Back to Languages
Chichewa - Chapter 93
Translation by Al Haji Yusuf Muhammad Kanyamula
Verse 1
Pali usana
Verse 2
Ndi pali usiku pamene ulipo
Verse 3
Ambuye wako sadakutaye iwe ndiponso sakudana nawe ayi
Verse 4
Ndipo, ndithudi, moyo umene uli nkudza ndi wabwino kwa iwe kuposa moyo uno
Verse 5
Ndithudi Ambuye wako adzakupatsa, ndipo iwe chidzakukondweretsa
Verse 6
Kodi sadakupeze iwe uli wa masiye ndipo adakupatsa malo okhala
Verse 7
Kodi sadakupeze uli wosochera ndipo Iye adakutsogolera
Verse 8
Kodi sadakupeze iwe waumphawi ndipo adakulemeretsa
Verse 9
Motero iwe usapondereze pansi mwana wa masiye
Verse 10
Ndipo usapirikitse munthu wopempha
Verse 11
Koma lengeza chisomo cha a Ambuye wako