“Ndi amene akukhulupirira zomwe zidavumbulutsidwa kwa iwe, ndi zomwe zidavumbulutsidwa kale iwe usadadze, nakhulupiriranso motsimikiza kuti lilipo tsiku lachimaliziro
“Iwowo (omwe ali ndi chikhalidwe chotere), ali pachiongoko chochokera kwa Mbuye wawo (Allah), ndipo iwowo ndi omwe ali opambana (pokapeza ulemelero wapamwamba ku Minda ya mtendere)
“Ndipo akakumana ndi amene akhulupirira, amanena: “Takhulupirira.” Koma akakhala pa okha ndi asatana awo, amati: “Ndithudi ife tili pamodzi nanu. Timangowachita chipongwe basi.”
“Choncho ngati simutha (kubweretsa sura imodzi yonga ya m’Qurani) ndiye kuti simudzatha. Choncho opani Moto omwe nkhuni zake ndi anthu ndi miyala umene wakonzedwera kwa osakhulupirira
“Ndithu Allah sachita manyazi kupereka fanizo la udzudzu ndi choposerapo (pa udzudzuwo). Koma amene akhulupirira akuzindikira kuti (fanizolo) ndiloona ndi lochokera kwa Mbuye wawo. Koma amene sadakhulupirire, akunena: “Kodi Allah akufunanji pa fanizo lotereli?” (Allah) amawalekelera ambiri kusokera ndi fanizo lotere, komanso amawaongola ambiri ndi fanizonso lotere. Komatu sawalekelera kusokera nalo kupatula okhawo opandukira chilamulo (Chake)
“Omwe akuswa chipangano cha Allah pambuyo pochimanga (kuti adzachikwaniritsa; ndi kutsatira malamulo a Allah), ndiponso amadula (chibale) chomwe Allah adalamula kuti chilumikizidwe, naononga pa dziko (poyambitsa nkhondo ndi ziwawa); iwo ndiamene ali otayika
“Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene Mudati: “E iwe Mûsa!; Sitingakukhulupirire iwe mpaka timuone Allah masomphenya.” Ndipo nkokomo wa moto udakugwirani uku inu mukuona
“Ndithu amene akhulupirira (aneneri akale), ndi Ayuda, ndi Akhirisitu ndi Asabayi*; aliyense wa iwo amene akhulupirire Allah (tsopano, monga momwe akunenera Mneneri Muhammad (s.a.w) nakhulupiriranso za tsiku lachimaliziro, uku akuchita ntchito zabwino, akalandira mphoto yawo kwa Mbuye wawo. Pa iwo sipadzakhala mantha, ndiponso sadzadandaula
“Koma pambuyo pazimenezo mudatembenuka ndikunyoza. Pakadapanda ubwino wa Allah ndi chifundo chake pa inu, mukadakhala mwa otayika (oonongeka pa dziko lapansi)
“Iwo adati: “Tipemphere kwa Mbuye wako kuti atifotokozere bwino za ng’ombeyo.” Iye adati: “Ndithudi Iye akunena kuti ng’ombeyo simkota kapena mthanthi, koma yapakatikati pa zimenezi. Tero chitani zimene mukulamulidwa.”
