Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 69 - Al-Haqqah
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Haqqah 69:1
“Chakudza cha choonadi (chomwe ndi Qiyâma)
Verse 2 — Surah Al-Haqqah 69:2
“Kodi chakudza cha choonadi nchiyani
Verse 3 — Surah Al-Haqqah 69:3
“Nanga nchiyani chikudziwitse za chakudza cha choonadicho
Verse 4 — Surah Al-Haqqah 69:4
“Asamudu ndi Âdi adatsutsa zakudza kwa Qiyâma (yomwe idzadzidzimutsa zolengedwa mwamphamvu ndi zoopsa zake)
Verse 5 — Surah Al-Haqqah 69:5
“Tsono Asamudu adaonongedwa ndi phokoso lopyola muyeso, (lamphamvu kwambiri)
Verse 6 — Surah Al-Haqqah 69:6
“Ndipo Âdi adaonongedwa ndi chimphepo cha mkuntho, chozizira, champhamvu kwambiri
Verse 7 — Surah Al-Haqqah 69:7
“Allah adachitumiza kwa iwo pa usiku usanu ndi uwiri ndi masana asanu ndi atatu mosadukiza; kotero ukadawaona ali lambalamba mmenemo ngati mathunthu a mitengo ya kanjedza yopanda kanthu m’kati mwake
Verse 8 — Surah Al-Haqqah 69:8
“Kodi nanga ukumuona wotsala mwa iwo
Verse 9 — Surah Al-Haqqah 69:9
“Ndipo Firiaun ndi amene adalipo iye asadabadwe, ndi khamu la anthu amidzi yotembenuzidwa (anthu a Luti) adadza ndi machimo (akulu)
Verse 10 — Surah Al-Haqqah 69:10
“Ndipo (yense wa iwowa) adanyoza Mtumiki wa Mbuye wawo; choncho adawalanga chilango chopitilira muyeso
Verse 11 — Surah Al-Haqqah 69:11
“Ndithu pamene madzi adasefukira mopyola muyeso (mpaka kumeza mapiri nthawi ya chigumula cha Nowa) Ife tidakukwezani mchombo choyandama ndi kuyenda
Verse 12 — Surah Al-Haqqah 69:12
“Kuti tichichite (chochitikacho chomwe okhulupirira adapulumuka nacho; osakhulupirira adaonongeka nacho) kukhala lingaliro ndi phunziro kwa inu, ndikuti lisunge (nkhaniyi) khutu losunga
Verse 13 — Surah Al-Haqqah 69:13
“Choncho likadzaimbidwa lipenga, kuimba kumodzi kokha (zamoyo zonse zidzafa)
Verse 14 — Surah Al-Haqqah 69:14
“Ndipo nthaka ndi mapiri nkuchotsedwa m’malo mwake ndi kuphwanyidwa kamodzi nkamodzi
Verse 15 — Surah Al-Haqqah 69:15
“Chomwecho tsiku limenelo, chochitika chidzachitika (imene ili Qiyâma)
Verse 16 — Surah Al-Haqqah 69:16
“Ndipo thambo lidzasweka choncho ilo tsiku limenelo lidzakhala lofooka (pamene lidali lolimba)
Verse 17 — Surah Al-Haqqah 69:17
“Ndipo angelo adzakhala m’mphepete mwake, ndipo pamwamba pawo tsiku limenero (angelo) asanu ndi atatu adzasenza Arsh (Mpando wachifumu) ya Mbuye wako
Verse 18 — Surah Al-Haqqah 69:18
“Tsiku limenelo mudzabweretsedwa ku chiweruzo; sichidzabisika chilichonse chobisika mwa inu
Verse 19 — Surah Al-Haqqah 69:19
“Tsono amene adzapatsidwa kaundula wake chakudzanja lakumanja kwake adzanena (mokondwa kwa amene ali m’phepete mwake): “Tengani! Werengani kaundula wanga!”
Verse 20 — Surah Al-Haqqah 69:20
““Ndithudi ine ndidatsimikiza (pa dziko lapansi) kuti ndidzakumana ndi chiwerengero changa.”
Verse 21 — Surah Al-Haqqah 69:21
“Choncho, iye adzakhala m’moyo wosangalatsa
Verse 22 — Surah Al-Haqqah 69:22
“M’munda wapamwamba
Verse 23 — Surah Al-Haqqah 69:23
“Zipatso zake zoyandikira pansi (zosavuta kuzithyola)
Verse 24 — Surah Al-Haqqah 69:24
“(Adzawauza kuti:) “Idyani, ndipo imwani mosangalala pa zimene mudatsogoza mmasiku aja adapita (a pa dziko lapansi).”
