Back to Languages

    Chichewa - Chapter 9

    Translation by Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula

    Verse 1

    Chidziwitso ichi chikhazikitsa malire oikidwa ndi Mulungu ndi Mtumwi wake, kwa anthu opembedza mafano amene mwapanga nawo lonjezo

    Verse 2

    Kotero yendani mwa ufulu miyezi inayi m’dziko lonse. Koma muyenera kudziwa kuti inu simungathawe Mulungu ndipo Mulungu adzachititsa manyazi anthu osakhulupirira

    Verse 3

    Chidziwitso chochokera kwa Mulungu ndi Mtumwi wake kunka kwa anthu onse pa tsiku la likulu kuti Mulungu ndi Mtumwi wake alibe udindo pa anthu opembedza mafano. Motero ngati inu mulapa zidzakhala zabwino kwa inu, koma ngati mukana, dziwani kuti inu simungamuthawe Mulungu ndipo auze anthu osakhulupirira za chilango chowawa

    Verse 4

    Kupatula opembedza mafano amene mwapangana nawo chipangano, ndipo sadakukhumudwitseni pa chilichonse ndipo sadamthandize aliyense kulimbana ndi inu. Kotero kwaniritsani chipangano chawo kufikira kunthawi yawo. Ndithudi Mulungu amakonda amene amaopa

    Verse 5

    Ndipo pamene masiku a miyezi yolemekezeka atha, iphani anthu opembedza mafano paliponse pamene muwapeza ndipo agwireni, azungulireni ndipo abisalireni m’njira iliyonse. Koma ngati iwo alapa ndipo achita mapemphero ndi kupereka msonkho wothandizira anthu osauka, muwasiye. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndipo ndi wachisoni chosatha

    Verse 6

    Ndipo ngati munthu opembedza mafano afuna chitetezo chako, muteteze kuti akhoza kumva Mau a Mulungu; ndipo mukatero muperekezeni kumalo a mtendere chifukwa iwo ndi anthu osadziwa chilichonse

    Verse 7

    Kodi pangakhale bwanji mgwirizano pakati pa Mulungu ndi Mtumwi wake ndi anthu opembedza mafano kupatula okhawo amene mudachita nawo lonjezo pafupi ndi Mzikiti Wolemekezeka? Ngati iwo asunga malonjezo awo kwa inu nanunso musunge malonjezo anu kwa iwo. Ndithudi Mulungu amakonda amene amaopa

    Verse 8

    Kodi pangakhale bwanji mgwirizano pamene iwo akapambana, salemekeza ubale kapena mgwirizano umene uli pakati panu? Ndi pakamwa pawo amakukondweretsani inu koma mitima yawo imakana ndipo ambiri a iwo ndi ochita zoipa

    Verse 9

    Iwo agula ndi chivumbulutso cha Mulungu zinthu za mtengo wochepa ndipo amaletsa anthu kunjira yake. Zoipa ndizo zimene iwo amachita

    Verse 10

    Akakhala okhulupilira, iwo salemekeza mgwirizano wa ubale kapena wa chipangano! Iwo ndiwo amene amaphwanya malamulo

    Verse 11

    Koma ngati iwo alapa, apitiliza mapemphero ndipo apereka msonkho wothandizira anthu osauka, iwo ndiye kuti ndi abale anu m’chipembedzo. Ife timalongosola chivumbulutso mwatsatane tsatane kwa anthu ozindikira

    Verse 12

    Koma ngati iwo aphwanya kulumbira kwawo pambuyo pa pangano lawo ndipo atukwana chipembedzo chanu, menyani atsogoleri osakhulupirira chifukwa, ndithudi, zolumbira zawo zilibe tanthauzo, kuti mwina asiye kuchita zoipa

    Verse 13

    Kodi inu simudzamenyana nawo anthu amene adaphwanya malonjezano awo ndi kutsimikiza zomuthamangitsa Mtumwi pamene iwo ndiwo amene adakuyambani? Kodi mukuwaopa iwo? Ndithudi Mulungu ndiye amene muyenera kumuopa ngati inu ndinu anthu okhulupirira

    Verse 14

    Amenyeni kuti Mulungu awalange iwo ndi manja anu ndi kuwachititsa manyazi, ndi kukupatsani inu kupambana ndi kuchiza mitima ya anthu okhulupirira

    Verse 15

    Ndi kuchotsa mkwiyo m’mitima mwawo. Mulungu amakhululukira aliyense amene Iye wamufuna. Mulungu ndi wodziwa ndipo ndi wanzeru

    Verse 16

    Kodi inu mukuganiza kuti mudzasiyidwa nokhanokha pamene Mulungu sadawayese iwo amene ali pakati panu, amene adamenya nawo nkhondo mwachamuna ndipo sadachite ubwenzi ndi wina kupatula Mulungu ndi Mtumwi wake ndi anthu okhulupirira? Mulungu amadziwa zimene mumachita

    Verse 17

    Sikoyenera kuti anthu opembedza mafano azisamala Mizikiti ya Mulungu pamene iwo avomereza okha kuti ndi anthu osakhulupirira. Ntchito zawo zidzakhala zopanda pake ndipo ku moto wa ku Gahena ndiko kumene iwo adzakhale

    Verse 18

    Mizikiti ya Mulungu idzasamalidwa ndi okhawo amene akhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza ndipo amapitiriza mapemphero ndipo amapereka msonkho wothandizira anthu osauka ndipo saopa wina aliyense koma Mulungu yekha. Ndi amenewa amene amaganiziridwa kuti amatsata njira yoyenera

