 137
“Zonse zimene uli kutiopseza nazo ndi chikhalidwe cha anthu amakedzana.”
Verse 138
“Ife sitidzalangidwa ayi.”
Verse 139
Iwo adamukana iye ndipo Ife tidawaononga onse. Ndithudi mu chimenechi muli phunziro koma ambiri sakhulupirira ayi
Verse 140
Ndithudi Ambuye wako ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini chisoni chosatha
Verse 141
Anthu a Thamoud adakana Atumwi awo
Verse 142
Pamene m’bale wawo Saleh adati, “Kodi inu simungakhale ndi mantha ndi Mulungu?”
Verse 143
“Ndithudi ine ndine Mtumwi wanu okhulupirika.”
Verse 144
“Motero opani Mulungu ndipo mundimvere ine.”
Verse 145
“Pa ntchito iyi ine sindili kukupemphani malipiro. Palibe wina amene angandilipire kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.”
Verse 146
“Kodi inu muganiza kuti mudzasiyidwa mu mtendere wa m’dziko lino?”
Verse 147
“M’kati mwa minda ndi a kasupe.”
Verse 148
“Minda ya chimanga ndi mitengo ya tende imene yapatsa zipatso zambiri.”
Verse 149
“Ndipo muboola mapiri ndi kumangamo nyumba zanu mwaukatswiri;”
Verse 150
“Khalani ndi mantha ndi Mulungu ndipo mundimvere ine.”
Verse 151
“Musamvere malamulo a anthu oononga.”
Verse 152
“Amene amachita zoipa padziko lapansi ndipo sakonza makhalidwe awo.”
Verse 153
Iwo adati, “Iwe uli mmodzi mwa olodzedwa.”
Verse 154
“Iwe ndiwe munthu wonga ife tomwe. Tilangize chizindikiro ngati zimene ukunenazi ndi zoona”
Verse 155
Iye adati, “Iyi ndi ngamira yaikazi. Iyo idzamwa madzi patsiku lake ndipo inu mudzamwa patsiku lanu lokhazikitsidwa.”
Verse 156
“Musaizunze ayi chifukwa mukatero chilango cha tsiku loopsa chidzadza kwa inu.”
Verse 157
Komabe iwo adaipha iyo ndipo adanong’oneza bombono
Verse 158
Chilango chidawapeza iwo. Ndithudi mu chimenechi muli chizindikiro koma ambiri a iwo sakhulupirira
Verse 159
Ndithudi Ambuye wako! Indedi ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini chisoni chosatha
Verse 160
Anthu a Loti adakana Atumwi awo
Verse 161
Pamene m’bale wawo Loti adati, “Kodi inu simungaope Mulungu?”
Verse 162
“Ndithudi ine ndine Mtumwi wanu wokhulupirika.”
Verse 163
“Opani Mulungu ndipo mundimvere ine.”
Verse 164
“Ine sindili kupempha kuti mundilipire chifukwa cha ichi ayi chifukwa palibe wina amene angandilipire kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.”
Verse 165
“Kodi inu mwasankha kuti muzigonana ndi amuna anzanu mwa zolengedwa zonse
Verse 166
“Kusiya akazi amene Mulungu adakulengerani? Koma inu ndinu anthu olakwa kwambiri.”
Verse 167
Iwo adati, “Iwe Loti! Ngati siusiya zimenezi ndithudi udzakhala mmodzi mwa othamangitsidwa.”
Verse 168
Iye adati, “Ine ndili kudana ndi makhalidwe anu.”
Verse 169
“Ambuye wanga! Ndipulumutseni ine pamodzi ndi a pabanja langa ku ntchito zawo zoipa.”
Verse 170
Ndipo Ife tidamupulumutsa iye pamodzi ndi anthu ake onse
Verse 171
Kupatula mayi wokalamba, pakati pa amene adatsalira m’mbuyo
Verse 172
Ndipo Ife tidawaononga kwambiri ena onse
Verse 173
Ndipo choipa chidali chilango cha mvula imene idagwa pa iwo amene adachenjezedwa koma sadamvere
Verse 174
Ndithudi mu ichi muli phunziro koma ambiri a iwo sakhulupirira
Verse 175
Ndithudi Ambuye wako ndiye mwini mphamvu zonse ndi mwini chisoni chosatha
Verse 176
Nawonso anthu okhala m’nkhalango adakana Atumwi
Verse 177
Pamene Shaibu adawauza kuti, “Kodi inu simungaope Mulungu?”
Verse 178
“Ndithudi ine ndine Mtumwi wanu wokhulupirira.”
Verse 179
“Opani Mulungu ndipo mundimvere ine.”
Verse 180
“Ine sindikupemphani malipiro chifukwa palibe wina aliyense amene angandilipire kupatula Ambuye wa zolengedwa zonse.”
Verse 181
“Perekani muyeso oyenera ndipo musachepetse.”
