Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 104 - Al-Humazah
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Humazah 104:1
“Kuonongeka koopsa kudzampeza aliyense wojeda ndi wonyoza anthu polozera (ndi maso kapena kuyankhula ndi lirime)
Verse 2 — Surah Al-Humazah 104:2
“Yemwe wasonkhanitsa chuma ndikumachiwerengera
Verse 3 — Surah Al-Humazah 104:3
“Akuganiza kuti chuma chakecho chimkhazika (pa dziko) nthawi yaitali (ndikumteteza ku zimene sakuzifuna)
Verse 4 — Surah Al-Humazah 104:4
“Sichoncho! (Asiye maganizo amenewo) ndithudi, akaponyedwa ku Moto woononga (chifukwa cha kuipa kwa zochita zake)
Verse 5 — Surah Al-Humazah 104:5
“Ndi chiyani chingakudziwitse za Moto woonongawu
Verse 6 — Surah Al-Humazah 104:6
“Umenewu ndi Moto wa Allah woyaka (nthawi zonse, woononga chilichonse choponyedwa mmenemo)
Verse 7 — Surah Al-Humazah 104:7
“Umene umakwera mpaka ku mtima
Verse 8 — Surah Al-Humazah 104:8
“Ndithu motowo ukawazinga (ndi kuwatsekera makomo)
Verse 9 — Surah Al-Humazah 104:9
“Munsanamira za zitalizitali (kotero kuti sakatha kugwedezeka mmenemo kapena kupulumuka)