    Verse 19

    Kodi mumaganiza kuti kupereka madzi kwa anthu a Hajji ndi kuyang’anira Mzikiti Wolemekezeka kukhala chimodzimodzi ndi iwo amene akhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza ndipo amalimbikira m’njira ya Mulungu? Iwo si ofanana pamaso pa Mulungu. Ndipo Mulungu satsogolera anthu ochita zoipa

    Verse 20

    Iwo amene adakhulupirira, nasamuka, ndipo analimbikira m’njira ya Mulungu ndi chuma chawo pamodzi ndi iwo eni, iwo ali ndi udindo waukulu pamaso pa Mulungu. Iwo ndiwo opambana

    Verse 21

    Ambuye wawo ali kuwauza nkhani yabwino ya chisomo kuchokera kwa Iye ndipo kuti Iye ndi wokondwa ndi ya minda imene ili ndi chisangalalo chosatha

    Verse 22

    Iwo adzakhala mmenemo mpaka kalekale. Ndithudi kwa Mulungu kuli mphotho yaikulu

    Verse 23

    oh inu anthu okhulupirira! Musasandutse atate ndi abale anu kukhala atetezi anu ngati iwo akonda kusakhulupirira kuposa chikhulupiriro. Ndipo aliyense wa inu amene achita ubwenzi ndi anthu otere ndi olakwa

    Verse 24

    Nena, “Ngati atate anu, ana anu, abale anu, akazi anu, a pabanja lanu, chuma chimene mwapeza, katundu wa malonda amene muopa kuonongeka, ndi nyumba zimene mukonda ndi zopambana kwambiri kwa inu kuposa Mulungu ndi Mtumwi wake ndi kulimbikira mu njira yake, ndiye dikirani mpaka pamene Mulungu abweretsa chilamulo chake. Mulungu satsogolera anthu ochita zoipa.”

    Verse 25

    Ndithudi Mulungu wakhala ali kukupambanitsani m’malo ankhondo osiyanasiyana ndi nkhondo ya tsiku la Hunain, pamene inu mudasangalala ndi kuchuluka kwanu koma sikudakuthandizeni chilichonse ndipo dziko linakupanikizani, ngakhale kuti lidali lalikulu, linaoneka laling’ono kwa inu ndipo munatembenuka kuthawa

    Verse 26

    Ndipo Mulungu adatsitsa chisomo chake pa Mtumwi wakendikwaokhulupirirandipoadatumizaAsirikaliamene inu simudawaone ndipo analanga anthu osakhulupirira. Amenewa ndiwo malipiro a anthu osakhulupirira

    Verse 27

    Ndipo pambuyo pake Mulungu adzavomera kulapa kwa aliyense amene Iye wamufuna. Ndipo Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha

    Verse 28

    oh inu anthu okhulupirira! Ndithudi anthu opembedza mafano ndi uve. Motero asayandikire pafupi ndi Mzikiti Wolemekezeka chikatha chaka chino ndipo ngati inu muopa umphawi, Mulungu, ngati afuna, adzakulemeretsani inu kuchokera ku chuma chake. Ndithudi Mulungu amadziwa chilichonse ndipo ndi Wanzeru

    Verse 29

    Menyanani nawo anthu amene sakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza kapena iwo amene saletsa zimene Mulungu ndi Mtumwi wake adaletsa kapena savomeleza chipembedzo choonadi amene ali pakati pa anthu amene adapatsidwa Buku, mpaka pamene iwo alipira msonkho umene amapereka anthu amene sali Asilamu ndipo adzichepetsa

    Verse 30

    Ndipo Ayuda amati: “Ezra ndiye mwana wa Mulungu” pamene Akhirisitu amati “Mesiya ndiye mwana wa Mulungu.” Izi ndi nkhambakamwa. Iwo amangotsatira zimene anthu opembedza mafano akale amanena. Matemberero a Mulungu akhale pa iwo. Kodi iwo akusocheretsedwa bwanji kunjira yoyenera

    Verse 31

    Iwo anasandutsa Abusa ndi atsogoleri awo a mpingo kukhala Ambuye mowonjezera pa Mulungu ndi Messiya, mwana wa Maria, ngati Mulungu pamene iwo adalamulidwa kuti asapembedze wina aliyense koma Mulungu mmodzi yekha basi. Kulibe mulungu wina koma Iye yekha. Kuyamikidwa ndi kulemekezedwa kukhale kwa Iye kuposa zonse zimene adazikhazikitsa mowonjezera pa Iye

    Verse 32

    Iwo amafuna kuzimitsa Muuni wa Mulungu ndi pakamwa pawo koma Mulungu sadzalora kupatula kuti Muuni wake ukhazikike ngakhale kuti anthu osakhulupirira amadana nawo

    Verse 33

    Iye ndiye amene adatumiza Mtumwi wake ndi chilangizo ndi chipembedzo choonadi kuti chipambane zipembedzo zina zonse ngakhale kuti anthu opembedza mafano amadana nazo

    Verse 34

    oh inu anthu okhulupirira! Ndithudi ambiri a Atsogoleri a Chiyuda ndi Abusa a Chikhristu amadya chumacha anthumunjirayosalungamandipoamatsekereza kunjira ya Mulungu. Ndi iwo amene amasonkhanitsa golide ndi siliva ndipo sapereka chumacho mu njira ya Mulungu, auzeni za chilango chowawa

    Verse 35

    Pa tsiku limene chuma chawo chidzasungunulidwa ndi moto wa ku Gahena, ndipo ndi icho mphumi zawo, nthiti zawo, ndi misana yawo idzalembedwa ,“Izi ndi zomwe munali kuzisonkhanitsa nokha. Tsopano lawani zomwe mudali kusonkhanitsa.”

