Back to Languages
Chichewa - Chapter 6
Translation by Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula
Verse 1
Kuyamikidwa ndi kwa Mulungu amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi kukhazikitsa mdima ndi kuwala, komabe anthu osakhulupirira amakhazikitsa milungu ina kuti ndi yolingana ndi Ambuye wawo
Verse 2
Iye ndiye amene adakulengani inu kuchokera ku dothi ndipo Iye adakhazikitsa nthawi. Ndipo Iye adakhazikitsanso nthawi ina, komabe inu mumakaika
Verse 3
Iye ndi Mulungu wa kumwamba ndi dziko lapansi. Iye amadziwa zonse zimene mumabisa ndi zonse zimene mumaulula. Ndipo amadziwa zimene mumachita
Verse 4
Ndipo chizindikiro sichidza kwa iwo kuchokera ku zizindikiro za Ambuye wawo, chimene iwo amachivomereza
Verse 5
Ndithudi iwo adakana choonadi pamene chidadza kwa iwo; koma kudzadza kwa iwo nkhani za zimene adali kuchita chipongwe
Verse 6
Kodi iwo sadaone kuti kodi ndi mibadwo ingati, iwo asanabadwe, imene Ife tidawononga imene tidakhazikitsa pa dziko kukhala ya mphamvu kwambiri kuposa inu? Ndipo timawatumizira mvula yochuluka kuchokera kumwamba ndi kuipanga mitsinje yamadzi kuyenda pansi pawo. Komabe tidawawononga chifukwa cha machimo awo ndipo tidalenganso, pambuyo pa iwo, mibadwo ina
Verse 7
Ngakhale Ife tikadakutumizira iwe uthenga wolembedwa kale papepala kuti alikhudze ndi manja awo, anthu osakhulupirira akadanena kuti: “Ichi si china ayi koma matsenga enieni.”
Verse 8
Iwo adati: Kodi ndi chifukwa chiyani mngelo sadatumizidwe kwa iye? Ife tikadatumiza mngelo, nkhani ikanaweruzidwa nthawi yomweyo, ndipo sakadapatsidwa mpata
Verse 9
Ndipo ngati Ife tikadamupanga iye kukhala mngelo, ndithudi Ife tikadamupanga iye kuti azioneka ngati munthu ndipo tikadawasokoneza ndi zimene iwo adasokonezeka nazo kale
Verse 10
Ndipo, ndithudi, Atumwi ena adasekedwa iwe usadadze, koma amene anali kuwaseka anazungulilidwa ndi zinthu zomwe iwo anali kuseka
Verse 11
Nena: “Yendani pa dziko lapansi ndipo muone mapeto a anthu amene anakana choonadi.”
Verse 12
Nena: “Kodi mwini wa chilichonse chimene chili kumwamba ndi dziko lapansi ndani?” Nena: “Mwini wake ndi Mulungu” ndipo Iye adadzilamula yekha kuti azionetsa chifundo. Ndipo, ndithudi, Iye adzakusonkhanitsani nonse pa tsiku la kuuka kwa akufa, tsiku lopanda chikaiko. Iwo amene asochera sadzakhulupirira
Verse 13
Ndipo zake ndi zonse zimene zimapezeka usiku ndi usana ndipo Iye ndi Wakumva ndi Wozindikira
Verse 14
Nena: “Kodi ine nditenge wina aliyense osati Mulungu kuti akhale Mtetezi wanga, Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi? Iye ndiye amene amadyetsa pamene Iye sadyetsedwa.” Nena: “Ndithudi ine ndalamulidwa kukhala woyamba wa anthu ogonjera kwa Mulungu.” Iwe usadzakhale mmodzi wa iwo amene amapembedza mafano
Verse 15
Nena: “Ine ndikuopa, ngati nditanyoza Ambuye wanga, chilango cha tsiku lalikulu.”
Verse 16
Aliyense amene adzapulumutsidwa ku mazunzo a tsiku limeneli adzakhala atalandira chifundo cha Mulungu. Kumeneko ndiko kudzakhala kupambana kwenikweni koonekeratu
Verse 17
Ndipo ngati Mulungu akupatsa mavuto, palibe wina amene angachotse mavutowo koma Iye yekha; ndipo ngati Iye akupatsa zinthu zabwino, Iye ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse
Verse 18
Iye ali ndi mphamvu pa akapolo ake ndipo Iye ndiye Wanzeru ndi Wodziwa zonse
Verse 19
Nena: “Kodi ndi chiani chili chachikulu mu umboni?” Nena: “Mulungu ndiye mboni pakati pa ine ndi inu. Buku la Korani lavumbulutsidwa kwa ine kuti ndikuchenjezeni inu ndi ena onse amene angalandire chivumbulutsochi. Kodi inu mungachitire umboni kuti pali milungu ina yoonjezera pa Mulungu weniweni?” Nena: “Ine sindingaikire umboni pa nkhani yotere.” Nena: “Iye ndi Mulungu mmodzi yekha. Ndipo, ndithudi, ine ndili kutali ndi milungu imene inu muli kupembedza powonjezera pa Iye.”
Verse 20
Kwa iwo amene tidawapatsa Buku amamudziwa Iye mongamomweamadziwiraanaawo. Komaiwoameneataya mizimu yawo sadzakhulupirira
Verse 21
Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu kapena amakana chivumbulutso chake? Ndithudi anthu ochita zoipa sadzapambana ayi
Verse 22
Ndipo patsiku limene tidzawasonkhanitsa onse pamodzi, Ife tidzati kwa anthu opembedza mafano: “Kodi ali kuti mafano anu aja munkawadalira?”
Verse 23
Iwo sadzawiringula china chili chonse koma adzati: “Tilumbira pali Mulungu, Ambuye wathu, kuti ife sitidali kupembedza mafano pambali pa Mulungu.”
Verse 24
Taona mmene iwo ali kudzinamiza okha! Koma bodza limene anali kupeka lidzawathawira
Verse 25
Ndipo ena a iwo amamvetsera kwa iwe koma Ife taika tchingo m’mitima mwawo kuti asazindikire ndipo m’makutu mwawo ndi mogontha ndipo iwo akaona chizindikiro chilichonse, sadzachikhulupirira ndipo amadza kwa iwe kudzatsutsana nawe, ndipo anthu osakhulupirira amati: “Ichi sichina chilichonse koma nkhani zopeka za anthu a kale kwambiri.”
