Back to Languages

    Chichewa - Chapter 30

    Translation by Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

    Verse 1

    Alif Lam Mim

    Verse 2

    Aroma agonjetsedwa

    Verse 3

    M’dziko loyandikana nalo ndipo iwo atagonja, pambuyo pake adzapambana

    Verse 4

    M’zaka zowerengeka. Mulungu ndiye Mwini ulamuliro ndipo pa tsiku limeneli onse okhulupirira adzakondwera

    Verse 5

    Ndi chithandizo cha Mulungu. Iye amathandiza aliyense amene wamufuna. Iye ndi wamphamvu, ndiponso Mwini chisoni chosatha

    Verse 6

    Ili ndi lonjezo la Mulungu. Mulungu saphwanya lonjezo lake ndipo anthu ambiri sadziwa

    Verse 7

    Iwo amangodziwa zokhazo zimene amaziona za m’moyo uno koma za m’moyo umene uli nkudza, iwo safuna kumva china chilichonse cha izo

    Verse 8

    Kodi iwo saganizira pa okha kuti Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi zinthu zonse zimene zikhala m’menemo mwachoonadi ndi mwa kanthawi yokhazikitsidwa? Ndipo, ndithudi, anthu ambiri amakana zoti adzakumana ndi Ambuye wawo

    Verse 9

    Kodi iwo sadayende pa dziko ndi kuona zimene zidawaonekera anthu amene adalipo kale? Iwo adali ndi mphamvu zambiri kuposa awa, ndipo adakumba nthaka ndiponso adamanga pa nthakayo nyumba zambiri kuposa zimene awa amanga. Ndipo kudadza kwa iwo Atumwi awo ndi chiphunzitso chomveka ndipo sikudali koyenera kuti Mulungu awachitire zinthu zosalungama koma kuti iwo adalakwira mizimu yawo

    Verse 10

    Choipa chidatsata munthu amene anali kuchita zoipa chifukwa iwo adakana chiphunzitso cha Mulungu ndipo anali kuwaseka iwo

    Verse 11

    Mulungu ndiye amene amalenga zolengedwa ndipo adzazibwereza ndipo ndi kwa Iye kumene mudzabwerera

    Verse 12

    Ndipo pa nthawi imene ola lidzadza, anthu onse ochita zoipa adzakhala ndi nkhawa

    Verse 13

    Ndipo iwo sadzakhala ndi ena alionse owathandiza ochokera pakati pa milungu yawo imene anali kupembedza kuonjezera pa Mulungu weniweni ndipo iwo adzakhala okana milungu yawo

    Verse 14

    Ndipo pa nthawi imene ola lidzadza, pa nthawi imeneyi, iwo adzasiyanitsidwa wina ndi mnzake

    Verse 15

    Ndipo onse amene adakhulupirira ndipo adachita ntchito zabwino, iwo adzasangalatsidwa m’munda wa Paradiso

    Verse 16

    Iwo amene sadakhulupirire ndipo adakana chiphunzitso chathu ndi kukumana kwa m’moyo umene uli nkudza, awa ndiwo amene adzatengedwa kupita ku chilango

    Verse 17

    Kotero lemekezani Mulungu pamene mulowa nthawi ya madzulo ndi pamene mulowa nthawi ya m’mawa

    Verse 18

    Inde. Kwa Iye kukhale kuyamikidwa kumwamba ndi padziko lapansi ndiponso pa nthawi yamasana ndi yamadzulo

    Verse 19

    Iye ndiye amene amadzutsa anthu kuchokera ku anthu akufa ndipo amadzutsa anthu akufa kuchokera ku anthu amoyo ndiponso amapereka moyo ku nthaka ikafa. Ndipo mmenemo ndi mmene mudzaukitsidwire

    Verse 20

    Ndipo chimodzi cha zizindikiro zake ndi chakuti Iye adakulengani inu kuchokera ku fumbi, ndipo inu, ndinudi, anthu amene mudamwazidwa

    Verse 21

    Ndipo pakati pa zizindikiro china ndi chakuti Iye adalenga akazi kuchokera mwa inu kuti mukhoza kupeza mpumulo mwa iwo ndipo adaika pakati panu chikondi ndi chisoni. Ndithudi muli phunziro muichi kwa anthu amene amaganiza bwino

    Verse 22

    Ndipo pakati pa zizindikiro zake ndi kalengedwe ka kumwamba ndi dziko lapansi ndi kusiyana kwa zilankhulo zanu ndiponso maonekedwe a makungu anu. Ndithudi mu chimenechimulizizindikirokwaanthuophunzira

    Verse 23

    Ndipo pakati pa zizindikiro zake ndi kugona kumene mumagona usiku ndi usana kufunafuna chisomo chake. Ndithudi mu chimenechi muli chizindikiro kwa anthu amene amatha kumva