“Ndipo akakumana ndi amene akhulupirira, amanena: Takhulupirira (kuti uyu, Muhammad (s.a.w) ndi mneneri woona, ndipo watchulidwa m’mabuku athu).” Koma akakhala kwaokha kuseli, amati: “Mukuwauza iwo (Asilamu) zimene Allah anakufotokozerani (m’buku la Taurat) kuti adzakhale ndi mtsutso pa inu kwa Mbuye wanu? Kodi mulibe nzeru
“Chilango cha ukali chili pa amene akulemba buku ndi manja awo, kenako nanena: “Ili lachokera kwa Allah,” (akunena bodzalo) kuti apeze zinthu za mtengo wochepa (za m’dziko lapansi); choncho kuonongeka kuli pa iwo chifukwa cha zomwe manja awo alemba, ndiponso kuonongeka n’kwawo chifukwa cha zomwe akupeza
“Ndipo (akumbutse nkhani iyinso) pamene tidalandira pangano lamphamvu la ana a Israyeli kuti: Musapembedze aliyense koma Allah; ndipo muwachitire zabwino makolo anu ndi achibale anu, ndi amasiye, ndi masikini (osoŵedwa); ndipo nenani kwa anthu mwaubwino; ndipo pempherani Swala moyenera ndi kupereka Zakaat, kenako mudatembenuka monyozera kupatula ochepa mwa inu, ndipo inu ndinu onyozera
“Tsono inu nomwe ndi amene mukuphana ndikuwatulutsa ena a inu m’nyumba zawo; mukuthandiza adani anu powachitira (abale anu masautso) mwauchimo ndi molumpha malire. Koma akakudzerani akaidi ogwidwa ku nkhondo, mukuwaombola, pomwe nkoletsedwa kwa inu kuwatulutsa. Kodi mukukhulupirira mbali ina ya buku, mbali ina nkuikana? Choncho palibe mphoto kwa ochita izi mwa inu koma kuyaluka pamoyo wa pa dziko lapansi; ndipo tsiku la chiweruziro adzalowetsedwa ku chilango chokhwima kwambiri. Ndipo Allah sali wonyalanyaza zimene mukuchita
“Ndithudi Mûsa tidampatsa buku (la Taurat) ndipo tidatsatiza pambuyo pake atumiki (ena). Ndipo Isa (Yesu) mwana wa Mariya tidampatsa zizizwa zoonekera, ndi kumulimbikitsa ndi Mzimu Woyera (Gabrieli). Nthawi iliyonse akakudzerani mtumiki ndi chomwe mitima yanu siikonda, mumadzikweza. Ena mudawatsutsa ndipo ena mudawapha
“(Iwo) adati: “Mitima yathu yakutidwa, (potero tikulephera kumvetsa ulaliki wako, iwe Muhammad (s.a.w).’’ Iwo ngabodza pa zimene akunenazi. Koma Allah wawatembelera chifukwa cha kusakhulupirira kwawo). Tero n’zochepa zimene akuzikhulupirira
“Ndipo pamene buku lidawadzera (m’nyengo ya mtumiki Muhammad {s.a.w}) lochokera kwa Allah, loikira umboni zomwe zili pamodzi ndi iwo (adalikana), pomwe kale (lisadadze bukulo) adali kupempha chithandizo (kupyolera kwa mtumiki wolonjezedwa) chogonjetsera amene sadakhulupirire. Koma pamene chidawadzera chimene adachidziwa, (Qur’an) adachikana. Choncho matembelero a Allah ali pa osakhulupirira
“N’choipa zedi chimene asinthanitsira (chisangalalo cha tsiku lachimaliziro cha) mitima yawo pa kukana kwao zimene Allah adavumbulutsa, chifukwa cha njiru basi kuti Allah watsitsira chifundo chake amene wamfuna mwa akapolo Ake (amene sali Myuda). Potero adabwerera ndi mkwiyo wa Allah kuonjezera pa mkwiyo wakale. Ndipo osakhulupirira adzakhala ndi chilango chosambula
“Koma sadzailakalaka (imfa) ngakhale pang’ono, chifukwa cha zomwe manja awo adatsogoza (chifukwa cha machimo omwe adadzichitira). Ndipo Allah akudziwa bwino za anthu oipa
“Nena: “Amene akhale mdani wa Gaburieli (chifukwa chobweretsa chivumbulutso kwa Muhammad {s.a.w}, iyeyo ndi mdani wa Allah). Ndithudi, iye waivumbulutsa Qur’an mumtima mwako mwachilolezo cha Allah. Kudzatsimikidzira zomwe zidali patsogolo pake, ndiponso ndi chiongoko ndi nkhani yabwino kwa okhulupirira
“Ndipo pamene (Ayuda) adawadzera Mtumiki wochokera kwa Allah uku akutsimikidzira chomwe iwo ali nacho, gulu lina mwa omwe adapatsidwa buku adataya buku la Allah kumbuyo kwa misana yawo ngati kuti sakulidziwa
“Amene sadakhulupirire mwa anthu a mabuku (Ayuda ndi Akhirisitu) ndi omphatikiza Allah (Arabu), safuna kuti chabwino chilichonse chochokera kwa Mbuye wanu chitsitsidwe kwa inu (Asilamu). Koma Allah amamsankhira chifundo Chake amene wamfuna. Ndipo Allah ndi Mwini ubwino ochuluka
“Ayi, koma amene nkhope yake yagonjera kwa Allah uku akuchita zabwino (kwa anthu anzawo) iye ndi amene adzapeza mphoto yake kwa Mbuye wake. Ndipo pa iwo sipadzakhala mantha, ndiponso iwo sadzadandaula
“Ndipo (osakhulupirira) akumanena: “Allah wadzipangira mwana.” (Allah) wapatukana ndi zimenezo. Koma (zolengedwa) zonse za kumwamba ndi pansi Nzake. Zonse zikumumvera Iye
“Anthu omwe tidawapatsa buku naliwerenga kuwerenga koyenera (kopanda kusintha mawu ake ndi matanthauzo ake), iwo ndi amene akulikhulupirira (bukuli la Qur’an). Koma amene angalikane iwowa ndi omwe ali oonongeka
“Ndipo kumbukirani pamene Ibrahim Mbuye wake (Allah) adamuyesa iye mayeso ndi malamulo ambiri; ndipo iye adakwaniritsa. Adamuuza: “Ndithudi, Ine ndichita iwe kukhala mtsogoleri wa anthu.” (Ibrahim adayankha kuti): “Kodi ndi ana anga omwe?” Adati: “(Inde; koma) lonjezo langa silingawafike ochita zoipa.”