Verse 26
Ndipo iwo amaletsa anthu kumvetsera ndipo iwo amadzitalikitsa okha kwa Iye. Koma iwo sali kuwononga wina aliyense koma akudziononga okha. Koma iwo sazindikira
Verse 27
Koma iwe ukadawaona pamene iwo adzaimitsidwe moyandikira moto! Iwo adzati: “Zikadakhala kuti tinabwezedwa! Ife sitikadakana chivumbulutso cha Ambuye wathu ndipo tikadakakhala anthu okhulupirira.”
Verse 28
Koma zonse zimene adali kuzibisa kale zidzaonekera poyera kwa iwo. Komabe akadabwezedwa, iwo akadakabwerera ku zinthu zimene adaletsedwa. Ndithudi iwo ndi anthu a bodza
Verse 29
Iwo adanenetsa kuti: “Kulibenso moyo wina uliwonse kupatula moyo wathu wadziko lapansi ndiponso ife sitidzaukitsidwa kwa akufa.”
Verse 30
Ndipo iwe ukadawaona pamene ali kusonkhanitsidwa kuima pamaso pa Ambuye wawo! Iye adzati: “Kodi izi sizoona?” Iwo adzayankha: “Ndi zoona pali Ambuye wathu.” Ndipo Iye adzati: “Motero lawani chilango chifukwa inu simunali okhulupilira.”
Verse 31
Ndithudi iwo ndi olephera kwambiri amene amakana kuti adzakumana ndi Ambuye wawo mpaka pamene ola loopsa lidza pa iwo mwadzidzidzi ndipo iwo adzafuula kuti: “Kalanga ife tidali kunyalanyaza kwambiri!” Iwo adzanyamula katundu wawo pa misana yawo ndipo zoipa kwambirizimeneadzasenza
Verse 32
Ndipomoyowapadzikolino lapansi siuli kanthu konse koma masewera ndi nthabwala. Koma yabwino kwambiri ndi nyumba m’moyo umene uli nkudza kwa amene amaopa. Kodi simungazindikire
Verse 33
Ife tili kudziwa kuti zonse zimene ali kunena zili kukukhumudwitsa. Sindiwe amene iwo ali kukana koma ndi chivumbulutso cha Mulungu chimene anthu ochita zoipa ali kukana
Verse 34
Ndithudi Atumwi ena adakanidwa iwe usanadze koma iwo adapilira pa zimene adali kuwanena ndipo anazunzidwa mpaka pamene thandizo lathu lidadza kwa iwo ndipo palibe amene angasinthe chilamulo cha Mulungu. Ndithudi iwe udamva nkhani zaAtumwi
Verse 35
Ngati uona kuti kukana kwawo kwanyanya ndipo kuti sungathe kupirira, peza ngati ungathe, njira yapansi pa nthaka kapena makwerero oti ukwere kumwamba, kuti ukhoza kuwabweretsera chizindikiro. Ngati Mulungu akadafuna, Iye akadawasonkhanitsa onse ku chilangizo choona ndipo iwe usakhale mmodzi wa mbuli
Verse 36
Ndi okhawo amene amamva, amene adzapindula koma anthu akufa Mulungu adzawadzutsa kwa akufa ndipo kwa Iye adzabwerera
Verse 37
Iwo amafunsa: “Kodi ndi chifukwa chiyani chizindikiro sichinadze kwa iye kuchokera kwa Ambuye wake?” Nena: “Ndithudi Mulungu ali ndi mphamvu zotumiza chizindikiro koma ambiri a iwo sazindikira.”
Verse 38
Palibe chinthu cha moyo padziko lapansi kapena mbalame imene imauluka ndi mapiko ake awiri imene ndi zosiyana ndi inu. Ife sitidasiye china chilichonse m’Buku ndipo kwa Ambuye wawo iwo adzasonkhanitsidwa
Verse 39
Koma iwo amene amakana zizindikiro zathu, ndi agonthi m’khutu ndi abububu mu mdima. Mulungu amasocheza aliyense amene Iye wamufuna ndipo amatsogolera, kunjira yoyenera, aliyense amene Iye wamufuna
Verse 40
Nena: “Ndiuzeni, ngati chilango cha Mulungu chitadza pa inu kapena ola loopsa lidza pa inu, kodi inu mudzapempha wina amene sali Mulungu kuti akuthandizeni inu? Yankhani ngati mukunena zoona.”
Verse 41
Iyayi! Ndi kwa Iye yekha kumene inu mumapempha ndipo ngati Iye atafuna akhoza kukuchotserani zovuta zanu, ndipo inu pa nthawi imeneyi mudzaiwala mafano anu
Verse 42
Ndithudi Ife tidatumiza, iwe usanadze, Atumwi ku mitundu ina. Ndipo tidawagwetsera umphawi, matenda ndi matsoka ochuluka kuti akhoza kukhulupilira modzichepetsa
Verse 43
Nanga ndi chifukwa chiyani iwo sadadzichepetse pamene mazunzo athu adadza pa iwo? Koma mitima yawo inalimba ndipo Satana adawakongoletsera zochita zawo zoipa zimene adali kuchita
Verse 44
Ndipo pamene iwo adaiwala zimene adachenjezedwa, Ife tidawatsegulira makomo a zinthu zonse zabwino mpaka pamene adasangalala ndi zimene adapatsidwa, mwadzidzidzi Ife tidawalanga ndipo ah! Iwo adalowa m’chionongeko wokhumudwa ndi a chisoni
Verse 45
Motero maziko a anthu ochimwa adaonongedwa. Ndipo kutamandidwa konse kukhale kwa Mulungu, Ambuye wa zolengezedwa zonse
Verse 46
Nena: “Tandiuzani! Ngati Mulungu akadakulandani kumva kwanu, kuona kwanu ndi kutseka mitima yanu, kodi pali mulungu wina, woonjezera pa Mulungu weniweni, amene angakubwezereni zimenezi?” Taonani mmene tifotokozera chivumbulutso chathu ndi mmene iwo sakhulupilira
Verse 47
Nena: “Ndiuzeni, ngati chilango cha Mulungu chitadza mwadzidzidzi kapena moonekera, kodi ndani angaonongeke kupatula anthu ochita zoipa?”
