Back to Languages

Chichewa - Chapter 42 - Ash-Shura

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Ash-Shura 42:1

Verse 2 — Surah Ash-Shura 42:2

“‘Aîn-Sîn-Qâf

Verse 3 — Surah Ash-Shura 42:3

“Chomwecho akukuvumbulutsira iwe ndi atumiki amene adadza kale, Allah Ngopambana Wanzeru zakuya

Verse 4 — Surah Ash-Shura 42:4

“Zonse za kumwamba ndi pansi ndi za Iye Yekha. Ndipo Iye ndi Wotukuka, Wamkulu

Verse 5 — Surah Ash-Shura 42:5

“(Chifukwa chakukula Kwake ndi ulemelero Wake) mitambo ikuyandikira kuphwasuka pamwamba pa iyo. Ndipo angelo akulemekeza ndi kutamanda Mbuye wawo, ndi kuwapemphera chikhululuko amene ali pa dziko lapansi. Dziwani kuti ndithu Allah Yekha ndiye Wokhululuka kwabasi, Wachisoni chosatha

Verse 6 — Surah Ash-Shura 42:6

“Ndipo awo amene adzipangira athandizi (a mafano) kusiya Allah, Allah ndi Wolondera (zochita) zawo; ndipo iwe si muyang’anili wawo (wosunga zochita zawo)

Verse 7 — Surah Ash-Shura 42:7

“Chomwechonso (monga chilili chivumbulutso chapoyerachi) takuvumbulutsira Qur’an m’Chiarabu (popanda chikaiko) kuti uchenjeze (eni) manthu wa mizinda (Makka) ndi amene ali m’mbali mwake, ndikutinso uchenjeze (anthu) za tsiku la msonkhano, lopanda chikaiko. (Pa tsikulo anthu adzagawikana mmagulu awiri): gulu lina ku Jannah, ndipo gulu lina ku Moto

Verse 8 — Surah Ash-Shura 42:8

“Ndipo akadafuna Allah akadawachita iwo kukhala mpingo umodzi; koma amamulowetsa ku chifundo Chake amene wamfuna ndipo odzichitira okha chinyengo (pokana Allah) alibe mtetezi kapena mthandizi

Verse 9 — Surah Ash-Shura 42:9

“Kapena adzichitira athandizi ena kusiya Iye (Allah)? Pomwe Allah Yekha ndiye Mthandizi woona ndipo Iye amaukitsa akufa. Ndipo Iye ndi Wokhoza pa chilichonse

Verse 10 — Surah Ash-Shura 42:10

“Ndipo chilichonse chimene mwasiyana mmenemo (mchipembedzo: za kukhulupirira ndi kusakhulupirira) chiweruzo chake nkwa Allah; (bwererani ku Buku la Allah ndi Hadith za mtumiki Wake). Ndipo Ameneyo ndi Allah, Mbuye wanga; kwa Iye Yekha ndatsamira, ndipo kwa Iye Yekha (ndiko) ndikutembenukira

Verse 11 — Surah Ash-Shura 42:11

“(Iye ndi) Mlengi wa kumwamba ndi pansi. Adakupangirani akazi kuchokera mwa inu nomwe, ndipo nazo ziweto mitundu iwiri, (zazimuna ndi zazikazi. Choncho) akukuchulukitsani mmenemo (mchikonzero Chake chanzeru) palibe chilichonse chofanana ndi Iye. Iye ndi Wakumva zonse ndiponso Woona zonse

Verse 12 — Surah Ash-Shura 42:12

“Makiyi a kumwamba ndi pansi ndi Ake. Amamchulukitsira rizq amene wamfuna ndipo amamchepetsera amene wamfuna. Ndithu Iye Ngodziwa chilichonse (pochiika pamalo oyenera)

Verse 13 — Surah Ash-Shura 42:13

“Wakhazikitsa kwa inu chipembedzo chonga chomwe adam’langiza Nuh. Ndipo chimene takuvumbulutsira iwe ndi chimenenso tidavumbulutsira Ibrahim, Mûsa, ndi Isa (Yesu) kuti: Mulimbike chipembedzo (potsatira malamulo) ndikuti musalekane pa chipembedzo. Koma ndizovuta kwa opembedza mafano (kuvomera) zimene ukuwaitanira. Allah amadzisankhira amene wam’funa ndipo amamuongolera amene akutembenukira kwa Iye

Verse 14 — Surah Ash-Shura 42:14

“Ndipo sadagawikane (pa chipembedzo otsatira a aneneri oyamba) kufikira pamene kudawadzera kudziwa kwa choonadi, chifukwa chachidani ndi dumbo pakati pawo. Kukadapanda liwu lochokera kwa Mbuye wako pachiyambi (lowachedwetsera chilango) mpaka nthawi yoikidwa kukadaweruzidwa pakati pawo koma ndithu amene adalandira buku pambuyo pawo (makolo awo, ndipo ndikukumana ndi nthawi yako,) ali mchikaiko cholikaikira (buku lawo)