“Ndipo (kumbukirani nkhani iyi) pamene Ibrahim adanena: “E Mbuye wanga! Uchiteni mzinda uwu (wa Makka) kukhala wa chitetezo, ndipo zipatseni nzika zake zipatso, amene akukhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro mwa iwo. Allah adati: “Nayenso wosakhulupirira ndinkondweretsa pang’ono; kenako ndidzamkankhira ku chilango cha Moto. Taonani kunyansa malo obwerera
“Ndipo (kumbukiraninso) pamene Ibrahim ndi Ismail ankakhazikitsa maziko a nyumba (uku akupempha kwa Allah): “E Mbuye wathu! Tilandireni (ntchito yathuyi), ndithudi, Inu ndinu Akumva; Odziwa.”
“Kodi ndani anganyozere chipembedzo cha Ibrahim posakhala yemwe mtima wake uli wopusa? Ndithudi, tidamsankha (Ibrahim) pa dziko lapansi; ndipo iye tsiku lachimaliziro adzakhala m’modzi wa anthu abwino.”
“Ndipo Ibrahim adalangizanso ana ake za zimenezi, chonchonso Ya’qub (adalangizanso ana ake kuti): “E inu ana anga! Ndithudi, Allah wakusankhirani chipembedzo; choncho musafe pokhapokha muli Asilamu (ogonjera Mulungu).”
“Kapena inu (Ayuda ndi Akhrisitu) mudalipo pamene Ya’qub idamdzera imfa, pamene adati kwa ana ake: “Kodi pambuyo panga mudzapembedza yani?” Iwo adayankha nati: “Tidzapembedza Mulungu wako, Mulungu wa makolo ako; Ibrahim, Ismail ndi Ishâq; Mulungu mmodzi basi. Ndipo ife kwa Iye tili Asilamu (ogonjera).”
“Ndipo (Ayuda ndi Akhrisitu) adati (kwa Asilamu): “Khalani Ayuda kapena Akhrisitu mukhala oongoka.” Nena: “Koma (tikutsata) chipembedzo cha Ibrahim yemwe adaleka zipembedzo zopotoka, ndipo sadali mwa ophatikiza (Allah ndi mafano).”
“Nenani (inu Asilamu kuwauza Ayuda ndi Akhrisitu); “Takhulupirira Allah ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa ife, ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa Ibrahim, Ismail, Ishâq, Ya’qub ndi zidzukulu (zake) ndi zimene adapatsidwa Mûsa, Isa (Yesu), ndiponso zimene adapatsidwa aneneri (ena) kuchokera kwa Mbuye wawo. Sitilekanitsa pakati pa mmodzi wa iwo (koma onse tikuwakhulupirira). Ndipo ife kwa Iye tili Asilamu (ogonjera).”
“Nena (iwe Muhammad {s.a.w} kwa Ayuda ndi Akhrisitu): “Ha! Mukutsutsana nafe za Allah (ponena kuti bwanji wapereka uneneri kumbali ya ife), pomwe Iye ndi Mbuye wathu ndiponso Mbuye wanu? (Pamene mudali olungama adakupatsani uneneri, ndipo pamene mudakhota adakulandani natipatsa ife). Ife tili ndi zochita zathu; inunso muli ndi zochita zanu, ndipo ife tikudzipereka kwathunthu kwa Iye (Allah).”