Verse 48
Ndipo Ife sititumiza Aneneri koma kuti azikawauza anthu nkhani yabwino ndi kuwachenjeza. Motero aliyense amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, iye sadzakhala ndi nkhawa kapena kudandaula
Verse 49
Koma iwo amene akana chivumbulutso chathu, chilango chidzawapeza chifukwa cha kusakhulupilira kwawo
Verse 50
Nena: “Ine sindili kukuuzani kuti ndili ndi chuma cha Mulungu kapena kuti ndimadziwa zinthu zobisika kapena kuti ine ndine mngelo. Ine sinditsatira china chilichonse kupatula zokhazo zimene zavumbulutsidwa kwa ine.” Nena: “Kodi munthu wakhungu ndi munthu openya angafanane? Kodi inu simungaganize?”
Verse 51
Ndipo achenjeze iwo amene amaopa kuti adzasonkhanitsidwa kupita kwa Ambuye wawo, amene alibe wowasamalira kapena mkhalapakati woonjezera pa Mulungu, kuti akhoza kumalewa zoipa
Verse 52
Ndipo usawathamangitse iwo amene amapembedza Ambuye wawo m’mawa ndi madzulo pofuna chisangalalo chake. Iwe siudzaimbidwa mlandu pa zochita zawo ndipo nawonso sadzaimbidwa mlandu pa zochita zako ndipo ngati iwe uwathamangitsa udzakhala mugulu la anthu opanda chilungamo
Verse 53
Motero ife tinawayesa ena a iwo kupyolera mwa anzawo kuti akhoza kunena, “Kodi awa ndiwo amene Mulungu wawadalitsa pakati pathu?” Kodi Mulungu sazindikira anthu othokoza
Verse 54
Ngati atadza kwa iwe anthu amene amakhulupirira chivumbulutso chathu. Nena, “Mtendere ukhale pa inu.” Ambuye wanu adadzilamulira yekha kuti azionetsa chisoni kuti ngati wina wa inu achita choipa chifukwa chosadziwa ndipo alapa pambuyo pake ndipo achita ntchito zabwino, ndithudi Iye ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha
Verse 55
Motero Ife timafotokoza chivulumbutso chathu poyera kuti njira ya anthu ochita zoipa ionekere poyera
Verse 56
Nena, “Ine ndaletsedwa kupembedza milungu imene inumumaipembedzapowonjezerapa Mulungu.” Nena,“Ine sindidzatsatira zilakolako zanu zachabe. Ngati nditatero ndiye kuti ndasochera ndipo ine sindikhala mugulu la anthu otsogozedwa bwino.”
Verse 57
Nena, “Ine ndalandira umboni wokwana kuchokera kwa Ambuye wanga komabe inu muli kuukana. Ine ndilibe mphamvu yobweretsa msangamsanga chilango chimene mufuna. Chiweruzo chili m’manja mwa Mulungu yekha, Iye amanena zoona ndipo ndi yekhayo amene ali wabwino poweruza.”
Verse 58
Nena, “Ine ndikadakhala nacho chimene mufuna mwamsanga msanga, mkangano wa pakati pa inu ndi ine ukadaweruzidwa kalekale koma Mulungu amadziwa anthu onse ochita zoipa.”
Verse 59
Iye ali ndi makiyi a zinthu zonse zobisika, palibe wina amene azidziwa koma Iye yekha. Iye amadziwa zonse zimene zili m’nthaka ndiponso m’nyanja; ndipo lisadagwe tsamba Iye amalidziwa. Palibe mbewu mu mdima wa nthaka kapena china chilichonse cha chiwisi kapena chouma koma zonsezo zidalembedwa mu Buku looneka bwino
Verse 60
Iye ndiye amene amachotsa mizimu yanu nthawi yausiku ndipo amadziwa zonse zimene mwachita masana ndipo amakudzutsani kuti mukwaniritse nthawi imene idaperekedwa pa moyo wanu ndipo pambuyo pake nonse mudzabwerera kwa Iye. Ndipo Iye adzakuuzani zonse zimene mumachita
Verse 61
Iye ndi wamphamvu pa akapolo ake ndipo amatumiza atetezi amene amakuyang’anirani inu mpaka pamene mmodzi wa inu imufikira imfa; Atumiki athu amachotsa moyo wake ndipo iwo sanyoza zimene alamulidwa
Verse 62
Ndipo iwo amabwerera kwa Mulungu, Ambuye wawo woona. Ndithudi Iye ndiye muweruzi ndipo Iye ndi wachangu powerengera zochita zanu
Verse 63
Nena, “Kodi ndani amakupulumutsani m’mavuto a pa mtunda ndi a pa nyanja ndi pamene inu mumamupempha Iye modzichepetsa ndi mwamseri, ponena kuti: ‘Ngati Iye atipulumutsa ife pa mavuto awa, ndithudi, ife tidzakhala othokoza.”
Verse 64
Nena, “Mulungu amakupulumutsani inu ku zovuta izi ndi kumavuto ena onse, komabe inu mumapembedzabe mafano mowonjezera pa Iye.”
Verse 65
Nena, “Iye ali ndi mphamvu yotumiza chilango chake pa inu kuchokerapamutupanukapenapansipamapazianukapena kukugawani inu kukhala m’magulu a anthu osagwirizana ndi kukulawitsani mazunzo ochokera kwa anzanu. Taonani mmene timaonetsera poyera chivumbulutso chathu kuti akhale ozindikira.”
Verse 66
Koma anthu ako alikana ili ngakhale lili choonadi chenicheni. Nena: “Ine sindine Msungi wanu ayi.”