Verse 182
“Yesani ndi miyeso yabwino.”
Verse 183
“Ndipo musawachepetsere anthu zinthu zawo kapena kulowetsa chisokonezo m’dziko.”
Verse 184
“Muopeni Iye amene adakulengani inu ndi mibadwo yakale.”
Verse 185
Iwo adati, “Ndithudi iwe walodzedwa.”
Verse 186
“Iwe ndiwe munthu wolingana ndi ife. Ndithudi ife tili kuganiza kuti iwe uli kunama.”
Verse 187
“Tigwetsere mtambo kuchokera kumwamba ngati zimene uli kunena ndi zoonadi.”
Verse 188
Iye adati, “Ambuye wanga amadziwa kwambiri chimene inu mumachita.”
Verse 189
Iwo adamukana iye kotero chilango cha thambo ndi moto chidawaononga. Ichi chidali chilango cha tsiku loopsa
Verse 190
Ndithudi mu chimenechi muli chiphunzitso koma ambiri a iwo sakhulupirira
Verse 191
Ndithudi Ambuye wako ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini chisoni chosatha
Verse 192
Buku lolemekezekali lavumbulutsidwa ndi Ambuye wa zolengedwa zonse
Verse 193
Mzimu wokhulupirika udabweretsa Bukuli
Verse 194
Ku mtima wako kuti ukhoza kuchenjeza mitundu ya anthu
Verse 195
Mu chinenero chomveka cha Chiarabu
Verse 196
Ndithudi lili kupezeka mu mawu a Mulungu akale
Verse 197
Kodi si chizindikiro kwa iwo kuti anthu ophunzira a ana a Israyeli amalidziwa
Verse 198
Ngati Ife tikadaivumbulutsa kwa munthu wa mtundu wina uliwonse yemwesi wa Chiarabu
Verse 199
Kuti iye ailakatule kwa iwo ndipo sakadakhulupirira iwo mwa Bukulo
Verse 200
Kotero Ife tidaipanga iyo kuti ilowe m’mitima ya anthu ochitazoipa
Verse 201
Iwosadzakhulupiriramuilompakapamene adzaona chilango chowawa
Verse 202
Ndipo icho chidzadza kwa iwo mwadzidzidzi pamene iwo sakudziwa
Verse 203
Ndipo iwo adzati, “Kodi ife sitidzapatsidwanso nthawi?”
Verse 204
Kodi iwo angafune kuti chilango chathu chidze msanga
Verse 205
Tandiuza. Ngati Ife titawalola kukhala mu mtendere wa zaka zambiri
Verse 206
Ndipo pambuyo pake chilango chimene chidalonjezedwa chidza pa iwo
Verse 207
Chisangalalo chawo chimene adapatsidwa chidzakhala chopanda phindu
Verse 208
Palibe mtundu wa anthu umene tidaonongapo kale umene sitidautumizire owachenjeza
Verse 209
Monga chenjezo ndipo Ife si ndife opondereza ayi
Verse 210
Si a Satana amene adabweretsa Korani ino ayi
Verse 211
Si koyenera kwa iwo ndiponso sangathe kutero
Verse 212
Ndithudi iwo amanidwa kumva za Bukuli
Verse 213
Musapembedze milungu ina kuonjezera pa Mulungu weniweni chifukwa mukatero mudzakhala m’gulu limene lidzalangidwa
Verse 214
Achenjeze abale ako amene ali pafupi ndi iwe
Verse 215
Ndipo onetsa chifundo kwa anthu okhulupirira amene amakutsatira iwe
Verse 216
Ngati iwo sakumvera iwe, unene kuti, “Ine sindidzaimbidwa mlandu chifukwa cha zimene mumachita.”
Verse 217
Ika chikhulupiriro chako mwa Mwini mphamvu zonse ndi Mwini chisoni chosatha
Verse 218
Amene amakuona pamene umaimirira popemphera
Verse 219
Ndi machitidwe ako pakati pa anthu opemphera
Verse 220
Mulungu amamva chilichonse ndipo amadziwa china chilichonse
Verse 221
Kodi ndi kuuzeni za munthu amene Satana amamutsikira
Verse 222
Iwo amadza pa munthu wabodza ndi wochimwa
Verse 223
Iwo amamvera mabodza okhaokha ndipo komaambiriaiwondiabodza
Verse 224
Alakatuliamatsatidwandi anthu ochita zoipa
Verse 225
Kodi simuona kuti iwo amangonena nkhani iliyonse mu zolakatula zawo
Verse 226
Ndipo iwo amakamba zinthu zimene iwo sachita
Verse 227
Kupatula okhawo amene akhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino ndi kumakumbukira Mulungu kwambiri ndi kudziteteza pambuyo pa kuponderezedwa. Ndipo iwo amene amachita zoipa adzadziwa chimene chidzawagadabuza