Back to Languages
Chichewa - Chapter 87
Translation by Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula
Verse 1
Lemekeza dzina la Ambuye wako wapamwambamwamba
Verse 2
Amene adalenga zonse ndi kuzikonza bwinobwino
Verse 3
Amene adalamula tsogolo lawo ndi kuwatsogolera
Verse 4
Amene amameretsa msipu
Verse 5
Ndipo amausanduliza kukhala udzu ouma
Verse 6
Tidzakuphunzitsa kulakatula chivumbulutso chathu ndipo sudzaiwala
Verse 7
Kupatula chokhacho chimene Mulungu amafuna. Ndithudi Iye amadziwa chilichonse chooneka ndi chobisika
Verse 8
Ndipo Ife tidzakufupikitsira, m’njira yaifupi
Verse 9
Motero kumbutsa mwina chikumbutso chingawathandize
Verse 10
Chikumbutso chidzalandiridwa ndi iye amene amaopa Mulungu
Verse 11
Koma munthu wochimwa adzachisiya
Verse 12
Amene adzaponyedwa mu ng’anjo yamoto ndi kulawa ululu wake
Verse 13
Mmene iye sadzafa kapena kukhala ndi moyo
Verse 14
Zoonadi iye amene adziyeretsa adzakhala wopambana
Verse 15
Amene amakumbukira dzina la Ambuye wake ndipo amapemphera panthawi yake
Verse 16
Iyayi, koma inu mumasangalala ndi zinthu za m’moyo uno
Verse 17
Ndipo moyo umene uli nkudza ndi wabwino ndi wosatha
Verse 18
Ndithudi! Zonsezi zidalembedwa mu Mabuku akale a Mulungu
Verse 19
Mabuku a Abrahamu ndi Mose