    Verse 36

    Ndithudi chiwerengero cha miyezi kwa Mulungu ndi khumi ndi iwiri ndipo inakhazikitsidwa ndi Mulungu, pa tsiku limene Iye adalenga kumwamba ndi dziko lapansi. Pa iyi, miyezi inayi ndi yopatulika. Ichi ndi chipembedzo choonadi, motero musadzipondereze nokha m’miyezi imeneyi, ndipo menyanani nawo anthu osakhulupirira monga momwe amenyana nanu. Koma dziwani kuti Mulungu ali pamodzi ndi anthu olungama

    Verse 37

    Kusintha, ndithudi, ndi kuonjezera kusakhulupirira, motero anthu osakhulupirira amasokera chifukwa iwo amaikhazikitsa chaka chino ndi kusintha m’chaka china kuti akonze miyezi imene Mulungu waletsa ndi kusandutsa imene inaletsedwa kukhala yololedwa. Ntchito zawo zoipa zimawasangalatsa. Ndipo Mulungu satsogolera anthu osakhulupirira

    Verse 38

    Oh inu anthu okhulupirira! Kodi mwatani? Kodi ndi chifukwa chiani zimati zikanenedwa kwa inu kuti muyende m’njira ya Mulungu, inu mumakondweretsedwa ndi zadziko? Kodi inu mukonda moyo wa dziko lapansi kuposa moyo umene uli nkudza? Chisangalalo chadziko lapansi ndi chochepa kufanizira ndi moyo umene uli nkudza

    Verse 39

    Ngati inu simupita nawo ku nkhondo, Iye adzakulangani ndi chilango chowawa ndipo adzaika m’malo mwanu anthu ena ndipoinusimungathekumupweteka Iyechifukwa Mulungu ali ndi mphamvu pa chinthu china chilichonse

    Verse 40

    Ngati inu simudzathandiza Mtumwi, Mulungu adamuthandiza iye pamene anthu osakhulupirira adamupilikitsa, mmodzi mwa awiri, pamene iwo adali kuphanga ndipo iye ananena kwa mnzake kuti: Usade nkhawa, ndithudi Mulungu ali nafe. Ndipo Mulungu adatsitsa chisomo chake pa iye ndipo adamulimbikitsa ndi Asirikali omwe sadawaone ndipo Iye adapanga mawu a anthu osakhulupirira kukhala a pansi, ndi a Mulungu kukhala a pamwamba. Ndithudi Mulungu ndi Wamphamvu ndi Wanzeru

    Verse 41

    Pitani kunkhondo kaya muli opepukidwa kapena olemedwa. Limbikirani kwambiri ndi chuma chanu pamodzi ndi inu nomwe m’njira ya Mulungu. Ichi ndi chinthu chabwino kwa inu ngati mukadadziwa

    Verse 42

    Kukadakhala kuti zinali zinthu zopezako mosavuta kapena ulendo waufupi, iwo akadakutsatira iwe koma ulendo unali wautali kwa iwo ndiponso wovuta ndipo iwo akanalumbira m’dzina la Mulungu kuti: “Ife tikadatha, ndithudi, tikadapita nanu. Iwo akudziononga okha ndipo Mulungu amadziwa kuti iwo ndi abodza.”

    Verse 43

    Mulungu akukhululukire iwe: Kodi ndi chifukwa chiyani unawapatsa chilolezo mpaka pamene iwo onena zoona anaoneka kwa iwe poyera ndi kuwadziwa onama

    Verse 44

    Iwo amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku la chimaliziro sadzapempha kuti asamenyane nawo nkhondo ndi chuma chawo ndiponso iwo eni. Ndipo Mulungu amadziwa anthu olungama

    Verse 45

    Ndi okhawo amene sakhulupilira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza, iwo amene m’mitima mwawo muli chikaiko, amene amapempha chilolezo. Motero chifukwa cha chikaiko, iwo ndi wosakhazikika

    Verse 46

    Iwo akadafuna kuti apite kunkhondo, ndithudi, akadaikonzekera koma Mulungu sadafune kuti apite nawo ndipo adawakhalitsa, ndipo zidanenedwa kwa iwo, “Khalani pamodzi ndi anthu otsalira.”

