Back to Languages

Chichewa - Chapter 98 - Al-Bayyinah

Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink

Verse 1 — Surah Al-Bayyinah 98:1

“Amene adakanira (Allah ndi Mthenga Wake) mwa omwe adapatsidwa buku ndi opembedza mafano sadali olekana (ndi umbuli wawo ndi kusalabadira kwawo choona) mpaka pomwe chidawadzera chisonyezo choonekera poyera

Verse 2 — Surah Al-Bayyinah 98:2

“(Yemwe ndi) Mtumiki wochokera kwa Allah akuwawerengera makalata oyeretsedwa (ku zonama)

Verse 3 — Surah Al-Bayyinah 98:3

“Omwe mkati mwake muli malamulo oongoka (ofotokoza za choona)

Verse 4 — Surah Al-Bayyinah 98:4

“Sadalekane omwe adapatsidwa mabuku mpaka pomwe chidawafikira chisonyezo (chosonyeza kuti Muhammad (s.a.w) ndi mthenga wa Allah yemwe adalonjezedwa mmabuku awo

Verse 5 — Surah Al-Bayyinah 98:5

“Ndipo sadalamulidwe (china) koma kuti ampembedze Allah (Mmodzi yekha) ndikuyeretsa chipembedzo chake popendekera ku choona (ndi kusiya njira zonama) ndi kuti asunge Swala ndiponso apereke chopereka (cha pachuma chawo); chimenecho (ndicho) chipembedzo choongoka

Verse 6 — Surah Al-Bayyinah 98:6

“Ndithu amene sadakhulupirire (Mneneri) (s.a.w) pakati pa anthu a mabuku ndi opembedza mafano adzalowetsedwa ku Jahannam ndikukhala m’menemo nthawi yaitali; iwowo ndiwo zolengedwa zoipa

Verse 7 — Surah Al-Bayyinah 98:7

“Ndithu amene akhulupirira (mwa Allah ndi Mthenga Wake) ndikumachita zabwino, iwo ndiwo zolengedwa zabwino

Verse 8 — Surah Al-Bayyinah 98:8

“Malipiro awo kwa Mbuye wawo, ndi minda yamuyaya momwe ikuyenda pansi pake mitsinje; adzakhala m’menemo muyaya. Allah adzawayanja nawonso adzamuyanja (chifukwa cha zomwe adzawapatse); zimenezo ndi za yemwe awope Mbuye wake (Allah)