Verse 67
Nkhani iliyonse ili ndi nthawi yake ndipo posachedwapa mudzazindikira
Verse 68
Ndipo pamene iwe uwaona iwo amene amanyoza chivumbulutso chathu, usakhale nawo pamodzi mpaka pokhapokha akamba nkhani ina. Ngati satana akuiwalitsa, ndipo pambuyo pake ukumbukira usakhale mgulu la anthu ochita zoipa
Verse 69
Iwo amene amaopa Mulungu alibe udindo pa iwo koma kungowakumbutsa kuti apewe kunyoza
Verse 70
Apewe iwo amene amasandutsa chipembedzo chawo kukhala masewera kapena nthabwala ndipo asokonezeka ndi zokoma za moyo wa dziko lapansi. Koma achenjeze ndi ilo kuti ungadzaonongeke mzimu wawo chifukwa cha zimene udachita pamene siudzakhala ndi wousamalira kapena kuwuteteza kupatula Mulungu, ndipo ngakhale iwo apereka chuma chopepesera, sichidzalandiridwa konse. Otere ndiwo amene aonongedwa chifukwa cha zimene anachita. Iwo adzalandira zakumwa zowira ndi chilango chowawa chifukwa cha zinthu zimene sadakhulupirire
Verse 71
Nena, “Kodi ife tizipembedza ena powonjezera pa Mulungu amene sangathe kutithandiza kapena kutiwononga ndipo kodi ife tibwerere m’mbuyo pamene Mulungu watitsogolera? Monga ngati munthu amene alodzedwa ndi Satana, kumangoyenda uku ndi uku ngakhale kuti abwenzi ake ali kumuitana kuti atsatire njira yoyenera, ponena: Bwerani kuno?” Nena, “Ndithudi utsogoleri wa Mulungu ndiwo utsogoleri weniweni ndipo Ife talamulidwa kugonjera Mulungu Ambuye wa zolengedwa zonse.”
Verse 72
Ndi kuti muzipemphera moyenera, kumvera Mulungu ndi kumuopa Iye ndipo ndi kwa Iye kumene nonse mudzasonkhanitsidwa
Verse 73
Iye ndiye amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi mwachoonadi ndipo patsikuli Iye adzati: “Khala” ndipo chidzakhala. Liwu lake ndi loonadi. Wake udzakhala Ufumu pa tsiku limene lipenga lidzaombedwa. Iye amadziwa zonse zosaoneka ndi zooneka. Iye ndi wanzeru ndi wodziwa zinthu zonse
Verse 74
Ndi pamene Abrahamu adati kwa abambo ake a Uzar: “Kodi inu muzipembedza mafano ngati milungu yanu? Ndithudi ine ndili kuona kuti inu pamodzi ndi anthu anu mwasochera moonekera.”
Verse 75
Motero tidamuonetsa Abrahamu Ufumu wa kumwamba ndi wa dziko lapansi kuti akhale mmodzi wa wokhulupirira kweniweni
Verse 76
Ndipo pamene usiku udamukuta ndi mdima, iye adaona nyenyezi. Iye adati: “Iyo ndiyo Ambuye wanga.” Koma pamene iyo idalowa, iye adati: “Ine sindikonda zimene zimalowa.”
Verse 77
Ndipo pamene iye adaona mwezi uli kutuluka, iye adati: “Uwo ndiwo Ambuye wanga.” Koma pamene iwo unalowa, Iye adati: “Ngati Ambuye wanga sanditsogolera ine, ndithudi, ine ndidzakhala m’gulu la anthu osochera.”
Verse 78
Ndipo pamene adaona dzuwa lili kutuluka, iye adati: “Ili ndilo Ambuye wanga. Ndipo ilo ndi lalikulu koposa.” Koma pamene ilo lidalowa, iye adati: “oh inu anthu anga! Ine ndatalikirana ndi zimene inu mukusakaniza popembedza Mulungu.”
Verse 79
Ndithudi ine ndayang’anitsa nkhope yanga kwa Iye amene adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Ine sindine mmodzi wa iwo opembedza mafano
Verse 80
Anthu ake adatsutsana naye ndipo iye adati: “Kodi inu mukutsutsana ndi ine za Mulungu pamene Iye wanditsogolera? Ndipo ine sindiopa mafano anu kupatula ngati Ambuye wanga atafuna chilichonse. Ambuye wanga amadziwa bwino chilichonse. Kodi inu simungakumbukire
Verse 81
Ndipo kodi ine ndingaope bwanji milungu yanu yabodza pamene inuyo mulibe mantha pomapembedza mafano amene Mulungu sadakupatseniumboniwake? Kodindaniwamaguluawiriwa amene afuna chitetezo ngati inu mumadziwa?”
Verse 82
Ndiwo amene ali okhulupirira ndipo sasakaniza chikhulupiriro chawo pochita ntchito zoipa, kwa iwo kuli mtendere ndipo ndi otsogozedwa
Verse 83
Chimenechi chinali chizindikiro chathu chimene tidamupatsa Abrahamu kuti agonjetsere anthu ake. Ife timakweza wina aliyense amene tamufuna. Ndithudi Ambuye wako ndi wanzeru ndi wodziwa zinthu zonse
Verse 84
Ndipo tidamupatsa iye Isake ndi Yakobo, aliyense tidamutsogolera ndipo iye asanadze, tidatsogolera Nowa ndipo pakati pa adzukulu wake Davide, Solomoni, Yobu, Yosefe, Mose ndi Aroni. Motero ndi mmene timalipirira anthu ochita abwino
Verse 85
Ndi Zakariya, Yohane, Yesu, ndi Eliya, aliyense adali wangwiro
Verse 86
Ndi Ishimayeli, Elisa, Yona ndi Loti, onsewa tidawalemekeza pakati pa zolengedwa zonse
Verse 87
Ndiponso makolo awo, ana awo, ndi abale awo Ife tidawasankha ndi kuwatsogolera ku njira yoyenera
Verse 88
Ichi ndi chilangizo cha Mulungu chimene amalangiza nacho aliyense amene wamufuna wa akapolo ake. Koma iwo akadatumikira milungu ina yoonjezera pa Mulungu m’modzi, ntchito zawo zonse zikadakhala zopanda phindu
Verse 89
Awa ndi amene tidawapatsa Buku, chiweruzo ndi Utumwi. Koma ngati awa sakhulupirira mwa ilo, ndithudi Ife tawapatsa iwo amene akhulupilira mwa ilo
Verse 90
Amenewa ndi anthu amene Mulungu adawatsogolera. Choncho tsatira chilangizo chawo. Nena, “Ine sindili kufuna malipiro chifukwa cha ntchito iyi ayi. Ili ndi chenjezo kwa zolengedwa zonse.”