“Choncho takusankhani (inu Asilamu) kukhala mpingo wabwino (wapakatikati) kuti mukhale mboni pa anthu ndi kuti Mtumiki (s.a.w) akhale mboni pa inu. Ndipo chibula (choyang’ana mbali ya ku Yerusalemu) chomwe udali nacho sitidachichite koma kuti timdziwitse (adziwike kwa anthu) amene akutsata Mtumiki (s.a.w), ndi yemwe akutembenukira m’mbuyo. Ndipo ndithudi, chidali chinthu chovuta kupatula kwa omwe Allah wawaongola. Ndipo nkosayenera kwa Allah kusokoneza Swala zanu, pakuti Allah Ngoleza kwabasi kwa anthu, Ngwachifundo chambiri
“Ndipo awo adapatsidwa buku ngakhale utabwera ndi chisonyezo cha mtundu uliwonse satsata chibula chako, ngakhalenso iwe sutsata chibula chawo. Ndipo ena a iwo sali otsatira chibula cha ena (Akhrisitu satsata chibula cha Ayuda, ndipo Ayuda satsata chibula cha Akhrisitu). Ngati utsatira zofuna zawo, pambuyo pakuti kwakudzera kudziwa ndiye kuti ukhala mwa ochita zoipa
“Aja amene tidawapatsa buku akumuzindikira (Mtumiki Muhammad {s.a.w}) monga momwe amawazindikilira ana awo. Koma ena mwa iwo akubisa choonadi uku akudziwa
“Ndipo ndithu tikuyesani ndi chinachake monga mantha, njala, kuchepa kwa chuma, kutaika kwa miyoyo ndi kuonongeka kwa mbeu. Tero auze nkhani yabwino opirira
“Ndithudi, m’kulenga kwa thambo ndi nthaka, ndi kusinthana kwa usiku ndi usana, ndi (kuyenda kwa) zombo zikulu-zikulu zomwe zikuyenda pa nyanja (zitasenza zinthu) zothandiza anthu, ndi madzi amene Allah wawatsitsa kuchokera ku mitambo, naukitsira nawo nthaka pambuyo pokhala youma, nawanditsa m’menemo mtundu uliwonse wa nyama (chifukwa cha madziwo), ndi m’kusinthanasinthana kwa mphepo, ndi mitambo yomwe yalamulidwa kuyenda pakati pa thambo ndi nthaka; ndithudi, (m’mzimenezo) muli zisonyezo kwa anthu anzeru, (kuti Allah alipo)
“Ndipo fanizo la amene sadakhulupirire (omwe akulalikidwa mawu a Allah, ndi makani awo) lili ngati (mbusa) yemwe akukuwira ziweto zake ndi kuzikalipira pomwe izo sizimva tanthauzo la mawu oitanawo, koma kuitana (chabe) ndi kufuula. (Iwo) ndi agonthi, abubu ndi akhungu. Tero iwo sangazindikire
“Zimenezo nchifukwa chakuti Allah adavumbulutsa buku Lake mwa choonadi (ndipo iwo adalikana). Koma amene asemphana pa zabukuli ali mu nkangano wonkera nawo kutali kusiya choonadi
“Ubwino suli potembenuzira nkhope zanu mbali yakuvuma ndi kuzambwe (popemphera Swala); koma ubwino weniweni ndi (wa omwe) akukhulupirira Allah, tsiku lachimaliziro, angelo, buku ndi aneneri; napereka chuma - uku eni akuchifunabe - kwa achibale ndi amasiye, ndi masikini ndi a paulendo (omwe alibe choyendera), ndi opempha, ndi kuombolera akapolo; napemphera Swala, napereka chopereka (Zakaat); ndi okwaniritsa malonjezo awo akalonjeza, ndi opirira ndi umphawi ndi matenda ndi panthawi yankhondo. Iwowo ndi amene atsimikiza (Chisilamu chawo). Ndiponso iwowo ndi omwe ali oopa Allah