    Verse 47

    Ngati iwo akadapita nawe kunkhondo, iwo sakadaonjezera china chilichonse koma chisokonezo, ndipo iwo akadayenda uku ndi uku pakati panu kufalitsa zoipa ndipo ena mwa inu akanawamvera. Ndipo Mulungu amawadziwa anthu ochita zoipa

    Verse 48

    Ndithudi iwo adakonza chiwembu chokuukira ndipo anasokoneza chili chonse mpaka pamene chilungamo chinadza ndipo ulamuliro wa Mulungu unakhazikika angakhale iwo anali kudana nawo

    Verse 49

    Ndipo pakati pawo pali iye amene amati: “Ndipatseni chilolezo ndipo musandiike m’mayesero.” Ndithudi iwo adagwa kale m’mayesero. Ndipo ndithudi, moto wa ku Gahena uli kukuta anthu osakhulupirira

    Verse 50

    Ngati upeza chabwino, iwo chimawanyansa koma ngati mavuto adza pa iwe, iwo amati: “Ife tidadziteteza kale.” Ndipo iwo amabwerera m’mbuyo mosangalala

    Verse 51

    Nena, “Palibe chimene chingationekere ife kupatula chokhacho chimene Mulungu analamula kuti chidze pa ife. Iye ndiye Ambuye wathu.” Ndipo mwa Mulungu, anthu onse okhulupirira ayike chikhulupiliro chawo

    Verse 52

    Nena, “Kodi muli kudikira kuti chimodzi mu zinthu ziwiri zabwino kwambiri kuti chitionekere? Pamene ife tiri kuyembekezera kuti Mulungu adzakubweretserani chilango chochokera kwa Iye kapena kuchokera ku manja athu. Motero dikirani nafenso tiri kudikira pamodzi ndi inu.”

    Verse 53

    Nena, “Perekani mwachifuniro chanu kapena mokakamizidwa, koma palibe chimene chidzalandiridwa kuchokera kwa inu. Ndithudi inu ndinu anthu ochita zoipa.”

    Verse 54

    Palibe chimene chaletsa kuti zopereka zawo zilandiridwe kupatula kuti iwo sanakhulupilire mwa Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo iwo samabwera ku mapemphero kupatula mwaulesi ndipo samapereka zopereka zawo kupatula modandaula

    Verse 55

    Motero usalole kuti chuma chawo kapena ana awo kuti akudabwitse. Cholinga cha Mulungu ndikufuna kuwalanga ndi izi m’moyo uno ndipo kuti mizimu yawo idzachoke pamene iwo ali osakhulupirira

    Verse 56

    Iwo amalumbira M’dzina la Mulungu kuti iwo ali pamodzi ndi inu pamene iwo sali ndi inu ayi, koma iwo ndi anthu a mantha

    Verse 57

    Ngati iwo akadapeza pothawira kapena phanga kapena pobisala, iwo akadathamangira kumeneko mosacheuka

    Verse 58

    Ndipo pakati pawo alipo ena amene amanena zoipa za iwe pa kagawidwe ka katundu. Ngati iwo atapatsidwa gawo la katunduyo, iwo amasangalala, koma ngati sapatsidwa china chilichonse, amakwiya kwambiri

    Verse 59

    Iwo akadangokhutitsidwa ndi zinthu zimene Mulungu ndi Mtumwi wake adawapatsa, ndi kunena kuti: “Mulungu ndi okwanira kwa ife. Mulungu adzatipatsa zabwino zake ndiponso Mtumwi wake. Ife timpempha Mulungu.”

    Verse 60

    Ndithudi chopereka chaulele chiperekedwe kwa anthu osauka, osowa ndi iwo amene amagwira ntchito yosonkhanitsa zoperekazo, ndi iwo amene angolowa chipembedzo cha Chisilamu, kuombola akapolo, anthu amene apanikizidwa ndi ngongole, amene agwira ntchito ya Mulungu ndi munthu wa paulendo; limeneli ndi lamulo la Mulungu. Mulungu ndi wodziwa chilichonse ndi Wanzeru

    Verse 61

    Ndipo pakati pawo alipo ena amene amanyoza Mtumwi ponena kuti: “Iye amangomvera chili chonse.” Nena: “Iye amamvetsera zinthu zimene zili zabwino kwa inu. Iye amakhulupirira mwa Mulungu ndipo Iye amakhulupilira anthu okhulupirira, ndipo iye ndi madalitso kwa ena a inu amene amakhulupilira.” Koma iwo amene amanyoza Mtumwi wa Mulungu adzakhala ndi chilango chowawa

    Verse 62

    Iwo amalumbira M’dzina la Mulungu kwa inu kuti akukondweretseni chabe, koma ndi kwabwino kuti iwo akondweretse Mulungu ndi Mtumwi wake ngati iwo ndi okhulupilira

    Verse 63

    Kodi iwo sadziwa kuti aliyense amene apikisana ndi Mulungu ndi Mtumwi wake, ndithudi, iye adzakhala ku moto wa ku Gahena nthawi zonse? Kumeneko ndiko kunyozedwa kwakukulu

    Verse 64

    Anthu a chinyengo aopa kuti mwina mutu ungavumbulutsidwewonenazaiwo. Nena,“Nyozani!Koma, ndithudi, Mulungu adzaonetsa poyera zonse zimene muli kuopa.”

    Verse 65

    Ngati uwafunsa, iwo amati: “Ife timangocheza ndi kusewera basi.” Nena: “Kodi ndi Mulungu, chivumbulutso chake ndi Mtumwi wake amene munali kunyoza?”

