Back to Languages

Chichewa - Chapter 46 - Al-Ahqaf

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Ahqaf 46:1

Verse 2 — Surah Al-Ahqaf 46:2

“Chivumbulutso cha bukuli nchochokera kwa Allah Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya

Verse 3 — Surah Al-Ahqaf 46:3

“Sitidangolenga thambo ndi nthaka ndiponso zonse zapakati pa izo koma mwachoonadi ndi nyengo yoikidwa (yodziwika). Koma amene akana kukhulupirira (Allah) ngonyozera zimene achenjezedwa

Verse 4 — Surah Al-Ahqaf 46:4

“Nena: Tandiuzani amene mukuwapembedza ndi kumusiya Allah, ndisonyezeni chimene adalenga panthaka? Kapena ali ndi gawo la kuthangata polenga thambo? Ndibweretsereni buku limene lidadza kale, ili lisanadze, kapena zizindikiro zanzeru, ngati inu mukunena zoona

Verse 5 — Surah Al-Ahqaf 46:5

“Kodi ndindani amene ali osokera kwambiri kuposa amene akupembedza zina kusiya Allah zomwe sizingathe kumuyankha mpaka tsiku la chiweruziro ndipo izo (zimafano) sizikuzindikira za mapemphero awo

Verse 6 — Surah Al-Ahqaf 46:6

“Ndipo anthu onse akadzasonkhanitsidwa adzakhala adani awo ndikuwakanira mapemphero awo

Verse 7 — Surah Al-Ahqaf 46:7

“Ndipo pamene zikuwerengedwa kwa iwo Ayah Zathu zolongosola chilichonse (cha m’chipembedzo), amene sadakhulupirire amanena pa choonadi chikawadzera: “Awa ndi matsenga oonekera.”

Verse 8 — Surah Al-Ahqaf 46:8

“Kapena akunena kuti: “Waipeka (Qur’an)?” Nena: “Ngati ine ndaipeka, tero simungapeze chondithandizira nacho kwa Allah (ku chilango Chake). Iye ndiwodziwa kwambiri zimene mukuzijijirikira. Iye akukwana kukhala mboni pakati pa ine ndi inu ndipo Iye Ngokhululuka kwabasi, Wachisoni chosatha.”

Verse 9 — Surah Al-Ahqaf 46:9

“Nena: “Ine sindine woyamba pa aneneri, ndipo sindikudziwa zimene zidzachitike kwa ine ngakhale kwa inu. Sinditsatira koma zokhazo zimene zikuvumbulutsidwa kwa ine; ndipo ine sindili kanthu koma mchenjezi wolongosola (zofunika).”

Verse 10 — Surah Al-Ahqaf 46:10

“Nena: “Tandiuzani, ngati (buku ili) litachokera kwa Allah, ndipo inu nkulikana uku mboni yochokera mu ana a Israyeli itachitira umboni kuti idaliona longa limeneli, ndipo iyo nkulikhulupirira (bukuli) pomwe inu mwadzitukumula, ndithu Allah saongola anthu osalungama.”

Verse 11 — Surah Al-Ahqaf 46:11

“Ndipo amene sadakhulupirire adanena kwa amene adakhulupirira: “(Chipembedzo ichi) chikadakhala chabwino, awa sakadakhala otsogola ku chimenechi pa ife.” Ndipo chifukwa choti sadaongoke nalo (bukuli), akhala akunena: “Ili ndi bodza lakale.”

Verse 12 — Surah Al-Ahqaf 46:12

“Ndipo lisadadze ili lidalipo buku la Mûsa monga mtsogoleri ndi chifundo. Ndipo buku ili likuikira umboni (za bukulo) m’chiyankhulo cha Chiarabu kuti liwachenjeze amene adzichitira okha chinyengo, ndi kuti likhale uthenga wabwino kwa ochita zabwino

Verse 13 — Surah Al-Ahqaf 46:13

“Ndithu amene anena (kuti): “Mbuye wathu ndi Allah.” Kenako ndikulungama, sadzakhala ndi mantha (tsiku lakufa kwawo ngakhale pambuyo pake), ndiponso sadzadandaula

Verse 14 — Surah Al-Ahqaf 46:14

“Iwowo ndiwo anthu aku Jannah adzakhala kumeneko nthawi yaitali kukhala mphoto ya zimene amachita