Verse 91
Iwo sadapereke ulemu woyenera Mulungu pamene adati: “Mulungu sadavumbulutse china chilichonse kwa munthu.” Nena, “Kodi ndani yemwe adavumbulutsa Buku limene Mose anabwera nalo, muuni ndi chilangizo kwa anthu onse; amene mwalemba pa mipukutu ya mapepala, kuulula zina ndi kubisa zambiri? Ndipo mudaphunzitsidwa zimene inu ndiponso makolo anu sadazidziwe ndi kale lomwe.” Nena: “Ndi Mulungu.” Ndipo asiye okha kuti abadzisangalatsa ndi nkhani zopusa
Verse 92
Ndipo ili ndi Buku lodalitsika limene tavumbulutsa, kuchitira umboni zimene zinadza ilo lisadadze kuti uchenjeze Mzinda wa Makka ndi iwo amene amakhala mouzungulira. Iwo amene ali ndi chikhulupiriro mu zamoyo umene uli nkudza amakhulupirira ilo ndipo amasamala kwambiri m’mapemphero awo
Verse 93
Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa iye amene amapeka bodza lonamizira Mulungu kapena amati: “Ine ndalandira chibvumbulutso pamene sichidavumbulutsidwe kwa iye chilichonse?” Kapena munthu amene amati: “Ine ndikhoza kuvumbulutsa zinthu zofanana ndi zimene Mulungu wavumbulutsa?” Ndipo iwe ukadangoona anthu ochimwa pamene ali kufa ndi pamene angelo ali kutambasula manja awo akuti: “Perekani mizimu yanu. Inu mudzalipidwa mphotho yochititsa manyazi lero chifukwa cha zimene munali kunena zabodza zokhudza Mulungu. Ndiponso inu munali kukana chivumbulutso chake mwa mwano.”
Verse 94
“Ndipo, ndithudi, mwadza kwa Ife, nokha, monga momwe tidakulengerani inu poyamba. Inu mwasiya zonse zimene tidakupatsani kumbuyo kwanu. Ndiponso Ife sitili kuona pamodzi ndi inu zimene mumazipembedza, zija mumati ndi zofanana ndi Mulungu. Tsopano ubale wonse umene umakugwirizitsani waduka ndipo zonse zimene mumaziganizira kuti zingakuthandizeni zakuthawirani.”
Verse 95
Ndithudi! Ndi Mulungu amene amasiyanitsa mbewu ndi khoko lake kuti imere. Iye amatulutsa chamoyo kuchokera mu chakufa ndipo ndiye amatulutsa chakufa kuchokera ku chamoyo. Ameneyo ndiye Mulungu, nanga ndi chifukwa chiyani mukusokera kusiya choonadi
Verse 96
Iye amadzetsa kuwala kwa m’mawa. Ndipo Iye waika usiku kuti ikhale nthawi yopumula, dzuwa ndi mwezi kuti zikhale zothandiza kuwerengera; umenewo ndiwo muyeso wa Mwini mphamvu zonse ndi wodziwa chilichonse
Verse 97
Iye ndiye amene adakulengerani nyenyezi kuti zizikutsogolerani mu mdima wa pa mtunda ndi pa nyanja. Ife tafotokoza chivumbulutso kwa anthu odziwa kwambiri
Verse 98
Iye ndiye amene adakulengani inu kuchokera kwa munthu mmodzi ndipo adakupatsani malo okhalamo ndi osungidwa. Ife ndithudi tafotokoza chivumbulutso chathu kwa anthu omvetsa
Verse 99
Iye ndiye amene amatumiza mvula kuchokera kumwamba ndipo ndi iyo, Ife timameretsa mbewu zosiyana siyana ndipo kuchokera ku izo timatulutsa mphesi za ziwisi zimene zimabereka mbeu mothinana. Ndipo kuchokera ku mitengo ya tende kumadza zipatso za tende zotsika pansi, minda ya mphesa ndi mitengo ya mafuta ya azitona, chimanga cha chizungu, zipatso zofanana koma zosiyanasiyana. Taonani zipatso zake pamene zili kubereka, kukhwima ndi kumapsya. Ndithudi! Mu izi muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira
Verse 100
Komabe iwo amasankha majini kukhala milungu kuonjezera pa Mulungu weniweni ngakhale kuti Iye ndiye amene anawalenga ndipo amamunamizira Mulungu kuti ali ndi ana amuna ndi akazi. Ulemerero ukhale kwa Iye! Alemekezeke Iye koposa zonse zimene akunena
Verse 101
Iye ndi Namalenga wa kumwamba ndi dziko lapansi. Kodi Iye angakhale ndi ana bwanji pamene Iye alibe mkazi? Iye adalenga zinthu zonse ndipo amadziwa chilichonse
Verse 102
Ameneyo ndiye Mulungu, Ambuye wanu. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha, Namalenga wa zinthu zonse. Motero mpembedzeni Iye yekha. Iye ndiye wosamalira zinthu zonse
Verse 103
Palibe amene angamuone Iye koma Iye amaona chili chonse. Iye ndiye wachifundo ndipo amadziwa zonse
Verse 104
Ndithudi zizindikiro zonse zadza kwa inu kuchokera kwa Ambuye wanu ndipo aliyense amene aona zidzampindulira iye koma aliyense amene ali wakhungu adzalephera yekha ndipo ine sindine wokuyang’anirani
Verse 105
Motero Ife timafotokoza chivumbulutso chathu, kuti iwo anene kuti: “Iwe waphunzira” ndi kuti tifotokoze momveka kwa anthu ozindikira
Verse 106
Choncho tsatira zonse zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Ambuye wako. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha ndipo alewe anthu osakhulupirira
Verse 107
Ngati Mulungu akadafuna, iwo sakanapembedza mafano. Ndipo Ife sitikadakusankha iwe kukhala owayang’anira ayi ndiponso iwe sindiwe wowasamalira wawo
Verse 108
Ndipo musatukwane iwo amene amapembedza mafano poonjezera pa Mulungu weniweni kuti mwina iwo angathe kutukwana Mulungu molakwa ndi mwa umbuli. Motero tazipanga zochita zawo kukhala zosangalatsa ndipo ndi kwa Ambuye wawo kumene onse adzabwerera ndipo Iye adzawauza iwo zonse zimene anali kuchita
Verse 109
Ndipo iwo amalumbira pali Mulungu motsindika kuti ngati chizindikiro chitaperekedwa kwa iwo, iwo adzachikhulupirira. Nena, “Ndithudi zizindikiro zonse zili ndi Mulungu ndipo kodi inu mungadziwe bwanji ngati chidza kwa iwo kuti iwo sadzachikhulupirira?”