“E inu amene mwakhulupirira! Kwalamulidwa kwa inu Qiswas (kubwezerana) molingana kwa ophedwa; mfulu kwa mfulu, kapolo kwa kapolo, mkazi kwa mkazi. Koma amene wakhululukidwa ndi m’bale wakeyo pa chinthu Chilichonse, atsatire ndi kulonjelera dipolo mwaubwino. (Nayenso wolipa) apereke kwa iye mwa ubwino. Kumeneko ndikufewetsa kumene kwachokera kwa Mbuye wanu, ndiponso chifundo. Ndipo amene alumphe malire pambuyo pa izi, iye adzapeza chilango chopweteka
“Kwalamulidwa kwa inu kuti mmodzi wanu imfa ikamuyandikira, ngati asiya chuma, apereke malangizo (pa zachumacho) kwa makolo ake awiri ndi achibale ake, mwa ubwino. Ichi nchilamulo kwa oopa Allah
“(Mwezi mwalamulidwa kusalawu ndi) mwezi wa Ramadan womwe mkati mwake Qur’an idavumbulutsidwa kuti ikhale chiongoko kwa anthu ndi zizindikiro zoonekera poyera za chiongoko. Ndikutinso ikhale cholekanitsa (pakati pa choonadi ndi bodza). Ndipo mwa inu amene akhalepo (pa mudzi) m’mweziwu, asale. Koma amene ali wodwala, kapena ali pa ulendo, akwaniritse chiwerengero m’masiku ena (cha masiku amene sadasale). Allah akukufunirani zopepuka ndipo samakufunirani zovuta, ndiponso (akufuna) kuti mukwaniritse chiwerengerocho ndi kumlemekeza Allah chifukwa chakuti wakutsogolerani, ndikutinso mukhale othokoza
“Ndipo musadye chuma chanu pakati panu mwachinyengo pochipereka kwa oweruza (m’njira ya ziphuphu) ndi cholinga choti mudye gawo la chuma cha anthu mwa uchimo uku inu mukudziwa
“Akukufunsa za miyezi nena: “Imeneyi ndi miyeso ya nthawi yozindikilira anthu zinthu zawo ndi nthawi ya Hajj.” Ndipo Siubwino kulowera m’nyumba zanu mbali ya kumbuyo kwake, koma ubwino ndiwayemwe akuopa Allah. Ndipo lowerani m’nyumba podzera m’makomo ake. Opani Allah kuti inu mupambane
“Ndipo menyanani nao nkhondo pa njira ya Allah (modziteteza) amene akukuthirani nkhondo. Koma musalumphe malire (powamenya amene sadakuputeni), ndithu Allah sakonda olumpha malire
“Ndipo perekani chuma chanu pa njira ya Allah, ndiponso musadziponye ku chionongeko ndi manja anu; chitani zabwino. Ndithudi, Allah amakonda ochita zabwino
“Ndipo alipo ena mwa iwo omwe akunena kuti: “E Mbuye wathu! tipatseni zabwino pa dziko lapansi komanso pa tsiku lachimaliziro mudzatipatsenso zabwino, ndi kutitchinjiriza ku chilango cha Moto.”
“Ndipo mtamandeni Allah m’masiku owerengeka. Koma amene wachita changu pa masiku awiri okha (nabwerera kwawo) palibe tchimo pa iye. Ndipo amene wachedwerapo palibenso tchimo pa iye kwa amene akuopa Allah. Choncho opani Allah, ndipo dziwani kuti kwa Iye nkumene mudzasonkhanitsidwa
“Ndipo mwa anthu alipo amene zoyankhula zake zikukondweretsa (iwe) pano pa dziko la pansi, (koma tsiku lachimaliziro kuipa kwake kudzadziwika). Ndipo iye akutsimikizira Allah kuti akhale mboni pa zomwe zili mu mtima mwake pomwe iye ndi wa makani kwambiri
