Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 82 - Al-Infitar
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Infitar 82:1
“Pamene thambo lidzasweke
Verse 2 — Surah Al-Infitar 82:2
“Ndi pamene nyenyezi zidzayoyoke (ndi kumwazikana)
Verse 3 — Surah Al-Infitar 82:3
“Pamenenso nyanja zikuluzikulu zidzaphwasulidwe
Verse 4 — Surah Al-Infitar 82:4
“Ndiponso pamene manda adzafukulidwe (ndikutuluka akufa omwe adali mmenemo)
Verse 5 — Surah Al-Infitar 82:5
“(Panthawiyo) mzimu uliwonse udzadziwa zimene udatsogoza (zabwino ndi zoipa) ndi zimene udasiya m’mbuyo
Verse 6 — Surah Al-Infitar 82:6
“E iwe munthu! Nchiani chakunyenga kumsiya Mbuye wako wa ufulu (kufikira pomnyoza)
Verse 7 — Surah Al-Infitar 82:7
“Amene adalenga iwe nakulinganiza (ziwalo zako) ndi kukulongosola (moyenera)
Verse 8 — Surah Al-Infitar 82:8
“Ndipo maonekedwe amtundu uliwonse omwe adawafuna adakuveka (popanda chifuniro chako)
Verse 9 — Surah Al-Infitar 82:9
“Ayi, sichoncho! Koma inu mukutsutsa za (tsiku) lamalipiro
Verse 10 — Surah Al-Infitar 82:10
“Ndithu pa inu alipo okuyang’ anirani
Verse 11 — Surah Al-Infitar 82:11
“Olemekezeka, olemba (zochita zanu)
Verse 12 — Surah Al-Infitar 82:12
“Akudziwa (zonse) zimene mukuchita (zabwino ndi zoipa)
Verse 13 — Surah Al-Infitar 82:13
“Ndithudi ochita zabwino adzakhala mu mtendere
Verse 14 — Surah Al-Infitar 82:14
“Ndipo ndithu amene ali olakwira malamulo a Allah adzakhala ku Moto wopsereza
Verse 15 — Surah Al-Infitar 82:15
“Adzaulowa tsiku la malipiro
Verse 16 — Surah Al-Infitar 82:16
“Ndipo iwo kumeneko sadzachokako
Verse 17 — Surah Al-Infitar 82:17
“Kodi nchiyani chingakudziwitse za tsiku la malipiro
Verse 18 — Surah Al-Infitar 82:18
“Ndipo nchiyani chingakudziwitse za tsiku lamalipiro
Verse 19 — Surah Al-Infitar 82:19
“Limeneli ndi tsiku limene mzimu uliwonse sudzakhala ndi mphamvu (yodzetsa mtendere kapena yochotsa chovuta) pa mzimu wina. Ndipo lamulo pa tsiku limeneli ndi la Allah yekha