Verse 110
Ndipo Ife tidzatembenuza mitima yawo ndi maso awo monga mmene adakana kukhulupirira nthawi yoyamba ndipo Ife tidzawasiya mukusochera kwawo akusowa chochita
Verse 111
Ngakhale Ife tikadawatumizira iwo angelo ndi kupangaanthuakufakutialankhulenawondikusonkhanitsa zinthu zonse pamaso pawo, iwo sakadakhulupirirabe pokhapokha ngati Mulungu afuna koma ambiri a iwo ndi anthu osadziwa
Verse 112
Kotero Ife tidakhazikitsa mdani kwa Mtumwi aliyense. A satana amene ali pakati pa anthu ndi majini, amene amauzana wina ndi mnzake mawu okoma ndiponso a chinyengo. Koma Ambuye wako akadafuna, iwo sakadachita zotero ayi motero asiyeni okha ndi zimene akupeka
Verse 113
Kuti mitima ya anthu amene sakhulupirira m’moyo umene uli nkudza ipendekere kuzolankhula zawo ndipo kuti azitsatira zimene apeka okha ndi kumasangalala kuti mwina akhoza kuchita zimene ali nkuchita
Verse 114
“Kodi ine ndifune wina woweruza oposa Mulungu pamene ndiye amene adavumbulutsa Korani kwa inu ndi malamulo ofotokozedwa bwino?” Iwo amene tidawapatsa Mau athu amadziwa kuti lidavumbulutsidwa kuchokera kwa Ambuye wako mwa choonadi. Motero usakhale mmodzi wa anthu okaika
Verse 115
Ndipo Mau a Ambuye wako akwaniritsidwa moona ndi mwachilungamo. Palibe wina amene angasinthe Mau ake. Iye amamva ndipo ndi wozindikira chili chonse
Verse 116
Ndipo ngati iwe umvera zonena za anthu ambiri apa dziko lapansi iwo adzakusocheza ku njira ya Mulungu. Iwo satsatira chilichonse koma nkhani zongoganiza chabe ndipo sachita china chilichonse koma kunama
Verse 117
Ndithudi Ambuye wako! Ndiye amene amadziwa anthu onse amene amasochera ku njira yake ndiponso Iye amadziwa iwo amene atsogozedwa bwino bwino
Verse 118
Motero idyani nyama yokhayo imene yaphedwa m’dzina la Mulungu ngati inu mukhulupiriradi mu chivumbulutso chake
Verse 119
Kodi inu simungadye bwanji nyama imene yaphedwa m’dzina la Mulungu pamene Iye adaulula poyera zimene adakuletsani pokhapokha ngati mwasimidwa? Ndithudi ambiri amasochera potsatira zilako lako zawo mwa umbuli. Ndithudi Ambuye wako amadziwa onse oswa malamulo
Verse 120
Pewa machimo oonekera kapena obisika. Ndithudi iwo amene amachita zoipa adzalangidwa chifukwa cha zoipa zawo
Verse 121
Musadye nyama iliyonse imene sidaphedwe m’dzina la Mulungu chifukwa kutero ndi kulakwa. Ndithudi a Satana amaphunzitsa anthu awo kuti azikangana ndi inu ndipo ngati inu muwamvera, ndithudi, nanunso mudzakhala opembedza mafano
Verse 122
Kodi munthu amene adafa, ndipo tamuukitsa kwa akufa ndipo wapatsidwa kuwala kumene kukhoza kumutsogolera pakati pa anthu, angafanizidwe ndi iye amene ali kusochera mumdima umene sadzatulukamo? Chomwecho zimakongoletsedwa kwa anthu osakhulupirira zimene adali kuchita
Verse 123
Motero Ife tidakhazikitsa mu Mzinda uliwonse atsogoleri a anthu olakwa kwambiri amene amakonza njira zoswera malamulo m’kati mwa Mzindawo. Koma iwo amakonza njira zoti zibweretse chiwonongeko pa iwo eni ndipo iwo sadziwa
Verse 124
Ndipo pamene zizindikiro ziwafikira iwo amati: “Ife sitidzakhulupirira mu ichi pokhapokha ngati tipatsidwa chimene Atumwi a Mulungu adapatsidwa.” Mulungu amadziwa bwino ndani amene akhoza kumupatsa uthenga wake. Kunyozedwa ndi kuchititsidwa manyazi kochokera kwa Mulungu ndiponso chilango chowawa chidzadza pa anthu oipa chifukwa cha zimene anali kuchita
Verse 125
Ndipo aliyense amene Mulungu afuna kumutsogolera, Iye amatsegula mtima wake kuti akhale Msilamu ndipo aliyense amene Iye afuna kumusocheretsa, Iye amachititsa mtima wake kukhala opapatizika ndi ovutika ngati kuti akukwera kumwamba. Mmenemo ndi mmene Mulungu amaikira mkwiyo pa anthu osakhulupirira
Verse 126
Iyi ndi njira ya Ambuye wako, yoyenera. Ife tafotokoza chivumbulutso kwa anthu oganizira
Verse 127
Kwa iwo kudzakhala nyumba ya mtendere imene ili ndi Ambuye wawo. Iye adzakhala Mtetezi wawo chifukwa cha zimene anali kuchita
Verse 128
Ndipo patsiku limene adzawasonkhanitsa onse, ndi kuti: “oh inu gulu la majini! Inu mudali kusokeletsa anthu mu unyinji wawo.” Ndipo anzawo ochokera m’gulu la anthu adzati: “Ambuye ife tidapindula kuchokera kwa wina ndi mnzake, koma tsopano tafika pa mapeto ya nthawi yathu imene mudatikhazikitsira ife.” Mulungu adzati: “Kumoto ndiko kumalo kwanu ndipo kumeneko mukakhala mpaka kalekale kufikira pamene Mulungu adzafuna.” Ndithudi Ambuye wako ndi Wanzeru ndi Wozindikira
Verse 129
Ndipo motero ndi mmene timapangira anthu olakwa kuthandizana wina ndi mzake chifukwa cha zimene anali kuchita
Verse 130
Inu gulu la majini ndi anthu! “Kodi sikudadze kwa inu Atumwi a mtundu wanu amene adali kukuuzani za zizindikiro zanga ndi kuchenjeza za kukumana kwa tsiku lanuli?” Iwo adzayankha, “Ife tidzichitira umboni wodzitsutsa tokha.” Ndi moyo wa dziko lino lapansi umene udawanyenga. Ndipo iwo adzadzichitira umboni okha kuti iwo adali osakhulupirira
Verse 131
Ichi ndi chifukwa chakuti Ambuye wako samaononga Mizinda chifukwa cha zochita zawo, pamene anthu ake sadali kudziwa
Verse 132
Kwa aliyense kudzaperekedwa gawo molingana ndi zimene adachita. Sikuti Ambuye wako sadziwa zimene iwo achita
Verse 133
Ambuye wako ndi wolemera ndiponso ndi wachisoni ndipo ngati Iye afuna, akhoza kukuonongani ndi kuika m’malo mwanu ena amene Iye wafuna monga momwe Iye adakulengerani inu kuchokera ku mbeu ya anthu ena
Verse 134
Ndithudi chimene inu mukulonjezedwa chidzachitika ndipo inu simungachizembe ayi
Verse 135
Nena, “oh anthu anga! Chitani chimene mungachite, ndithudi, nanenso ndili kuchita chimene ndimachita ndipo inu mudzadziwa kuti ndani wa ife amene adzakhala ndi mapeto abwino m’moyo umene uli nkudza. Ndithudi anthu olakwa sadzapambana.”