“Ndipo akauzidwa kuti: “Opa Allah”, Akugwidwa ndi mwano womupititsa ku machimo, choncho Jahannam ikukwana kwa iye (kuwuchotsa mwano wakewo). Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo
“Kodi pali china chimene akuyembekeza posakhala kuwadzera Allah m’mithunzi ya mitambo ndi (kuwadzera) angelo; nkuweruzidwa chilamulo (chakuonongeka kwawo)? Komatu zinthu zonse zimabwezedwa kwa Allah
“Afunse ana a Israyeli kuti ndizizindikiro zingati zopenyeka zomwe tidawapatsa? Komatu amene angasinthe chisomo cha Allah pambuyo pomudzera, (Allah adzamulanga), ndithudi, Allah ngolanga mwaukali
“Moyo wa pa dziko lapansi wakometsedwa kwa amene sadakhulupirire, ndipo amawachitira chipongwe amene akhulupirira. Koma amene aopa Allah adzakhala pamwamba pawo tsiku la chiweruziro, ndipo Allah amapatsa amene wamfuna popanda chiwerengero
“Anthu onse adali a chipembedzo chimodzi (cha Chisilamu panthawi ya Adam kufikira Nuh kenako adayamba kupatukana), ndipo Allah adatumiza aneneri onena nkhani zabwino ndi ochenjeza; ndipo pamodzi nawo adavumbulutsa mabuku achoonadi kuti aweruzire pakati pa anthu pa zimene adasemphana. Ndipo sadasemphane pa zimenezo koma aja amene adapatsidwa mabukuwo pambuyo powadzera zizindikiro zoonekera poyera, chifukwa chakuchitirana dumbo pakati pawo. Koma Allah adawaongolera amene adakhulupirira kuchoonadi cha zomwe adasempaniranazo, mwachifuniro chake. Ndipo Allah amamutsogolera ku njira yolunjika amene wamfuna
“Akukufunsa kuti apereke chiyani? Nena: “Chuma chilichonse chimene mungachipereke, (chiperekeni) kwa makolo awiri, achibale, kwa ana amasiye, kwa osauka, ndi kwa apaulendo. Ndipo chabwino chilichonse chimene mungachite, ndithudi, Allah akuchidziwa. “
“Kwalamulidwa kwa inu kumenya nkhondo (yotetezera chipembedzo cha Allah ) pomwe iyo (nkhondoyo) njodedwa ndi inu. Komatu mwina mungachide chinthu pomwe icho chili chahwino kwa inu. Mwinanso mungakonde chinthu pomwe icho chili choipa kwa inu. Koma Allah ndiyemwe akudziwa, ndipo inu simudziwa
“Ndithudi, amene akhulupirira, ndi amene asamuka namenya nkhondo pa njira ya Allah, iwo ndi amene akuyembekezera chifundo cha Allah. Ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha
“Akukufunsa za mowa ndi njuga. Nena: “M’zimenezo muli (masautso ndi) uchimo waukulu, ndi zina zothandiza kwa anthu. Koma uchimo wake ngwaukulu zedi kuposa zothandiza zake.” Ndipo akukufunsa kuti aperekenji: Auze: “Chimene chapyolerapo (pa zofuna zanu).” Umo ndi momwe Allah akukufotokozerani ma Ayah (malamulo) kuti mulingalire
“Za m’dziko lapansi ndi (zinthu) za tsiku lachimaliziro. Ndipo akukufunsa za ana amasiye, nena: “Kuwachitira zabwino ndiwo ubwino; ngati mutasakanikirana nawo, (ndibwinonso). Iwo ndi abale anu; ndipo Allah akumdziwa woononga ndi wochita zabwino. Ndipo Allah akadafuna, akadakukhwimitsirani malamulo. Ndithudi, Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngwanzeru zakuya.”
