Back to Languages

    Chichewa - Chapter 47

    Translation by Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

    Verse 1

    Iwo amene sakhulupirira ndipo amaletsa anzawo kutsatira njira ya Mulungu, Iye adzasandutsa ntchito zawo kukhala zopanda pake

    Verse 2

    Koma iwo amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino, ndipo amakhulupirira mu chivumbulutso chimene chatumizidwa kwa Muhammad, chifukwa icho ndi choonadi chochokera kwa Ambuye wawo, Iye adzawachotsera zoipa ndi kulongosola machitidwe awo

    Verse 3

    Ichi ndi chifukwa chakuti onse amene sakhulupirira amatsatira zabodza pamene iwo amene amakhulupirira amatsatira choonadi chochokera kwa Ambuye wawo. Mmenemo ndi mmene Mulungu amaonetsera zitsanzo zake kwa anthu

    Verse 4

    Motero pamene inu mukumana ndi anthu osakhulupirira pa nkhondo, thyolani makosi awo, mpaka pamene mukupha ndi kuvulaza ambiri ndipo muwagwire kukhala akaidi ndipo pambuyo pake mukhoza kuwamasula powaonetsa chisoni kapena akhale ngati chigwiriro mpaka pamene nkhondo itatha. Motero inu mwalamulidwa. Koma chikadakhala chifuniro cha Mulungu, ndithudi, Iye Mwini wake akadawapatsa chilango chowayenera. Koma Iye wafuna kuti inu mumenyane nawo ndi cholinga chokuyesani wina ndi mnzake. Koma iwo amene aphedwa m’njira ya Mulungu, Iye sadzalola kuti ntchito zawo zipite pachabe

    Verse 5

    Iye adzawatsogolera ndi kulemekeza malo awo

    Verse 6

    Iye adzawalowetsa ku Paradiso kumene adawalonjeza kale

    Verse 7

    Oh inu anthu okhulupirira! Ngati inu muthandiza m’ntchito za Mulungu, Iye adzakuthandizani inu ndipo adzakulimbikitsani

    Verse 8

    Koma iwo amene sakhulupirira, kwa iwo kuli chionongeko ndipo Mulungu adzapanga kuti ntchito zawo zonse zikhale zopanda phindu

    Verse 9

    Ichi ndi chifukwa chakuti iwo amadana ndi chivumbulutso cha Mulungu, ndipo Iye wapanga ntchito zawo kukhala zopanda pake

    Verse 10

    Kodi iwo sadayende padziko lapansi ndi kuona zimene zidawachitikira iwo amene adalipo kale? Mulungu adaponya chionongeko pa iwo ndipo onse osakhulupirira adzaona mavuto a mtundu womwewo

    Verse 11

    Ichi ndi chifukwa chakuti Mulungu ndi Mtetezi wa iwo amene amakhulupirira pamene anthu osakhulupirira alibe wowateteza

    Verse 12

    Ndithudi Mulungu adzalowetsa ku minda imene pansi pake pamayenda mitsinje yamadzi onse amene amakhulupirira ndipo amachita ntchito zabwino. Pamene onseamenesakhulupirirandipoamadzisangalatsandikudya ngati momwe zimadyera nyama kumoto ndiko kudzakhala malo awo okhala

    Verse 13

    Ndi mizinda yambiri imene idali ndi mphamvu zoposa Mzinda umene wakupirikitsa iwe imene Ife tidaiononga. Ndipo padalibe wina wowathandiza

    Verse 14

    Kodi iye amene watsogozedwa bwino ndi Ambuye wake ndi wofanana ndi iwo amene ntchito zawo zoipa zimaoneka ngati zabwino ndipo amatsatira zilakolako zawo zopanda pake

    Verse 15

    Mwaonekedwe amunda umene iwo amene amalewa zoipa alonjezedwa ndi akuti m’menemo muli mitsinje yamadzi amene sakuphwa ndi mitsinje yamkaka umene siusintha kukoma kwake, ndipo mitsinje ya vinyo ndi mitsinje ya uchi wabwino. Imo muli zipatso zosiyanasiyanandichikhulupirirochochokerakwaAmbuye wawo. Kodi awa ali ngati iwo amene adzakhala kumoto mpaka kalekale ndipo amapatsidwa madzi ogaduka amene amaboola m’matumbo

    Verse 16

    Ndipo pakati pawo pali iwo amene amamva zimene iwe umanena, mpaka pamene akusiya iwe, iwo amati kwa amene adapatsidwa nzeru, “Kodi ndi chiyani chimene wanena posachedwapa?” Awa ndiwo amene mitima yawo yatsekedwa ndi Mulungu ndipo amatsatira zilakolako zopanda pake

    Verse 17

    Pamene iwo amene amatsatira njira yoyenera, Iye amawatsogolera ndi kuwonjezera chikhulupiriro chawo

    Verse 18

    Kodi iwo akudikira china kuposa Ola kuti lidze kwa iwo mwadzidzidzi? Koma zizindikiro zina zadza kale, ndipo chitadza pa iwo, kodi iwo adzapindula chiyani ndi chikumbutso

