Back to Languages

    Chichewa - Chapter 32

    Translation by Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

    Verse 1

    Alif Lam Mim

    Verse 2

    Ichi ndi chivumbulutso cha Buku Lopatulika limene mulibe zokayikitsa ndi chochokera kwa Ambuye wa zolengedwa zonse

    Verse 3

    Kodi kapena iwo amati wapeka yekha? Iyayi, ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wake kuti uchenjeze anthu amene kuyambira kale mchenjezi sanadze kwa iwo, kuti iwo akhoza kutsatira njira yoyenera

    Verse 4

    Mulungu ndiye amene adalenga kumwamba ndi dziko Sajda 439 lapansi ndi zonse zimene zili m’menemo m’masiku asanu ndi limodzi. Ndipo atatero Iye adabuka pa mpando wake wachifumu. Inu mulibe wokuyang’anirani kapena wokuthandizani kupatula Iye yekha. Kodi simungaganize

    Verse 5

    Iye amalamulira zinthu kuchokera kumwamba mpaka pa dziko lapansi ndipo zidzakwera kudza kwa Iye m’tsiku limene muyeso wake ungathe kuyerekezedwa ndi zaka chikwi chimodzi mwa chiwerengero chomwe inu mumachidziwa

    Verse 6

    Uyundiyewodziwazobisikandizooneka, Mwini mphamvu, ndi Mwini chisoni chosatha

    Verse 7

    Amene adalenga chilichonse m’maonekedwe abwino. Ndipo adalenga munthu kuchokera ku dothi

    Verse 8

    Ndipo adalenga ana ake kuchokera ku dontho lamadzi onyozeka

    Verse 9

    Ndipo iye adamuumba munthu mwaubwino ndipo adamuuzira Mzimu wake. Ndipo Iye adakupatsani inu makutu, maso ndi mitima, inu simuthokoza nthawi zambiri

    Verse 10

    Iwo adati, “Chiyani! Pamene ife taikidwa m’manda, kodi tingadzalengedwenso?” Ndithudi iwo adakana kuti adzakumana ndi Ambuye wawo

    Verse 11

    Nena “Mngelo wa imfa, amene adasankhidwa kukuyang’anirani inu, adzakupangitsani kuti mufe. Kotero inu mudzabwerera kwa Ambuye wanu.”

    Verse 12

    Iwe ukadangodzaona mmene anthu ochimwa adzagwetsera mitu yawo pamaso pa Ambuye wawo nati, “Ambuye wathu! Ife taona ndipo tamva. Tsopano tibwezereni pa dziko lapansi ndipo ife tidzagwira ntchito zachilungamo chifukwa ife, ndithudi, takhulupirira.”

    Verse 13

    Ife tikadafuna, ndithudi, tikadatsogolera mzimu uliwonse ku njira yoyenera. Koma kuti mawu ochokera kwa Ine adakwanitsidwa. “Ine ndidzadzadza Gahena ndi majini pamodzi ndi anthu.”

    Verse 14

    Lawani chilango tsopano, chifukwa inu mudaiwala za tsikuli. Ndipo nafenso takuiwalani. Kotero inu lawani chilango chosatha chifukwa cha ntchito zanu zoipa

    Verse 15

    Ndi okhawo amene amakhulupirira chiphunzitso chathu amene chiphunzitsocho chimati chikaphunzitsidwa, amagwa pansi kupembedza ndipo amayamikandikulemekeza Mulunguwawomodzichepetsa

    Verse 16

    Iwo amasiya makama awo ndi cholinga chopempha kwa Ambuye wawo mwamantha ndi mwa chikhulupiriro. Ndipo amapereka zaulere kuchokera ku chuma chimene tidawapatsa

    Verse 17

    Tsopano palibe munthu amene amadziwa madalitso amene ali kuwasungira m’nkhokwe ngati malipiro a ntchito zawo zabwino

    Verse 18

    Kodi munthu wokhulupirira angafanane ndi munthu woswa malamulo ndi woipa? Iyayi, sangafanane

    Verse 19

    Iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, adzalandira minda ngati malo awo okhala chifukwa cha ntchito zawo zabwino zimene anachita

    Verse 20

    Ndipo iwo amene amaswa malamulo, malo awo okhala ndi kumoto ndipo nthawi zonse zimene iwo adzafuna kuchokako, adzabwezedwanso komweko. Ndipo kudzanenedwa kwa iwo kuti, “Lawani ululu wa moto umene munkati ndi bodza.”

    Verse 21

    Ndipo, ndithudi, Ife tidzawalawitsa, chilango cha m’moyo uno chisanadze, chilango choyamba kuti mwina akhoza kutembenuka

    Verse 22

    Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amati akakumbutsidwa chiphunzitso cha Ambuye wake, iye amabwerera m’mbuyo? Ndithudi Ife tidzalanga anthu ochimwa

    Verse 23

    Ndipo, ndithudi, Ife tidamupatsa Buku Mose ndipo musakayike za kulandira kwake ndipo tidalipanga ilo kukhala chotsogolera ana a Israyeli

    Verse 24

    Ndipo tidasankha pakati pawo, atsogoleri amene amapereka malangizo potsatira malamulo athu, pamene iwo anali kupirira ndi kukhulupirira mu chiphunzitso chathu

    Verse 25

    Ndithudi Ambuye wako adzaweruza pakati pawo pa tsiku louka kwa akufa pa nkhani zimene anali kutsutsana

    Verse 26

    Kodi icho sichiwaphunzitsa phunziro kuti kodi ndi mibadwo ingati imene tidaononga iwo asanadze, m’nyumba zawo zimene amalowa ndi kutulukamo? Ndithudi mu izo muli chiphunzitso. Kodi iwo sangamve

    Verse 27

    Kodi iwo saona kuti Ife timagwetsa mvula panthaka youma ndi kumeretsa mbewu zimene iwo ndi ziweto zawo zimadya? Kodi alibe maso oti angaone

    Verse 28

    Iwo amafunsa kuti “Kodi chiweruzo chimenechi chidzachitika liti ngati zimene munenazi ndi zoona?”

    Verse 29

    Nena, “Pa tsiku lachiweruzo, chikhulupiriro cha iwo amene sakhulupirira sichidzawathandiza ndiponso sadzapeza mpumulo.”

    Verse 30

    Kotero asiye okha ndipo dikira ndithudi nawonso ali kudikira