“Ndipo musakwatire akazi opembedza mafano mpaka atakhulupirira. Ndithudi, mdzakazi wokhulupirira (Allah) ngwabwino kuposa mfulu ya chikazi yopembedza mafano, ngakhale itakukondweretsani. (Ndipo ana anu aakazi a Chisilamu) musawakwatitse kwa amuna osakhulupirira, mpaka akhulupirire. Ndipo kapolo wokhulupirira (Allah) ngwabwino kuposa mfulu yopembedza mafano, ngakhale ikukukondweretsani. Iwowo akuitanira ku Moto. Koma Allah akuitanira ku Munda wamtendere ndi ku chikhululuko mwa lamulo lake. Ndipo Iye akulongosola mwatsatanetsatane ndime za mawu ake kwa anthu, kuti athe kukumbukira
“Ndipo kulumbilira kwanu dzina la Allah musakuchite kukhala chokuletsani kuchita zinthu zabwino (za m’Chisilamu) ndi kuopa Allah, ndi kuyanjanitsa pakati pa anthu. Ndipo Allah Ngwakumva, Ngodziwa
“Allah sangakulangeni pa kulumbira kwanu kopanda pake, koma adzakulangani chifukwa cha malumbiro anu amene mitima yanu yatsimikiza mwa mphamvu. Ndipo Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngoleza
“Ndipo akazi osiidwa (asakwatiwe) ayembekezere mpaka kuyeretsedwa kutatu kukwanire. Ndipo nkosafunika kwa iwo kubisa chimene Allah walenga m’mimba zawo, ngati akukhulupiriradi Allah ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo amuna awo ali ndi udindo wowayenereza kuwabwerera m’nthawi imeneyi ngati akufuna kuchita chimvano. Nawonso azimayi ali ndi zofunika kuchitiridwa (ndi amuna awo) monga m’mene ziliri kwa azimayiwo kuchitira amuna awo mwachilamulo cha Shariya. Koma amuna ali ndi udindo okulirapo kuposa iwo. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngwanzeru zakuya
“Kodi ndani angamkongoze Allah ngongole yabwino (yochokera m’chuma chake powapatsa amphawi ndi kupereka pa njira ya Allah) kuti amuonjezere zoonjezera zambiri? Ndipo Allah ndi yemwe amafumbata ndi kutambasula, ndipo kwa Iye nkumene mudzabwezedwa
“Kodi sudamve nkhani ya akuluakulu a ana a Israyeli pambuyo pa Mûsa? Adanena kwa mneneri wawo: “Tidzozere mfumu kuti timenye nkhondo pa njira ya Allah.” Iye (mneneri wawoyo) adati: “Mwinatu simungamenye nkhondoyo ngati kutalamulidwa kwa inu. (Iwo) adati: “Nchotani kuti tisamenye nkhondo pa njira ya Allah pomwe tatulutsidwa m’nyumba zathu pamodzi ndi ana athu?” Koma pamene adalamulidwa kumenya nkhondoyo, adatembenuka, kupatula ochepa mwa iwo. Ndipo Allah akudziwa bwinobwino za anthu ochita zoipa
“Ndipo mneneri wawo adawauza (kuti): “Ndithu chizindikiro cha ufumu wake, ndikukudzerani bokosi lomwe mkati mwake muli mpumulo wa miyoyo yanu wochokera kwa Mbuye wanu, ndi zotsalira zomwe adazisiya anthu a Mûsa ndi anthu a Harun, atanyamula angelo. Ndithu m’zimenezo muli chisonyezo kwa inu (chosonyeza kuyenera kwa ufumu wake pa inu) ngati mulidi okhulupirira.”
“Choncho, Taluti pamene adapita ndi magulu (ake) a nkhondo, adati: “Allah akuyesani mayeso ndi mtsinje (womwe mukumane nawo panjira komwe mukupitako). Choncho amene akamwe mmenemo sali nane. Koma amene sakamwa adzakhala pamodzi nane kupatula amene watunga ndi dzanja lake (ndikumwa; iyeyo ndiye kuti sadalakwe). Koma (iwo) adamwa m’menemo kupatula ochepa mwa iwo. Choncho pamene adaoloka iye pamodzi ndi aja omwe adakhulupirira limodzi naye, (iwo) adati: “Lero sitingamuthe Jaluti ndi magulu ake a nkhondo.” Omwe adali ndi chitsimikizo chokumana ndi Allah adati: “Kodi ndimagulu angati ochepa amene adagonjetsa magulu ambiri mwa chilolezo cha Allah! Ndipo Allah Ali pamodzi ndi opirira
“Choncho, adawagonjetsa mwa chilolezo cha Allah. Ndipo Daud adapha Jaluti; ndipo Allah adampatsa ufumu ndi uneneri, namphunzitsanso zimene adafuna. Allah akadapanda kuwakankha anthu ena kupyolera mwa ena ndiye kuti dziko likadaonongeka. Koma Allah ndi mwini kuchita zabwino pa zolengedwa zonse
