Back to Languages

    Chichewa - Chapter 81

    Translation by Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

    Verse 1

    Pamene dzuwa lidzavundikiridwa

    Verse 2

    Ndi pamene nyenyezi zidzagwa pansi

    Verse 3

    Ndi pamene mapiri adzachotsedwa

    Verse 4

    Ndi pamene ngamila zabele zizakhala zosasamalidwa

    Verse 5

    Ndi nyama za m’tchire zidzasonkhanitsidwa pamodzi

    Verse 6

    Ndi pamene nyanja zidzayatsidwa moto kapena zidzasefukira

    Verse 7

    Ndi pamene mizimu idzakumanitsidwa ndi matupi awo

    Verse 8

    Ndi pamene mwana wa mkazi wa mng’ono, amene adaundilidwa wa moyo adzafunsidwa

    Verse 9

    Chifukwa chimene anamuphera

    Verse 10

    Ndi pamene mabuku olembamo ntchito za munthu aliyense adzatulutsidwa

    Verse 11

    Ndi pamene kumwamba kudzafafanizidwa ndi kuchotsedwa ku malo ake

    Verse 12

    Ndi pamene Gahena idzatenthetsedwa kwambiri

    Verse 13

    Ndi pamene Paradiso idzafikitsidwa pafupi

    Verse 14

    Ndithudi munthu aliyense adzadziwa chimene adachita

    Verse 15

    Motero, ndithudi, Ine ndili kulumbira pali nyenyezi zimene zimalowa

    Verse 16

    Ndi pali maiko zimene zimayenda mofulumira ndi kudzibisa okha

    Verse 17

    Ndi pali usiku pamene uchoka

    Verse 18

    Ndipalim’mawapamenekulikucha

    Verse 19

    Ndithudi awa ndi Mau a Mtumwi wolemekezeka

    Verse 20

    Mwini mphamvu amene amalemekezedwa ndi Ambuye, Mwini Mpando wa Chifumu

    Verse 21

    Amamveredwa ndi wokhulupirika

    Verse 22

    Ndipo m’bale wanu uyu si wa misala ayi

    Verse 23

    Ndipo, ndithudi, iye adamuona iye mu mlengalenga

    Verse 24

    Iye sabisa zinthu zosaoneka

    Verse 25

    Ndipo zimene alankhula sizochokera kwa Satana wotembereredwa

    Verse 26

    Kodi inu muli kupita kuti

    Verse 27

    Ndithudi ichi si china chilichonse ayi koma chikumbutso kwa anthu a mitundu yonse

    Verse 28

    Kwa aliyense wa inu amene afuna kuyenda moongoka

    Verse 29

    Koma inu simungathe kutero pokhapokha ndi chifuniro cha Mulungu, Ambuye wa zolengedwe zonse