Verse 15 — Surah Ash-Shura 42:15

“(Chifukwa cha umodzi wa zipembedzo ndikuti pasakhale kugawikana pa chipembedzo) choncho aitanire (ku chipembedzo chimodzi); ndipo lungama (poitanapo) monga momwe walamulidwira. Ndipo usatsatire zofuna zawo. Ndipo nena: “Ndakhulupirira mmabuku onse omwe adawavumbulutsa Allah; ndipo ndalamulidwa kuchita chilungamo pakati panu. Allah ndiye Mbuye wathu ndiponso Mbuye wanu; ife tili ndi ntchito zathu (zomwe tidzalipidwa nazo); inunso muli ndi ntchito zanu (zomwe mudzalipidwa nazo). Palibe kukangana pakati pa ife ndi inu (chifukwa chakuonekera poyera choona). Allah adzatisonkhanitsa (kuti atiweruze); kwa Iye yekha ndiko kobwerera

Verse 16 — Surah Ash-Shura 42:16

“Ndipo amene akutsutsana ndi Allah pambuyo povomerezedwa (ndi anthu ambiri), mtsutso wawo ndiwachabe kwa Mbuye wawo; mkwiyo waukulu (wa Allah) uli pa iwo. Ndipo iwo adzakhala ndi chilango chokhwima

Verse 17 — Surah Ash-Shura 42:17

“Allah ndi Amene wavumbulutsa buku (la Qur’an ndi mabuku ena) moona ndi mwachilungamo. Nanga nchiyani chikudziwitse kuti mwina Qiyâma ili pafupi

Verse 18 — Surah Ash-Shura 42:18

“Akuifulumizitsa amene sakuikhulupirira; koma amene akhulupirira ali oopa za iyo, ndipo akudziwa kuti imeneyo ndiyoonadi, (za kupezeka kwake palibe chikaiko). Dziwani kuti ndithu amene akutsutsana za nthawi (ya Qiyâma) ali mkusokera konka nako kutali

Verse 19 — Surah Ash-Shura 42:19

“Allah Ngoleza kwa akapolo (Ake). Amapereka rizq kwa amene wamfuna. Ndipo Iye ndi Wamphamvu zoposa, Wopambana

Verse 20 — Surah Ash-Shura 42:20

“Amene akufuna (pantchito yake) zokolola za tsiku lachimaliziro, timuonjezera zokolola zakezo; ndipo amene akufuna pa ntchito yake yabwino zokolola za chisangalalo cha m’dziko lapansi timpatsa chimene chidagawidwa kwa iye, ndipo iye sadzakhala ndi gawo (la zabwino) pa tsiku lachimaliziro

Verse 21 — Surah Ash-Shura 42:21

“Kodi iwo alinayo milungu imene idawakhazikitsira m’zipembedzo zimene Allah sadaziloleze? Ndipo pakadapanda kutsogola (lonjezo lochedwetsa) liwu la chiweruziro (mpaka pa tsiku la Qiyâma); pakadaweruzidwa pakati pawo (okanira ndi okhulupirira pompano pa dziko lapansi). Ndipo ndithu opondereza chawo nchilango chowawa

Verse 22 — Surah Ash-Shura 42:22

“Udzawaona (tsiku la Qiyâma) amene adadzichitira okha zoipa (popembedza mafano) akuopa chifukwa cha (zoipa) zomwe adachita, ndipo (chilangocho) chidzawapezabe. Koma amene adakhulupirira ndi kuchita zabwino (udzawaona akusangalala) m’Madimba abwino a ku Minda ya mtendere. Iwo akapeza chilichonse chimene akafune kwa Mbuye wawo. Umenewo ndiwo ulemelero wawukulu

Verse 23 — Surah Ash-Shura 42:23

“Umenewu ndi (ulemelero) umene Allah akuwasangalatsira akapolo Ake nkhani yabwino; amene akhulupirira ndi kuchita zabwino. Nena (iwe Mtumiki {s.a.w} kwa iwo): “Sindikupemphani malipiro (kapena chuma) pofikitsa uthenga (kwa inu), koma kuti musunge chikondi pachibale chimene chili pakati pathu. (Musandizunze kufikira ndifikitse kwa inu uthenga wa Mbuye wanga.)” Amene achita chabwino timuonjezera pachabwinocho ndithu Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngolandira kuthokoza

