Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 88 - Al-Ghashiyah
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Ghashiyah 88:1
“Kodi yakudzera, (iwe Mtumiki) (s.a.w) nkhani ya Qiyâma (imene idzaphimba anthu ndi zoopsa zake)
Verse 2 — Surah Al-Ghashiyah 88:2
“Nkhope zina tsiku limenelo, zidzakhala zonyozeka
Verse 3 — Surah Al-Ghashiyah 88:3
“Zogwira ntchito yotopetsa kwambiri
Verse 4 — Surah Al-Ghashiyah 88:4
“Zikalowa ku Moto wotentha kwambiri
Verse 5 — Surah Al-Ghashiyah 88:5
“Zikamwetsedwa mu kasupe wotentha kwabasi
Verse 6 — Surah Al-Ghashiyah 88:6
“Sadzakhala ndichakudya koma minga
Verse 7 — Surah Al-Ghashiyah 88:7
“Yosanenepetsa (thupi) ndiponso yosathetsa njala
Verse 8 — Surah Al-Ghashiyah 88:8
“Nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zosangalala
Verse 9 — Surah Al-Ghashiyah 88:9
“Zidzakondwera ndi malipiro a zochita zake (za pa dziko lapansi)
Verse 10 — Surah Al-Ghashiyah 88:10
“M’minda ya pamwamba (Jannah)
Verse 11 — Surah Al-Ghashiyah 88:11
“Sizikamva m’menemo mawu oipa, (otukwana ndi kulaula)
Verse 12 — Surah Al-Ghashiyah 88:12
“Mmenemo muli kasupe woyenda (mokongola)
Verse 13 — Surah Al-Ghashiyah 88:13
“Mmenemo muli makama a pamwamba
Verse 14 — Surah Al-Ghashiyah 88:14
“Ndi zikho zoikidwa bwino (pamaso pawo)
Verse 15 — Surah Al-Ghashiyah 88:15
“Ndi misamiro yoikidwa bwino m’mizeremizere
Verse 16 — Surah Al-Ghashiyah 88:16
“Ndi mphasa (zamtengo wapatali, carpet) zoyalidwa ponseponse
Verse 17 — Surah Al-Ghashiyah 88:17
“Kodi (akunyozera kulingalira zisonyezo za Allah), sakulingalira kungamira idalengedwa motani
Verse 18 — Surah Al-Ghashiyah 88:18
“Ndi thambo (limene akuliona nthawi zonse) m’mene lidatukulidwira (kutali popanda mzati)
Verse 19 — Surah Al-Ghashiyah 88:19
“Ndi mapiri momwe adakhazikitsidwira (molimba)
Verse 20 — Surah Al-Ghashiyah 88:20
“Ndi nthaka momwe idayalidwira
Verse 21 — Surah Al-Ghashiyah 88:21
“Basi, kumbutsa (anthu) ndithu iwe, ndiwe mkumbutsi
Verse 22 — Surah Al-Ghashiyah 88:22
“Sindiwe wokakamiza anthu (kuti akhulupirire)
Verse 23 — Surah Al-Ghashiyah 88:23
“Koma amene anyoza ndi kukanira (ulaliki wako)
Verse 24 — Surah Al-Ghashiyah 88:24
“Allah amulanga chilango chachikulu zedi
Verse 25 — Surah Al-Ghashiyah 88:25
“Ndithu kobwerera kwawo ndi kwa Ife basi
Verse 26 — Surah Al-Ghashiyah 88:26
“Ndipo ndithu kuwerengedwa kwawo kuli kwa Ife