    Verse 66

    Musawilingule ai. Inu mudakana pambuyo pokhulupirira. Ngati Ife tikhululukira gulu lina mwa inu, Ife tidzalanga gulu lina pakati panu chifukwa iwo anali anthu ochita zoipa

    Verse 67

    Anthu achinyengo, amuna ndi akazi, onse ndi chimodzimodzi. Iwo amalamulira zinthu zoipa ndi kuletsa zimene zili zabwino ndiponso iwo amaumila. Iwo amuiwala Mulungu, motero nayenso wawaiwala. Ndithudi anthu a chinyengo ndi anthu wochita zoipa

    Verse 68

    Mulungu walonjeza anthu a chinyengo, amuna ndi akazi ndiponso anthu osakhulupirira moto wa ku Gahena ndipo iwo adzakhala kumeneko mpaka kalekale. Chimenechi ndi chilango chowayeneradi. Mulungu wawatemberera ndipo chawo chidzakhala chilango chosatha

    Verse 69

    Monga iwo amene adalipo inu musanadze, iwo adali ndi mphamvu zambiri zoposa inu ndipo adali ndi chuma chambiri ndi ana ochuluka. Iwo adasangalala ndi zawo pa kanthawi motero nanunso munasangalala ndi zanu pa kanthawi monga momwe iwo anasangalalira. Ndipo inu mwalowa m’masewera ndi kutaya nthawi monga momwe iwo amachita masewera ndi kutaya nthawi. Awa ndiwo amene ntchito zawo zaonongeka m’moyo uno ndi m’moyo umene uli nkudza. Amenewa ndiwo amene ali olephera

    Verse 70

    Kodi iwo sanamve mbiri ya anthu akale? Za anthu a Nowa, a Thamoud, a Abrahamu ndi anthu a ku Midiyani ndi a mizinda yoonongeka? Kwa iwo kunadza Atumwi awo ndi zizindikiro zooneka. Motero Mulungu sadawalakwire ayi koma iwo adadzilakwira okha

    Verse 71

    Anthu okhulupirira, amuna ndi akazi ndi othandizana wina ndi mnzake. Iwo amalamulira zabwino ndi kuletsa zoipa, amapitiriza mapemphero ndipo amapereka msonkho wothandiza anthu osauka ndipo amamvera Mulungu ndi Mtumwi wake. Mulungu adzaonetsa chisoni chake pa iwo. Ndithudi Iye ndi Wamphamvu ndi Wanzeru

    Verse 72

    Mulungu wawalonjeza okhulupirira amuna ndi akazi, minda imene pansipake pamayenda mitsinje yamadzi, kuti adzakhalamo mpaka kalekale ndi Nyumba zokongola za m’munda wa Edeni. Koma chisomo chachikulu ndi chisangalalo cha Mulungu. Kumeneko ndiko kupambana kweni kweni

    Verse 73

    oh Iwe Mtumwi! Limbana kwambiri ndi anthu osakhulupirira ndiponso ndi anthu a chinyengo ndipo uwaonetsere nkhanza. Gahena ndiyo idzakhala mudzi wawo. Ndipo malo oipa kwambiri ndi amenewo

    Verse 74

    Iwo amalumbira pali Mulungu kuti sanena china chilichonse. Koma iwo adalankhula mawu oonetsa kusakhulupirira ndipo iwo sanakhulupirire atalowa Chisilamu. Ndipo iwo anatsimikiza kuchita zimene sadathe kuzichita. Ndipo iwo sanathe kupeza chifukwa choyenera kuti atero kupatula kuti Mulungu ndi Mtumwi wake adawalemeretsa ndi katundu wake. Ngati iwo alapa, zikhala zabwino kwa iwo, koma ngati atembenuka, ndithudi, Mulungu adzawalanga ndi chilango chowawa pa dziko lino ndi mdziko limene lili nkudza. Iwo alibe wina aliyense Wowateteza padziko lapansi

    Verse 75

    Ndipo pakati pawo pali ena amene anachita lonjezo ndi Mulungu ponena kuti: “Ngati Iye atipatsa ife chuma, ndithudi, tidzapereka zopereka ndipo tidzakhala m’gulu la anthu abwino.”

    Verse 76

    Koma pamene Mulungu adawapatsa kuchokera ku chuma chake, iwo anayamba umbombo ndipo adatembenuka mophwanya lonjezo lawo

    Verse 77

    Motero Iye adawalanga pokhazikitsa chinyengo m’mitima mwawo mpaka pa tsiku limene iwo adzakumana Naye, chifukwa chakuphwanya kwawo zimene analonjeza kwa Iye ndi chifukwa chakulankhula kwawo kwabodza

    Verse 78

    Kodi iwo sadziwa kuti Mulungu amadziwa zinsinsi zawo ndi maupo awo a m’nseri ndi kuti Mulungu amadziwa zobisika

    Verse 79

    Iwo amene amaononga mbiri ya anthu okhulupirira amene amapereka mosaumilizidwa ndi iwo amene sanapeza chopereka kupatula chimene ali nacho, motero iwo amanyoza. Mulungu adzawabwezera mtozo wawo. Motero chawo chidzakhala chilango chowawa

    Verse 80

    Kaya iwe uwapemphera chikhululukiro kapena usawapemphere, ngakhale iwe utawapemphera chikhululukiro kokwana makumi asanu ndi awiri, Mulungu sadzawakhululukira chifukwa iwo sanakhulupilire mwa Mulungu ndi Mtumwi wake. Ndipo Mulungu satsogolera anthu ochita zoipa

    Verse 81

    Iwo amene adasiyidwa m’mbuyo adasangalala chifukwa cha kukhala kwawo pambuyo pa Mtumwi wa Mulungu, iwo amadana ndi kukamenya nkhondo ndi chuma chawo ndiponsoiwoeniyokhazikitsaulamulirowa Mulungundipo iwo adati, “Musapite ku nkhondo chifukwa kuli kutentha kwambiri.” Nena, “Moto wa ku Gahena ndi wotentha kwambiri,” iwo akadangozindikira

    Verse 82

    Motero iwo aseke pang’ono ndi kudzalira kwambiri ngati malipiro a ntchito zimene adachita

    Verse 83

    Ngati Mulungu akubweretserani gulu lina la iwo ndipo akapempha chilolezo kuti atuluke; nena, “Inusimudzatulukandiinekapenakukamenyankhondondi adani pamodzi ndi ine. Inu munasangalatsidwa kukhala ku nyumba kwanu pa nthawi yoyamba ndipo khalani pamodzi ndi anthu otsalira m’mbuyo.”