Verse 24 — Surah Ash-Shura 42:24

“Kapena akunena kuti: “Wampekera Allah bodza?”Allah akadafuna akadadinda mu mtima mwako (kuti usathe kunena chilichonse; koma kuti chilichonse chimene ukunena chikuchokera kwa Iye). Ndipo Allah amachotsa chabodza (shirik), ndi kuchilimbikitsa choona (Chisilamu), ndi mau Ake (amene adawavumbulutsa kwa Mneneri Wake). Ndithu Iye Ngodziwa (zobisika) za mmitima

Verse 25 — Surah Ash-Shura 42:25

“Ndipo Iye (Yekha) ndi amene amalandira kulapa (kuchokera) kwa akapolo Ake. Ndipo amakhululuka machimo (awo); komanso akudziwa zimene mukuchita

Verse 26 — Surah Ash-Shura 42:26

“Ndipo Iye (Allah) akuwayankha amene akhulupirira ndi kuchita zabwino; ndi kuwaonjezera ubwino Wake. Ndipo okana, chilango chaukali chili pa iwo

Verse 27 — Surah Ash-Shura 42:27

“Allah akadachulukitsa rizq (chuma) kwa akapolo Ake onse (monga anthuwo akufunira), akadapyola malire poononga pa dziko; koma (Allah) akutsitsa (chumacho) mwamuyeso monga momwe Iye afunira. Ndithu Iye pa za akapolo Ake Ngodziwa, Ngopenya

Verse 28 — Surah Ash-Shura 42:28

“Ndipo Iye yekha ndi amene akutsitsa mvula (pambuyo poti anthu)atataya mtima (pa zamvulayo); ndipo amafalitsa madalitso Ake ndipo ndi Mthandizi Wotamandidwa

Verse 29 — Surah Ash-Shura 42:29

“Ndipo zina mwa zisonyezo zake ndi kulenga kwa thambo ndi nthaka, ndi zamoyo zimene wazifalitsa mmenemo (zooneka ndi zosaoneka). Ndipo Iye ndi Wamphamvu zowasonkhanitsira (anthu kuchokera ku imfa) akadzafuna

Verse 30 — Surah Ash-Shura 42:30

“Ndipo mavuto amtundu uliwonse amene akukupezani nchifukwa cha (zochita zoipa) zimene achita manja anu, koma (Allah) akukhululuka zambiri

Verse 31 — Surah Ash-Shura 42:31

“Ndipo simungathe kum’lepheretsa (Allah kukutsitsirani mavuto) padziko lapansi (ngati mutachimwa); ndipo inu mulibenso mthandizi kapena mpulumutsi kupatula Allah

Verse 32 — Surah Ash-Shura 42:32

“Ndipo zina mwa zisonyezo Zake ndi zombo zoyenda panyanja zonga mapiri ataliatali (koma osabira)

Verse 33 — Surah Ash-Shura 42:33

“Atafuna akhoza kuiyimitsa mphepo choncho nkungokhala duu, (osayenda) pamwamba pake (panyanja). Ndithu mzimenezi muli zisonyezo kwa aliyense wopirira ndi wothokoza

Verse 34 — Surah Ash-Shura 42:34

“Kapena akhoza kuziononga (potumiza mphepo yamkuntho) chifukwa cha machimo amene adawachita. Koma amakhululuka zambiri

Verse 35 — Surah Ash-Shura 42:35

“Ndipo adzadziwa (tsiku la Qiyâma) amene akutsutsana ndi zisonyezo Zathu kuti alibe pothawira (kuchilango cha Allah)

Verse 36 — Surah Ash-Shura 42:36

“Ndipo chilichonse chimene mwapatsidwa, nzosangalatsa za moyo wa pa dziko. Koma zimene zili kwa Allah ndi zabwino ndiponso zamuyaya za amene akhulupirira ndi kutsamira kwa Mbuye wawo

Verse 37 — Surah Ash-Shura 42:37

“Ndipo amene akupewa machimo akuluakulu omwe Allah waletsa ndi machimo onse oipitsitsa; ndipo iwo akakwiya (chifukwa choputidwa) iwo amakhululuka

Verse 38 — Surah Ash-Shura 42:38

“Ndipo amene adayankha kuitana kwa Mbuye wawo ndi kusunga mapemphero (popemphera mnthawi yake mkapempheredwe koyenera); ndipo zinthu zawo zonse zimakhala zokambirana pakati pawo; ndipo mzimene tawapatsa amapereka (pa njira ya Allah)

