Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 94 - Ash-Sharh
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Ash-Sharh 94:1
“Kodi sitidachiphanule chifuwa chako (pokupatsa chiongoko ndi chikhulupiliro ndi nzeru zambiri)
Verse 2 — Surah Ash-Sharh 94:2
“Ndipo takuchotsera mtolo wako (pa ntchito yolalikira pokuthandiza ndi kukufewetsera zinthu zako)
Verse 3 — Surah Ash-Sharh 94:3
“Mtolo umene udalemetsa msana wako
Verse 4 — Surah Ash-Sharh 94:4
“Ndipo takukweza kutchulidwa kwako
Verse 5 — Surah Ash-Sharh 94:5
“Ndipo ndithu pali chovuta palinso zabwino (Zambiri)
Verse 6 — Surah Ash-Sharh 94:6
“Ndithu pali chovuta palinso zabwino (zambiri)
Verse 7 — Surah Ash-Sharh 94:7
“Basi, ukamaliza ntchito (yolalikira ndi Jihâd) limbikira kupemphera
Verse 8 — Surah Ash-Sharh 94:8
“Ndipo khala wolakalaka (zabwino zomwe zili) kwa Mbuye wako