“Ndipo ampatsa rizq kuchokera momwe samayembekezeramo. Ndipo amene akutsamira kwa Allah (pa zinthu zake zonse), ndiye kuti Allah ali wokwana kwa iye (kumkonzera chilichonse), ndithu Allah Ngokwaniritsa cholinga Chake ndi chofuna Chake. Ndithu chinthu chilichonse Allah wachipatsa mlingo wake woyenera (ndipo sichingaupyole)
“Ndipo Edda ya amene asiya kudwala kumwezi mwa akazi anu chifukwa cha kukula, ngati mukukaika (nthawi ya Edda yawo), Edda yawo ndi miyezi itatu. Ndi omwe sadathe nsinkhu Edda yawo ndi momwemonso. Tsono akazi apakati nthawi yothera Edda yawo ndipomwe abereka. Ndipo amene aopa Allah amfewetsera zinthu zake (kuti zikhale zosavuta)
“Wopeza bwino apereke malinga ndi kupeza bwino kwake; ndipo amene wachepekedwa rizq lake, apereke (kangachepe) pa zomwe Allah wampatsa. Allah sakakamiza aliyense kupatula zomwe wampatsa. Allah apereka kupeza bwino pambuyo pa masautso
“Mtumiki (amene) akukuwerengerani ndime za Allah zolongosola (choonadi ndi chonama) kuti awatulutse mu mdima ndi kuwaika ku dangalira amene wakhulupirira ndi kumachita zabwino. Ndipo amene akhulupirira Allah ndi kumachita zabwino, adzamlowetsa m’minda momwe mitsinje ikuyenda pansi pake; akakhala m’menemo muyaya. Ndithu Allah wamkonzera rizq (dalitso) labwino (Jannah)