    Verse 19

    Motero dziwani kuti kulibe mulungu wina koma Mulungu weniweni ndipo pempha chikhululukiro chako ndi cha amuna ndi akazi amene amakhulupirira. Ndipo Mulungu amadziwa mmene inu mumayendera ndi mmene mumakhalira m’nyumba zanu

    Verse 20

    Iwo amene amakhulupirira amati, “Kodi bwanji Mutu wina siudavumbulutsidwe?” Koma pamene mutu wotsimikiza uvumbulutsidwa ndipo kumenya nkhondo kulamulidwa mmenemo iwe udzaona iwo amene m’mitima mwawo muli matenda ali kukuyang’ana iwe ngati munthu amene ali kukomoka pamene imfa ili kudza kwa iye. Koma zinali bwino kwa iwo

    Verse 21

    Kumvera ndi mau abwino (zikadakhala zinthu zabwino). Ndipo pamene nkhani iweruzidwa, ndipo iwo akadadzipereka mwachoonadi kwa Mulungu, ndithudi, zikadakhala zabwino kwa iwo

    Verse 22

    Kodi ngati inu mukadapatsidwa udindo wolamulira, mukadachita zinthu zoipa padziko ndi kuphwanya ubale wanu ndi anthu a mtundu wanu

    Verse 23

    Amenewa ndiwo amene Mulungu wawatemberera ndipo Iye wawapanga iwo kukhala osamva ndi akhungu

    Verse 24

    Kodi iwo sangaganize za uthenga wa m’Korani? Kodi kapena mitima yawo ndi yotsekedwa

    Verse 25

    Ndithudi iwo amene amabwerera m’mbuyo ndi kukhalanso osakhulupirira pamene atalandira kale ulangizi, amatsogozedwa ndi Satana amene amawanamiza ndi zinthu zopanda pake

    Verse 26

    Ichi ndi chifukwa chakuti iwo amanena kwa iwo amene amadana ndi zimene Mulungu wavumbulutsa kuti, “Ife tidzakumverani mu zina za nkhani zimenezi.” Koma Mulungu amadziwa zinsinsi zawo zonse

    Verse 27

    Kodi iwo adzachita chiyani pamene angelo adzalanda miyoyo yawo ndi kuwamenya pa nkhope ndi m’misana yawo

    Verse 28

    Ichi ndi chifukwa chakuti iwo amatsatira zinthu zimene zimakwiyitsa Mulungu ndipo amadana ndi zimene zimamukondweretsa Iye. Kotero Mulungu adasandutsa ntchito zawo kukhala zinthu zopanda pake

    Verse 29

    Kodi iwo amene m’mitima mwawo muli matenda amaganiza kuti Mulungu sadzaulula zoipa zawo zonse

    Verse 30

    Ife tikadafuna tikadakuonetsa iwe ndipo iwe ukadawadziwa chifukwa cha zizindikiro zawo ndipo, ndithudi, udzawadziwa chifukwa cha mayankhulidwe awo. Mulungu amadziwa ntchito zanu

    Verse 31

    Ndithudi Ife tidzakuyesani mpaka pamene tiyesa onse amene amalimbikira kwambiri ndi iwo amene opirira ndipo Ife tidzayesa ntchito zanu

    Verse 32

    Ndithudi iwo amene sakhulupirira ndipo amaletsa anthu kutsata njira ya Mulungu ndipo amatsutsana ndi Mtumwi pamene atalandira kale langizo loyenera, iwo sangathe kugonjetsa Mulungu mwanjira ina iliyonse. Koma Iye adzafafaniza ntchito zawo zonse ndi kuzisandutsa kukhala zopanda pake

    Verse 33

    Oh inu anthu okhulupirira! Mverani Mulungu ndipo mverani Mtumwi wake ndipo musasandutse ntchito zanu kukhala zopanda pake

    Verse 34

    Ndithudi onse amene sakhulupirira ndipo amaletsa anthu kutsatira njira ya Mulungu, ndipo amafa ali osakhulupirira Mulungu sadzawakhululukira

    Verse 35

    Motero inu musafoke ndipo musafunse kuti kukhale mtendere pamene muli kupambana. Mulungu ali ndi inu ndipo Iye sadzapungula mphotho ya ntchito zanu zabwino

    Verse 36

    Moyo wa pa dziko lino ndi masewera enieni ndiponso kotayira nthawi koma ngati inu mukhulupirira ndi kulewa machimo, Iye adzakulipirani inu ndipo sadzakufunsani za katundu amene muli naye

    Verse 37

    Ngati Iye akadakufunsani za katundu wanu ndi kukuumirizani, ndithudi, inu mukadachita umbombo ndipo Iye adzaulula zinsinsi zanu zonse

    Verse 38

    Taonani! Inu ndinu amene mwaitanidwa kupereka m’njira ya Mulungu koma pakati panu pali anthu omwe ndi mbombo. Ndipo aliyense amene achita umbombo amadzimana yekha. Mulungu sasowa kanthu pamene inu ndinu osauka. Ndipo ngati inu mubwerera m’mbuyo Iye adzaika m’malo mwanu anthu ena ndipo sadzakhala olingana ndi inu