    Verse 84

    Iwe usampempherere aliyense wa iwo amene afa, ndipo usadzaime pa manda ake. Ndithudi iwo sanakhulupirire mwa Mulungu ndi Mtumwi wake ndipo adafa ali ochita zoipa

    Verse 85

    Ndipousalolekutichumandianaawokutizikudabwitse iwe. Cholinga cha Mulungu ndi kuwalanga iwo ndi izi m’moyo uno ndikuti mizimu yawo idzachoke ali anthu osakhulupirira

    Verse 86

    Ndipo pamene Mutu uvumbulutsidwa kuwauza kuti akhulupirire mwa Mulungu ndi kuti amenye nkhondo limodzi ndi Mtumwi, anthu olemera pakati pawo amakupempha kuti, asakamenye nawo ndipo amati: “Tisiye ife tikhale pamodzi ndi anthu okhala m’mbuyo.”

    Verse 87

    Iwo amasangalala kuti akhale limodzi ndi iwo amene adakhalira m’mbuyo! Mitima yawo ndi yomatidwa, motero iwo sazindikira

    Verse 88

    Koma Mtumwi ndi amene adakhulupirira pamodzi ndi iye, analimbikira ndipo adamenya nkhondo pogwiritsa ntchito chuma chawo pamodzi ndi iwo eni. Awa ndiwo amene wawasungira zinthu zabwino ndipo ndiwo amene adzakhale opambana

    Verse 89

    Awa ndiwo amene Mulungu wawakonzera minda yothiriridwa ndi mitsinje yoyenda pansi, mmene adzakhalemo mpaka kalekale. Kumeneku ndiko kupambana kwakukulu

    Verse 90

    Ndipo iwo amene adali ndi zifukwa kuchokera ku gulu la anthu a mchipululu adabwera, kuti apatsidwe chilolezo choti asakamenye nkhondo ndipo iwo amene adanama kwa Mulungu ndi kwa Mtumwi wake adakhala kumudzi. Chilango chowawa chidzadza pa iwo amene sakhulupirira

    Verse 91

    Palibe mlandu kwa anthu ofoka, odwala ndi iwo amene alibe chopereka, ngati ali ndi cholinga chabwino kwa Mulungu ndi Mtumwi wake. Anthu angwiro sadzaimbidwa mlandu ayi! Ndipo Mulungu amakhululukira ndipo ndi wachisoni chosatha

    Verse 92

    Ndipo palibe cholakwa kwa iwo amene adadza kwa iwe kuti uwapezere choti akwere ndipo iwe udati: “Sindingapeze choti ndikutengerenimo” ndipo iwo amabwerera kwawo m’maso mwawo muli misozi yodandaula kuti sadapeze zoti apereke

    Verse 93

    Mlandu uli ndi anthu olemera, omwe amapempha kuti asakamenye nawo nkhondo. Iwo amasangalala kukhalira limodzi ndi iwo amene atsalire m’mbuyo ndipo Mulungu waphimba mitima yawo kotero iwo sadziwa

    Verse 94

    Iwo adzapereka zodandaula zawo pamene mudza kwa iwo. Nena: “Inu musanene china chili chonse chifukwa ife sitidzakukhulupirirani. Mulungu watiuza kale nkhani zanu. Mulungu ndi Mtumwi wake adzayang’ana ntchito zanu zonse. Ndipo pomaliza inu mudzabwerera kwa Iye amene amadziwa zinthu zobisika ndi zooneka, ndipo Iye adzakuuzani zonse zimene munkachita.”

    Verse 95

    Iwo adzalumbira kwa inu M’dzina la Mulungu pamene mubwerera kwa iwo kuti muwasiye okha. Motero asiyeni okha chifukwa iwo ndi uve chifukwa cha ntchito zawo. Ndipo yawo ndi Gahena, omwe ndi malipiro antchito zimene ankachita

    Verse 96

    Iwo adzalumbira kwa inu pofuna kuti musangalale nawo. Koma ngati inu musangalala nawo ndithudi Mulungu sasangalalira anthu ochita zoipa

    Verse 97

    Maarabu amene amakhala m’chipululu ndiwo oipa kwambiri posakhulupirira ndi m’chinyengo, ndipo ndi oyenera kusadziwa malire amene Mulungu wavumbulutsa kwa Mtumwiwake. Ndipo Mulunguamadziwazinthuzonse ndipo ndi Wanzeru

    Verse 98

    Pakati pa Maarabu amene amakhala m’chipululu, alipo ena amene amaganiza kuti zonse zimene amapereka kuti ndi dipo lolipira mlandu ndipo amadikira kuti mupeze tsoka. Kwa iwo kukhale tsoka loipa! Ndipo Mulungu amamva zonse ndipo amadziwa chilichonse