    Verse 24

    Ndipo pakati pa zizindikiro zake ndi chakuti Iye amakuonetsani mphezi imene imakuchititsani mantha ndiponso kukupatsani chikhulupiriro. Ndipo amatumiza mvula kuchokera ku mitambo ndiponso amapereka moyo ku nthaka ikafa. Ndithudi mu chimenechi muli zizndikiro kwa anthu ozindikira

    Verse 25

    Ndipo pakati pa zizindikiro zake ndi chakuti kumwamba ndi dziko lapansi zimadzichepetsa potsatira malamulo ake ndipo pamene Iye akuitanani inu kamodzi kokha kuchokera m’nthaka, Taonani inu mudzadza mwamsanga msanga

    Verse 26

    Ndipo chilichonse chimene chili kumwamba ndi padziko lapansi ndi chake ndipo zonse zimamumvera Iye

    Verse 27

    Ndipo Iye ndiye amene amayambitsa chilengedwe ndipo adzachibwerezanso ndipo zimenezi ndi zapafupi kwa Iye. Ndipo wake ndi ulemerero kumwamba ndi padziko lapansi. Ndipo Iye ndiye Mwini mphamvu zonse ndi Mwini nzeru zonse

    Verse 28

    Iye ali kupereka chitsanzo chokhudza inu nomwe. Kodi inu muli nawo akapolo amene amakhala anzanu pa zinthu zimene takupatsani ndipo kuti mumagawana nawo zinthuzo mofanana ndiponso mumawaopa iwo monga momwe mumaoperana? Mmenemo ndi mmene timasiyanitsira chiphunzitso chathu kwa anthu amene amazindikira

    Verse 29

    Iyayi! onse osalungama amatsatira zilakolako zawo mosadziwa. Kotero ndani angatsogolere iye amene Mulungu wamusocheretsa? Ndipo iwo sadzakhala ndi wowathandiza

    Verse 30

    Kotero dzipereke kwathunthu ku chipembedzo choonadi, chipembedzo, chenicheni, chimene Mulungu adalamula kuti munthu ayenera kutsatira. Chilengedwe chimene Mulungu adalenga mtundu wa anthu sichingasinthidwe. Ndithudi pali Mulungu, icho ndicho chipembedzo choona. Koma ambiri a mtundu wa anthu sadziwa

    Verse 31

    Lapani kwa Iye ndiponso muopeni Iye. Pitirizani kupemphera nthawi zonse ndipo musakhale inu pakati pa iwo amene amafanizira milungu ina ndi Mulungu weniweni

    Verse 32

    Pali anthu amene amagawa chipembedzo chawo ndi kukhala mipingo yosiyanasiyana ndipo mpingo uliwonse umasangalala ndi zimene uli nazo

    Verse 33

    Ndipo pamene mavuto adza pa anthu, iwo amalira kwa Ambuye wawo ndi kudza kwa Iye modzichepetsa. Koma pamene Mulungu awaonetsa gawo lachisoni chochokera kwa Iye Mwini, ena a iwo amayamba kupembedza milungu ina yoonjezera pa Ambuye wawo

    Verse 34

    Akhala ngati ali kuonetsakusathokozapazimenetawachitira. Basangalalani mwa kanthawi kochepa ndipo posachedwapa mudzadziwa kupusa kwanu

    Verse 35

    Kodi kapena Ife tidawatumizira lamulo limene limanena za zinthu zimene iwo amazipembedza zoonjezera pa Mulungu

    Verse 36

    Ndipo pamene tiwaonetsera anthu chifundo chathu, iwo amasangalala kwambiri chifukwa cha chifundocho ndipo ngati choipa chidza pa iwo chifukwa cha zimene iwo achita ndi manja awo, taonani! Iwo amadandaula kwambiri

    Verse 37

    Kodi iwo saona kuti Mulungu amapereka moolowa manja kwa aliyense amene Iye wamufuna ndiponso zomupatsazochepa munthu yemwe wamufuna. Ndithudi mu chimenechi muli phunziro kwa anthu okhulupirira

    Verse 38

    Kotero apatseni zosowa zawo abale anu, anthu osauka ndi a paulendo. Ichi ndicho chinthu chabwino kwambiri kwa iwo amene afuna chisangalalo cha Mulungu ndipo awa ndiwo amene ali opambana

    Verse 39

    Chimene mumapereka ngati chiongoladzanja kuti chionjezere chuma cha anthu, sichidzakhala ndi chionjezero kwa Mulungu. Koma zopereka zimene mupereka ngati chaulere ndi cholinga chopeza madalitso a Mulungu ndi chimenechi chimene chidzaonjezeredwa kwambirimbiri

    Verse 40

    Ndi Mulungu amene anakulengani inu amene amakupatsani zofuna zanu. Iye adzakonza kuti mufe patsogolopakepanondipokenakaadzakupatsaninsomoyo. Kodi chilipo china chilichonse chimene mungachifanizire ndi chimene chingachite zimenezi? Ulemerero ukhale kwa Iye ndipo Iye akhale zopambana kuposa zonse zimene amazifanizira ndi Iye

    Verse 41

    Zinthu zoipa zalowa m’dziko ndiponso m’nyanja chifukwa cha ntchito za anthu zimene amachita ndi manja awo. Mulungu akhoza kuwalawitsa chilango chifukwa cha ntchito zawo kuti mwina athe kutembenuka

    Verse 42

    Nena “Pitani paliponse pa dziko ndi kuona zimene zidawaonekera anthu amene adalipo kale. Ambiri a iwo adali opembedza mafano.”