Verse 136
Ndipo iwo amaika pa mbali gawo la mbewu ndi gawo la ziweto kuti ndi za Mulungu ndipo amati: “Izi ndi za Mulungu pamene izi ndi za mafano athu.” Koma gawo limene amati ndi la mafano awo silifika kwa Mulungu ayi pamene gawo la Mulungu limafika lonse kwa mafano awo! Chiweruzo chawo ndi choipa kwambiri
Verse 137
Motero kwa anthu opembedza mafano, mafano awo adapangitsa kupha ana awo kukhala chinthu chokondweretsa ndi cholinga chakuti awawononge iwo ndi kuwasokonezera chipembedzo chawo. Koma ngati Mulungu akadafuna, iwo sakadachita choncho. Motero asiyeni okha ndi zimene akupeka
Verse 138
Potsatira zofuna zawo, iwo amati: “Nyama izi ndiponso mbewu izi ndi zoletsedwa ndipo palibe munthu amene adye kupatula okhawo amene tawaloleza.” Ndipo pali nyama zina zimene amaletsa anthu kuti asakwere kapena kugwira ntchito, ndi zina zimene satchulapo dzina la Mulungu komwe ndi kumunamizira Iye. Mulungu adzawalipira chifukwa cha mabodza awo amene amapeka
Verse 139
Ndipo iwo amati: “Zam’kati zanyamazi ndi zololedwa kudyedwa ndi anthu athu amuna okha ndipo ndi zoletsedwa kwa anthu a akazi koma ngati izo zibadwa zakufa onse amagawana. Mulungu adzawalanga chifukwa cha zonse zimene amamunamizira Iye. Ndithudi Iye ndi Wanzeru ndi Wodziwa.”
Verse 140
Ndithudi olephera ndi amene, adapha ana awo mwaumbuli ndipo adaletsa zinthu zimene Mulungu adawapatsa iwo ndi kupeka bodza lokhudza Mulungu. Ndithudi iwo asokera ndipo siotsogozedwa
Verse 141
Iye ndiye amene amapanga minda ya mbewu za mitundumitundu; zoyanga ndi zosayanga, mitengo ya tende ndi mbeu zosiyanasiyana kukoma kwake, azitona ndi chimanga cha chizungu zofanana ndi zosiyana. Idyani zipatso zake pamene zibereka ndipo perekani chaulere chake nthawi yake. Koma musawononge ayi. Ndithudi Mulungu sakonda anthu owononga
Verse 142
Ndipo pakati pa nyama, pali zina zonyamula katundu ndi zina zosanyamula katundu. Idyani zimene Mulungu wakupatsani ndipo musatsatire mapazi a Satana ayi. Ndithudi iye ndi mdani wooneka
Verse 143
Tengani ng’ombe zisanu ndi zitatu, ndi nkhosa ziwiri, ndi mbuzi ziwiri. Nena, “Kodi Iye adaletsa zazimuna ziwiri kapena zazikazi ziwiri kapena ana amene ali m’mimba? Ndiyankheni mozindikira ngati mukunena zoona.”
Verse 144
Ndipo kuchokera ku ngamira, ziwiri ndi ng’ombe ziwiri. Nena, “Kodi Iye adaletsa zazimuna ziwiri kapena zazikazi ziwiri kapena ana amene ali m’mimba mwawo? Kodi mudalipo pamene Mulungu adakupatsani malamulo awa? Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene amapeka bodza lokhudza Mulungu ndi kusocheretsa anthu popanda kuzindikira? Ndithudi Mulungu satsogolera anthu ochita zoipa.”
Verse 145
Nena, “Ine sindipeza china chilichonse mu zimene zavumbulutsidwa kwa ine choletsa aliyense kudya chakudya china chilichonse kupatula nyama yofa yokha kapena liwende kapena nyama ya nkhumba, chifukwa zimenezo ndi zauve ndi zodetsedwa kapena nyama ina iliyonse imene yaphedwa osati mu dzina la Mulungu. Koma aliyense amene waumirizidwa kudya chilichonse cha izi, osati mokondweretsedwa kapena ndi cholinga chofuna kuswa malamulo, ndithudi, Ambuye wako ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha.”
Verse 146
Ife tidawaletsa Ayuda kudya nyama zonse zosabsyukula ndipo tinawaletsa mafuta a ng’ombe ndi a nkhosa kupatula amene ali pa msana ndi m’matumbo kapena amene adasakanizika ndi mafupa. Motero tidawapatsa chilango chifukwa cha kulakwa kwawo. Ndithudi Ife tili kunena zoonadi
Verse 147
Ngati iwo akukunamizani, nena, “Ambuye wanu ndi Mwini chifundo chosatha koma mkwiyo wake siungachotsedwe pa anthu ochita zoipa.”