    Verse 99

    Pakati pa Maarabu ena a m’chipululu pali amene amakhulupirira mwa Mulungu ndi tsiku lomaliza, ndipo amaona zopereka zawo m’njira ya Mulungu ngati zinthu zowabweretsa kufupi ndi Mulungu ndi mapemphero a Mtumwi. Ndithudi zimenezo zidzawabweretsa kufupi. Ndipo Mulungu adzawalowetsa iwo ku chisomo chake. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndi wachisoni chosatha

    Verse 100

    Ndipo iwo amene adalowa Chisilamu poyamba, kuchokera ku gulu limene lidachoka ku Makka ndi ku Medina, ndi ena amene anawatsatira. Mulungu ndi wosangalala kwambiri ndi iwo monga momwe iwo ali osangalalandi Iye. Iyewawakonzeramindayothiriridwandi madzi a mitsinje yoyenda pansi pake kumene adzakhalako mpaka kalekale. Kumeneku ndiko kupambana kwakukulu

    Verse 101

    Ndipo pakati pa Maarabu amene amakhala m’chipululu amene akuzungulira iwe, ena ndi anthu a chinyengo, chimodzi modzi anthu ena a ku Medina. Iwo amanena zabodza ndipo ndi a chinyengo. Iwe siuwadziwa koma Ife timawadziwa. Ife tidzawalanga kawiri ndipo pambuyo pake adzabwezedwa ku chilango chachikulu

    Verse 102

    Ena alipo amene avomera zoipa zawo, iwo asakaniza ntchito zawo zabwino ndi ntchito zawo zoipa. Mwina Mulungu adzawalandira kulapa kwawo. Ndithudi Mulungu ndi wokhululukira ndi Mwini chisoni chosatha

    Verse 103

    Landira chopereka chaulele kuchokera ku chuma chawo kuti uwayeretse nacho ndipo uwapempherere, ndithudi mapemphero ako adzawapatsa mpumulo ndipo Mulungu amamva zonse ndipo amadziwa zinthu zonse

    Verse 104

    Kodi iwo sadziwa kuti Mulungu amalandira kulapa kwa akapolo ake ndipo amavomera zopereka zawo ndipo kuti ndi Mulungu yekha amene amakhululukira ndi kuvomera kulapa, ndi Mwini chisoni chosatha

    Verse 105

    Nena, “Chitani monga momwe mufunira! Mulungu adzaona ntchito zanu ndi Mtumwi wake ndi anthu okhulupirira. Ndipo inu mudzabwezedwa kwa Iye amene amadziwa zobisika ndi zoonekera. Ndipo Iye adzakuuzani zonse zimene mumachita.”

    Verse 106

    Ndipo ena akudikira chilamulo cha Mulungu, kaya Iye adzawalanga kapena adzawakhululukira. Mulungu ndi wodziwa chili chonse ndi wanzeru zonse

    Verse 107

    Ndipo iwo amene anamanga Mzikiti ndi cholinga choyambitsachisokonezondikulimbikitsakusakhulupirira ndi kugawanitsa anthu okhulupirira, poyembekezera kwa amene adachita nkhondo ndi Mulungu ndi Mtumwi wake pambuyo pake, iwo adzalumbira kuti cholinga chawo chidali chabwino. Mulungu achitira umboni kuti iwo ndi onama

    Verse 108

    Usapemphere m’menemu. Ndithudi Mzikiti umene udamangidwa ndi cholinga chomuopa Mulungu kuchokera tsiku loyamba ndi woyenera kuti iwe upemphere mmenemo. Mmenemo muli anthu okonda kudziyeretsa. Ndipo Mulungu amakonda iwo amene amadziyeretsa

    Verse 109

    Kodi amene waika maziko a nyumba yake ndi cholinga choopa Mulungu ndikufuna chisangalalo chake ndi wabwino kapena iye amene waika maziko a nyumba yake m’mphepete mwadzenje limene likugumukira dothi lake kugwera pamodzi ndi nyumbayo kumoto wa ku Gahena? Mulungu satsogolera anthu ochita zoipa

    Verse 110

    Nyumba imene amanga siidzasiya kukhala yachinyengo ndi yokaikitsa m’mitima mpaka pamene mitima yawo idulidwa m’timagawomagawo. Ndipo Mulungu ndi wodziwa ndi wanzeru

    Verse 111

    Ndithudi Mulungu wagula miyoyo ya anthu okhulupilira ndi chuma cha pa mtengo wakuti chawo chidzakhale Paradiso. Iwo amamenya nkhondo munjira ya Mulungu kotero amapha ndi kuphedwa. Ili ndi lonjezo loonadi kwa Iye limene lidzakwaniritsidwa ndipo liri m’Buku la Chipangano chakale, Chipangano chatsopano ndi Korani. Kodi ndani amene amakwaniritsa lonjezo lake kuposa Mulungu? Iwo ali kusangalala ndi mgwirizano omwe mwachita. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu

    Verse 112

    Iwo amene amalapa zoipa zawo kwa Mulungu, iwo amene amapembedza, amayamika, amasala zilakolako zawo, amawerama, amagwada, amagwetsa mphumi zawo pansi, amalamulira zabwino, amaletsa zoipa ndi amene amasunga malire a Mulungu. Motero lalikira nkhani yabwino kwa anthu okhulupirira