Verse 15 — Surah Al-Ahqaf 46:15

“Ndipo tamulangiza munthu kuchitira zabwino makolo ake. Mayi wake adatenga pathupi pake mwamasautso; ndipo adam’bala mwamasautso. Kutenga pakati pake ndi kumsiitsa kuyamwa ndi miyezi makumi atatu. Kufikira atakula nsinkhu nkukwana zaka makumi anayi, (akakhala mwana wabwino) amanena: “E Mbuye wanga! Ndilimbikitseni kuthokoza mtendere Wanu umene mwandipatsa pamodzi ndi makolo anga, ndipo ndilimbitseni kuti ndizichita zabwino zimene (Inu) muziyanja ndipo ndikonzereni ndi kundilungamitsira ana anga. Ine ndatembenukira kwa Inu; ndiponso ine ndine m’modzi mwa ogonjera (Inu).”

Verse 16 — Surah Al-Ahqaf 46:16

“Iwowo ndiamene tikuwalandira zabwino zimene adachita ndipo tikuwakhululukira zolakwa zawo. Adzakhala m’gulu la anthu a ku Jannah. Ili ndi lonjezo loona lomwe adalonjezedwa

Verse 17 — Surah Al-Ahqaf 46:17

“Tsono (mwana woipa) amene akunena kwa makolo ake, (akamuitanira ku chikhulupiliro kuti): “Ndithu ndinu oipa (pa zimene mukundiitanirazi)! Mukundilonjeza kuti ndidzatulutsidwa mmanda ndili wamoyo, chikhalirecho mibadwo ndi mibadwo idapita kumanda ine kulibe (koma mpaka lero siidauke)?” Ndipo uku makolo ake akupempha Allah kuti ampulumutse ndi kumuongola ndi kunena kwa iye: “Tsoka kwa iwe khulupirira (Allah ndi kuuka ku imfa, ngati sutero waonongeka). Ndithu lonjezo la Allah ndiloona.” Koma iye nkumanena (kuti): “Mukunenazi sikanthu koma ndi nthano za anthu akale.”

Verse 18 — Surah Al-Ahqaf 46:18

“Iwowo ndiamene latsimikizika pa iwo liwu (la chilango) pamodzi ndi mibadwo ya ziwanda ndi anthu, imene idanka kale iwo kulibe; ndithu iwo adali otaika

Verse 19 — Surah Al-Ahqaf 46:19

“Ndipo aliyense wokhulupirira adzakhala ndi nyota molingana ndi zimene adachita, ndi kuti (Allah) awalipire zochita zawo ndipo iwo sadzaponderezedwa

Verse 20 — Surah Al-Ahqaf 46:20

“Ndipo (akumbutse za) tsiku limene adzaikidwa pafupi ndi moto amene sadakhulupirire (adzawauza kuti) “Mudaononga zabwino zanu mmoyo wa dziko lapansi, (choncho lero simuzipezanso), ndipo inu mudasangalala nazo zimenezo, choncho lero mupatsidwa chilango chokusambulani chifukwa cha kudzikweza kwanu pa dziko popanda choona, ndiponso chifukwa cha kulakwa kwanu.”

Verse 21 — Surah Al-Ahqaf 46:21

“Ndipo kumbuka za m’bale wa Âdi, (mtumiki Hûd) pamene adachenjeza anthu ake kudziko la milu ya mchenga. Ndithu adaliponso achenjezi iye asadadze ndiponso iye atapita. (Iye adawauza anthu ake): “Musampembedze aliyense koma Allah; ndithu ine ndikukuoperani chilango cha tsiku lalikulu.”

Verse 22 — Surah Al-Ahqaf 46:22

“Adanena: “Ha! Kodi watidzera kuti utipatule ku milungu yathu? Choncho tibweretsere zimene ukutilonjezazo ngati uli mwa onena zoona.”

