“Sitidangolenga thambo ndi nthaka ndiponso zonse zapakati pa izo koma mwachoonadi ndi nyengo yoikidwa (yodziwika). Koma amene akana kukhulupirira (Allah) ngonyozera zimene achenjezedwa
“Kapena akunena kuti: “Waipeka (Qur’an)?” Nena: “Ngati ine ndaipeka, tero simungapeze chondithandizira nacho kwa Allah (ku chilango Chake). Iye ndiwodziwa kwambiri zimene mukuzijijirikira. Iye akukwana kukhala mboni pakati pa ine ndi inu ndipo Iye Ngokhululuka kwabasi, Wachisoni chosatha.”
“Nena: “Ine sindine woyamba pa aneneri, ndipo sindikudziwa zimene zidzachitike kwa ine ngakhale kwa inu. Sinditsatira koma zokhazo zimene zikuvumbulutsidwa kwa ine; ndipo ine sindili kanthu koma mchenjezi wolongosola (zofunika).”
“Ndipo lisadadze ili lidalipo buku la Mûsa monga mtsogoleri ndi chifundo. Ndipo buku ili likuikira umboni (za bukulo) m’chiyankhulo cha Chiarabu kuti liwachenjeze amene adzichitira okha chinyengo, ndi kuti likhale uthenga wabwino kwa ochita zabwino
“Iwowo ndiamene tikuwalandira zabwino zimene adachita ndipo tikuwakhululukira zolakwa zawo. Adzakhala m’gulu la anthu a ku Jannah. Ili ndi lonjezo loona lomwe adalonjezedwa
“Tsono (mwana woipa) amene akunena kwa makolo ake, (akamuitanira ku chikhulupiliro kuti): “Ndithu ndinu oipa (pa zimene mukundiitanirazi)! Mukundilonjeza kuti ndidzatulutsidwa mmanda ndili wamoyo, chikhalirecho mibadwo ndi mibadwo idapita kumanda ine kulibe (koma mpaka lero siidauke)?” Ndipo uku makolo ake akupempha Allah kuti ampulumutse ndi kumuongola ndi kunena kwa iye: “Tsoka kwa iwe khulupirira (Allah ndi kuuka ku imfa, ngati sutero waonongeka). Ndithu lonjezo la Allah ndiloona.” Koma iye nkumanena (kuti): “Mukunenazi sikanthu koma ndi nthano za anthu akale.”
“Iwowo ndiamene latsimikizika pa iwo liwu (la chilango) pamodzi ndi mibadwo ya ziwanda ndi anthu, imene idanka kale iwo kulibe; ndithu iwo adali otaika
“Ndipo kumbuka za m’bale wa Âdi, (mtumiki Hûd) pamene adachenjeza anthu ake kudziko la milu ya mchenga. Ndithu adaliponso achenjezi iye asadadze ndiponso iye atapita. (Iye adawauza anthu ake): “Musampembedze aliyense koma Allah; ndithu ine ndikukuoperani chilango cha tsiku lalikulu.”
“Adanena (Hûd): “Ndithu kudziwa (kwenikweni kwa zimenezo) kuli kwa Allah; ndipo ine ndikungofikitsa kwa inu zimene ndatumidwa koma ine ndikukuonani kuti inu ndinu anthu amene mukuchita (zinthu za) umbuli
“Ndipo ndithu tidawapatsa mphamvu (yochitira zinthu ndi kukhala ndi chuma chambiri ndi moyo wautali) zomwe sitidakupatseni inu (Aquraish) ndipo tidawapatsa makutu ndi maso ndi mitima, koma makutu awo ndi maso awo ndi mitima yawo sizidawapindulire chilichonse chifukwa chotsutsa Ayah za Allah; ndipo zidawazinga zomwe adali kuzichitira chipongwe
“Ngati wina samuvomera woitanira kwa Allah, sangamulepheretse (Allah) pa dziko (akafuna kumuchita kanthu), ndipo iye alibe atetezi ena kupatula Iye (Allah). Otere akusokera koonekera poyera.”
“Kodi iwo saona kuti Allah Amene adalenga thambo ndi nthaka, ndipo sadatope pozilenga, ndi Wakutha kuwaukitsa anthu ku irnfa? Inde, ndithu Iye Ngokhoza kuchita chilichonse