Verse 39 — Surah Ash-Shura 42:39

“Ndi amene amati akachitiridwa mtopola amadzipulumutsa

Verse 40 — Surah Ash-Shura 42:40

“Malipiro a choipa ndi choipa chonga icho; (wochita choipa alipidwe choipa chonga chimene wachita). Koma amene wakhululukira wochita choipa (pomwe akhoza kubwezera), ndi kuyanjana naye (mdani wakeyo), malipiro ake ali kwa Allah; ndithu Allah sakonda ochitira anzawo mtopola

Verse 41 — Surah Ash-Shura 42:41

“Koma amene abwezera pambuyo pakuchitiridwa mtopola, kwa iwo palibe njira yowadzudzulira

Verse 42 — Surah Ash-Shura 42:42

“Ndithu njira yodzudzulidwira ili kwa amene akupondereza anthu ndi kuchita mtopola pa dziko popanda chifukwa choyenera. Iwowo ndi amene adzalandira chilango chowawa

Verse 43 — Surah Ash-Shura 42:43

“Ndipo amene akupirira ndi kukhululuka, (Allah adzamlipira mphoto yaikulu); ndithu kupirirako ndi chimodzi mwa zinthu zazikulu (chofunika kudzilimbikitsa nacho Msilamu pa chikhalidwe chake)

Verse 44 — Surah Ash-Shura 42:44

“Ndipo amene Allah wamsiya kuti asokere, alibe mthandizi (wina) kupatula Iye (Allah). ndipo udzawaona osalungama pamene adzachiona (masomphenya) chilango, adzanena (modandaula): “Kodi pali njira yobwerera (padziko lapansi kuti tikachite zabwino tidzalowe ku Jannah)?”

Verse 45 — Surah Ash-Shura 42:45

“Udzawaona (osalungama) akusonyezedwa ku Moto ali okhumata chifukwa chakunyozeka uku akuyang’ana (Moto) mkayang’anidwe kobisa (kotsinzina). Ndipo amene adakhulupirira adzanena pa tsiku la Qiyâma: “Ndithu otaika ndi amene adadzitaya okha pamodzi ndi maanja awo.” Dziwani kuti osalungama adzakhala mchilango chamuyaya

Verse 46 — Surah Ash-Shura 42:46

“Ndipo sadzakhala ndi athangati owapulumutsa (kuchilango cha Moto) kupatula Allah. Ndipo amene Allah wamusiya kuti asokere (chifukwa cha zochita zake zoipa) sangapeze njira (yopezera kulungama)

Verse 47 — Surah Ash-Shura 42:47

“Muyankheni Mbuye wanu lisadadze tsiku losapeweka lochokera kwa Allah; tsiku limenelo simudzapeza pothawira, ndipo simudzakhala ndi njira (yokanira zimene mudzachitidwa)

Verse 48 — Surah Ash-Shura 42:48

“Ngati anyalanyaza (Allah awalanga) sitidakutume kwa iwo kukhala muyang’aniri. Udindo wako ndikufalitsa uthenga. Ndipo ndithu tikamulawitsa munthu mtendere wochokera kwa Ife, akuunyadira (modzikweza), koma choipa chikawapeza kupyolera mzoipa zimene manja awo adatsogoza, pompo munthuyo sathokoza (Allah)

Verse 49 — Surah Ash-Shura 42:49

“Ufumu wakumwamba ndi pa dziko lapansi ngwa Allah; amalenga zimene wafuna; amene wam’funa amampatsa ana achikazi (okhaokha) ndiponso amene wamfuna amampatsa ana achimuna (okhaokha)

Verse 50 — Surah Ash-Shura 42:50

“Kapena kuphatikiza (ana) achimuna ndi achikazi, ndipo amene wam’funa amamchita kukhala chumba. Ndithu Iye Ngodziwa, Wokhoza (chilichonse)

Verse 51 — Surah Ash-Shura 42:51

“Nkosayenera kwa munthu kuti Allah alankhule naye koma kupyolera mkumzindikiritsa, kapena kuchokera kuseri kwa chotsekereza, kapena pomtuma mtumiki (Jiburil) kuti amvumbulutsire zimene Iye akufuna mwa chilolezo Chake. Ndithu Iye Ngwapamwamba, Ngwanzeru zakuya

Verse 52 — Surah Ash-Shura 42:52

“Momwemonso takuvumbulutsira chivumbulutso (Chathu) mwa lamulo Lathu. Siudali kudziwa kuti buku ndi chiyani, chikhulupiliro ndi chiyani; koma bukuli (Qur’an) talichita kukhala kuunika; ndi kuunikaku tikumuongola amene tam’funa mwa akapolo Athu. Ndithu iwe ukuongolera kunjira yoongoka

Verse 53 — Surah Ash-Shura 42:53

“Njira ya Allah Amene zonse za kumwamba ndi za mdziko lapansi ndi Zake. Dziwani kuti zinthu zonse zimabwerera kwa Allah