“Ndipo awo amene adzipangira athandizi (a mafano) kusiya Allah, Allah ndi Wolondera (zochita) zawo; ndipo iwe si muyang’anili wawo (wosunga zochita zawo)
“Kapena adzichitira athandizi ena kusiya Iye (Allah)? Pomwe Allah Yekha ndiye Mthandizi woona ndipo Iye amaukitsa akufa. Ndipo Iye ndi Wokhoza pa chilichonse
“Ndipo chilichonse chimene mwasiyana mmenemo (mchipembedzo: za kukhulupirira ndi kusakhulupirira) chiweruzo chake nkwa Allah; (bwererani ku Buku la Allah ndi Hadith za mtumiki Wake). Ndipo Ameneyo ndi Allah, Mbuye wanga; kwa Iye Yekha ndatsamira, ndipo kwa Iye Yekha (ndiko) ndikutembenukira
“(Iye ndi) Mlengi wa kumwamba ndi pansi. Adakupangirani akazi kuchokera mwa inu nomwe, ndipo nazo ziweto mitundu iwiri, (zazimuna ndi zazikazi. Choncho) akukuchulukitsani mmenemo (mchikonzero Chake chanzeru) palibe chilichonse chofanana ndi Iye. Iye ndi Wakumva zonse ndiponso Woona zonse
“Wakhazikitsa kwa inu chipembedzo chonga chomwe adam’langiza Nuh. Ndipo chimene takuvumbulutsira iwe ndi chimenenso tidavumbulutsira Ibrahim, Mûsa, ndi Isa (Yesu) kuti: Mulimbike chipembedzo (potsatira malamulo) ndikuti musalekane pa chipembedzo. Koma ndizovuta kwa opembedza mafano (kuvomera) zimene ukuwaitanira. Allah amadzisankhira amene wam’funa ndipo amamuongolera amene akutembenukira kwa Iye
“Akuifulumizitsa amene sakuikhulupirira; koma amene akhulupirira ali oopa za iyo, ndipo akudziwa kuti imeneyo ndiyoonadi, (za kupezeka kwake palibe chikaiko). Dziwani kuti ndithu amene akutsutsana za nthawi (ya Qiyâma) ali mkusokera konka nako kutali
“Amene akufuna (pantchito yake) zokolola za tsiku lachimaliziro, timuonjezera zokolola zakezo; ndipo amene akufuna pa ntchito yake yabwino zokolola za chisangalalo cha m’dziko lapansi timpatsa chimene chidagawidwa kwa iye, ndipo iye sadzakhala ndi gawo (la zabwino) pa tsiku lachimaliziro
“Kapena akunena kuti: “Wampekera Allah bodza?”Allah akadafuna akadadinda mu mtima mwako (kuti usathe kunena chilichonse; koma kuti chilichonse chimene ukunena chikuchokera kwa Iye). Ndipo Allah amachotsa chabodza (shirik), ndi kuchilimbikitsa choona (Chisilamu), ndi mau Ake (amene adawavumbulutsa kwa Mneneri Wake). Ndithu Iye Ngodziwa (zobisika) za mmitima
“Allah akadachulukitsa rizq (chuma) kwa akapolo Ake onse (monga anthuwo akufunira), akadapyola malire poononga pa dziko; koma (Allah) akutsitsa (chumacho) mwamuyeso monga momwe Iye afunira. Ndithu Iye pa za akapolo Ake Ngodziwa, Ngopenya
“Ndipo zina mwa zisonyezo zake ndi kulenga kwa thambo ndi nthaka, ndi zamoyo zimene wazifalitsa mmenemo (zooneka ndi zosaoneka). Ndipo Iye ndi Wamphamvu zowasonkhanitsira (anthu kuchokera ku imfa) akadzafuna
“Ndipo chilichonse chimene mwapatsidwa, nzosangalatsa za moyo wa pa dziko. Koma zimene zili kwa Allah ndi zabwino ndiponso zamuyaya za amene akhulupirira ndi kutsamira kwa Mbuye wawo
“Ndithu njira yodzudzulidwira ili kwa amene akupondereza anthu ndi kuchita mtopola pa dziko popanda chifukwa choyenera. Iwowo ndi amene adzalandira chilango chowawa
“Ndipo amene akupirira ndi kukhululuka, (Allah adzamlipira mphoto yaikulu); ndithu kupirirako ndi chimodzi mwa zinthu zazikulu (chofunika kudzilimbikitsa nacho Msilamu pa chikhalidwe chake)
“Ndipo sadzakhala ndi athangati owapulumutsa (kuchilango cha Moto) kupatula Allah. Ndipo amene Allah wamusiya kuti asokere (chifukwa cha zochita zake zoipa) sangapeze njira (yopezera kulungama)
“Nkosayenera kwa munthu kuti Allah alankhule naye koma kupyolera mkumzindikiritsa, kapena kuchokera kuseri kwa chotsekereza, kapena pomtuma mtumiki (Jiburil) kuti amvumbulutsire zimene Iye akufuna mwa chilolezo Chake. Ndithu Iye Ngwapamwamba, Ngwanzeru zakuya
“Momwemonso takuvumbulutsira chivumbulutso (Chathu) mwa lamulo Lathu. Siudali kudziwa kuti buku ndi chiyani, chikhulupiliro ndi chiyani; koma bukuli (Qur’an) talichita kukhala kuunika; ndi kuunikaku tikumuongola amene tam’funa mwa akapolo Athu. Ndithu iwe ukuongolera kunjira yoongoka