Back to Languages

Chichewa - Chapter 65 - At-Talaq

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah At-Talaq 65:1

“E iwe Mneneri (s.a.w) ngati mufuna kusudzula akazi ukwati, asudzuleni mnyengo yowerengera Edda yawo (kuwerengera Edda kumayambika mkazi akakhala ndi Twahara akachira matenda akumwezi), ndipo werengerani nyengo ya Edda. Ndipo muopeni Allah Mbuye wanu. Ndipo musawatulutse m’nyumba zawo ndiponso asatuluke kupatula akachita tchimo lalikulu loonekera (loyenera chilango, apo atha kutulutsidwa). Ndipo amenewa ndiwo malire a Allah (amene wawakhazikitsa kwa anthu Ake). Ndipo amene apyola malire a Allah wadzichitira yekha zoipa. Sukudziwa (cholinga cha malamulo amenewa) mwina Allah adzadzetsa chinthu pambuyo pake (chosonyeza kuyanjana)

Verse 2 — Surah At-Talaq 65:2

“Choncho pamene iwo (osiyidwawo) nyengo yawo (Edda) itayandikira kutha, abwelereni mwa ubwino kapena asiyeni mwaubwino (polekelera nyengoyo kuti ithe); ndipo (powabwerera) funani mboni ziwiri zolungama zochokera mwa inu (zimene zichitire umboni kuti inu mukubwererana) ndipo perekani umboni chifukwa choopa Allah. Zimenezo ndizo akulangizidwa nazo amene akhulupirira mwa Allah ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo amene akumuopa Allah (potsatira malamulo Ake), amkonzera njira yotulukira (m’mavuto)

Verse 3 — Surah At-Talaq 65:3

“Ndipo ampatsa rizq kuchokera momwe samayembekezeramo. Ndipo amene akutsamira kwa Allah (pa zinthu zake zonse), ndiye kuti Allah ali wokwana kwa iye (kumkonzera chilichonse), ndithu Allah Ngokwaniritsa cholinga Chake ndi chofuna Chake. Ndithu chinthu chilichonse Allah wachipatsa mlingo wake woyenera (ndipo sichingaupyole)

Verse 4 — Surah At-Talaq 65:4

“Ndipo Edda ya amene asiya kudwala kumwezi mwa akazi anu chifukwa cha kukula, ngati mukukaika (nthawi ya Edda yawo), Edda yawo ndi miyezi itatu. Ndi omwe sadathe nsinkhu Edda yawo ndi momwemonso. Tsono akazi apakati nthawi yothera Edda yawo ndipomwe abereka. Ndipo amene aopa Allah amfewetsera zinthu zake (kuti zikhale zosavuta)

Verse 5 — Surah At-Talaq 65:5

“Limenelo ndilamulo la Allah (lomwe) walikhazikitsa kwa inu. Ndipo amene aopa Allah (posunga malamulo ake), amam’fafanizira zoipa zake, ndiponso amamkulitsira malipiro ake

Verse 6 — Surah At-Talaq 65:6

“Akhazikeni (osiyidwawo) m’mene mukukhala inumo monga momwe kulili kupeza kwanu (ndi mphamvu zanu ngakhale kuti mwawasiya ukwati). Musawavute ndi cholinga chowapana (kuti athawe okha). Ngati ali ndi pakati, apatseni zonse zofunika pa moyo mpaka adzabereke. Ngati akukuyamwitsirani ana anu apatseni malipiro awo mokwanira; gwirizanani pakati panu mwa ubwino ndi mofatsa. Ngati wina apereka mavuto kwa mnzake (ndiye kuti mwanayo) adzamuyamwitsira (mkazi) wina

Verse 7 — Surah At-Talaq 65:7

“Wopeza bwino apereke malinga ndi kupeza bwino kwake; ndipo amene wachepekedwa rizq lake, apereke (kangachepe) pa zomwe Allah wampatsa. Allah sakakamiza aliyense kupatula zomwe wampatsa. Allah apereka kupeza bwino pambuyo pa masautso

Verse 8 — Surah At-Talaq 65:8

“Ndipo ndimidzi ingati yomwe idanyoza lamulo la Mbuye wawo ndi Atumiki Ake, ndipo tidawawerenga ndi chiwerengero chokhwima (posanthula zochita zawo zonse). Ndiponso tidawalanga ndi chilango chaukali

Verse 9 — Surah At-Talaq 65:9

“Choncho adalawa kuipa kwa zinthu zawo ndipo mapeto azinthu zawo adali kutayika (kuonongeka kwakukulu)

Verse 10 — Surah At-Talaq 65:10

“Allah wawakonzera iwo chilango chokhwima, choncho muopeni Allah, E inu eni nzeru, amene mwakhulupirira, ndithu Allah wavumbulutsa chikumbutso (cholemekezeka kwa inu)

Verse 11 — Surah At-Talaq 65:11

“Mtumiki (amene) akukuwerengerani ndime za Allah zolongosola (choonadi ndi chonama) kuti awatulutse mu mdima ndi kuwaika ku dangalira amene wakhulupirira ndi kumachita zabwino. Ndipo amene akhulupirira Allah ndi kumachita zabwino, adzamlowetsa m’minda momwe mitsinje ikuyenda pansi pake; akakhala m’menemo muyaya. Ndithu Allah wamkonzera rizq (dalitso) labwino (Jannah)

Verse 12 — Surah At-Talaq 65:12

“Allah ndiYemwe adalenga thambo zisanu ndi ziwiri, nthakanso chimodzimodzi. Malamulo Ake akutsika pakati pa izo kuti mudziwe kuti ndithu Allah pachilichonse ndi Wokhoza ndikutinso Allah wachizinga chilichonse m’kuchidziwa