    Verse 43

    Kotero dziperekeni kwathunthu ku chipembedzo choona lisanadze tsiku loopsa kuchokera kwa Mulungu limene silidzatheka kulizemba. Pa tsiku limeneli anthu adzagawidwa m’magulu

    Verse 44

    onse osakhulupirira adzalangidwa chifukwa cha kusakhulupirira kwawo ndipo onse amene amachita ntchito zabwino adzadzisungira zinthu zabwino kumwamba

    Verse 45

    Ndipo Iye adzawapatsa malipiro abwino onse amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino kuchokera ku zokoma zake. Ndipo Iye sakonda anthu osakhulupirira

    Verse 46

    Ndipo chimodzi mwa zizindikiro zake ndi chakuti amatumiza mphepo imene imabweretsa zabwino ndi cholinga choti mulawe chisomo chake ndiponso kuti zombo ziyende mwamalamulo ake ndiponso kuti inu muzifunafuna chifundo chake ndi kumuthokoza

    Verse 47

    Ndithudi Ife tidatumiza, Atumwi kwa anthu awo iwe usanabadwe ndipo iwo adadza kwa iwo ndi chiphunzitso choyenera. Ife tidapereka chilango kwa anthu ochimwa ndipo kuthandiza anthu okhulupirira ndi udindo wosatha kwa Ife

    Verse 48

    Mulungu ndiye amene amatumiza mphepo kuti iyendetse mtambo ndipo amaumwaza mlengalenga monga momwe wafunira. Iye amauphwanya ndipo inu mumaona mvula ili kugwa kuchokera mu mtambowo. Iye amagwetsa mvula pa akapolo ake amene wawafuna. Taonani! Iwo amakhala osangalala

    Verse 49

    Ngakhale kuti, iyo isanadze, iwo anali kuda nkhawa

    Verse 50

    Taonani zizindikiro za chisoni cha Mulungu mmene amaperekera moyo ku nthaka imene inali yakufa. Ndithudi Iye adzadzutsa zakufa kuti zikhale zamoyo. Iye ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse

    Verse 51

    Ndipo ngati Ife tikatumiza mphepo imene imapangitsa mbewu zawo kusanduka za chikasu, iwo amakhala osathokoza

    Verse 52

    Ndithudi iwe siungathe kumupanga munthu wakufa kuti amve ndiponso siungathe kumupanga munthu wosamva kuti amve kuitana pamene iwo atembenuka ndi kuthawa

    Verse 53

    Ndipo iwe siungathe kumutsogolera munthu wakhungu kuti asiye kulakwa kwake. Palibe amene adzakumvera kupatula okhawo amene amakhulupirira mu chiphunzitso chathu

    Verse 54

    di Mulungu amene adakulengani inu ofoka ndipo adakupatsani mphamvu pambuyo pa kufoka. Ndipo atakupatsani mphamvu adakupatsani kufoka ndi imvi. Iye amalenga chilichonse chimene wafuna ndipo ndiye amene amadziwa zonse ndipo ndiye Mwini mphamvu

    Verse 55

    Ndipo pamene ola lidzadza, anthu ochimwa adzalumbira kuti adangokhala ola limodzi lokha. Kotero iwo amakhala onamizidwa

    Verse 56

    Ndipo iwo amene adapatsidwa nzeru ndi chikhulupiriro adzati, “Ndithudi inu mwakhala molingana ndi malamulo a Mulungu mpaka pa tsiku louka kwa akufa. Kotero ili ndilo tsiku louka kwa akufa koma inu simunalidziwe ayi.”

    Verse 57

    Koma patsiku limeneli zodandaula zawo sizidzawathandiza anthu onse ochimwa ndipo sizidzamveka ayi

    Verse 58

    Ndithudi m’Buku ili la Korani anthu tawaikiramo zitsanzo zambiri zosiyanasiyana ndipo ngati iwe utawabweretsera chiphunzitso iwo amene sakhulupirira adzati, “Iwe siuli kutsatira china chilichonse koma bodza ndi matsenga.”

    Verse 59

    Mmenemo ndi mmene Mulungu amatsekera mitima ya anthu osadziwa

    Verse 60

    Kotero pirirani. Lonjezo la Mulungu ndi loona ndipo usalole anthu opanda chikhulupiriro kuti akuderere iwe

    Unexpected Application Error!

    Unexpected token '<', "<!DOCTYPE "... is not valid JSON

    SyntaxError: Unexpected token '<', "<!DOCTYPE "... is not valid JSON