Verse 148
Anthu opembedza mafano adzati: “Mulungu akadafuna, ife kapena makolo athu, sitikadatumikira milungu ina yoonjezera pa Iye ndipo ife sitikadaletsa china chilichonse.” Mmenemu ndi mmene anthu amene adalipo kale adanamira mpaka pamene analawa mkwiyo wathu. Nena, “Kodi inu muli ndi umboni uliwonse umene mungatisonyeze Ife?” Ndithudi inu simutsatira china koma zinthu zongoganiza ndiponso simuchita china chilichonse koma bodza basi
Verse 149
Nena, “Ndi Mulungu yekha amene ali ndi umboni weniweni ndipo Iye akadafuna akadakutsogolerani nonse.”
Verse 150
Nena, “Bweretsani mboni zanu zonse zimene zikhoza kuchitira umboni kuti Mulungu adakuletsani izi. Ngati iwo apereka umboni, iwe usapereke umboni wako. Ndipo usatsatire zilakolako za iwo amene amati chivumbulutso chathu ndi chabodza, amene sakhulupirira za m’moyo umene uli nkudza ndipo amapanga milungu ina kukhala yofanana ndi Ambuye wawo.”
Verse 151
Nena, “Bwerani! Ine ndikuwerengerani zimene Ambuye wanu wakulamulani inu kuti musachite. Musapembedze milungu ina yowonjezera pa Iye; Muzionetsa chifundo kwa makolo anu; musaphe ana anu chifukwa chaumphawi, Ife timakudyetsani inu pamodzi ndi iwo; musayandikire zinthu zoipa zimene zili zoonekera kapena zili zobisika ndipo musaphe munthu amene Mulungu waletsa pokhapokha ngati pali chifukwa choyenera.” Ichi wakulamulani inu kuti muzindikire
Verse 152
“Ndipo musayandikire chuma cha ana a masiye kupatula m’njira yabwino yowakonzera tsogolo lawo mpaka pamene iwo akula msinkhu. Kwaniritsani muyeso woyenera ndipo muyese mwachilungamo. Ife sitinyamulitsa munthu wina aliyense katundu wolemera amene iye sangathe kunyamula. Ndipo mukamalankhula, muzilankhula mwachilungamo ngakhale kuti nkhanizo zikhudza abale anu ndipo kwaniritsani malonjezo a Mulungu. Ichi wakulamurani inu kuti mudzikumbukira.”
Verse 153
Ndithu iyi ndi njira yanga yoyenera motero itsatireni ndipo musatsatire njira zina zake chifukwa izo zidzakusocheretsani inu ku njira yake. Ichi Iye wakulamulani kuti mukhale angwiro
Verse 154
Ndipo Ife tidamupatsa Mose Buku, kumaliza ubwino wathu kwa aliyense wochita zabwino ndiponso lofotokoza chinthu chilichonse, ulangizi ndi chisomo kuti akhulupirire mukukumana kwawo ndi Ambuye wawo
Verse 155
Ili ndi Buku lodalitsika limene talivumbulutsa, motero opani Mulungu kuti mulandire chisomo
Verse 156
Kuti inu musadzanene kuti: “Buku lidangovumbulutsidwa ku magulu awiri pambuyo pathu, ndipo ife sitidadziwe zimene adali kuwerenga.”
Verse 157
Kapena mukhoza kudzanena kuti: “Buku la Mulungu likanavumbulutsidwa kwa ife, ndithudi, tikadalangizidwa bwino kuposa iwo.” Ndithudi chizindikiro chosakaikitsa chadza tsopano kuchokera kwa a Ambuye wanu; chilangizo ndi madalitso. Kodi wolakwa kwambiri ndani kuposa munthu amene akana chivumbulutso cha Mulungu ndipo safuna kuchitsatira? Ife tidzawalipira onse amene amakana zizindikiro zathu ndi chilango chowawa chifukwa chokana kwawo
Verse 158
Kodi iwo ali kudikira wina kupatula angelo kuti adze kwa iwo kapena kuti Ambuye wako adze kapena zina mwa zizindikiro za Ambuye wako zidze? Tsiku limene zina mwa zizindikiro za Ambuye wako zidzadza, chikhulupiriro sichidzathandiza mzimu umene unalibe chikhulupiriro kale kapena umene siudagwiritse ntchito bwino chikhulupiriro. Nena, “Dikirani! Nafenso tili kudikira.”
Verse 159
Ndithudi iwo amene apatukana m’chipembedzo ndi kupanga mipingo yosiyanasiyana, iwe sizikukhudza zimenezo. Nkhani yawo adzathetsa ndi Mulungu ndipo Iye adzawauza zomwe amachita
Verse 160
Aliyense amene amachita ntchito yabwino adzalipidwa magawo khumi olingana ndi iyo ndipo aliyense amene amachita zoipa adzalandira choipa chomwecho ndipo iwo sadzaponderezedwa ayi
Verse 161
Nena, “Ndithudi Ambuye wanga wanditsogolera ine ku njira yoyenera, ku chipembedzo changwiro, chikhulupiriro cha Abrahamu wangwiro chifukwa Abrahamu sadali mmodzi wa anthu opembedza mafano.”
Verse 162
Nena, “Ndithudi mapemphero anga, nsembe yanga, moyo wanga ndi imfa yanga zonse zili m’manja mwa Mulungu Ambuye wazolengedwa zonse.”
Verse 163
Iye alibe wothandizana naye. Pa izi ine ndalamulidwa ndipo ine ndine woyamba wa iwo ogonjera malamulo a Mulungu
Verse 164
Nena, “Kodi ine ndifune Ambuye wina osati Mulungu pamene Iye ndi Ambuye wa zinthu zonse? Munthu aliyense adzakolola zipatso za ntchito yake ndipo palibe mzimu umene udzanyamula katundu wa wina wake. Pomaliza nonse mudzabwerera kwa Ambuye wanu; ndipo Iye adzakuuzani zomwe munali kutsutsana.”
Verse 165
Ndipo ndiye amene anakulengani kukhala mibadwo yodza pambuyo pa mibadwo yina, kulowa m’malo mwa uzake padziko lapansi. Ndipo anakukwezani m’maudindo, ena kuposa anzawo kuti akhoza kukuyesani ndi zimene wakupatsani. Ndithudi Ambuye wanu ndi wachangu polanga koma ndithudi Iye amakhululuka, Mwini chisoni chosatha