    Verse 113

    Sizili zoyenera kwa Mtumwi ndi anthu okhulupirira kuwapemphera chikhululukiro anthu opembedza mafano ngakhale kuti iwo ndi a chibale awo pambuyo podziwika kwa iwo kuti iwo ndi anthu a kumoto

    Verse 114

    Sichinali cholinga cha Abrahamu kuwapempherera abambo wake koma chifukwa cha lonjezo limene iye adachita nawo. Koma pamene iye adazindikira kuti abambo wake adali mdani wa Mulungu, iye adawakana iwo. Ndithudi Abrahamu adali wodzichepetsa ndi munthu woleza mtima

    Verse 115

    Ndipo Mulungu sadzasocheretsa anthu amene wawatsogolera pokhapokha Iye wawafotokozera zonse zimene ayenera kuzipewa, Ndithudi Mulungu amadziwa chinthu china chilichonse

    Verse 116

    Ndithudi Mulungu! Ndiye Mwini Ufumuwa Kumwamba ndi dziko lapansi, Iye ndiye amene amapereka moyo ndi imfa. Ndipo kupatula Mulungu, inu mulibe wina amene angakutetezeni kapena kukuthandizani

    Verse 117

    Mulungu adakhululukira Mtumwi, anthu osamuka ndi anthu a ku Medina, amene adamtsatira iye pa nthawi ya mavuto, pamene ena adali pafupifupi kutaya mitima. Koma Iye adavomera kulapa kwawo. Ndithudi Iye, kwa iwo, ndi wachifundo ndi wachisoni chosatha

    Verse 118

    Iye adakhululukira anthu atatu amene adasiyidwa m’mbuyo, mpaka pamene kwa iwo dziko, ngakhale ndi lalikulu, linali lochepa ndipo mizimu yawo idapanikizika ndipo iwo adakhulupirira kuti kudalibe komuthawira Mulungu koma kupita kwa Iye. Motero Iye adavomera kulapa kwawo. Ndithudi Mulungu ndiye amene amavomera kulapa ndipo ndi wachisoni chosatha

    Verse 119

    oh inu anthu okhulupirira! Muopeni Mulungu ndipo khalani pamodzi ndi iwo amene amanena zoona

    Verse 120

    Sikunali koyenera kwa anthu a ku Medina ndi Maarabu a mchipululu a m’mbali mwawo kutsalira m’mbuyo mwa Mtumwi wa Mulungu kapena kukonda miyoyo yawo kuposa moyo wake. Icho ndi chifukwa chakuti iwo savutika ndi ludzu kapena kutopa kapena njala mu njira ya Mulungu kapena sachita chinthu chowanyasa anthu osakhulupirira kapena kubweretsa mavuto pa adani koma kudalembedwa kwa iwo kuti ndi ntchito yabwino. Ndithudi Mulungu saononga mphotho ya a anthu ochita zabwino

    Verse 121

    Ndipo iwo sapereka chopereka chochepa kapena chochuluka kapena kudutsa dambo lililonse koma kuti zidalembedwa ngati mphotho zabwino kwa iwo ndi kuti Mulungu adzawalipire zabwino zimene ankachita

    Verse 122

    Si chinthu chabwino kuti anthu onse okhulupirira apite ku nkhondo nthawi imodzi. Pa gulu lili lonse, kagulu kochepa kokha kayenera kupita kuti kakhoza kuphunzira ndipo kuti iwo amene atsalira akhoza kudzachenjeza anthu awo pamene adza kwa iwo kuti achenjere

    Verse 123

    oh inu anthu okhulupirira! Menyanani nawo anthu onse osakhulupilira amene ali pafupi ndi inu ndipo iwo apeze nkhanza kwa inu ndipo dziwani kuti Mulungu ali pamodzi ndi anthu olungama

    Verse 124

    Ndipo nthawi zonse pamene mutu uli kuvumbulutsidwa, ena a iwo amanena kuti: “Kodi ndani wa inu amene chikhulupiriro chake chaonjezeka chifukwa cha mutu uwu?” Akakhala iwo okhulupirira, uwaonjezere chikhulupiriro chawo ndipo amasangalala

    Verse 125

    Koma iwo amene m’mitima mwawo muli matenda, udzangoonjezela chikaiko pamwamba pa chikaiko chawo, ndipo iwo adzafa ali osakhulupirira

    Verse 126

    Kodi iwo saona kuti amayesedwa kamodzi kapena kawiri chaka chili chonse? Komabe iwo safuna kulapa kapena kuphunzira kuchokera kwa iwo

    Verse 127

    Nthawi zonse pamene mutu uvumbulutsidwa, iwo amayang’anitsitsana ndi kufunsa kuti: “Kodi akukuonani wina aliyense?” Akatero iwo amabwerera m’mbuyo. Mulungu watembenuza mitima yawo, chifukwa iwo ndi anthu osazindikira

    Verse 128

    Ndithudi kwadza kwa inu Mtumwi wochokera pakati panu. Zimamudandaulitsa kuti mupeze mavuto. Iye amafunitsitsa kuti inu mukhulupilire ndipo kwa anthu okhulupirira iye ndi wachifundo ndi wachisoni chosatha

    Verse 129

    Koma ngati iwo akana Nena, “Mulungu ndi wokwana kwa ine. Kulibe Mulungu wina koma Iye yekha. Mwa Iye ine ndaika chikhulupiliro changa ndipo Iye ndiye Ambuye wa Mpando wa Chifumu.”