Verse 25 — Surah Al-Haqqah 69:25
“Ndipo amene adzapatsidwe kaundula wake kudzanja lake lamanzere, adzanena (modandaula): “Kalanga ine! Ndiponi ndikadapanda kupatsidwa kaundula wangayu!”
Verse 26 — Surah Al-Haqqah 69:26
““Nkusadziwa chiwerengero changa!”
Verse 27 — Surah Al-Haqqah 69:27
““Ha! imfa ija ikadandimaliziratu (ndi kundilekanitsa ine ndi zimenezi).”
Verse 28 — Surah Al-Haqqah 69:28
““Chuma changa sichidandithandize!”
Verse 29 — Surah Al-Haqqah 69:29
““Mphamvu zanga (ndi moyo wanga wathanzi) zandichokera!”
Verse 30 — Surah Al-Haqqah 69:30
“(Kudzanenedwa kwa angelo oyang’anira Jahena): Mgwireni ndipo mnjateni (pomphatikiza manja ndi khosi)
Verse 31 — Surah Al-Haqqah 69:31
“Kenako mponyeni ku Moto
Verse 32 — Surah Al-Haqqah 69:32
“Kenakonso mulowetseni mtcheni lotalika mikwamba makumi asanu ndi awiri
Verse 33 — Surah Al-Haqqah 69:33
“Ndithudi, iye sadali kukhulupirira mwa Allah wamkulu
Verse 34 — Surah Al-Haqqah 69:34
“Sadalinso kulimbikitsa zodyetsa osauka
Verse 35 — Surah Al-Haqqah 69:35
“Basi, lero kuno alibe bwenzi (lomthandiza)
Verse 36 — Surah Al-Haqqah 69:36
“Ngakhale chakudya kupatula mafinya (a anthu a ku Moto)
Verse 37 — Surah Al-Haqqah 69:37
“Zomwe palibe angazidye kupatula ochimwa (mwadala)
Verse 38 — Surah Al-Haqqah 69:38
“Choncho ndikulumbilira zimene mukuziona
Verse 39 — Surah Al-Haqqah 69:39
“Ndi zimene simukuziona
Verse 40 — Surah Al-Haqqah 69:40
“Ndithudi iyi (Qur’an) ndiliwu la mthenga wolemekezeka (Jibril)
Verse 41 — Surah Al-Haqqah 69:41
“Ndipo simawu a mlakatuli, ndi zochepa zimene mukuzikhulupirira
Verse 42 — Surah Al-Haqqah 69:42
“Ndiponso simawu a mlosi, ndizochepa zimene mmakumbukira
Verse 43 — Surah Al-Haqqah 69:43
“(Ichi ndi) chivumbulutso chochokera kwa Mbuye wa zolengedwa
Verse 44 — Surah Al-Haqqah 69:44
“Ndipo (Mneneri) akadatipekera bodza linalake
Verse 45 — Surah Al-Haqqah 69:45
“Tikadamgwira (mwamphamvu) ndimkono wamanja
Verse 46 — Surah Al-Haqqah 69:46
“Ndipo tikadadula mwa iye mtsempha wa moyo (kotero kuti ndikuferatu nthawi yomweyo)
Verse 47 — Surah Al-Haqqah 69:47
“Sipakadapezeka aliyense mwa inu womteteza (kuchilango Chathu)
Verse 48 — Surah Al-Haqqah 69:48
“Ndithu iyi (Qur’an) ndi phunziro labwino kwa owopa (Allah)
Verse 49 — Surah Al-Haqqah 69:49
“Ndithu Ife, tikudziwa kuti ena mwa inu ndiotsutsa (Qur’an)
Verse 50 — Surah Al-Haqqah 69:50
“Ndipo ndithu iyi (Qur’an) idzakhala chowadandaulitsa (chachikulu) osakhulupirira (pamene adzaona chilango chawo ndi mtendere wa okhulupirira)
Verse 51 — Surah Al-Haqqah 69:51
“Ndithu iyoyi ndichoonadi Chotsimikizika; (mulibe chikaiko)
Verse 52 — Surah Al-Haqqah 69:52
“Basi, lemekeza dzina la Mbuye wako Wamkulu (pitiriza kutamanda dzina Lake)