Verse 23 — Surah Al-Ahqaf 46:23

“Adanena (Hûd): “Ndithu kudziwa (kwenikweni kwa zimenezo) kuli kwa Allah; ndipo ine ndikungofikitsa kwa inu zimene ndatumidwa koma ine ndikukuonani kuti inu ndinu anthu amene mukuchita (zinthu za) umbuli

Verse 24 — Surah Al-Ahqaf 46:24

“Kenako pamene adauona (mtambo) ukulunjika ku zigwa zawo, adanena: “(Mtambo) uwu ndi wotivumbwitsira mvula!” (Adauzidwa): “Iyayi, chimenechi ndichimene mudachifulumizitsa chija (kuti chidze mwachangu), mphepo (ya mkutho) yomwe mkati mwake muli chilango chowawa

Verse 25 — Surah Al-Ahqaf 46:25

“Yoononga chinthu chilichonse mwa lamulo la Mbuye wake!” Kenako adali osaonedwanso, kupatula nyumba zawo (ndizimene zidatsalira). Umo ndim’mene timawalipirira anthu oipa

Verse 26 — Surah Al-Ahqaf 46:26

“Ndipo ndithu tidawapatsa mphamvu (yochitira zinthu ndi kukhala ndi chuma chambiri ndi moyo wautali) zomwe sitidakupatseni inu (Aquraish) ndipo tidawapatsa makutu ndi maso ndi mitima, koma makutu awo ndi maso awo ndi mitima yawo sizidawapindulire chilichonse chifukwa chotsutsa Ayah za Allah; ndipo zidawazinga zomwe adali kuzichitira chipongwe

Verse 27 — Surah Al-Ahqaf 46:27

“Ndithu tidaiononga midzi imene yakuzungulirani; ndipo tidawafotokozera momveka Ayah Zathu kuti abwelere

Verse 28 — Surah Al-Ahqaf 46:28

“Chifukwa chiyani siidawapulumutse milungu imene adaipangayo kusiya Allah kuti iwayandikitse kwa Iye (Allah)? Koma idasoweka kwa iwo (pomwe iwo adali pamavuto ofuna kulandira chithandizo). Ndipo zimenezo ndizo zotsatira zabodza lawo ndi zomwe adali kupeka

Verse 29 — Surah Al-Ahqaf 46:29

“Ndipo (kumbuka iwe Mtumiki{s.a.w}) pamene tidakutumizira gulu la ziwanda (majini) kudzamvera Qur’an ndipo pamene izo zidafika pamalopo zidanena pakati pawo: “Khalani chete!” Pomwe kuwerenga (kwa Qur’an) kudatha, zidabwerera ku mtundu wawo kukawachenjeza (za chilango cha Allah)

Verse 30 — Surah Al-Ahqaf 46:30

“Zidanena: “E inu anzathu! Ife tamva (zowerengedwa) za m’buku (lolemekezeka) lomwe lavumbulutsidwa pambuyo pa Mûsa, loikira umboni zimene zidalitsogolera; likuongolera ku choona ndi kunjira yolunjika.”

Verse 31 — Surah Al-Ahqaf 46:31

““E inu anzathu! Muvomereni woitana wa Allah, ndipo mkhulupirireni; (Allah) akukhululukirani machimo anu ndi kukutetezani ku chilango chowawa

Verse 32 — Surah Al-Ahqaf 46:32

“Ngati wina samuvomera woitanira kwa Allah, sangamulepheretse (Allah) pa dziko (akafuna kumuchita kanthu), ndipo iye alibe atetezi ena kupatula Iye (Allah). Otere akusokera koonekera poyera.”

Verse 33 — Surah Al-Ahqaf 46:33

“Kodi iwo saona kuti Allah Amene adalenga thambo ndi nthaka, ndipo sadatope pozilenga, ndi Wakutha kuwaukitsa anthu ku irnfa? Inde, ndithu Iye Ngokhoza kuchita chilichonse

Verse 34 — Surah Al-Ahqaf 46:34

“Ndipo (akumbutse za) tsiku limene adzaperekedwa ku moto amene sadakhulupirire (uku akuuzidwa): “Kodi izi sizoona?” Adzanena: “Inde, pali Mbuye wathu!” (Allah) adzanena: “Choncho, lawani chilango chifukwa cha kukana kwanu (choonadi).”

Verse 35 — Surah Al-Ahqaf 46:35

“Choncho pirira (Mtumiki {s.a.w}) monga adapirira aneneri, eni mphamvu ndi kulimba pa chipembedzo, (monga Nuh. Ibrahimu, Mûsa ndi Isa (Yesu); ndipo usawachitire changu. Tsiku limene adzaziona zimene adalonjezedwa kudzakhala monga iwo sadakhalitse pa dziko koma ngati adakhala ola limodzi lokha lamasana. (Zomwe mukuuzidwazi) ndi ulaliki okwana. Palibe adzaonongedwe (ndi chilango cha Allah), kupatula anthu ochimwa (otuluka m’chilamulo cha Allah)