Back to Languages

Chichewa - Chapter 87 - Al-Ala

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Ala 87:1

“Lemekeza dzina la Mbuye wako Wapamwambamwamba (ndikuliyeretsa ku zinthu zosayenera)

Verse 2 — Surah Al-Ala 87:2

“Amene adalenga (chilichonse) ndikuchikonza bwinobwino (mkalengedwe kolingana)

Verse 3 — Surah Al-Ala 87:3

“Amene adalamuliratu (chilichonse zochita zake) ndi kuchiongolera

Verse 4 — Surah Al-Ala 87:4

“Ndi Yemwenso akumeretsa msipu

Verse 5 — Surah Al-Ala 87:5

“Ndipo nausandutsa kukhala wouma ndi wodera

Verse 6 — Surah Al-Ala 87:6

“Tikulakatulira (chivumbulutso Chathu) ndipo siuyiwala

Verse 7 — Surah Al-Ala 87:7

“Kupatula chimene wafuna Allah (kuti uchiiwale); ndithu Iye amadziwa zoonekera ndi zimene zimabisika

Verse 8 — Surah Al-Ala 87:8

“Ndipo tikufewetsera (njira yochitira zinthu) zabwino

Verse 9 — Surah Al-Ala 87:9

“Choncho akumbutse (wanthu powalalikira) ngati kukumbutsa kuthandiza

Verse 10 — Surah Al-Ala 87:10

“(Palibe chikaiko ulalikiwo) aukumbukira (ndikuthandizidwa nawo) amene akuopa Allah

Verse 11 — Surah Al-Ala 87:11

“Ndipo wamavuto ambiri, (wamakani ndi wokanira), adzitalikitsa ndi ulalikiwo

Verse 12 — Surah Al-Ala 87:12

“Amene adzalowa ku moto waukulu (umene wakonzedwa kuti udzakhale malipiro ake)

Verse 13 — Surah Al-Ala 87:13

“Ndipo sakafa m’menemo (ndikupumula kumazunzo), ndiponso sakakhala ndi moyo (wamtendere)

Verse 14 — Surah Al-Ala 87:14

“Ndithu wapambana amene wadziyeretsa (ku machimo)

Verse 15 — Surah Al-Ala 87:15

“Ndikukumbukira dzina la Mbuye wake (ndi mtima wake, ndi lirime lake) uku akumapemphera

Verse 16 — Surah Al-Ala 87:16

“Koma inu mukukonda kwambiri moyo wa dziko lapansi

Verse 17 — Surah Al-Ala 87:17

“Pamene moyo wa tsiku lachimaliziro ndiwabwino kwambiri ndiponso wamuyaya

Verse 18 — Surah Al-Ala 87:18

“Ndithu izi (mukuuzidwa m’Qur’an) zilipo m’mabuku oyamba, akale

Verse 19 — Surah Al-Ala 87:19

“Mabuku a Ibrahim ndi Mûsa