“۞ Amenewo ndi aneneri tidawapatsa ulemelero mosiyanitsa pakati pawo, ena kuposa ena. Mwa iwo alipo amene Allah adawalankhula; ndipo ena adawakwezera kwambiri maulemelero awo. Naye Isa (Yesu) mwana wa Mariya tidampatsa zisonyezo zooneka, ndi kumlimbikitsa ndi Mzimu Woyera (rnngelo Gabriel). Allah akadafuna skadamenyana amene adalipo pambuyo pawo, (pa atumikiwo) pambuyo powadzera zizindikiro zooneka, koma adasiyana. Choncho mwa iwo alipo amene adakhulupirira, ndipo ena mwa iwo sadakhulupirire. Ndipo Allah akadafuna, sakadamenyana; koma Allah amachita zimene akufuna
Allah palibe wopembedzedwa wina koma Iye, Wamoyo wamuyaya, Woimira ndi Woteteza chilichonse. Kusinza sikumgwira ngakhale tulo. Zonse za kumwamba ndi za pansi nza Iye. Kodi ndani angathe kuombola kwa Iye popanda chilolezo chake? Akudziwa za patsogolo ndi zomwe zili pambuyo pawo ndipo zolengedwazo sizidziwa chilichonse pa zomwe zili m’kudziwa Kwake kupatula chimene wafuna. Mpando wake wachifumu wakwanira kumwamba ndi pansi ndipo sizimamvuta kuzisunga zimenezo. Ndipo Iye (Yekha) Njemwe ali Wapamwambamwamba, Ngwamkulu kwabasi, (Ngolemekezeka kwambiri)
“Allah ndi Mtetezi wa amene akhulupirira, amawatulutsa kumdima ndikuwalowetsa mkuunika, koma amene sadakhulupirire, atetezi awo ndi asatana. Amawatulutsa m’kuunika ndi kuwalowetsa mu mdima; iwo ndi anthu a ku Moto. M’menemo adzakhalamo nthawi yaitali
“Kodi sudamve za yemwe adatsutsana ndi Ibrahim pa za Mbuye wake (Allah)? (Ankanyada) pachifukwa chakuti Allah adampatsa ufumu. Ibrahim adati: “Mbuye wanga ndi yemwe amapereka moyo ndi imfa.” Iye adati: “Inenso ndimapereka moyo ndi imfa.” Ibrahim Adati: “Ndithu Allah amatulutsa dzuwa ku vuma, choncho iwe ulitulutse ku zambwe.” Ndipo uja wosakhulupirira adangoti kakasi, (kusowa chonena). Ndipo Allah satsogolera anthu ochita zoipa
“(Anthu) amene akupereka chuma chawo pa njira ya Allah napanda kutsatiza pa zomwe aperekazo kukumba, ndiponso masautso, iwo ali ndi mphoto kwa Mbuye wawo ndipo pa iwo sipadzakhala mantha; ndiponso sadzadandaula
“Kodi mmodzi wa inu angakonde kukhala ndi munda wa mitengo ya kanjedza ndi mphesa womwe pansi pake mitsinje ikuyenda, iye mmenemo napeza dzinthu dzamitundumitundu, numpeza ukalamba uku ali ndi ana ofooka; ndipo kamvuluvulu wa moto naugwera (mundawo), nupseleratu (angazikonde zimenezi)? Umo ndimomwe Allah akukulongosolerani ma Ayah (ndime za mawu Ake) kuti muganizire
“Satana amakuopsezani ndi umphawi ndi kukulamulirani kuchita zoipa (monga umbombo), pomwe Allah akukulonjezani chikhululuko kuchokera kwa Iye ndi ubwino (waukulu ngati mupereka); ndipo Allah ali nazo zambiri, Ngodziwa
“Amene akupereka chuma chawo usiku ndi usana, mobisa ndi moonekera, ali ndi malipiro awo kwa Mbuye wawo; ndipo pa iwo sipadzakhala mantha, ndiponso sadzadandaula
“Amene akudya riba (chuma cha katapira) sadzauka (m’manda) koma monga momwe amaimira munthu okhudzidwa ndi ziwanda, mwamisala. (Ndipo) izi nchifukwa chakuti amanena: “Malonda ngolingana ndi katapira,” pomwe Allah waloleza malonda ndipo waletsa katapira. Ndipo amene wamufika ulaliki wochokera kwa Mbuye wake (woletsa katapira) nasiya, choncho chomwe chidapita nchake. Ndipo chiweruzo chake chili kwa Allah (akaona chochita naye). Koma amene abwerera (kuchita malonda a katapira), amenewo ndiwo anthu a ku Moto, mmenemo adzakhalamo nthawi yaitali
“Ngati simuchita (zimenezo), dziwani kuti mukulimbana ndi Allah ndi Mtumiki Wake. Ndipo ngati mulapa, maziko a chuma chanu ndi anu. Musapondereze, ndiponso musaponderezedwe